December
Sondo, December 1
Cikundiletsa kubatizidwa n’ciyani?—Mac. 8:36.
Kodi nduna ya ku Itiyopiya inali yokonzekadi kubatizika? Ganizilani izi: Mwamuna wa ku Itiyopiya uja “anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu.” (Mac. 8:27) Iye ayenela kuti anali wotembenukila ku Ciyuda. Mosakayikila, anaphunzila za Yehova m’Malemba Opatulika Aciheberi. Ngakhale n’conco, anali wofunitsitsa kuphunzila zambili. Mwacitsanzo, pamene Filipo anakumana na mwamunayo pamsewu, iye anali kuŵelenga mpukutu wa mneneli Yesaya. (Mac. 8:28) Anali wofunitsitsa kudziŵa zambili. Anayenda ulendo wautali kucokela ku Itiyopiya kupita ku Yerusalemu kuti akalambile Yehova pakacisi. Ndunayo inaphunzila mfundo zingapo zatsopano za coonadi kwa Filipo, kuphatikizapo yakuti Yesu anali Mesiya. (Mac. 8:34, 35) Anakulitsa cikondi cake pa Yehova na Mwana wake. Izi zinam’limbikitsa kupanga cisankho cacikulu cakuti abatizike, n’kukhala wotsatila wa Yesu Khristu. Conco, Filipo ataona kuti munthuyo anali wokonzeka, anam’batiza. w23.03 8-9 ¶3-6
Mande, December 2
Nthawi zonse mawu anu azikhala acisomo.—Akol. 4:6.
Sitingakondweletse Yehova ngati timanama. (Miy. 6:16, 17) Ngakhale kuti anthu ambili masiku ano amaona kuti kunama kulibe vuto kwenikweni, ife timaona bodza mmene Yehova amalionela. (Sal. 15:1, 2) Mwa ici, timapewelatu bodza lililonse, ngakhalenso kupeleka mwadala cithunzi colakwika. Tiyenelanso kupewa kufalitsa mijedo yovulaza. (Miy. 25:23; 2 Ates. 3:11) Mukaona kuti makambilano anu akuyamba kukhala misece, conde sinthani nkhani. Popeza tikukhala m’dziko limene makambidwe oipa ni ofala, tiyenela kuyesetsa kuti zokamba zathu zizikondweletsa Yehova. Iye adzatidalitsa tikamayesetsa kukamba mawu olimbikitsa mu ulaliki, pa misonkhano, komanso poceza na anthu ŵena. Cisonkhezelo coipa ca dzikoli cikadzatha, cidzakhala cosavuta kulemekeza Yehova mwa mawu athu.—Yuda 15. w22.04 9 ¶18-20
Ciŵili, December 3
Koma ife timasonyeza cikondi, cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.—1 Yoh. 4:19.
Tikaganizila mmene Yehova na Yesu amatikondela, ifenso timalimbikitsidwa kuwakonda. (1 Yoh. 4:10) Timawakonda kwambili tikaganizilanso zakuti Yesu anafela aliyense wa ife payekha. Mtumwi Paulo anavomeleza mfundoyi, ndipo anaonetsa ciyamikilo cake m’kalata imene analembela Agalatiya. Iye anati: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” (Agal. 2:20) Pa maziko a dipo limenelo, Yehova anakukokelani kwa iye kuti mukhale bwenzi lake. (Yoh. 6:44) Kodi sizikulimbikitsani kudziŵa kuti Yehova anaona cina cake cabwino mwa inu, ndipo anapeleka malipilo okwela kwambili kuti mukhale bwenzi lake? Kodi izi sizikupangitsani kukulitsa cikondi canu pa Yehova na Yesu? Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi cikondico cidzanilimbikitsa kucita ciyani?’ Cikondi cathu pa Mulungu na Khristu cimatilimbikitsa kuonetsa ena cikondi.—2 Akor. 5:14, 15; 6:1, 2. w23.01 28 ¶6-7
Citatu, December 4
Ndidzapatsa mitundu ya anthu cilankhulo coyela.—Zef. 3:9.
Baibo ndiyo cida cacikulu cimene Yehova amaseŵenzetsa pothandiza anthu ake kuti ‘azim’tumikila mogwilizana.’ Iye anapangitsa kuti Malemba ambili alembedwe m’njila yakuti anthu odzicepetsa okha ndiwo angathe kuwamvetsa. (Luka 10:21) Anthu kulikonse amaiŵelenga Baibo. Koma ni anthu odzicepetsa okha amene amaimvetsetsa Baibo na kugwilitsa nchito mfundo zake. (2 Akor. 3:15, 16) Baibo imaonetsa nzelu za Yehova. Iye amagwilitsa nchito Malemba kuti atiphunzitse monga gulu, komanso kuti alangize na kutonthoza munthu aliyense payekha-payekha. Tonsefe tikamaŵelenga Baibo, timatha kuona kuti Yehova amacita cidwi na aliyense wa ife. (Yes. 30:21) Nthawi zambili, kodi simumaloŵa m’Baibo na kuŵelenga lemba lokhala ngati anacita kulembela inu? Ngakhale n’telo, Baibo imathandiza anthu onse. Nanga zinatheka bwanji kuti ikhale na malangizo okuthandizani inuyo panokha pa zosoŵa zanu? Izi zinatheka cifukwa Mwiniwake wa Baibo ni wanzelu koposa m’cilengedwe conse.—2 Tim. 3:16, 17. w23.02 4-5 ¶8-10
Cinayi, December 5
Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipeleke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.—1 Tim. 4:15.
