December
Mande, December 1
Akufa amaukitsidwa.—Luka 20:37.
Kodi Yehova ali na mphamvu zoukitsa akufa? Mosapeneka konse! Iye ni ‘Wamphamvuzonse.’ (Chiv. 1:8) Conco, ali na mphamvu zacikwanekwane zogonjetsa mdani aliyense kuphatikizapo imfa. (1 Akor. 15:26) Cina cimene timadziŵila kuti Mulungu akhoza kuukitsa akufa n’cakuti iye amakumbukila cina ciliconse. Amachula dzina la nyenyenyezi iliyonse. (Yes. 40:26) Conco, amakumbukilanso amene anamwalila. (Yobu 14:13; Luka 20:38) Angakumbukile mosavuta ngakhale zinthu zing’ono-zing’ono zokhudza amene iye adzawaukitsa, monga maonekedwe na umunthu wawo, zinawacitikila mu umoyo, komanso zimene zinali m’maganizo mwawo. Mwacionekele, tingalikhulupilile lonjezo la Yehova lakuti kutsogolo akufa adzauka, cifukwa tidziŵa kuti ali na cifuno komanso mphamvu zotha kukwanilitsa lonjezolo. Cifukwa cina cokhulupilila lonjezo la Mulungu la ciukitso n’cakuti Yehova kumbuyoku anaukitsapo anthu ena. M’nthawi za anthu a m’Baibo, Mulungu anapatsa Yesu komanso amuna ena mphamvu zoukitsa akufa. w23.04 9-10 ¶7-9
Ciŵili, December 2
Nthawi zonse mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima ndipo azikhala okoma ngati kuti mwawathila mcele.—Akol. 4:6.
Tikafotokoza cikhulupililo cathu mwaluso komanso mofatsa, anthu angakhale ofunitsitsa kumvetsela na kupitiliza makambilano. Komabe, ngati munthu angofuna kukangana nafe, kapena kutinyodola pa cikhulupililo cathu, sitiyenela kupitiliza makambilanowo. (Miy. 26:4) Koma ni anthu ocepa cabe amene angacite zimenezi, ambili angakhale ofunitsitsa kumvetsela. N’zoonekelatu kuti kudziikila colinga cokhala wofatsa kuli na mapindu ambili. Muzipemphela kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu zofunikila kuti mukhalebe ofatsa poyankha anthu otsutsa kapena onyodola. Kumbukilani kuti kukhala wofatsa kungathandize kuti kusiyana maganizo kusakule n’kukhala mkangano. Ndipo kuyankha kwanu mofatsa kungalimbikitse anthu ena kusintha kapenyedwe kawo pa ife komanso pa coonadi ca m’Baibo. “Khalani okonzeka nthawi zonse” kuteteza cikhulupililo canu. “Koma muziwayankha mofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.” (1 Pet. 3:15) Inde, pangani kufatsa kukhala khalidwe lanu lalikulu! w23.09 19 ¶18-19
Citatu, December 3
Valani . . . kuleza mtima.—Akol. 3:12.
Tingakhale oleza mtima m’njila zinayi izi. Yoyamba, munthu woleza mtima sakwiya msanga. Amayesetsa kukhalabe wodekha, na kusabwezela anthu ena akamukhumudwitsa kapena akapanikizika maganizo. (Eks. 34:6) Yaciŵili, munthu woleza mtima amayembekezela modekha. Ngati cinthu sicinacitike panthawi imene anali kuciyembekezela, iye amakhalabe wodekha, ndipo sakhumudwa. (Mat. 18:26, 27) Yacitatu, munthu woleza mtima sacita zinthu mwaphuma. Munthu woleza mtima akamagwila nchito yofunika kwambili, saigwila mothamanga kuti aimalize mmangu-mmangu. M’malo mwake, amapatula nthawi yokwanila yolinganiza bwino mmene agwilile nchitoyo. Kenaka, amadekha poigwila. Yacinayi, munthu woleza mtima amayesetsa kupilila mavuto popanda kudandaula. Munthu woleza mtima amakhalanso wopilila. Koma amaganizila madalitso amene ali nawo, ndipo amatumikilabe Yehova mwacimwemwe. (Akol. 1:11) Monga Akhristu, tiyenela kukhala oleza mtima pambali zonsezi. w23.08 20-21 ¶3-6
Cinayi, December 4
Yehova ndi amene amayesa mitima.—Miy. 17:3.
Cifukwa cacikulu cotetezela mtima wathu wophiphilitsa, n’cakuti Yehova amasanthula mitima yathu. Izi zitanthauza kuti iye amaona umunthu wathu wamkati umene anthu saona. Iye adzatikonda tikamadzaza mitima yathu na nzelu zake zopatsa moyo. (Yoh. 4:14) Tikatelo, tidzapewa makhalidwe oipa, komanso mabodza a Satana na dziko lake. (1 Yoh. 5:18, 19) Ndipo tikamayandikila kwambili Yehova, tidzayamba kum’konda ngako na kum’lemekeza. Popeza sitifuna kukhumudwitsa Atate wathu, tidzapewa ngakhale maganizo ofuna kucita zoipa. Mlongo Marta wa ku Croatia, amene anayesedwa kucita zaciwelewele anati: “Sicinali copepuka kwa ine kuganiza bwino, komanso kugonjetsa cilakolako cofuna kucita zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo. Koma kuopa Yehova kunaniteteza.” Kodi kunam’teteza bwanji? Mlongoyo anati anasinkhasinkha zotsatilapo za cisankho coipa. Nafenso tizicita cimodzimodzi. w23.06 20-21 ¶3-4
Cisanu, December 5
Anthu a mitundu inawo adzadziŵa kuti ine ndine Yehova, akadzaona zimene ndakucitilani komanso adzadziŵa kuti ndine Mulungu woyela,’ akutelo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.—Ezek. 36:23.
