LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es24 masa. 108-118
  • November

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • November
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2024
  • Tumitu
  • Cisanu, November 1
  • Ciŵelu, November 2
  • Sondo, November 3
  • Mande, November 4
  • Ciŵili, November 5
  • Citatu, November 6
  • Cinayi, November 7
  • Cisanu, November 8
  • Ciŵelu, November 9
  • Sondo, November 10
  • Mande, November 11
  • Ciŵili, November 12
  • Citatu, November 13
  • Cinayi, November 14
  • Cisanu, November 15
  • Ciŵelu, November 16
  • Sondo, November 17
  • Mande, November 18
  • Ciŵili, November 19
  • Citatu, November 20
  • Cinayi, November 21
  • Cisanu, November 22
  • Ciŵelu, November 23
  • Sondo, November 24
  • Mande, November 25
  • Ciŵili, November 26
  • Citatu, November 27
  • Cinayi, November 28
  • Cisanu, November 29
  • Ciŵelu, November 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2024
es24 masa. 108-118

November

Cisanu, November 1

Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa.​—Aef. 4:29.

Pakamwa pa Mkhristu pasamatuluke mawu otukwana alionse. Ndiponso, pali makambidwe ena amene angamveke monga si acipongwe. Naonso tiyenela kuwapewa. Mwacitsanzo, tizipewa kuyelekezela cikhalidwe ca anthu ena, mtundu wawo, kapena dziko lawo. Cina, tiyenela kupewelatu kukhumudwitsa ena powakambila mawu olasa. Muzikamba mawu olimbikitsa. Khalani wofulumila kuyamikila ena, m’malo mosuliza kapena kudandaula. Aisiraeli anali na zifukwa zambili zokhalila oyamikila, koma mobweleza-bweleza anali kudandaula. Mzimu wodandaula umayambukila anthu ŵena. Kumbukilani kuti lipoti loipa limene azondi 10 anabweletsa, linapangitsa ‘ana onse a Isiraeli “kudandaula za Mose.” (Num. 13:31–14:4) Kumbali ina, ciyamikilo cingathandize ena kupitiliza kucita zabwino. Conco, muziyesa kupeza mipata yoyamikila ena mocokela pansi pa mtima. w22.04 8 ¶16-17

Ciŵelu, November 2

Ndinaponyedwa m’manja mwanu kucokela m’mimba. Kuyambila ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.​—Sal. 22:10.

Kuyambila kale-kale, Yehova wakhala akuthandiza acicepele ambili kukhala mabwenzi ake. Iye angathandizenso ana anu kukula kuuzimu, ngati n’zimene iwo akufuna. (1 Akor. 3:6, 7) Ngakhale kuti ana anu sakutumikila Yehova na mtima wonse, iye adzapitilizabe kuwayang’anila mwacikondi. (Sal. 11:4) Iwo akaonetsa kuti ali na “maganizo abwino,” iye ni wokonzeka kuwathandiza kuti akhale mabwenzi ake. (Mac. 13:48; 2 Mbiri 16:9) Angakuthandizeni kukamba zoyenela pa nthawi imene ana anu akufunikila kumva zimenezo. (Miy. 15:23) Kapena angalimbikitse m’bale kapena mlongo mu mpingo mwanu kuwaonetsa cidwi. Ngakhale ana anu atakula, Yehova adzawathandiza kukumbukila zimene munawaphunzitsa ali acicepele. (Yoh. 14:26) Mukapitiliza kuphunzitsa ana anu mwa mawu na citsanzo canu, Yehova adzakufupani. w22.04 21 ¶18

Sondo, November 3

Cinjokaco cinakwiya.​—Chiv. 12:17.

Popeza tsopano alibe malo kumwamba, iye wakwiyila otsalila odzozedwa amene amaimilako Ufumu wa Mulungu padziko lapansi, komanso amene “ali ndi nchito yocitila umboni za Yesu.” (2 Akor. 5:20; Aef. 6:19, 20) Mu 1918, abale 8 otsogolela amenewo anasemeledwa mlandu wabodza, ndipo anagamulidwa kuti adzakhala m’ndende kwa nthawi yaitali. Zinaoneka monga kuti nchito ya odzozedwa amenewa ‘yaphedwa.’ (Chiv. 11:3, 7-11) Koma ca kuciyambi kwa 1919, abale odzodzedwa amenewa anatulutsidwa m’ndende, ndipo posapita nthawi mlandu wawo unatha. Nthawi yomweyo, abalewo anayambanso kugwila nchito ya Ufumu. Koma Satana sanaleke kuukila anthu a Mulungu. Kungocokela nthawiyo, Satana wakhala akubweletsa “mtsinje” wa mazunzo kwa anthu a Mulungu. (Chiv. 12:15) Kunena zoona, “apa m’pamene [aliyense wa ife] akufunika kupilila, ndiponso kukhala ndi cikhulupililo.”​—Chiv. 13:10. w22.05 5-6 ¶14-16

Mande, November 4

Ndinamva ciŵelengelo ca amene anadindidwa cidindo. Anthu okwana 144,000.​—Chiv. 7:4.