Pokhala Akhristu oona, timam’konda ngako Yehova. Timafuna kum’patsa zabwino koposa. Koma kuti ticite zimenezo, tiyenela kudziikila zolinga zauzimu, monga kukulitsa makhalidwe acikhristu, kuphunzila maluso othandiza, komanso kupeza mipata yotumikila ena. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala ofunitsitsa kupita patsogolo kuuzimu? Cifukwa cacikulu n’cakuti timafuna kukondweletsa Atate wathu wacikondi wakumwamba. Yehova amakondwela akaona kuti tikuseŵenzetsa maluso athu mokwanila pom’tumikila. Cina, timafuna kupita patsogolo kuti tizithandiza kwambili abale na alongo athu. (1 Ates. 4:9, 10) Kaya takhala m’coonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tisaleke kupitabe patsogolo kuuzimu. w22.04 22 ¶1-2
Cisanu, December 6
Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto.—Chiv. 17:16.
Magulu andale adzaukila Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. Kuukila kumeneko kudzakhala ciyambi ca cisautso cacikulu. Kodi izi zidzapangitsa anthu ambili-mbili kusankha kutumikila Yehova? Ayi. M’malo mwake, Chivumbulutso caputala 6 imati pa nthawi yovuta imeneyo, anthu amene satumikila Yehova adzafuna-funa citetezo ku maboma a dzikoli komanso mabungwe a zamalonda, amene amawayelekezela na mapili. Popeza anthuwo sadzaiima kumbali ya Ufumu wa Mulungu, Yehova adzawaona kuti ni otsutsa. (Luka 11:23; Chiv. 6:15-17) Ndithudi, atumiki a Yehova okhulupilika adzakhala osiyana kwambili na anthu a m’dzikoli pa nthawi yovuta ya cisautso cacikulu imeneyo. Ni okhawo amene padziko lapansi azidzatumikila Yehova Mulungu, na kukana kucilikiza “cilombo.”—Chiv. 13:14-17. w22.05 16-17 ¶8-9
Ciŵelu, December 7
Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.—Chiv. 14:6.
Uthenga wabwino wa Ufumu si uthenga wokhawo umene anthu a Mulungu afunika kulengeza. (Mat. 24:14) Iwo afunikanso kucilikiza nchito ya angelo ochulidwa pa Chivumbulutso caputala 8 mpaka 10. Ndiye cifukwa cake, Mboni za Yehova zakhala zikulengeza uthenga waciweluzo umene uli ngati “matalala ndi moto.” Uthengawo umaonetsa ciweluzo ca Mulungu pa mbali zosiyana-siyana za dziko loipali la Satana. (Chiv. 8:7, 13) Anthu ayenela kudziŵa kuti mapeto ali pafupi, n’colinga cakuti apange masinthidwe mwamsanga kuti akapulumuke mkwiyo wa Yehova. (Zef. 2:2, 3) Koma uthenga waciweluzowo ambili saudziŵa. Timafunika kukhala olimba mtima kuti tiulengeze. Pa cisautso cacikulu, uthenga waciweluzo wothela udzakhala woŵaŵa kwambili.—Chiv. 16:21. w22.05 7 ¶18-19
Sondo, December 8
Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.—Mat. 22:37.
Ganizilani za Akhristu okwatilana amene afuna kukhala makolo. Kwa zaka, iwo akhala akumvetsela nkhani zokamba za kulela ana. Koma tsopano, mfundo za m’nkhanizo zidzakhala zofunika kwambili kwa iwo. Adzayamba kuzigwilitsa nchito polela ana awo. Uwu ni udindo waukulu! Zinthu zikasintha mu umoyo wathu, m’pamenenso mfundo zina za m’Baibo zimakhala zothandiza kwa ife. Ndiye cifukwa cake, alambili a Yehova amaŵelenga Malemba nthawi zonse. Izi n’zimenenso mafumu aciisiraeli anauzidwa kuti azisinkhasinkha malemba “masiku onse” a moyo wawo. (Deut. 17:19) Inu makolo, muli na udindo waukulu wophunzitsa ana anu za Yehova. Koma muyenela kucita zambili kuposa pa kuwaphunzitsa za Mulungu wathu. Muyenela kuthandiza ana anu kuti azim’konda kwambili Mulungu. w22.05 26 ¶2-3
Mande, December 9
Muvale umunthu watsopano.—Akol. 3:10.