Yesu anali kudziŵa kuti colinga ca Yehova ni kuyeletsa dzina Lake, kucotsa citonzo ciliconse pa dzinalo. Ndiye cifukwa cake Ambuye wathu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.” (Mat. 6:9) Yesu anadziŵa kuti iyi ndiyo nkhani yaikulu imene ikhudza cilengedwe conse. Pa zolengedwa zonse zanzelu, palibe amene wacita zambili poyeletsa dzina la Yehova kuposa Yesu. Ngakhale n’telo, adani ake atamugwila, anamuimba mlandu wakuti ananyoza Mulungu! Yesu anadziŵa bwino kuti kunyoza dzina loyela la Atate wake, kapena kulineneza linali chimo lalikulu zedi. Iye anasokonezeka maganizo kwambili poona kuti akumugwila na kumupeza na mlandu pa nkhani imeneyi. Ici ciyenela kuti ndico cinali cifukwa cacikulu comwe cinacititsa Yesu ‘kuzunzika koopsa mumtima mwake’ kutatsala maola ocepa kuti amugwile.—Luka 22:41-44. w24.02 11 ¶11
Ciŵelu, December 6
Nzelu zimamanga nyumba ya munthu.—Miy. 24:3.
Pa mpikisano wathu wokalandila moyo, tizim’konda kwambili Yehova komanso Yesu kuposa mmene timakondela acibale athu. (Mat. 10:37) Koma izi sizitanthauza kuti tiyenela kunyanyala maudindo athu m’banja, poganiza kuti angatilepheletse kukondweletsa Mulungu na Khristu. Kuti Mulungu na Khristu atiyanje, tizikwanilitsa maudindo athu m’banja. (1 Tim. 5:4, 8) Tikatelo, tidzakhala acimwemwe. Yehova adziŵa kuti banja limakhala lacimwemwe ngati mwamuna na mkazi amakondana na kulemekezana, makolo amakonda ana awo na kuwaphunzitsa, komanso ngati ana amamvela makolo awo. (Aef. 5:33; 6:1, 4) Kaya udindo wanu ni wotani m’banja, muzidalila ulangizi wa m’Baibo. Musamacite zinthu motengela mmene mukumvela, cikhalidwe ca kwanuko, kapena zimene ochedwa alangizi a mabanja amanena. Muzifufuza m’zofalitsa zathu kuti mupeze malangizo othandiza a m’Baibo, na kuona mmene mungawagwilitsile nchito. w23.08 28 ¶6-7
Sondo, December 7
Uziliŵelenga ndi kuganizila mozama masana ndi usiku, kuti uzitsatila bwino-bwino zonse zimene zalembedwamo. Ukamatelo, zizikuyendela bwino ndipo uzicita zinthu mwanzelu.—Yos. 1:8.
Mkazi wacikhristu ayenela kuphunzila maluso othandiza. Maluso amene mtsikana amaphunzila ali mwana, amakhalabe othandiza pa umoyo wake wonse. Mwacitsanzo, phunzilani kuŵelenga na kulemba. M’zikhalidwe zina, amaona kuti m’posafunika kuti akazi aphunzile kuŵelenga na kulemba. Komabe malusowa ni ofunika kwambili kwa Mkristu aliyense. (1 Tim. 4:13) Conco, musalole ciliconse kukulepheletsani kukulitsa luso loŵelenga na kulemba bwino. Kodi mudzapindula motani? Maluso amenewa adzakuthandizani kupeza nchito na kukhalitsa pa nchitoyo. Cidzakhala cosavuta kwa inu kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuphunzitsa ena. Koposa zonse, adzakuthandizani kumuyandikila kwambili Yehova pamene mukuŵelenga na kusinkhasinkha Mawu ake.—1 Tim. 4:15. w23.12 20 ¶10-11
Mande, December 8
Yehova amadziŵa kupulumutsa anthu odzipeleka kwa iye akakhala pa mayeselo.—2 Pet. 2:9.
Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukaniza mayeselo. Pokhala anthu opanda ungwilo, nthawi zonse timalimbana na mayeselo ofuna kucita zinthu zoipa. Satana akucita ciliconse cotheka kuti cikhale covuta kwa ife kukaniza mayeselo amenewa. Imodzi mwa njila zimene amagwilitsa nchito pofuna kuwononga kaganizidwe kathu, ni kuonelela zosangalatsa zoipa. Zosangalatsa zimenezo zingapangitse kuti tikhale na maganizo oipa. Ndipo maganizo oipawo angacititse kuti tikhale odetsedwa pamaso pa Yehova, komanso angatitsogolele ku chimo lalikulu. (Maliko 7:21-23; Yak. 1:14, 15) Tifunikila thandizo la Yehova kuti tikanize mayeselo akuti ticite zoipa. M’pemphelo lake lacitsanzo, Yesu anachula cinanso cimene tingapemphe. Anati: “Musatiloŵetse m’mayeselo, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Yehova afuna kutithandiza, koma tiyenela kum’pempha kuti atithandize. Cina, tiyenela kucita mogwilizana na mapemphelo athu. w23.05 6-7 ¶15-17
Ciŵili, December 9
Cingwe copotedwa ndi zingwe zitatu sicingaduke msanga.—Mlal. 4:12.
Okwatilana akamaona ubale wawo na Atate wawo wakumwamba kukhala wofunika, amaseŵenzetsa ulangizi wake. Akatelo, amapewa komanso kuthana na mavuto amene angapangitse cikondi cawo kuzima. Anthu auzimu amayesetsa kutengela makhalidwe a Yehova, monga kukoma mtima, kuleza mtima, komanso kukhululuka. (Aef. 4:32–5:1) Okwatilana akamaonetsana makhalidwe amenewa, cikondi cawo cimakula. Mlongo Lena, amene wakhala mu ukwati zaka zoposa 25 anati: “Ngati mnzako wa mu ukwati ni wauzimu, n’cosavuta kum’konda na kum’lemekeza.” Ganizilani citsanzo ici ca m’Baibo. Pakati pa mbadwa zonse za Davide, Yehova anasankha Yosefe na Mariya kuti akhale makolo a Mesiya. Cifukwa ninji? Cifukwa onse aŵili anali pa ubale wolimba na Yehova, ndipo anadziŵa kuti cifukwa com’konda, banja lawo lidzakhala lolimba mwauzimu. w23.05 21 ¶3-4
Citatu, December 10
Muzimvela amene akukutsogolelani.—Aheb. 13:17.
Mtsogoleli wathu Yesu, ni wangwilo. Koma anthu amene akuseŵenzetsa kuti atitsogolele pano padziko lapansi, ni opanda ungwilo. Cingakhale covuta kuwamvela maka-maka ngati atipempha kucita zinthu zimene sitifuna. Panthawi ina, mtumwi Petulo sanafune kutsatila malangizo amene anapatsidwa. Mngelo atamuuza kuti adye nyama zimene zinali zoletsedwa malinga na Cilamulo ca Mose, mtumwi Petulo anakana—osati kamodzi, koma katatu konse! (Mac. 10:9-16) Cifukwa ciyani? Cifukwa sanawakonde malangizo atsopano amenewo. Koma Mtumwi Paulo anamvela’ pamene Akhristu acikulile ku Yerusalemu, anamuuuza kuti atenge amuna anayi na kupita nawo ku kacisi kuti akadziyeletse malinga na mwambo poonetsa kuti anali kusunga Cilamulo ca Mose. Paulo anali kudziŵa kuti Akhristu sanalinso pansi pa Cilamulo ca Mose, ndipo sanalakwitse ciliconse. Ngakhale n’telo “tsiku lotsatila, Paulo anatenga amunawo nʼkukacita nawo mwambo wa kudziyeletsa.” (Mac. 21:23, 24, 26) Kumvela kwa Paulo kunalimbikitsa mgwilizano pakati pa abale.—Aroma 14:19, 21. w23.10 10 ¶15-16
Cinayi, December 11
Anthu amene amaopa Yehova ndi amene amakhala naye pa ubwenzi wolimba.—Sal. 25:14.
N’kutheka kuti simunaganizileko za mantha kukhala khalidwe lofunika popalana ubwenzi wabwino na ena. Komabe, aja amene afuna kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova ayenela ‘kumuopa.’ Kaya tatumikila Yehova kwa utali wotani, tonsefe tiyenela kupitilizabe kumuopa kwambili. Koma kodi kuopa Mulungu kumatanthauzanji? Munthu amene ali na mantha oyenela amakonda Mulungu, ndipo sangacite ciliconse cimene cingawononge ubwenzi wake na iye. Yesu anali na mantha otelo aumulungu. (Aheb. 5:7) Iye sanali kuopa Yehova mopambanitsa. (Yes. 11:2, 3) M’malo mwake, anali kum’konda kwambili ndiponso anali kumumvela. (Yoh. 14:21, 31) Monga Yesu, nafenso timam’lemekeza kwambili Yehova cifukwa amatikonda, ni wanzelu, wacilungamo, komanso wamphamvu. Cina, timadziŵa kuti Yehova amatikonda , komanso kuti amakhudzika mtima akaona mmene timacitila zinthu pambuyo potiphunzitsa. Zocita zathu zingam’kondweletse Yehova kapena kum’pweteka mtima.—Sal. 78:41; Miy. 27:11. w23.06 14 ¶1-2; 15 ¶5
Cisanu, December 12
Atangokhala wamphamvu, mtima wake unayamba kudzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa. Iye anacita zosakhulupilika kwa Yehova.—2 Mbiri 26:16.