M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona magulu aŵili a anthu amene amacilikiza ulamulilo wa Yehova, ndipo iwo analandila madalitso a moyo wosatha. M’gulu loyamba muli anthu 144,000. Iwo amatengedwa padziko lapansi kuti akapange boma, kapena kuti Ufumu kumwamba pamodzi na Yesu. Limodzi naye adzalamulila dziko lapansi. (Chiv. 5:9, 10; 14:3, 4) M’masomphenya, Yohane anawaona ataimilila na Yesu kumwamba pa Phili la Ziyoni. (Chiv. 14:1) Kuyambila m’nthawi ya atumwi, anthu masauzande akhala akusankhidwa kuti akhale m’gulu la 144,000. (Luka 12:32; Aroma 8:17) Komabe, Yohane anauzidwa kuti ni otsalila a 144,000 ocepa cabe amene adzakhala na moyo padziko lapansi m’masiku otsiliza. (Chiv. 12:17) Ndiyeno, pa nthawi ya cisautso cacikulu, otsalila amenewo adzatengedwa kupita kumwamba kuti akakhale na odzozedwa anzawo, amene anamwalila ali okhulupilika. Kumeneko adzalamulila na Yesu mu Ufumu wa Mulungu.​—Mat. 24:31; Chiv. 5:9, 10. w22.05 16 ¶4-5

Ciŵili, November 5

Muzimvela malamulo anga.​—Yes. 48:18.

Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti azidziona moyenela. Iye anawatsimikizila kuti: “Tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliŵelenga.” (Mat. 10:30) Mfundo imeneyi ni yolimbikitsa kwa ife, maka-maka tikamadziona mosayenela. Izi zionetsa kuti Atate wathu wakumwamba amasamala kwambili za ife, ndipo ndife a mtengo wapatali kwa iye. Sitiyenela kukaikila mwayi umene Yehova watipatsa wokhala alambili ake, komanso wokalandila moyo wosatha, n’kumadziona kuti sindife oyenelela madalitso amenewa. Zaka ngati 15 zapitazo, Nsanja ya Mlonda inakamba kuti tiyenela kudziona moyenela. Inati: “Sitiyenela kuganiza kuti ndife ofunika kwambili mpaka kuyamba kunyada, komanso tisacite kudzitsitsa monyanyila n’kufika pomadziona ngati ndife opanda nchito. Colinga cathu ciyenela kukhala comadziona moyenela, moganizila zinthu zimene timakwanitsa kucita na zimene sitingathe kucita.” w22.05 24-25 ¶14-16

Citatu, November 6

[Ndikupempha] . . . kuti onsewa akhale amodzi.​—Yoh. 17:20, 21.

Kodi aliyense wa ife angacite ciyani kuti alimbikitse mgwilizano mumpingo? Tiyenela kukhala anthu obweletsa mtendele. (Mat. 5:9; Aroma 12:18) Nthawi iliyonse tikacitapo kathu kuti tikhazikitse mtendele na ena mumpingo, timapangitsa kuti paradaiso wauzimu akongoleleko. Tizikumbukila kuti Yehova ndiye anakokela aliyense m’paradaiso wauzimu ameneyu, mmene muli kulambila koyela. (Yoh. 6:44) Tangoganizani mmene Yehova amasangalalila akaona kuti tikuyesetsa kulimbikitsa mtendele na mgwilizano pakati pa atumiki ake, amene amawaona kuti ni amtengo wapatali! (Yes. 26:3; Hag. 2:7) Kodi tingacite ciyani kuti tizipindula kwambili na madalitso amene timalandila monga atumiki a Mulungu? Tiyenela kuganizila mozama zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu, komanso m’zofalitsa zathu zozikika pa Baibo. Kuŵelenga na kusinkhasinkha, kudzatithandiza kukulitsa makhalidwe acikhristu amene adzatilimbikitsa kukonda abale athu na “cikondi ceniceni” mumpingo.​—Aroma 12:10. w22.11 12-13 ¶16-18

Cinayi, November 7

Ndidzawakhululukila zolakwa zawo ndipo macimo awo sindidzawakumbukilanso.​—Yer. 31:34.

Tikavomeleza kuti Yehova anatikhululukila, timakondwela na “nyengo zotsitsimutsa,” ndipo timakhala na mtendele wamaganizo komanso cikumbumtima coyela. Cikhululuko cotelo ‘cimacokela kwa Yehova,’ osati kwa anthu. (Mac. 3:19) Yehova akatikhululukila, amakonzanso ubwenzi wathu ndipo zimakhala monga sitinacimwepo kumbuyoku. Yehova akatikhululukila, sakatiimbanso mlandu kapena kutilanga pa chimo limenelo. (Yes. 43:25) Yehova amatiikila ‘kutali zolakwa zathu monga mmene kum’mawa kulili kotalikilana na kumadzulo.’ (Sal. 103:12) Tikaganizila mmene Yehova amatikhululukila mwapadela, timakhala oyamikila ndipo timakhudzika mtima. (Sal. 130:4) Yehova pofuna kukhululukila munthu sayang’ana kukula kapena kucepa kwa chimo limene wacita. Yehova amaseŵenzetsa cidziŵitso cake monga Mlengi wathu, Wopanga Malamulo, komanso Woweluza akafuna kukhululukila munthu. w22.06 5 ¶12-14

Cisanu, November 8

Aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.​—Aheb. 11:6.