Kungodzimvela cabe cisoni pa chimo limene tinacita si kokwanila. Tiyenela kukhala okonzeka kucitapo kanthu. Cinthu cofunika kwambili cimene Yehova amaona kuti akhululuke, ni kusintha kwa munthu. Kusintha kumatanthauza “kutembenuka.” M’mawu ena, munthu ayenela kusintha umoyo wake mwa kuleka kucita zoipa, na kuyamba kucita zimene Yehova amafuna. (Yes. 55:7.) Munthuyo ayenela kusanduliza maganizo ake n’colinga cakuti aziona zinthu mmene Yehova amazionela. (Aroma 12:2; Aef. 4:23) Ayenela kuyesetsa kuleka khalidwe lake loipa, na kucotsa maganizo osayenela. (Akol. 3:7-9) Koma kuti Yehova atikhululukile na kutiyeletsa ku macimo athu, tiyenela kukhulupilila nsembe ya dipo la Khristu. Iye adzatikhululukila pogwilitsa nchito nsembe imeneyo, akaona kuti tayesetsa kusintha khalidwe lathu.—1 Yoh. 1:7. w22.06 6 ¶16-17
Ciŵili, December 10
Usacite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.—Chiv. 2:10.
Kungocokela pamene Adamu na Hava anapandukila Yehova, anthu akhala akupweteka anthu anzawo. (Mlal. 8:9) Mwacitsanzo, anthu amagwilitsa nchito ulamulilo molakwika, ophwanya malamulo amacita zaciwawa, ana a sukulu ena amanyoza anzawo a m’kalasi na kuwaopseza, ndipo anthu ena amacitila nkhanza ngakhale anthu a m’banja mwawo. Conco, n’zosadabwitsa kuti anthufe timaopana. Tikamaopa anthu, Satana amatengelapo mwayi wakuti atikole. Motani? Satana amagwilitsa nchito msampha woopa anthu pofuna kutilepheletsa kucita zimene Mulungu amafuna, komanso kugwila nchito yolalikila. Mosonkhezeledwa na Satana, maboma aletsa nchito yathu yolalikila, komanso amatizunza. (Luka 21:12) M’dzikoli lolamulidwa na Satana, anthu ambili amafalitsa nkhani zosoceletsa, komanso mabodza amkunkhuniza okhudza Mboni za Yehova. Anthu amene amakhulupilila mabodza amenewa angayambe kutiseka, ngakhale kuticitila zacipongwe. (Mat. 10:36) Kodi macenjela a Satana ni acilendo kwa ife? Kutalitali! Iye anali kugwilitsa nchito macenjela amenewo ngakhale m’nthawi ya atumwi.—Mac. 5:27, 28, 40. w22.06 16 ¶10-11
Citatu, December 11
Amene akuthandiza anthu ambili kukhala olungama adzawala ngati nyenyezi mpaka kalekale, inde, kwamuyaya.—Dan. 12:3.
Kodi ena mwa “ambili” amene adzakhala olungama ndani? Amenewa aphatikizapo oukitsidwa, komanso opulumuka Aramagedo pamodzi na ana amene angadzabadwe m’dziko latsopano. Podzafika kumapeto kwa zaka 1,000, aliyense padziko lapansi adzakhala wangwilo. Tiyenela kukumbukila kuti kukhala wangwilo pakokha sikutanthauza kuti basi munthu adzalandila moyo wosatha. Ganizilani za Adamu na Hava. Iwo anali angwilo. Koma anafunika kum’khutilitsa Yehova Mulungu kuti ni omvela asanawapatse moyo wosatha. Ndipo zacisoni n’zakuti iwo analephela kumumvela. (Aroma 5:12) Popeza anthu onse padziko lapansi adzakhala atafika pa ungwilo kumapeto kwa zaka 1,000, kodi anthu onse angwilo amenewo adzamvela Yehova na mtima wawo wonse kwamuyaya? Kapena kodi ena adzacita monga Adamu na Hava, amene anali angwilo koma anakhala osakhulupilika? Mafunso amenewa ayenela kuyankhidwa. w22.09 22-23 ¶12-14
Cinayi, December 12
Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.—Chiv. 11:15.
Tikayang’ana mmene zinthu zikuyendela m’dzikoli, kodi sizikuwonjezela nkhawa kwa inu? Anthu m’mabanja sakondana. M’dzikoli anthu akuipilaipila pa kukhala ankhanza, odzikonda, ndiponso aciwawa. Ndipo ambili cimawavuta kukhulupilila anthu audindo. Koma zocitika zimenezi zingatipatse cidalilo cakuti zinthu zidzakhala bwino. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa zimene anthu amacita n’zogwilizana ndendende na zimene Baibo inakambilatu ponena za “masiku otsiliza.” (2 Tim. 3:1-5) Kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu, kumene palibe munthu angatsutse, ni umboni wakuti Khristu Yesu akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kuwonjezela pa ulosi umenewu, palinso maulosi ena ambili okamba za Ufumu. Maulosi osiyana-siyana amenewo, amatithandiza kudziŵa bwino pamene tafika na zocitika pa pulogilamu ya Yehova. w22.07 2 ¶1-2
Cisanu, December 13
Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.—Mat. 11:19.