Mfumu Uziya atakhala wamphamvu, anaiŵala kuti ni Yehova amene anam’patsa mphamvu na cipambano. Pali phunzilo lanji kwa ife? Tizikumbukila kuti madalitso na mautumiki amene tili nawo amacokela kwa Yehova. M’malo modzitama na zimene takwanitsa kucita, tiyenela kupeleka ulemu wonse kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Modzicepetsa, tiyenela kukumbukila kuti ndife opanda ungwilo, ndipo timafunikila cilango. M’bale wina wa zaka za m’ma 60 anati: “Naphunzila kusadziona wofunika kwambili kuposa ena. M’malo mokhumudwa na uphungu umene nalandila cifukwa cocita zinthu mwacibwana, nimayesetsa kuwongolela na kupitiliza kutumikila.” Zoona zake n’zakuti, tikamaopa Yehova na kukhalabe odzicepetsa, zinthu zidzatiyendela bwino.—Miy. 22:4. w23.09 10 ¶10-11
Ciŵelu, December 13
Mukufunika kukhala opilila komanso kucita cifunilo ca Mulungu kuti mudzalandile zimene Mulunguyo walonjeza.—Aheb. 10:36.
Akhristu oyambilila anafunikila kupilila. Kuwonjezela pa kukumana na mavuto amene amagwela anthu onse, iwo anakumananso na mavuto ena. Ambili a iwo anazunzidwa na atsogoleli acipembedzo aciyuda mu ulamulilo wa Aroma. Anazunzidwanso na mabanja awo enieni. (Mat. 10:21) Cina, anayenela kuonetsetsa kuti akupewa ziphunzitso zabodza za ampatuko, amene anali kufuna kubweletsa magaŵano mu mpingo. (Mac. 20:29, 30) Akhristuwo anapilila zinthu zonsezi mokhulupilika. (Chiv. 2:3) Motani? Iwo anasinkhasinkha zitsanzo za m’Malemba za anthu amene anapilila, monga Yobu. (Yak. 5:10, 11) Anapemphelanso kwa Mulungu kuti awalimbitse mtima. (Mac. 4:29-31) Cina, iwo anaganizila madalitso omwe adzapeza akakhalabe opilila. (Mac. 5:41) Nafenso tingakulitse khalidwe la kupilila, tikamaŵelenga na kusinkhasinkha zitsanzo za kupilila zopezeka m’Baibo, komanso m’zofalitsa zathu. w23.07 3 ¶5-6
Sondo, December 14
Conco nthawi zonse muziika Ufumu ndi mfundo zolungama za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.—Mat. 6:33.
Yehova na Yesu sadzakusiyani. Mtumwi Petulo atakana Khristu, anayenela kupanga cisankho cofunika kwambili. Kodi adzangosiya kulimbana na zifooko zake, kapena adzapitiliza kukhala wophunzila wa Khristu? Yesu anali atapemphela kwa Yehova kuti cikhulupililo ca Petulo cisafooke. Iye anauza Petulo za pemphelo limenelo, ndipo anali na cidalilo cakuti patsogolo pake adzalimbikitsa abale ake. (Luka 22:31, 32) Kukumbukila mawu a Yesu amenewa, kunali kum’limbikitsa ngako Petulo! Tikafuna kupanga cisankho cofunika kwambili, Yehova angagwilitse nchito akulu acikondi kuti atithandize kukhalabe okhulupilika. (Aef. 4:8, 11) Monga mmene Yehova anasamalila zosoŵa za kuthupi za Petulo na atumwi anzake, adzacitanso cimodzimodzi kwa ife tikaika Ufumu wake patsogolo. w23.09 24-25 ¶14-15
Mande, December 15
Amene amakomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzamʼbwezela zimene anacitazo.—Miy. 19:17.
Yehova amaona ngakhale zocepa zimene timacitila anthu ena. Iye amaziona kuti ni nsembe zamtengo wapatali komanso ngati nkhongole imene adzatibwezela. Ngati kale munali mkulu kapena mtumiki wothandiza, dziŵani kuti Yehova amakumbukila nchito zanu, komanso cikondi cimene cinakulimbikitsani kucita zimenezo. (1 Akor. 15:58) Amaonanso cikondi cimene mwakhala mukucionetsa mpaka pano. Yehova amafuna kuti tonsefe tikule m’cikondi pa iye komanso pa anthu anzathu. Tingakule m’cikondi cathu pa Yehova mwa kuŵelenga Mawu ake na kuwasinkhasinkha, komanso kumakamba naye m’pemphelo. Tingakulitse cikondi cathu pa abale na alongo, mwa kupeleka thandizo lofunikila kwa iwo. Cikondi cathu cikamakula, tidzamuyandikila kwambili Yehova na banja lathu lauzimu mpaka muyaya. w23.07 10 ¶11; 11 ¶13; 13 ¶18
Ciŵili, December 16
Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Mkhristu aliyense ayenela kusankha mmene angasamalile thanzi lake. Pali malamulo ocepa cabe okhudza cithandizo camankhwala amene Mkhristu ayenela kutsatila, monga kupewa magazi na zamizimu. (Mac. 15:20; Agal. 5:19, 20) Koma mbali zina zonse ni nkhani ya munthu mwini. Ngakhale titaona kuti cithandizo cinacake camankhwala ndico cabwino koposa, tiyenela kulemekeza ufulu wa ena wodzisankhila pa nkhani imeneyi. Cotelo, tiyenela kukumbukila mfundo zinayi izi: (1) Ni Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetselatu matenda. (Yes. 33:24) (2) Mkhristu aliyense ayenela kukhala “wotsimikiza ndi mtima wonse” zimene zili zothandiza kwa iye. (Aroma 14:5) (3) Sitiyenela kuweluza ena kapena kuwaikila copunthwitsa. (Aroma 14:13) (4) Akhristu ayenela kuonetsa cikondi ndipo amaona mgwilizano wa mu mpingo kukhala wofunika kwambili kuposa ufulu wawo wodzisankhila pa nkhani ya munthu mwini.—Aroma 14:15, 19, 20. w23.07 24 ¶15
Citatu, December 17
Iye ndi woyela kwa Yehova masiku onse a unazili wake.—Num. 6:8.