Yehova anapeleka ciyembekezo cabwino kwa onse omukonda. Ndipo posacedwa iye adzacotsapo matenda, cisoni, na imfa. (Chiv. 21:3, 4) “Anthu ofatsa” amene akuyembekezela pa iye, adzawathandiza kukonza dziko lapansi kukhala paradaiso. (Sal. 37:9-11) Pa nthawiyo, aliyense wa ife adzakhala pa ubale wabwino kwambili na iye kuposa umene tili nawo pali pano. Ici n’ciyembekezo cabwino ngako! Koma n’cifukwa ciyani timakhulupilila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwa? Cifukwa Yehova salephela kukwanilitsa zimene walonjeza. Mwa ici, tili na cifukwa cabwino ‘coyembekezela Yehova.’ (Sal. 27:14) Timaonetsa izi poyembekezela moleza mtima komanso mwacimwemwe kuti Mulungu adzakwanilitsa malonjezo ake. (Yes. 55:10, 11) Conco, tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa Yehova, podziŵa kuti iye adzapeleka mphoto kwa “anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.” w22.06 20 ¶1; 25 ¶18

Ciŵelu, November 9

Mulungu Atate wanu amadziŵa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.​—Mat. 6:8.

Tingakhale otsimikiza kuti Yehova pokhala Mutu wa banja, adzalemekeza mfundo imene anailemba pa 1 Timoteyo 5:8. Tikamakhulupilila kuti Yehova amatikonda pamodzi na banja lathu, tingakhale na cidalilo cakuti tidzapeza zofunikila pa umoyo. (Mat. 6:31-33) Yehova amatipatsa zosoŵa pa umoyo, ndipo iye ni wacikondi komanso Mpatsi wowolowa manja. Polenga dziko lapansi, sanangotipatsa cabe zinthu zofunikila pa umoyo. Mwa cikondi cake, Mulungu anadzaza dziko lapansi na zinthu zambili zabwino kuti tizisangalala na umoyo. (Gen. 2:9) Ngakhale kuti nthawi zina sitingakhale na zonse zimene tingafune pa umoyo, tizikumbukila kuti zofunikila kwenikweni zimene tili nazo ni Yehova amene watipatsa. (Mat. 6:11) Tizikumbukilanso kuti zinthu zakuthupi zimene tingadzimane pali pano, sizingalingane na zimene Mulungu wathu wacikondi angatipatse pa nthawi ino komanso m’tsogolo.​—Yes. 65:21, 22. w22.06 15 ¶7-8

Sondo, November 10

Cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu.​—Aheb. 5:14.

Si anthu acidwi okha amene afunikila cakudya cotafuna cauzimu. Tonsefe timafunikila cakudyaci. Mtumwi Paulo analemba kuti kugwilitsa nchito zimene timaphunzila m’Baibo kudzatithandiza “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” M’nthawi yovuta ino pamene makhalidwe abwino akuloŵela-loŵela pansi, cingakhale covuta kumamatila mfundo za Yehova. Koma Yesu amaonetsetsa kuti cakudya cauzimu cokoma cimene timadya cikulimbitsa cikhulupililo cathu. Cakudya cauzimu cimeneci cimazikika pa Mawu a Mulungu ouzilidwa, Baibo. Mofanana na Yesu, timalemekeza dzina la Mulungu. (Yoh. 17:6, 26) Mwacitsanzo, mu 1931 tinatenga dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. Kudziŵika na dzina limeneli kumatipangitsa kuyandikana kwambili na Atate wathu wakumwamba. (Yes. 43:10-12) Kuwonjezela apo, mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, dzina la Mulungu linabwezeletsedwa pamalo ake oyenelela. w22.07 11 ¶11-12

Mande, November 11

Mawu anu ndi nyale younikila kumapazi anga, ndi kuwala kounikila njila yanga.​—Sal. 119:105.

Coonadi ca m’Baibo ciphatikizaponso uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu. Yesu anayelekezela coonadi cokamba za Ufumu na cuma cobisika. Pa Mateyu 13:44 Yesu anati: “Ufumu wakumwamba uli ngati cuma cobisika m’munda, cimene munthu anacipeza n’kucibisa. Cifukwa ca cimwemwe cimene anali naco, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Pa lembali, munthuyu sanali kufuna-funa cuma ayi. Koma atacipeza, anadzimana zinthu zambili kuti akhale naco. Iye anacita kugulitsa zonse zimene anali nazo. Cifukwa ciyani? Cifukwa anaona kuti cumaco n’camtengo wapatali. Tidziŵa kuti palibe cingalingane na cimwemwe cimene timakhala naco cifukwa cotumikila Yehova pali pano, tili na ciyembekezo ca moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu. Kukhala pa ubale wolimba na Yehova n’kofunika kwambili kuposa ciliconse cimene tingadzimane. Ndipo timakondwela kucita ‘zomukondweletsa pa ciliconse.’​—Akol. 1:10. w22.08 15 ¶8-9; 17 ¶12

Ciŵili, November 12

Ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?​—Gen. 39:9.