Pa nthawi ya mlili wa COVID-19, tinalandila malangizo omveka bwino a mocitila misonkhano ya mpingo na ulaliki. Mwamsanga ndithu, tinayamba kucita misonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo kupitila pa vidiyo. Cina, tinayamba kucita kwambili ulaliki wa makalata komanso wa pafoni. Yehova anadalitsa khama lathu. Malipoti a maofesi ambili a nthambi aonetsa kuti ciŵelengelo ca ofalitsa cawonjezeka kwambili. Ndipo ambili anakhala na zocitika zolimbikitsa za mu ulaliki panthawi ya mliliwo. Mwina ena anali kuona kuti gulu lathu likukhwimitsa kwambili zinthu panthawi ya mliliwu. Koma nthawi zonse, zinali kuonekelatu kuti malangizo amene talandila ni anzelu. Ndipo tikamaganizila mmene Yesu amatsogolela anthu ake mwacikondi, timakhala otsimikiza kuti kaya tikumane na zotani kutsogoku, Yehova na Mwana wake wokondeka adzakhalabe nafe.—Aheb. 13:5, 6. w22.07 13 ¶15-16
Ciŵelu, December 14
Muzipemphela mosalekeza. Muziyamika pa ciliconse, pakuti cimeneci ndi cifunilo ca Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.—1 Ates. 5:17, 18.
Kuwonjezela pa kum’tamanda Yehova m’mapemphelo athu, tiyenelanso kumuyamikila pa zabwino zimene amatipatsa. Mwacitsanzo, tingamuyamikile pa maluŵa amitundu-mitundu, zakudya zabwino zosiyana-siyana, komanso mabwenzi a pamtima otsitsimula. Atate wathu wacikondi amatipatsa zinthu zimenezi na zina zambili kuti tizikondwela. (Sal. 104:12-15, 24) Ndipo coposa zonse, timamuyamikila Yehova cifukwa ca cakudya cauzimu ca mwana alilenji cimene amatipatsa, ndiponso ciyembekezo cabwino ca zam’tsogolo. Tikhoza kuiŵala kumuyamikila Yehova pa zonse zimene amaticitila. Ndiye n’ciyani cingatithandize kuti tizikumbukila? Tingalembe mndandanda wa mapempho athu acindunji, ndipo nthawi na nthawi tiziona mmene Yehova watiyankhila. Kenako, timuyamikile pa thandizo lake.—Akol. 3:15. w22.07 22 ¶8-9
Sondo, December 15
Amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku.—Sal. 1:2.
Tidziŵa kuti kungophunzila coonadi pakokha sikokwanila. Kuti tipindule kwambili, tiyenela kukhala m’coonadi. Kutanthauza kuti tiyenela kugwilitsa nchito zimene timaphunzila pa umoyo wathu. Tikatelo, coonadi cidzatibweletsela cimwemwe ceniceni. (Yak. 1:25) Tingacite ciyani kuti tionetsetse kuti tikukhala m’coonadi? M’bale wina anakamba kuti tiyenela kudzifufuza kuti tione zimene timacita bwino, na zimene siticita bwino kuti tiwongolele. Mtumwi Paulo anati: “Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenela m’njila yomweyo.” (Afil. 3:16) Tangoganizilani mapindu amene timapeza tikamayesetsa ‘kuyendabe m’coonadi.’ Timakhala na umoyo wabwino, komanso timakondweletsa Yehova na okhulupilila anzathu. (Miy. 27:11; 3 Yoh. 4) Izi n’zifukwa zabwino zotipangitsa kukonda coonadi, na kugwilitsa nchito zimene timaphunzila. w22.08 18-19 ¶16-18
Mande, December 16
Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.—1 Pet. 5:2.
Kodi akulu angaonetse bwanji kuti amakonda Yehova na Yesu? Njila imodzi yofunika ni kusamalila zosoŵa za nkhosa za Yesu. (1 Pet. 5:1, 2) Yesu anaimveketsa bwino mfundoyi kwa mtumwi Petulo. Pambuyo pokana Yesu katatu, Petulo ayenela kuti anali kufunitsitsa kuonetsa kuti amam’konda Yesu. Yesu ataukitsidwa, anafunsa Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Sitikayikila kuti Petulo anali wokonzeka kucita ciliconse poonetsa kuti anali kukonda Mbuye wake. Yesu anauza Petulo kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Pa umoyo wake wonse, Petulo anasamalila nkhosa za Ambuye mwacikondi, poonetsa kuti anali kum’konda Yesu. Inu akulu, kodi mungaonetse bwanji kuti mawu amene Yesu anauza Petulo ni ofunika kwa inu? Mungaonetse kuti mumam’konda Yehova na Yesu, mwa kucita maulendo aubusa nthawi zonse, komanso kuyesetsa kuthandiza ozilala kubwelela kwa Yehova.—Ezek. 34:11, 12. w23.01 29 ¶10-11
Ciŵili, December 17
Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile.—1 Akor. 10:13.