Kodi mumaona ubwenzi wanu na Yehova kukhala wa mtengo wapatali? N’zosacita kufunsa! Kuyambila nthawi zamakedzana, anthu ankhani-nkhani amaona ubwenzi wawo na Mulungu kukhala wofunika zedi. (Sal. 104:33, 34) Anthu ambili adzimanapo zina zake kuti alambile Yehova. Umu ni mmenenso zinalili na anthu ena a mu Isiraeli wakale odziŵika kuti Anazili kapena wodzipeleka mwapadela. Mawu amenewa amafotokoza bwino cangu ca Aisiraeli amene anadzimana zina zake pa umoyo kuti atumikile Yehova m’njila yapadela. Cilamulo ca Mose cinalola mwamuna kapena mkazi kupanga lumbilo lina lake lapadela kwa Yehova losankha kukhala Mnazili kwa nthawi imene wadziikila. (Num. 6:1, 2) Lumbilo limenelo, kapena kuti lonjezo ya lamulo linaphatikizapo kutsatila mfundo zina zake pa umoyo zomwe Aisiraeli ena onse sanali kuzitsatila. Ndiye, n’ciyani cinali kulimbikitsa Mwisiraeli kupanga lumbilo lokhala Mnazili? Mwacionekele, cinali cikondi cake cacikulu pa Yehova, komanso mtima woyamikila madalitso Ake.—Deut. 6:5; 16:17. w24.02 14 ¶1-2
Cinayi, December 18
Yehova . . . mumasonyeza cikondi cokhulupilika kwa anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu.—Dan. 9:4.
M’Baibo, liwu laciheberi lomasulidwa kuti “kukhulupilika” kapena kuti “cikondi cokhulupilika,” limapeleka lingalilo la mmene Mulungu amadzipelekela mwacikondi kwa atumiki ake. Liwulo, limagwilitsidwanso nchito pofotokoza cikondi cimene atumiki a Mulungu amaonetsana. (2 Sam. 9:6, 7) Kukhulupilika kwathu kumalimbilako m’kupita kwa nthawi. Izi ndizo zinacitika kwa Danieli. Pa umoyo wake wonse, Danieli anakumana na zocitika zimene zinayesa kukhulupilika kwake kwa Yehova. Koma mayeso aakulu kwambili anakumana nawo ali na zaka za m’ma 90. Nduna za mfumu zinali kudana naye Danieli, ndipo sizinali kulemekeza Mulungu wake. Conco, anakonza ciwembu kuti Danieli aphedwe. Ndunazo zinanyengelela mfumu Dariyo kukhazikitsa lamulo limene linayesa kukhulupilika kwa Danieli, cifukwa anafunika kusankha kaya kukhala wokhulupilika kwa Mulungu wake kapena kwa mfumu. Kuti Danieli aonetse kuti anali wokhulupilika kwa mfumu, anangofunikila kuleka kupemphela kwa Yehova kwa masiku 30 cabe. Koma Danieli sanagonje pa mayesowo.—Dan. 6:12-15, 20-22. w23.08 5 ¶10-12
Cisanu, December 19
Tipitilize kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Yehova amafuna kuti tipitilize kuwaonetsa cikondi abale na alongo athu. M’bale kapena mlongo akacita nafe mopanda cikondi, tizikumbukila kuti sicinali colinga cake. Amafunitsitsa kucita zimene Mulungu amafuna, koma wangocita zinthu mosaganiza bwino. (Miy. 12:18) Yehova amawakonda alambili ake, ngakhale kuti nthawi zina amalakwitsa. Amapitilizabe kukhala bwenzi lathu tikalakwitsa; ndipo satisungila cakukhosi. (Sal. 103:9) M’pofunika kwambili kuti tizitengela citsanzo ca Atate wathu wa kumwamba pa nkhani ya kukhululuka! (Aef. 4:32–5:1) Kumbukilaninso kuti pamene mapeto akuyandikila, m’pamene tiyenela kukhala ogwilizana kwambili na abale na alongo athu. Tikuyembekezela kudzazunzidwa m’tsogolo, moti tingafike pomangidwa cifukwa ca cikhulupililo cathu. Izi zikadzacitika, tidzafunikila abale na alongo athu kuposa n’kale lonse.—Miy. 17:17. w24.03 15-16 ¶6-7
Ciŵelu, December 20
Yehova ndi amene amatsoglela mapazi a munthu.—Miy. 20:24.