Kodi Yosefe anadziŵa bwanji kuti Mulungu wake anali kuona kuti cigololo ni “coipa cacikulu”? Cilamulo ca Mose, cimene cinaphatikizapo lamulo lomveka bwino lakuti “usacite cigololo” cinali cisanalembedwe kufikila patapita zaka pafupifupi 200. (Eks. 20:14) Koma Yosefe anali kudziŵa bwino kuti Yehova amadana nalo kwambili khalidwe laciwelewele. Mwacitsanzo, Yosefe anali kudziŵa kuti Yehova anakonza zakuti ukwati uzikhala pakati pa mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi. Ndipo ayenelanso kuti anamva kuti kaŵili konse, Yehova anateteza Sara ambuye ŵake kuti asacitidwe zaciwelewele. (Gen. 2:24; 12:14-20; 20:2-7) Yosefe poganizila nkhani ngati zimenezi, anadziŵa cimene cinali coyenela komanso cosayenela pamaso pa Mulungu. Cifukwa cokonda Mulungu wake, Yosefe anali kukondanso malamulo olungama a Yehova, ndipo anali wofunitsitsa kuwatsatila. w22.08 26 ¶1-2

Citatu, November 13

Ambili amene agona munthaka adzauka. Ena adzalandila moyo wosatha.​—Dan. 12:2.

Ulosi umenewu sukamba za ciukitso cophiphilitsa, kapena kuti kuuka kwauzimu kwa atumiki a Mulungu kumene kunacitika kumayambililo kwa masiku otsiliza, monga tinali kudziŵila kale. M’malo mwake, mawu a pa lembali amakamba za kuukitsidwa kwa akufa kumene kudzacitike m’dziko latsopano limene likubwelalo. N’cifukwa ciyani tikutelo? Mawu akuti “nthaka” pa Danieli 12:2 ni ofanana na mawu ochulidwa pa Yobu 17:16 akuti “fumbi.” Mawu onsewa amatanthauza “Manda.” Pa cifukwa cimeneci, Danieli 12:2 imakamba za ciukitso ceniceni cimene cidzacitika pambuyo pakuti masiku otsiliza atha, komanso pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo. Koma kodi Danieli 12:2 imatanthauza ciyani ponena kuti ena adzauka kuti ‘akalandile moyo wosatha’? Imatanthauza kuti anthu amene adzaukitsidwa kenako n’kupitiliza kuphunzila za Yehova na Yesu na kuwadziŵa bwino, komanso kuwamvela mu ulamulilo wa zaka 1,000, pamapeto pake adzalandila moyo wosatha.​—Yoh. 17:3. w22.09 21 ¶6-7

Cinayi, November 14

[Cikondi] cimakhulupilila zinthu zonse.​—1 Akor. 13:7.

Mawuwa satanthauza kuti Yehova amafuna kuti tizidalila ena mwacimbuli-mbuli aya. Koma amafuna tiziwadalila cifukwa amaonetsa kuti ni okhulupilika. Ulemu umabwela wokha. N’cimodzimodzinso kuti anthu ayambe kutidalila, ndipo izi zimatenga nthawi. Kodi tingacite ciyani kuti tiyambe kuwadalila abale athu? Tiyenela kuwadziŵa bwino. Tingacite zimenezi mwa kuceza nawo pa misonkhano ya mpingo, na kumalalikila nawo. Ndipo tizileza nawo mtima kuti tiwapatse mwayi woonetsa kuti ni okhulupilika. Mwacitsanzo, munthu amene mwangoyamba kumene kudziŵana naye, simungamuuze nkhani zanu zonse zacinsinsi. Koma pamene mwafika pom’dziŵa bwino munthuyo, pang’ono-m’pang’ono mungayambe kumasuka kumuuzako nkhani za inu mwini. (Luka 16:10) Nanga mungacite ciyani ngati m’bale kapena mlongo anaulula cinsinsi canu? Musafulumile kuthetsa ubwenzi wanu. Ndipo musalole kuti zophophonya za ocepa zikupangitseni kuleka kudalila abale na alongo. w22.09 4 ¶7-8

Cisanu, November 15

Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi.​—2Mb 16:9.

Mkulu wina dzina lake Miqueas, anaona kuti abale apaudindo amuweluza molakwika. Ngakhale n’telo, iye anakhalabe woganiza bwino, ndipo anayesetsa kuwongolela maganizo ake. Anali kupemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili kuti am’patse mzimu woyela na mphamvu zom’thandiza kupilila. Anafufuzanso mfundo zina m’zofalitsa zathu zimene zinam’thandiza. Kodi tiphunzilapo ciyani? Ngati mwaona kuti m’bale kapena mlongo wakukhumudwitsani, khalanibe wodekha ndipo yesetsani kuwongolela maganizo alionse olakwika amene mungakhale nawo. Sitingadziŵe zimene zinapangitsa munthuyo kulankhula kapena kucita zinthu mwa njila imeneyo. Conco, muuzeni Yehova m’pemphelo na kum’pempha kuti akuthandizeni kuona zinthu mmene munthuyo amazionela. Onani m’baleyo kapena mlongoyo kuti sanali na colinga cokukhumudwitsani, ndipo mukhululukileni. (Miy. 19:11) Yehova amaona zimene mukupitamo, ndipo adzakupatsani mphamvu zofunikila kuti mupilile.​—Mlal. 5:8. w22.11 21 ¶5