Pewani kuganiza kuti palibe angamvetse vuto limene mukulimbana nalo. Kuganiza mwanjila imeneyi kungakupangitseni kuona kuti vuto lanu silingathe, na kuti palibe zimene mungacite kuti mugonjetse zilakolako zoipazo. Baibo imati: “Pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” Conco, ngakhale cilakolako coipa cikhale camphamvu motani, n’zotheka kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Ndipo mwa thandizo lake, tidzapewa kucita zinthu motsatila zilakolako zathu. Nthawi zonse muzikumbukila mfundo iyi: Pokhala anthu opanda ungwilo, sitingaletse zilakolako zoipa kubwela m’maganizo mwathu. Koma zikabwela m’maganizo mwanu, muyenela kuzicotsa mwamsanga, monga anacitila Yosefe kuthaŵa mkazi wa Potifara mwamsanga. (Gen. 39:12) Musazitsatile zilakolako zanu zoipazo. w23.01 12-13 ¶16-17
Citatu, December 18
Mulungu alibe tsankho.—Aroma 2:11.
Cilungamo ni khalidwe linanso la Yehova. (Deut. 32:4) Khalidwe limeneli n’logwilizana kwambili na kupanda tsankho, ndipo Yehova sakondela. (Mac. 10:34, 35) Kupanda tsankho kwake kumaonekela bwino tikaona zinenelo zimene anagwilitsa nchito polemba Baibo. Yehova analonjeza kuti m’nthawi yamapeto anthu oculuka “adzadziŵa zinthu zambili zoona” zopezeka m’Baibo. (Dan. 12:4) Njila imodzi imene yathandiza anthu oculuka kuimvetsa Baibo, ni kupitila m’nchito yomasulila Baibo, na mabuku ofotokozela Baibo, kuwafalitsa, na kuwagaŵila kwa anthu. Pofika pano, anthu a Yehova amasulila Mawu a Mulungu athunthu kapena mbali yake m’zinenelo zopitilila 240. Ndipo munthu aliyense akhoza kulipeza Baibo popanda kulipila. Cotulukapo n’cakuti anthu a mitundu yonse akumvetsela ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Mulungu wathu wacilungamo akupeleka mwayi kwa anthu ambili kuti amudziŵe mwa kuŵelenga Mawu ake. Akucita zimenezi cifukwa tonsefe amatikonda kwambili. w23.02 5 ¶11-12
Cinayi, December 19
Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma 12:2.
Kodi inu cilungamo mumacikonda? Mosakayika konse. Koma popeza kuti tonse ndife opanda ungwilo, ngati sitingasamale tingayambe kuona cilungamo mmene dzikoli limacionela. (Yes. 5:20) Anthu ambili amaganiza kuti munthu wolungama ni munthu wonyada, wokonda kuweluza ena, kapena amene amadziona kuti ni wocita bwino kwambili kuposa ena. Koma Mulungu sakondwela nawo makhalidwe amenewa. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anadzudzula mwamphamvu atsogoleli acipembedzo cifukwa cokhazikitsa malamulo awo-awo pa nkhani ya cilungamo. (Mlal. 7:16; Luka 16:15) Munthu amene amacita zimene Yehova amati n’zoyenela, saona kuti amacita bwino kuposa ena. Cilungamo ni khalidwe labwino ngako. Mwacidule, tingati cilungamo cimatanthauza kucita zoyenela pamaso pa Yehova Mulungu. M’Baibo, mawu otanthauzila “cilungamo” amapeleka lingalilo la kutsatila mfundo zapamwamba kwambili za Yehova. w22.08 27 ¶3-5
Cisanu, December 20
Ndakuchani mabwenzi.—Yoh. 15:15.
Ngakhale kuti ophunzila a Yesu anali kulakwitsa zinthu zina, iye anali kuwadalilabe. (Yoh. 15:16) Pamene Yakobo na Yohane anapempha Yesu kuti akawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu, iye sanakayikile zolinga zawo potumikila Yehova, kapena kuwacotsa pa utumwi. (Maliko 10:35-40) Patapita nthawi, ophunzila ake onse anathaŵa n’kumusiya yekha usiku wakuti aphedwa maŵa lake. (Mat. 26:56) Ngakhale n’conco, Yesu sanaleke kuwadalila. Anali kudziŵa kuti iwo anali opanda ungwilo, koma “anawakonda mpaka pa mapeto a moyo wake.” (Yoh. 13:1) Ndipo Yesu ataukitsidwa, anapatsa ophunzila ake 11 okhulupilika udindo waukulu wotsogolela pa nchito yopanga ophunzila, na kusamalila nkhosa zake za mtengo wapatali. (Mat. 28:19, 20; Yoh. 21:15-17) Iye anali na zifukwa zabwino zowadalila ophunzila ake opanda ungwilo. Onse anatumikila mokhulupilika mpaka mapeto a moyo wawo wa padziko lapansi. Kukamba zoona, Yesu ni citsanzo cabwino pa nkhani yodalila anthu opanda ungwilo. w22.09 6 ¶12
Ciŵelu, December 21
Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.—Sal. 118:6.