M’malemba muli nkhani za acinyamata omwe anakhala mabwenzi a Yehova, anapeza ciyanjo cake, ndipo zinthu zinawayendela bwino. Mmodzi wa iwo ni Davide. Ali wacicepele, anasankha kukhala kumbali ya Mulungu, ndipo m’kupita kwa nthawi anakhala mfumu yokhulupilika. (1 Maf. 3:6; 9:4, 5; 14:8) Kuphunzila za umoyo wa Davide na utumiki wake wokhulupilika kungakulimbikitseni ngako. Kapena mungasankhe kuphunzila za acinyamata ena monga Maliko kapena Timoteyo. Anayamba kutumikila Yehova ali acicepele, ndipo anapitiliza kum’tumikila mokhulupilika. Kuti mukhale na tsogolo labwino, zidalila mmene mukuseŵenzetsela moyo wanu pali pano. Mukamakhulupilila Yehova na kupewa kudzidalila, adzakutsogolelani. Mungakhale na umoyo wosangalatsa komanso wokhutilitsa. Kumbukilani, Yehova amayamikila zimene mumam’citila. Palibe njila yabwino yoseŵenzetsela umoyo wathu yoposa kutumikila Atate wathu wa kumwamba? w23.09 13 ¶18-19
Sondo, December 21
Pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.—Akol. 3:13.
Mtumwi Paulo anali kudziŵa kuti abale na alongo ake anali opanda ungwilo. Mwa citsanzo, atangokhala Mkhristu abale na alongo sanakhulupilile kuti wasinthadi. (Mac. 9:26) Patapita nthawi, ena anali kumunenela zoipa zimene zinamuipitsila mbili. (2 Akor. 10:10) Paulo anaona mkulu akucita zolakwika zimene mwina zinakhumudwitsa ena. (Agal. 2:11, 12) Ndipo mmodzi wa mabwenzi ake apamtima, Maliko, anamugwilitsapo fuwa la moto. (Mac. 15:37, 38) Paulo sanalole ciliconse mwa zocitika zimenezi kumulepheletsa kugwilizana na amene anamulakwila. M’malo mwake, anapitilizabe kuona abale na alongo ake moyenela, ndipo anakhalabe wokangalika mu utumiki wa Yehova. N’ciyani cinam’thandiza? Paulo anali kuŵakonda abale na alongo ake. Cikondi cake pa abale cinamulimbikitsa kuika maganizo ake pa makhalidwe awo abwino, osati pa zophophonya zawo. Cikondi cinamulimbikitsanso kucita zimene zili mu lemba la lelo. w24.03 15 ¶4-5
Mande, December 22
Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu. Koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.—2 Tim. 2:24.
M’Baibo muli nkhani zambili zoonetsa kufunika kwa khalidwe la kufatsa. Ganizilani citsanzo ca Isaki. Atakhazikika m’dela la Afilisiti ku Gerari, Afilisitiwo anafocela zitsime zimene anchito a bambo ake anakumba. M’malo mokangana nawo, Isaki na banja lake anasamukako kumeneko ndipo anakumba zitsime zina. (Gen. 26:12-18) Koma Afilisiti ananena kuti madzi a m’zitsimezo analinso awo. Apanso, Isaki anacita zinthu mwa mtendele. (Gen. 26:19-25) N’ciyani cinam’thandiza kukhalabe wofatsa, ngakhale kuti anthu anapitiliza kum’puta? Mosakayika, anaona mmene atate ake Abulahamu anali kucitila zinthu mwa mtendele, komanso “mtima wodekha ndi wofatsa” wa Sara.—1 Pet. 3:4-6; Gen. 21:22-34. w23.09 15 ¶4
Ciŵili, December 23
Ndakonza kuti zimenezi zicitike komanso ndidzazicita.—Yes. 46:11.
Yehova mwacikondi anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa padziko lapansi kuti adzaphunzitse anthu za Ufumu wa Mulungu na kupeleka moyo wake monga dipo kutiwombola ku ucimo na imfa. Kenako Yesu anaukitsidwa na kupita kumwamba kukakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Nkhani yaikulu ya Baibo ni yakuti dzina la Yehova lidzayeletsedwa pamene iye adzakwanilitsa colinga cake cokhudza dziko lapansi kupitila mu Ufumu wake wolamulidwa na Khristu. Colinga ca Yehova sicingasinthe. Iye anatsimikiza kuti zonse zidzacitika mmene analonjezela. (Yes. 46:10; Aheb. 6:17, 18) M’kupita kwa nthawi dziko lapansi lidzakhala Paradaiso mmene ana a Adamu ndi Hava adzasangalala na “moyo mpaka kalekale.” (Sal. 22:26) Coposa pamenepa, Yehova alinso na colinga cina cacikulu. Colinga cake cacikulu, ni kugwilizanitsa gulu la atumiki ake padziko lapansi na gulu la kumwamba kuti likhale banja limodzi. Ndipo onse amene adzakhala na moyo panthawiyo, adzagonjela Yehova monga Wolamulila wacilengedwe conse. (Aef. 1:8-11) Kodi sizikucititsani cidwi kuona mmene Yehova akukwanilitsila colinga cake? w23.10 20 ¶7-8
Citatu, December 24
“Limbani mtima, . . . pakuti ine ndili ndi inu,” watelo Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.—Hag. 2:4.