Ciŵelu, November 16

Sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.​—Sal. 26:4

Sankhani mabwenzi okonda Yehova. Mabwenzi amene mungasankhe angakuthandizeni kukula kuuzimu. (Miy. 13:20) M’bale Julien, amene tsopano ni mkulu anati: “Pamene n’nali wacinyamata, kulalikila na ena kunanithandiza kupeza mabwenzi abwino. Mabwenzi amenewo anali okangalika, cakuti ananithandiza kuona kuti ulaliki ni wosangalatsa kwambili. . . . N’nazindikilanso kuti n’nalibe mabwenzi ambili abwino cifukwa n’nali kungofuna kukhala na mabwenzi a msinkhu wanga okha.” Nanga bwanji mukazindikila kuti winawake mu mpingo sangakhale bwenzi lanu labwino? Paulo anaona kuti anthu ena mu mpingo wacikhristu wa m’zaka za zana loyamba sanali kulemekeza zinthu zauzimu. Motelo, anacenjeza Timoteyo kuti awapewe. (Tim. 2:20-22) Ubwenzi wathu na Yehova ni wamtengo wapatali. Conco, tisalole aliyense kutiwonongela ubwenzi wathithithi umene tinapanga na Atate wathu wakumwamba. w22.08 5-6 ¶13-15

Sondo, November 17

Coka pamaso pa munthu wopusa.​—Miy. 14:7.

Mosiyana nawo anthu odana na uphungu wa Mulungu, ife timakonda kwambili njila zake, kuphatikizapo malamulo ake. Tingakulitse cikondi cimeneco poyelekezela zotulukapo zimene zimakhalapo ngati munthu amamvela, komanso ngati samvela. Ganizilani mavuto amene anthu amadzibweletsela pokana mwadala uphungu wanzelu wa Yehova. Kenako, ganizilani mmene umoyo wanu ulili wabwino cifukwa comvela Mulungu. (Sal. 32:8, 10) Yehova amapeleka nzelu kwa aliyense, koma sakakamiza munthu kuitsatila. Komabe, iye amanena zimene zimacitika kwa anthu okana kumvetsela nzelu yake. (Miy. 1:29-32) Iwo “adzadya zipatso za njila yawo.” M’kupita kwa nthawi, khalidwe lawo limawabweletsela mavuto, ndipo pamapeto pake adzawonongedwa. Koma anthu amene amamvela uphungu wanzelu wa Yehova na kuugwilitsa nchito, amawalonjeza kuti: “Munthu wondimvela adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka cifukwa coopa tsoka.”​—Miy. 1:33. w22.10 21 ¶11-13

Mande, November 18

Wodala ndi aliyense woopa Yehova, amene amayenda m’njila za Mulungu.​—Sal. 128:1.

Kuwopa Yehova kumatathauza kum’lemekeza kwambili mwa kupewa kucita ciliconse com’khumudwitsa. (Miy. 16:6) Conco, tiyenela kupitiliza kuyesetsa kutsatila malamulo a Mulungu a cabwino na coipa, monga mmene Baibo imafotokozela. (2 Akor. 7:1) Tikamacita zimene Yehova amakonda, na kupewa kucita zimene amadana nazo, tidzakhala na cimwemwe. (Sal. 37:27; 97:10; Aroma 12:9) Munthu angadziŵe kuti Yehova ndiye ali na mphamvu yotiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. Koma munthuyo payekha ayenelanso kutsatila zimene Mulungu amafuna. (Aroma 12:2) Mwa khalidwe lathu, timaonetsa kuti timakhulupililadi kuti kutsatila malamulo a Yehova kumatipindulila. (Miy. 12:28) Umu ni mmene Davide anamvela ponena za Yehova. Iye anati: “Mudzandidziŵitsa njila ya moyo. Cifukwa ca nkhope yanu, munthu adzakondwela mokwanila. Kudzanja lanu lamanja kuli cimwemwe mpaka muyaya.”​—Sal. 16:11. w22.10 8 ¶9-10

Ciŵili, November 19

Mwanayo sangacite ciliconse congoganiza payekha, koma cokhaco cimene waona Atate wake akucita.​—Yoh. 5:19.

Yesu anapitiliza kudziona moyenela na kukhala wodzicepetsa. Asanabwele padziko lapansi, iye anadzipangila mbili yabwino potumikila Yehova. Kudzela mwa Yesu, “zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” (Akol. 1:16) Pa ubatizo wake, mwacionekele iye anakumbukila zinthu zambili zimene anakwanitsa kucita ali limodzi na Atate wake. (Mat. 3:16; Yoh. 17:5) Koma zimenezo sizinapangitse Yesu kukhala wonyada. Komanso, iye sanacite zinthu moonetsa kuti amaposa ena. Anauza ophunzila ake kuti iye anabwela padziko lapansi “[osati] kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila ndi kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.” (Mat. 20:28) Iye modzicepetsa anakambanso kuti sanacite ciliconse congoganiza payekha. Kunali kudzicepetsa cotani nanga kumene Yesu anaonetsa! Iye n’citsanzo cabwino koposa cimene tingatengele. w22.05 24 ¶13

Citatu, November 20

Abwelele kwa Yehova.​—Yes. 55:7.