Tikakhulupilila kuti Yehova amatikonda komanso kuti ali kumbali yathu, tingagonjetse mayeso a Satana otipangitsa kuti ticite mantha. Mwacitsanzo, wolemba Salimo 118 anakumana na zinthu zina zothetsa nzelu. Iye anali na adani ambili, ndipo ena anali anthu audindo (vesi 9, 10). Nthawi zina anali kukhala wopanikizika kwambili (vesi 13). Cina, Yehova anam’patsa cilango camphamvu (vesi 18). Ngakhale zinali conco, wamasalimoyo anaimba kuti: “Sindidzaopa.” Iye anadziŵa kuti Yehova, Atate wake wakumwamba, anali kum’konda olo kuti anam’patsa cilango. Wamasalimoyo anali na cidalilo cakuti kaya akumane na mavuto otani, Mulungu wake wacikondi adzapitiliza kumuthandiza. (Sal. 118:29) Tiyenela kukhulupilila kuti Yehova amatikonda. Kukhulupilila zimenezi kudzatithandiza kugonjetsa mantha amene timakhala nawo, monga, (1) nkhawa yakuti sitidzakwanitsa kupeza zofunikila za banja lathu; (2) kuopa anthu, ndiponso (3) kuopa imfa. w22.06 15 ¶3-4
Sondo, December 22
Wodala ndi munthu wopilila mayeselo, chifukwa akadzavomelezedwa, adzalandila mphoto ya moyo, umene Yehova analonjeza onse omukonda.—Yak. 1:12.
Tizionetsetsa kuti tikuika kulambila Yehova patsogolo mu umoyo wathu. Yehova pokhala Mlengi wathu, ni woyenela kuti ife tizim’lambila. (Chiv. 4:11; 146, 7) Conco, tiyenela kuika patsogolo kulambila Mulungu m’njila imene iye amavomeleza, “motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.” (Yoh. 4:23, 24) Timafuna kuti mzimu woyela wa Mulungu uzititsogolela pa kulambila kwathu kuti kulambilako kukhale kogwilizana na mfundo za coonadi copezeka m’Mawu ake. Tiyenela kuika patsogolo kulambila kwathu olo kuti tikhala m’dziko limene nchito yathu inaikilidwa ziletso kapena kutsekedwa. Pano tikamba, abale na alongo oposa 100 ali m’ndende cabe cifukwa ni Mboni za Yehova. Ngakhale n’telo, iwo amacita mwacimwemwe zonse zimene angathe kuti azipemphela, kuŵelenga Mawu a Mulungu, na kuuzako ena za iye na Ufumu wake. Anthu akatinyoza kapena kutizunza, tingakhale acimwemwe podziŵa kuti Yehova ali nafe, ndiponso kuti adzatifupa.—1 Pet. 4:14. w22.10 9 ¶13
Mande, December 23
Nzelu zimateteza.—Mlal. 7:12.
M’buku lonse la Miyambo, muli uphungu wothandiza umene tingapindule nawo tikamaugwilitsa nchito. Onankoni zitsanzo ziŵili za uphungu wanzelu umenewo. Coyamba, muzikhutila na zimene muli nazo. Miyambo 23:4, 5 imapeleka langizo ili lakuti: “Usamadzitopetse ndi nchito kuti upeze cuma. . . . Cifukwa ndithu cimadzipangila mapiko ngati a ciwombankhanga n’kuulukila kumwamba.” Anthu olemela komanso osauka amadzitopetsa kufuna-funa cuma. Kudzitangwanitsa kotelo nthawi zambili kumawapangitsa kucita zinthu zimene zimawononga mbili yawo, ubwenzi wawo na ena, komanso ngakhale thanzi lawo. (Miy. 28:20; 1 Tim. 6:9, 10) Caciŵili, muziyamba mwaganiza musanalankhule. Ngati sitisamala, mawu athu akhoza kupweteka ena. Miyambo 12:18 imati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.” Timateteza ubale wathu na anthu ena ngati timapewa kuwajeda pa zolakwa zawo.—Miy. 20:19. w22.10 21 ¶14; 22 ¶16-17
Ciŵili, December 24
Idya mpukutu umene ndikukupatsawu, [ndipo] pita pakati pa nyumba ya Isiraeli ndipo ukawauze mawu anga.—Ezek. 3:3, 4.
Ezekieli anafunika kuumvetsetsa uthenga umene anali kudzaulengeza. Iye anafunika kuukhulupilila uthengawo kuti um’sonkhezele kukaulengeza kwa Aisiraeli. Ezekieli ataudya mpukutuwo, anaona kuti “unali wotsekemela ngati uci.” (Ezek. 3:3) Cifukwa ciyani? Kwa Ezekieli, kuimilako Yehova unali mwayi wotsekemela, kapena wokondweletsa. (Sal. 19:8-11) Iye anamuyamikila kwambili Yehova pomusankha kuti akhale mneneli wake. Patapita nthawi, Yehova anauza Ezekieli kuti: “Usunge mumtima mwako mawu anga onse amene ndikukuuza.” (Ezek. 3:10) Na mawu amenewa, Yehova anauza Ezekieli kuti azikumbukila mumtima wake mawu olembedwa mu mpukutuwo na kuwasinkhasinkha. Kucita zimenezo kunam’limbikitsa kwambili Ezekieli. Cina, mu mpukutuwo munali uthenga wamphamvu umene anafunika kukaulengeza kwa anthu. (Ezek. 3:11) Uthenga wa Mulungu utakhazikika mu mtima mwake komanso pa milomo yake, Ezekieli anali wokonzeka kugwila nchito yolalikila mpaka kumapeto kwake. w22.11 6 ¶12-14
Citatu, December 25
Kumvela kuposa nsembe.—1 Sam. 15:22.