Pamene Ayuda ocoka ku Babulo anafika ku Yerusalemu, iwo anayamba kukumana na mavuto a zacuma, a zandale, komanso citsutso. Conco, cinali covuta kwa ena kuika maganizo awo pa nchito yomanganso kacisi wa Yehova. Ndiye cifukwa cake Yehova anatumiza aneneli aŵili, Hagai komanso Zekariya kuti akadzutsenso cidwi cawo. (Hag. 1:1; Zek. 1:1) Komabe, patapita zaka pafupifupi 50, Ayudawo anafunikilanso cilimbikitso. Ezara anapita ku Yerusalemu kucokela ku Babulo, kuti akalimbikitse anthu a Mulungu kuika kulambila koona patsogolo. (Ezara 7:1, 6) Maulosi a Hagai komanso Zekariya analimbikitsa anthu a Mulungu kupitilizabe kudalila Yehova pa nthawi ya citsutso. Mofananamo, nafenso angatithandize kudalila thandizo la Yehova pa nthawi ya mavuto.—Miy. 22:19. w23.11 14-15 ¶2-3
Cinayi, December 25
Valani cikondi, cifukwa cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.—Akol. 3:14.
Kodi timaonetsa bwanji cikondi kwa okhulupilila anzathu? Njila imodzi ni mwa kuwatonthoza. “Tingapitilize kutonthoza ena” ngati timawamvela cifundo. (1 Ates. 4:18) Kodi tingasunge bwanji cikondi cathu pa ena cili colimba? Mwakucita zonse zotheka kuti tizikhululukila ena. N’cifukwa ciyani kuonetsana cikondi n’kofunika kwambili maka-maka masiku ano? Onani cifukwa cimene Petulo anapeleka: “Mapeto a zinthu zonse ayandikila. Conco, . . . khalani okondana kwambili.” (1 Pet. 4:7, 8) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, kodi tingayembekezele ciyani? Ponena za otsatila ake, Yesu ananena kuti: “Mitundu yonse idzadana nanu cifukwa ca dzina langa.” (Mat. 24:9) Kuti tikwanitse kupilila cidanici, tiyenela kukhalabe ogwilizana. Tikatelo, zoyesa-yesa za Satana kuti atigaŵanitse zidzalephela cifukwa ndife ogwilizana m’cikondi.—Afil. 2:1, 2. w23.11 13 ¶18-19
Cisanu, December 26
Ndife anchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.
Coonadi ca Mawu a Mulungu cili na mphamvu yaikulu. Pophunzitsa anthu za Yehova, komanso mmene iye alilidi, zotulukapo zimakhala zokondweletsa ngako! Cidima ca mabodza a Satana cimacoka m’maso mwawo pang’ono-pang’ono, ndipo amayamba kuona Atate wathu mmene ifeyo timamuonela. Amakhala na mantha aulemu akadziŵa za mphamvu zake zopanda malile. (Yes. 40:26) Amayamba kumukhulupilila poona mmene amacitila zinthu mwacilungamo. (Deut. 32:4) Amaphunzila zambili ku nzelu zake zakuya. (Yes. 55:9; Aroma 11:33) Ndipo amalimbikitsidwa akadziŵa kuti iye ndiye gwelo la cikondi. (1 Yoh. 4:8) Pamene akumuyandikila Yehova, ciyembekezo cawo codzakhala na moyo kwamuyaya monga ana ake cimakhala cotsimikizilika. Ni mwayi waukulu zedi umene tili nawo wothandiza anthu kuyandikila Atate wawo! Tikamatelo, Yehova amatitenga kukhala “anchito anzake.”—1 Akor. 3:5. w24.02 12 ¶15
Ciŵelu, December 27
Ndi bwino kuti usalonjeze kusiyana ndi kulonjeza koma osakwanilitsa zimene walonjezazo.—Mlal. 5:5.
Ngati mumaphunzila Baibo na Mboni za Yehova, kapena ndinu mwana wa Mboni, kodi mukuganizila zobatizika? Ici n’colinga cabwino! Koma musanabatizike, mufunika kudzipatulila kwa Yehova Kodi mungadzipatulile motani kwa Yehova? Mwa kum’lonjeza kupitila m’pemphelo kuti mudzalambila iye yekha na kutsogoza cifunilo cake mu umoyo wanu. Kwenikweni mumalonjeza Yehova kuti mudzapitiliza kumukonda “ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu wonse, ndi mphamvu zanu zonse.” (Maliko 12:30) Kudzipatulila kumacitika mseli pakati pa inu na Yehova. Mosiyana na zimenezi, ubatizo umacitika poyela pamaso pa anthu; kuwaonetsa kuti munadzipatulila. Kudzipatulila ni lumbilo lopatulika limene mumafuna kulikwanilitsa, ndipo n’zimene Yehova amayembekezela.—Mlal. 5:4. w24.03 2 ¶2; 3 ¶5
Sondo, December 28
Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.—Aef. 5:33.