Yehova pokhululukila munthu amaona ngati munthuyo anali kudziŵa kuti zimene anali kucita n’zoipa kapena ayi. Yesu anachula mfundo imeneyi momveka bwino pa Luka 12:47, 48. Munthu amene mwadala amakonzekela kuti acite coipa, pamene akudziŵa bwino kuti cimene akucitaco n’kucimwila Yehova, amacita chimo lalikulu. Munthu wotelo amakhala pa ciopsezo, cifukwa Yehova angasankhe kusam’khululukila. (Maliko 3:29; Yoh. 9:41) Koma kodi pali ciyembekezo cakuti Yehova angatikhululukile? Inde! Cina, Yehova amaona ngati wocimwayo ni wolapadi mocokela pansi pamtima. Kulapa kumatanthauza “kusintha kaganizidwe, kaonedwe ka zinthu, kapena kusintha zolinga.” Kuphatikizapo kudziimba mlandu komanso kudzimvela cisoni kwambili pa zoipa zimene anacita, kapena polephela kucita zoyenela. Munthu wolapa amadzimvela cisoni pa zoipa zimene anacita, komanso kufooka kwake kuuzimu kumene kunam’tsogolela kucita zoipazo. w22.06 5-6 ¶15-17

Cinayi, November 21

Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.​—2 Tim. 3:12.

Adani athu amafalitsa mabodza onena za abale otsogolela m’gulu la Yehova. (Sal. 31:13) Abale ena amangidwa na kuweluzidwa kuti ni ophwanya malamulo. Zaconco zinawacitikila Akhristu a m’zaka za zana loyamba pamene mtumwi Paulo anamuimba mlandu wabodza na kum’manga. Akhristu ena analeka kum’cilikiza Paulo pamene anali m’ndende ku Roma. (2 Tim. 1:8, 15; 2:8, 9) Ganizilani mmene Paulo anamvela. Iye anali atapilila mavuto ambili, ngakhale kuika moyo wake pa ciwopsezo cifukwa ca iwo. (Mac. 20:18-21; 2 Akor. 1:8) Conde, tisakhale monga Akhristu amene anasiya Paulo. Conco, sitiyenela kudabwa kuti Satana amaukila kwambili abale otsogolela. Iye amacita zimenezi pofuna kuwononga cikhulupililo cawo, komanso kuti atiwopseze. (1 Pet. 5:8) Pitilizani kuthandiza abale anu, na kuwamamatila mokhulupilika.​—2 Tim. 1:16-18. w22.11 16-17 ¶8-11

Cisanu, November 22

Kodi iwe suopa Mulungu eti?​—Luka 23:40.

Munthu wocita zoipa wolapayo amene anapacikidwa pamodzi na Yesu, ayenela kuti anali Myuda. Ayuda anali kulambila Mulungu mmodzi. Koma anthu a mitundu ina anali kukhulupilila milungu yambili. (Eks. 20:2, 3; 1 Akor. 8:5, 6) Ngati munthu wocita zoipayo anali wa mitundu ina, mwina akanafunsa kuti, “Kodi iwe suopa milungu eti?” Cina, Yesu anatumidwa kwa “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli,” osati kwa anthu a mitundu ina. (Mat. 15:24) Ndipo Mulungu kalelo anauza Aisiraeli kuti adzaukitsa akufa m’tsogolo. Wocita zoipa wolapayo ayenela kuti anali kudziŵa zimenezi, ndipo zimene anakamba zionetsa kuti Yehova adzaukitsa Yesu kuti akalamulile mu Ufumu wa Mulungu. Munthuyo ayenela kuti anali na ciyembekezo mwa Mulungu kuti adzamuukitsa. Pokhala Myuda, wocita zoipa wolapayo ayenela kuti anali kudziŵa mbili ya Adamu na Hava. Conco, iye ayenela kuti anazindikila kuti Paradaiso amene Yesu anachula pa Luka 23:43, adzakhala munda wokongola pano padziko lapansi.​—Gen. 2:15. w22.12 8-9 ¶2-3

Ciŵelu, November 23

Mogwilizana, onsewa analimbikila kupemphela.​—Mac. 1:14.