Ngati masinthidwe a gulu ayesa kukhulupilika kwanu, kodi muyenela kucita ciayni? Alabadileni na mtima wonse. Pa ulendo wawo wa m’cipululu, Akohati anali kunyamula likasa la pangano patsogolo pa anthu. (Num. 3:29, 31; 10:33; Yos. 3:2-4) Umenewo unali mwayi waukulu kwambili. Koma zinthu zinasintha pamene Aisiraeli anakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa. Likasalo silinafunikenso kumanyamulidwa kaŵili-kaŵili. Conco, Akohati anapatsidwa mautumiki ena. (1 Mbiri 6:31-33; 26:1, 24) Palibe paliponse m’Baibo pamene paonetsa kuti Akohati anadandaula kapena kufuna malo apamwamba cifukwa cakuti kumbuyoku anali kucita utumiki wapadela. Kodi tiphunzilapo ciyani? Tizilabadila na mtima wonse masinthidwe alionse amene gulu la Yehova lapanga, kuphatikizapo amene akhudza utumiki wathu. Tizisangalala na utumiki uliwonse umene tapatsidwa. Kumbukilani kuti utumiki wanu sindiwo umapangitsa kuti mukhale wofunika kwambili kwa Yehova. Iye amaona kuti kumvela ndiko kofunika kwambili kuposa utumiki uliwonse. w22.11 23 ¶10-11
Cinayi, December 26
Sanacite manyazi ndi maunyolo anga.—2 Tim. 1:16.
Onesiforo anafuna-funa mtumwi Paulo mwakhama, ndipo atam’peza anapeleka thandizo lofunikila kwa iye. Pocita zimenezo, iye anaika moyo wake pa ciwopsezo. Kodi tiphunzilapo ciyani? Tisalole kuti kuopa anthu kutilepheletse kuthandiza abale athu amene akuzunzidwa. Koma tiziwakhalila kumbuyo na kuwathandiza. (Miy. 17:17) Iwo afunikila cikondi cathu na thandizo lathu. Ganizilani mmene abale na alongo athu ku Russia akuthandizila abale awo amene ali m’ndende. Ena mwa abale athu akapita kukaonekela pamaso pa khoti, abale na alongo ambili amapita kukhotiko kukawalimbikitsa. Kodi tiphunzilapo ciyani? Abale otsogolela akanenezedwa, akamangidwa, kapena akamazunzidwa, tisamacite mantha. Koma tiziwapemphelela, kuthandiza a m’banja mwawo, komanso kuyesa kupeza njila zina za mmene tingawathandizile.—Mac. 12:5; 2 Akor. 1:10, 11. w22.11 17 ¶11-12
Cisanu, December 27
Amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa.—Akol. 4:11.
Akulu ali na udindo wopeleka thandizo lauzimu kwa abale na alongo, komanso kulimbikitsa amene ali na nkhawa. (1 Pet 5:2) Pakagwa tsoka, coyamba akulu ayenela kuonetsetsa kuti m’bale na mlongo aliyense ni wotetezeka, ali na cakudya, zovala komanso pokhala. Koma kwa miyezi ndithu pambuyo pake, opulumuka tsokawo angafunikile kuwalimbikitsa mwauzimu na kuwatonthoza. (Yoh. 21:15) M’bale Harold wa m’Komiti ya Nthambi, amene anakambilanapo na abale na alongo ambili amene akhudzidwapo na matsoka anati, “Zimatenga nthawi kuti ayambe kuiŵala zimene zinawagwela. Iwo angaiŵale zinthu zina zimene anatayikilidwa. Koma zingatenge nthawi kuti aiŵale wokondedwa wawo amene anafa pa tsokalo, cuma cawo ca mtengo wapatali cimene cinatayika, kapena mmene analipulumukila tsokalo. Pokumbukila zimenezi, angayambenso kumva cisoni. Izi zikacitika n’cibadwa kumva conco, osati kuti alibe cikhulupililo.” Akulu saiŵala mfundo yakuti ayenela ‘kulila ndi anthu amene akulila.’—Aroma 12:15. w22.12 22 ¶1; 24-25 ¶10-11
Ciŵelu, December 28
Pitilizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatila cilakolako ca thupi ngakhale pang’ono.—Agal. 5:16.