Ukwati ulionse umakhala na mavuto ake. Baibo imakamba mosapita m’mbali kuti okwatilana “adzakumana ndi mavuto pa moyo wawo.” (1 Akor. 7:28) Cifukwa? Cifukwa ukwati umabweletsa pamodzi anthu aŵili opanda ungwilo, osiyana zikhalidwe, komanso a makonda osiyana. Nthawi zina angakhale kuti anthuwo anakulila kosiyana. Nthawi zinanso angaonetse tumsawu tumene tunali tobisika asanakwatilane. Zinthu ngati zimenezi zingabweletse kukwesana m’banja. M’malo movomeleza kuti ni opanda ungwilo, ndipo naonso amalakwitsa zinthu, ena amalata cala mnzawo wa mu ukwati pa mavuto amene akukumana nawo m’banja. Angafike mpaka poona kuti kusalana kapena kuthetsa ukwati ndiwo mankhwala. Kodi n’zoona kuti kusudzulana n’kumene kungathetse mavuto awo? Ayi. Yehova amafuna kuti anthu ali pa banja asungebe ukwati wawo, ngakhale kuti mnzawoyo ni wovuta kukhala naye. w24.03 16 ¶8; 17 ¶11
Mande, December 29
Ciyembekezoco sicitikhumudwitsa.—Aroma 5:5.
Ngakhale pambuyo podzipatulila na kubatizika, ciyembekezo codzakhala na moyo wamuyaya mu paladaiso padziko lapansi cinapitlizabe kulimba pomwe munali kuphunzila zambili na kukhala wokhwima mwauzimu. Izi zinacititsa kuti ciyembekezo canu cipitilize kulimbilako. (Aheb. 5:13–6:1) Mwina munaona kukwanilitsidwa kwa Aroma 5:2-4 pa inu. Munakumana na masautso osiyana-siyana, koma munawapilila. Ndipo munaona kuti Mulungu akukuyanjani. Podziŵa kuti ndinu oyanjidwa na Mulungu, ndinu otsimikiza kuti mudzalandila zonse zimene analonjeza. Ciyembekezo canu calimbilako kuposa mmene cinalili poyamba. Cakhala ceniceni kwa inu, ndipo mwacipanga kukhala canu-canu. Cimakhudza mbali zonse za umoyo wanu. Cakuthandizani kusintha mmene mumacitila zinthu na a m’banja lanu, mmene mumapangila zisankho, komanso mmene mumaseŵenzetsela nthawi yanu. Mtumwi Paulo anawonjezela mfundo yofunika yokhudza ciyembekezo cimene munakhala naco mutayanjidwa na Mulungu. Iye anakutsimikizilani kuti ciyembekezo canu cidzakwanilitsidwa.—Aroma 15:13. w23.12 12-13 ¶16-19
Ciŵili, December 30
Mʼmasiku anu, [Yehova] adzacititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.—Yes. 33:6.
Tikakumana na vuto lalikulu, cimakhala covuta kukhala woganiza bwino, komanso kucita zinthu moyenela. Tingadzimve monga ngalawa imene ikukankhidwila uku na uku cifukwa ca mafunde a pa nyanja. Kodi Yehova angatithandize bwanji tikayamba kumila m’mikhalidwe yotele? Anatilonjeza kuti adzatithandiza kukhala otetezeka. Ngalawa ikakumana na namondwe pa nyanja, imayamba kukankhidwila uku ni uku moopsa. Ngalawa zambili zimakhala na zipangizo zina m’mbali mwake zimene zimaponyedwa pansi pa madzi. Zipangizo zimenezi zimathandiza kuti ngalawa isamakankhidwe kwambili na mafunde, ndipo zimathandizanso anthu a m’ngalawayo kukhala otetezeka. Komabe, zambili mwa zipangizo zimenezi zimaseŵenza bwino kwambili ngati ngalawa ikupitabe patsogolo. Mofananamo, Yehova adzatithandiza kukhala otetezeka ngati tipitabe patsogolo pa nthawi ya mavuto. w24.01 22 ¶7-8
Citatu, December 31
Ine ndimadalila Mulungu, sindikuopa.—Sal. 56:4.
Mukacita mantha, dzifunseni kuti, ‘Kodi Yehova wanicitilapo kale ciyani?’ Ganizilani zimene iye analenga. Mwacitsanzo, ‘tikaonetsetsa’ mmene Yehova amasamalila mbalame komanso maluŵa—zomwe sizinalengedwe m’cifanizilo cake, ndiponso sizimulambila—nafenso timalimbikitsa cidalilo cakuti adzatisamalila. (Mat. 6:25-32) Ganizilaninso zimene Yehova wacitila alambili ake. Mungaŵelenge za munthu wa m’Baibo amene anaonetsa cikhulupililo colimba, kapena kuŵelenga cocitika ca mtumiki wa Yehova wa masiku ano. Kuwonjezela apo, sinkhasinkhani mmene Yehova akusamalilani inuyo panokha. Kodi iye anakukokelani bwanji m’coonadi? (Yoh. 6:44) Ndipo kodi wayankha motani mapemphelo anu? (1 Yoh. 5:14) Nanga mumapindula motani tsiku na tsiku cifukwa ca nsembe ya Mwana wake wokondedwa?—Aef. 1:7; Aheb. 4:14-16. w24.01 4 ¶6; 7 ¶17