Masiku anonso, timakwanitsa kugwila nchito yolalikila kokha na thandizo la mzimu wa Mulungu. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa Satana akucita nafe nkhondo kuti aimitse nchito yathu yolalikila. (Chiv. 12:17) M’kaonedwe kaumunthu, zimaoneka monga Satana amatiposa mphamvu. Koma pamene tigwila nchito yathu yolalikila timamugonjetsa! (Chiv. 12:9-11) Kodi zimacitika motani? Tikamagwila nchito yolalikila, timaonetsa kuti siticita mantha na ziwopsezo za Satana. Nthawi iliyonse tikalalikila, timamugonjetsa Satana. Ndiye kodi ni mfundo iti yosatsutsika imene imaonekela tikamalalikilabe ngakhale kuti anthu amatitsutsa? Ni mfundo yakuti mzimu woyela ndiwo umatipatsa mphamvu, komanso kuti Yehova akutiyanja. (Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:14) Mzimu wa Mulungu ungatithandize kuthana na vuto lililonse limene tingakumane nalo mu ulaliki. (2 Akor. 4:7-9) Nanga tiyenela kucita ciyani kuti tipitilize kulandila mzimu wa Mulungu? Tiyenela kuupempha mobweleza-bweleza tili na cidalilo cakuti Yehova adzamva mapemphelo athu. w22.11 5 ¶10-11

Sondo, November 24

Tikukudandaulilani abale kuti, langizani ocita zosalongosoka, lankhulani molimbikitsa kwa amtima wacisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.​—1 Ates. 5:14.

Timaonetsanso cikondi kwa abale na alongo athu mwa kuyesetsa kukhala nawo pa mtendele. Timayesetsa kutengela citsanzo ca Yehova ca kukhululuka. Yehova mofunitsitsa anapeleka Mwana wake kuti afe kaamba ka macimo athu. Conco, nafenso tiyenela kukhala ofunitsitsa kukhululukila abale na alongo athu akatilakwila. Sitifuna kukhala monga kapolo woipa wochulidwa m’fanizo lina la Yesu. Ngakhale kuti mbuye wake anam’khululukila nkhongole yaikulu kwambili, kapoloyo analephela kukhululukila kapolo mnzake nkhongole yaing’ono. (Mat. 18:23-35) Ngati munasemphana maganizo na wina mumpingo, bwanji osayamba ndinu kukhazikitsa mtendele Cikumbutso cisanacitike? (Mat. 5:23, 24) Mukacita izi, mudzaonetsa kuti mumam’konda kwambili Yehova na Yesu. w23.01 29 ¶8-9

Mande, November 25

Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova.​—Miy. 19:17.

Njila imodzi imene mungadziŵile zimene abale na alongo anu afunikila, ni kuwafunsa mafunso mosamala kuti afotokoze za mu mtima mwawo. (Miy. 20:5) Kodi ali na cakudya cokwanila, mankhwala, na zofunikila zina? Kodi zioneka kuti nchito yawo ingathe kapena akhoza kusoŵa pokhala cifukwa colephela kulipila lendi? Kodi afunikila kuwathandiza kuti alembetse kulandilako mathandizo a boma? Yehova akupempha tonsefe kulimbikitsa ena na kuwathandiza. (Agal. 6:10) Ngakhale zazing’ono zimene tingacite poonetsa cikondi munthu wodwala, zingam’limbikitse kwambili. Wacicepele angatumizile m’bale kakhadi kapena cithunzi cojambula pa manja kuti am’limbikitse. Wacinyamata angathandizeko mlongo pa zina zake, monga kukamugulilako zinthu ku sitolo. Mwina mungakonzele wodwala cakudya. Mboni zina zawalembelapo mawu owayamikila. Zimakhala zolimbikitsa kwambili tikacita mbali yathu ‘popitiliza kutonthozana na kulimbikitsana’!​—1 Ates. 5:11. w22.12 22 ¶2; 23 ¶5-6

Ciŵili, November 26

Mukulakwitsa kwambili anthu inu.​—Maliko 12:27.

Asaduki anali kuwadziŵa bwino kwambili mabuku oyambilila asanu a Malemba Aciheberi. Koma iwo ananyalanyaza mfundo zofunika za m’mabuku ouzilidwa amenewo. Mwacitsanzo, onani mmene Yesu anawayankhila Asaduki atafuna kum’kola pa nkhani ya ciukitso. Iye anawafunsa kuti: “Kodi inu simunaŵelenge m’buku la Mose, m’nkhani ya citsamba caminga, mmene Mulungu anamuuzila kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?” (Maliko 12:18, 26) Ngakhale kuti Asaduki anaŵelenga nkhaniyo mobweleza-bweleza, funso la Yesu linaonetsa kuti iwo ananyalanyaza mfundo yofunika ya coonadi ca m’Malemba, imene ni ciphunzitso ca kuuka kwa akufa. (Luka 20:38) Kodi tiphunzilapo ciyani? Tikamaŵelenga Baibo tiyenela kuyesetsa kudziŵa zonse zimene vesi kapena nkhani ya m’Baibo imeneyo itiphunzitsa. Sitiyenela kungotengapo mfundo za pamwamba zosalila kukumba. Koma timafunanso kumvetsa mfundo za coonadi zobisika ngati cuma camtengo wapatali. w23.02 11 ¶9-10

Citatu, November 27

Tili ndi mtambo wa mboni waukulu . . . Wotizungulila.​—Aheb. 12:1.