Pofuna kutithandiza kuti tipambane pa nkhondo yolimbana na zilakolako zoipa, Yehova mowolowa manja amatipatsa mzimu wake woyela. Tikamaŵelenga Mawu a Mulungu, timalola mzimu woyela kutsogolela zocita zathu. Timalandilanso mzimu woyela tikamapezeka ku misonkhano. Pa misonkhano imeneyo, timakhala na nthawi yoceza na abale na alongo, amene mofanana na ife amayesetsa kucita zabwino, ndipo izi zimatilimbikitsa. (Aheb. 10:24, 25; 13:7) Cina, tikamacondelela Yehova mocokela pansi pa mtima kuti atithandize kugonjetsa zifooko, iye adzatigaŵila mzimu wake woyela umene udzatipatsa mphamvu zopitiliza kumenya nkhondoyo. N’zoona kuti kucita zimenezi sikungathetse zilakolako zoipa. Koma kudzatithandiza kupewa kucita zinthu motsatila zilakolako zimenezo. Tikangokhazikitsa pulogilamu yocita zauzimu, tiyenela kumamatilabe pulogilamu imeneyo na kupitiliza kukulitsa zikhumbo zabwino. w23.01 11 ¶13-14
Sondo, December 29
Sindidzalola kuti cinthu cina cizindilamulila.—1 Akor. 6:12.
Ngakhale kuti Baibo si buku la zacipatala kapena lophunzitsa za thanzi, imafotokoza maganizo a Yehova pa nkhani zimenezi. Mwacitsanzo, iye amatilangiza kuti ticotse zinthu zimene zingawononge thupi lathu. (Mlal. 11:10) Baibo imati tizipewa kudya kwambili na kumwa kwambili, cifukwa zimaika moyo wathu pa ciwopsezo. (Miy. 23:20) Yehova amafuna kuti tizisankha zimene timadya na kumwa, komanso kuculuka kwake. (1 Akor. 9:25) Mwa kugwilitsa nchito luntha la kuzindikila, tikhoza kupanga zisankho zoonetsa kuti mphatso ya Mulungu ya moyo timailemekeza kwambili. (Sal. 119:99, 100; Miy. 2:11) Mwacitsanzo, timakhala osamala kwambili na zakudya zimene timadya. Ngati timakonda cakudya cina cake koma tapeza kuti cimatidwalitsa, nzelu zimatithandiza kucipewa. Cina, timaonetsa kuti ndife oganiza bwino tikamagona mokwanila, tikamacita maseŵela olimbitsa thupi nthawi zonse, komanso tikamasunga mathupi athu na nyumba zathu zili zaukhondo. w23.02 21 ¶6-7
Mande, December 30
Umaŵelengamo zotani?—Luka 10:26.
Kodi tingacite ciyani kuti tizipeza cuma cauzimu poŵelenga Baibo? Ganizilani zimene 2 Timoteyo 3:16, 17 imakamba. Lembali limakamba kuti “Malemba onse . . . ndi opindulitsa” pa (1) kuphunzitsa, (2) kudzudzula, (3) kuwongola zinthu, komanso (4) kulangiza. Mapindu anayi amenewa mungawapeze ngakhale m’mabuku ena a m’Baibo amene simumaŵelenga kaŵili-kaŵili. Unikani nkhani imene mukuŵelenga kuti muone zimene ikukuphunzitsa za Yehova, colinga cake, kapena zokhudza mfundo zaumulungu. Onaninso mmene nkhaniyo ilili yothandiza pa kudzudzula. Citani izi mwa kuona mmene mavesi ake akukuthandizilani kuzindikila, mwa kupewa maganizo na makhalidwe oipa kuti mukhalebe wokhulupilika kwa Yehova. Cina, onani mmene nkhani imene mukuŵelenga mungaigwilitsile nchito poongola zinthu, mwina maganizo olakwika a munthu amene munakumana naye mu ulaliki. Ndiyeno, yesani kupeza mfundo zothandiza pa kulangiza zimene zingakuphunzitseni kuti muziona zinthu mmene Yehova amazionela. Mukamakumbukila mapindu anayi amenewa poŵelenga malemba, muzipeza cuma cauzimu cimene cidzapangitsa kuti kuŵelenga Baibo kwanu kuzikhala kwaphindu. w23.02 11 ¶11
Ciŵili, December 31
Ufumu wake sudzawonongedwa.—Dan. 7:14.
Ulosi wina wa m’buku la Danieli unakambilatu kuti Yesu adzalandila Ufumu wake kumapeto kwa nyengo yochedwa nthawi zokwanila 7. Kodi n’zotheka kudziŵa nthawi pamene cocitika cosangalatsaci cinacitika? (Dan. 4:10-17) “Nthawi zokwanila 7” ziimila nyengo ya zaka 2,520. Nyengo imeneyo inayamba mu 607 B.C.E. pamene Ababulo anacotsa mfumu yothela pa mpando wacifumu wa Yehova ku Yerusalemu. Inatha mu 1914 C.E. pamene Yehova anaika Yesu, “amene ali woyenelela mwalamulo,” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Ezek. 21:25-27) Kodi ulosi umenewu umatipindulila bwanji? Kudziŵa bwino “nthawi zokwanila 7” zimenezi, kumatipatsa cidalilo cakuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake pa nthawi yake. Monga mmene anaikilatu nthawi yokhazikitsa Ufumu wake, iye adzaonetsetsanso kuti maulosi ena onse akwanilitsidwa pa nthawi yake yoikika. Inde, tsiku la Yehova ‘silidzacedwa.’—Hab. 2:3. w22.07 3 ¶3-5