Mboni zonse zimene lemba la tsiku lalelo likulozako, zinakumanapo na mayeso aakulu, koma zinakhalabe zokhulupilika kwa Yehova. (Aheb. 11:36-40) Kodi kupilila kwawo komanso kugwila nchito kwawo molimbika kunangopita pacabe? Kutalitali! Ngakhale kuti iwo sanaone kukwanilitsidwa kwa malonjezo onse a Mulungu m’nthawi yawo , anayembekezelabe Yehova. Ndipo cifukwa anali kudziŵa bwino lomwe kuti Yehova anali kuwayanja, iwo anali na cidalilo cakuti adzaona kukwanilitsidwa kwa malonjezo ake. (Aheb. 11:4, 5) Citsanzo cawo cimatilimbikitsa kuti tisaleke kuyembekezela Yehova. Masiku ano, tikukhala m’dziko limene zinthu zikungoipilaipila. (2 Tim. 3:13) Satana akali kuwayesa anthu a Mulungu. Mosasamala kanthu na zopinga zimene tingakumane nazo kutsogolo, tiyeni tigwilebe nchito ya Yehova molimbika, tili na cidalilo cakuti “ciyembekezo cathu cili mwa Mulungu wamoyo.”​—1 Tim. 4:10. w22.06 25 ¶17-18

Cinayi, November 28

Kodi magazi anga angakhale ndi phindu lanji . . . ? Kodi fumbi lidzakutamandani?​—Sal. 30:9.

Cifukwa cina coyesetsela kukhala athanzi, n’cakuti m’pamene tingam’tumikile bwino kwambili Yehova. (Maliko 12:30) Conco, timapewa kucita zinthu zimene tidziŵa bwino kuti zingawononge thanzi lathu. (Aroma 12:1) Komabe, ngakhale tiyesetse bwanji kusamalila thanzi lathu, timadwala ndithu. Ngakhale n’telo, timayesetsa kucita zimene tingathe kuti tikhale na thanzi, cifukwa timafuna kuonetsa Atate wathu kuti timayamikila mphatso ya moyo. Matenda na ukalamba zingatiletse kucita zambili monga tinali kucitila kale. Zotulukapo n’zakuti tingalefuke. Koma tisataye mtima na kuleka kusamalila thanzi lathu. Cifukwa ciyani? Cifukwa kaya ndife okalamba kapena tikudwala, n’zotheka kutamandabe Yehova monga anacitila Mfumu Davide. N’zolimbikitsa kudziŵa kuti ndife amtengo wapatali kwa Mulungu olo kuti ndife opanda ungwilo. (Mat. 10:29-31) Ngati tingamwalile lelo, iye ni wofunitsitsa kudzatiukitsa. (Yobu 14:14, 15) Conco, tifuna kusamalila thanzi lathu na kuteteza moyo wathu tikali moyo mmene tingathele. w23.02 20-21 ¶3-5

Cisanu, November 29

Aliyense amene wanyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa kwamuyaya.​—Maliko 3:29.

Kodi maina a khamu lalikulu la nkhosa zina adzakhalamobe m’buku la moyo pambuyo pa Aramagedo? Inde. (Chiv. 7:14) Yesu anakamba kuti anthu onga nkhosa amenewa adzacoka kupita “ku moyo wosatha.” (Mat. 25:46) Koma opulumuka Aramagedo amenewo sikuti adzalandila moyo wosatha nthawi yomweyo. Mu Ulamulilo wa Zaka Cikwi (1,000), Yesu “adzawaweta ndi kuwatsogolela ku akasupe a madzi a moyo.” Anthu amene adzatsatila citsogozo ca Yesu na kuweluzidwa pamapeto pake kuti ni okhulupilika kwa Yehova, maina awo adzalembedwa mwacikhalile m’buku la moyo. (Chiv. 7:16, 17) Komabe, anthu onga mbuzi adzawonongedwa pa Aramagedo. Yesu anakamba kuti “adzacoka kupita ku ciwonongeko cothelatu.” (Mat. 25:46) Mouzilidwa na mzimu woyela, mtumwi Paulo anakamba kuti “amenewa adzawaweluza kuti alandile cilango ca ciwonongeko camuyaya.”​—2 Ates. 1:9; 2 Pet. 2:9. w22.09 16 ¶7-8

Ciŵelu, November 30

Ciliconse cili ndi nthawi yake.​—Mlal. 3:1.

Mabanja akamapatula nthawi yosangalala na cilengedwe ca Yehova, amalimbitsa cikondi pa wina na mnzake. Kudzela m’nchito ya manja ake, Yehova anatipatsa malo oculuka ocitilako zinthu zimene timasangalala nazo. Mabanja ambili amakonda kupita kumalo monga kumapaki, kumalo akumidzi, kumapili, komanso kunyanja. M’dziko latsopano la Mulungu, makolo komanso ana adzasangalala na cilengedwe ca Yehova kuposa kale lonse. Mosiyana na masiku ano, panthawiyo tidzakhala pa mtendele na nyama. (Yes. 11:6-9) Tidzasangalala na cilengedwe ca Yehova kosatha. (Sal. 22:26) Koma inu makolo, musacite kuyembekeza mpaka nthawi imeneyo kuti mudzayambe kuthandiza ana anu kusangalala na zinthu zacilengedwe. Mukamagwilitsa nchito zacilengedwe pophunzitsa ana anu za Yehova, iwo angafike povomeleza zimene Mfumu Davide ananena. Iye anati: “Inu Yehova . . . palibe nchito zilizonse zofanana ndi nchito zanu.”​—Sal. 86:8. w23.03 25 ¶16-17

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani