LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es25 masa. 108-118
  • November

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • November
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
  • Tumitu
  • Ciŵelu, November 1
  • Sondo, November 2
  • Mande, November 3
  • Ciŵili, November 4
  • Citatu, November 5
  • Cinayi, November 6
  • Cisanu, November 7
  • Ciŵelu, November 8
  • Sondo, November 9
  • Mande, November 10
  • Ciŵili, November 11
  • Citatu, November 12
  • Cinayi, November 13
  • Cisanu, November 14
  • Ciŵelu, November 15
  • Sondo, November 16
  • Mande, November 17
  • Ciŵili, November 18
  • Citatu, November 19
  • Cinayi, November 20
  • Cisanu, November 21
  • Ciŵelu, November 22
  • Sondo, November 23
  • Mande, November 24
  • Ciŵili, November 25
  • Citatu, November 26
  • Cinayi, November 27
  • Cisanu, November 28
  • Ciŵelu, November 29
  • Sondo, November 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
es25 masa. 108-118

November

Ciŵelu, November 1

Mwacititsa kuti mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda.​—Mat. 21:16.

Ngati ndinu kholo, thandizani ana anu kukonzekela ndemanga malinga na msinkhu wawo. Nthawi zina, timakambilana nkhani zikulu-zikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena ciyelo ca mpingo. Koma pamakhalabe ndime imodzi kapena ziŵili zimene ana angapelekepo ndemanga. Cina, fotokozelani ana anu kuti si nthawi zonse pomwe angapatsidwe mwayi woyankhapo akakweza dzanja. Kucita izi kudzawathandiza kuti asamakhumudwe mwayi woyankhapo ukapatsidwa kwa ena. (1 Tim. 6:18) Tonsefe tingakonzekele ndemanga zogwila mtima zimene zimalemekeza Yehova, na kulimbikitsa Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafunike kufotokoza mwacidule zocitika pa umoyo wathu, tiyenela kupewa kukamba kwambili za ife eni. (Miy. 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malo mwake, tiziika kwambili maganizo athu pa Yehova, Mawu ake, komanso anthu ake.​—Chiv. 4:11. w23.04 24-25 ¶17-18

Sondo, November 2

Tisapitilize kugona ngati mmene ena onse akucitila, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.​—1 Ates. 5:6.

Cikondi n’cofunika kwambili kuti tikhalebe maso komanso oganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kupilila mavuto amene tingakumane nawo tikamalalikila. (2 Tim. 1:7, 8) Popeza timakondanso anthu amene satumikila Mulungu, timapitilizabe kulalikila pafoni na m’makalata. Timakhala na ciyembekezo cakuti tsiku lina, iwo adzasintha umoyo wawo na kuyamba kucita zabwino. (Ezek. 18:27, 28) Timakondanso Akhristu anzathu. Ndipo timaonetsana cikondi cimeneco mwa “kutonthozana ndi kulimbikitsana.” (1 Ates. 5:11) Monga asilikali amene amaseŵenzela pamodzi pa nkhondo, timalimbikitsana. Sitingakhumudwitse abale na alongo athu mwadala, kapena kubwezela coipa pa coipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timaonetsanso cikondi cathu polemekeza abale amene akutsogolela mu mpingo.​—1 Ates. 5:12. w23.06 10 ¶6; 11 ¶10-11

Mande, November 3

[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephele kucita?​—Num. 23:19.

Njila imodzi imene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, ni kusinkhasinkha za dipo. Dipo limatitsimikizila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanitsidwa. Tikamasinkhasinkha mosamala cifukwa cake dipo linapelekedwa, komanso zimene Mulungu anadzimana, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano ndithu lidzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciyani tikutelo? Kodi kupeleka dipo kunaloŵetsamo ciyani? Yehova anatuma Mwana wake woyamba kubadwa komanso wokondeka, kuti acoke kumwamba n’kudzabadwa monga munthu wangwilo. Ali padziko lapansi, Yesu anapilila mazunzo a mtundu uliwonse. Ndipo anavutika mpaka kufa imfa yoŵaŵa. Umenewu unali mtengo waukulu cotani nanga umene Yehova analipila! Mulungu wathu wacikondi sakanalola Mwana wake kuvutika mpaka kufa, kuti tingokhala na umoyo wabwinopo palipano kwa nthawi yocepa. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Cifukwa analipila mtengo wokwela kwambili, Yehova adzaonetsetsa kuti lonjezo lake la moyo wamuyaya m’dziko latsopano lakwanilitsidwa. w23.04 27 ¶8-9

Ciŵili, November 4

Iwe Imfa amene umabweletsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?​—Hos. 13:14.

Kodi Yehova alidi na cifuno coukitsa akufa? Indedi. Iye anauzila olemba Baibo ambili kulemba lonjezo lake lakuti kutsogoloku adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Chiv. 20:11-13) Ndipo Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwanilitsa lonjezo lake. (Yos. 23:14) Yehova ni wofunitsitsa kuukitsa akufa. Ganizilani mawu a Yobu. Iye anali wotsimikiza kuti ngakhale atafa, Yehova adzalakalaka kumuonanso. (Yobu 14:14, 15) Yehova amalakalakanso kuukitsa alambili ake onse amene anamwalila. Amafunitsitsa kudzawaukitsa kuti akakhale na moyo wathanzi komanso wacimwemwe. Nanga bwanji za mabiliyoni amene anamwalila asanakhale na mwayi wophunzila coonadi cokhudza Yehova? Mulungu wathu wacikondi amafuna kuwaukitsa nawonso. (Mac. 24:15) Amafuna kuti akawapatse mwayi wokhala mabwenzi ake, komanso kuti akakhale na moyo kwamuyaya padziko lapansi.​—Yoh. 3:16. w23.04 9 ¶5-6

Citatu, November 5

Mulungu adzatipatsa mphamvu.​—Sal. 108:13.

Kodi mungalimbikitse bwanji ciyembekezo canu? Mwacitsanzo, ngati muli na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi, muziŵelenga Malemba amene amafotokoza mmene Paradaiso adzakhalile na kuwasinkhasinkha. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizila mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano. Yelekezelani kuti muli m’dzikolo. Tikamaganizila kwambili za ciyembekezo cathu ca dziko latsopano tidzaona mavuto athu kuti ni “akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Yehova adzakupatsani mphamvu kupitila mu ciyembekezo cimene wakupatsani. Wapeleka zonse zofunika kuti mulandile mphamvu zocokela kwa iye. Conco, mukafuna thandizo kuti mucite utumiki wina wake, kupilila mayeso, kapena kukhalabe na cimwemwe, mufikileni Yehova m’pemphelo mocokela pansi pa mtima, na kufuna-funa citsogozo cake mwa kucita phunzilo la munthu mwini. Cina landilani cilimbikitso kucokela kwa Akhristu anzanu. Komanso sungani ciyembekezo canu cili cowala. Citani zimenezi kuti “mulandile mphamvu zazikulu mogwilizana ndi mphamvu zake zocititsa mantha, nʼcolinga coti muthe kupilila zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwacimwemwe.”​—Akol. 1:11. w23.10 17 ¶19-20

Cinayi, November 6

Muzithokoza pa ciliconse.​—1 Ates. 5:18.

Tili na zifukwa zambili zoyamikila Yehova m’pemphelo. Tingamuyamikile pa zabwino zonse zimene tili nazo, cifukwa mphatso iliyonse yabwino imacokela kwa iye. (Yak. 1:17) Tingamuyamikile cifukwa cotipatsa dziko lapansi lokongola, na zinthu zacilengedwe zocititsa cidwi. Tingamuyamikilenso potipatsa moyo, banja, mabwenzi, komanso ciyembekezo. Ndipo tingamuyamikilenso potilola kukhala naye pa ubwenzi wamtengo wapatali. Aliyense pacake angafunike kuyesetsa kuti apeze zifukwa zomuyamikila Yehova. Anthu ambili m’dzikoli ni osayamika. Amaika maganizo awo pa zimene akufuna, m’malo moyamikila zimene ali nazo kale. Ngati mzimu umenewu ungatiyambukile, mapemphelo athu angamakhale mndandanda wa zopempha basi. Kuti tipewe zimenezi, tiyenela kupitiliza kukulitsa mzimu woyamikila pa zonse zimene Yehova amaticitila.​—Luka 6:45. w23.05 4 ¶8-9

Cisanu, November 7

Azipempha ndi cikhulupililo, asamakayikile ngakhale pangʼono.​—Yak. 1:6.

Monga Tate wathu wacikondi, Yehova samakondwela kutiona tikuvutika. (Yes 63:9) Ngakhale n’telo, iye satichinga ku mavuto onse omwe ali ngati mitsinje komanso lawi lamoto. (Yes. 43:2) Komabe, iye analonjeza kuti adzatithandiza ‘tikamadutsa’ m’mavutowo. Ndipo sadzalola kuti mavutowo ativulaze kothelatu. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyela womwe ni wamphamvu kuti utithandize kupilila. (Luka 11:13; Afil. 4:13) Conco, tizikhala otsimikiza kuti nthawi zonse tidzakhala na zonse zofunikila kuti tipilile, komanso kukhalabe okhulupilika kwa iye. Yehova amayembekezela kuti tizimudalila. (Aheb. 11:6) Nthawi zina mavuto athu angaoneke osatheka kuwapilila. Tingayambe kukaikila ngati Yehova adzatithandiza. Koma Baibo imatitsimikizila kuti na thandizo la Mulungu ‘tingakwele khoma’ (Sal. 18:29) Conco m’malo molola kuti zikaiko zimenezi zikule mumtima mwathu, tiyenela kupemphela kwa iye mwa cikhulupililo tili na cidalilo cakuti iye adzayankha mapemphelo athu.​—Yak. 1:6, 7. w23.11 22 ¶8-9

Ciŵelu, November 8

Kuyaka [kwa cikondi] kuli ngati kuyaka kwa moto. Cikondico ndi lawi la Ya. Madzi ambili sangathe kuzimitsa cikondi, ndipo mitsinje singacikokolole.​—Nyimbo 8:6, 7.

Iyi ni njila yabwino kwambili yofotokozela cikondi ceniceni! Mawu amenewa amatsimikizila okwatilana kuti n’zotheka ndithu kukhala na cikondi cosatha. Kuti okwatilana akhale na cikondi cosatha, pali zimene ayenela kucita. Mwacitsanzo, kuti moto usazime timasonkheza nkhuni. Tikaleka kusonkheza, pothela pake moto umazima. Mofananamo, mwamuna na mkazi wake ayenela kusonkheza cikondi cawo kuti cisazime. Nthawi zina, okwatilana angaone kuti cikondi cawo cayamba kuzima, maka-maka akakumana na mavuto azacuma, matenda, kapena akakhala na udindo wolela ana. Kuti “lawi la Ya” lisazime, mwamuna na mkazi wake ayenela kulimbitsa ubale wawo na Yehova. w23.05 20-21 ¶1-3

Sondo, November 9

Usacite mantha.​—Dan. 10:19.

Kuti tikhale olimba mtima, kodi tiyenela kucitanji? Makolo athu angatilimbikitse kukhala olimba mtima, koma kulimba mtima kumeneko si coloŵa cimene iwo angangosiyila ana awo. Kukhala olimba mtima kuli ngati kuphunzila luso latsopano. Njila imodzi imene tingakhalile na luso, ni kuyang’anitsitsa zimene wokuphunzitsani amacita, na kutengela citsanzo cake. Mofananamo, timaphunzila kukhala olimba mtima tikamayang’anitsitsa mmene ena amaonetsela khalidweli, na kutengela citsanzo cawo. Monga Danieli, tiyenela kuwadziŵa bwino Mawu a Mulungu. Tiyenela kupanga ubwenzi wathithithi na Yehova mwa kupemphela kwa iye nthawi zonse, na kumuuza mmene tikumvela. Ndipo tizim’dalila, na kukhala otsimikiza kuti adzatithandiza. Ndiyeno cikhulupililo cathu cikayesedwa, tidzakhala olimba mtima Anthu olimba mtima amalemekezedwa na anthu ena. Cina, amakopa anthu oona mtima kuti abwele kwa Yehova. Kukamba zoona, tili na zifukwa zabwino zokhalila olimba mtima. w23.08 2 ¶2; 4 ¶8-9

Mande, November 10

Muzifufuza zinthu zonse.​—1 Ates. 5:21.

Liwu la Cigiriki limene analimasulila kuti “muzufufuza,” analigwilitsa nchito pofotokoza mmene anthu amayesela miyala yamtengo wapatali kuti adziŵe ngati ni yeniyeni. Conco, tiyenela kuyesa kapena kuti kutsimikizila zimene timamva kapena kuŵelenga, kuti tidziŵe ngati n’zenizeni. Kudzakhala kofunika ngako kwa ife pamene cisautso cacikulu cikuyandikila. M’malo mokhulupilila m’cimbulimbuli zimene ena amakamba, timagwilitsa nchito luso la kuzindikila kuti tiyelekezele ngati zimene timaŵelenga komanso kumva, n’zogwilizana na zimene Baibo ndiponso gulu la Yehova limakamba. Tikatelo, sitidzapusitsidwa na mauthenga abodza a ziŵanda. (Miy. 14:15; 1 Tim. 4:1) Monga gulu, atumiki a Mulungu adzapulumuka cisautso cacikulu. Koma aliyense payekha amadziŵa kuti cakudza siciimba ng’oma. (Yak. 4:14) Kaya tidzapyola amoyo cisautso cacikulu kapena tidzamwalila cisanafike, tidzalandila mphoto ya moyo wosatha tikakhalabe okhulupilika. Conco, tiyeni tonse tiziganizila kwambili za ciyembekezo cathu cimeneci, ndipo tikhalebe okonzeka tsiku la Yehova. w23.06 13 ¶15-16

Ciŵili, November 11

[Anaulula] cinsinsi cake kwa atumiki ake.​—Amosi 3:7.

Sitidziŵa kuti maulosi ena a m’Baibo adzakwanilitsika motani. (Dan. 12:8, 9) Koma kusamvetsa mmene ulosi winawake udzakwanilitsikile sikutanthauza kuti ulosiwo sudzakwanilitsika. Sitipeneka konse kuti Yehova adzatiuza zoyenela kudziŵa pa nthawi yake, monga anacitila kumbuyoko. Coyamba, padzakhala cilengezo ca “bata ndi mtendele.” (1 Ates. 5:3) Kenako, maulamulilo andale adzaukila cipembedzo conyenga na kucifafanizilatu. (Chiv. 17:16, 17) Pambuyo pake, maulamulilowo adzaukila anthu a Mulungu. (Ezek. 38:18, 19) Izi n’zimene zidzabutsa nkhondo yothela ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Ndife otsimikiza kuti zonsezi zatsala pang’ono kucitika. Koma poyembekezela zimenezi, tisaleke kuonetsa ciyamikilo cathu kwa Atate wathu wakumwamba, mwa kuŵelenga maulosi a m’Baibo, komanso kuthandiza ena kucita cimodzimodzi. w23.08 13 ¶19-20

Citatu, November 12

Tiyeni tipitilize kukondana, cifukwa cikondi cimacokela kwa Mulungu.​—1 Yoh. 4:7.

Pamene mtumwi Paulo anali kufotokoza za cikhulupililo, ciyembekezo, na cikondi, anamaliza na mawu akuti “koma cacikulu pa zonsezi ndi cikondi.” (1 Akor. 13:13) N’cifukwa ciyani Paulo ananena zimenezi? M’tsogolo, sitidzafunikanso kuonetsa khalidwe la cikhulupililo pa malonjezo a Mulungu onena za dziko latsopano kapena kukhala na ciyembezo cakuti malonjezowo adzakwanilitsidwa cifukwa adzakhala atakwanilitsidwa kale. Koma nthawi zonse tidzafunika kukonda Yehova na anthu ena. Ndipo cikondi cathu pa iwo cidzapitiliza kukula mpaka kale-kale. Mfundo inanso ni yakuti cikondi cimatidziŵikitsa monga Akhristu oona. Yesu anauza atumwi ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Komanso, kukondana kumatithandiza kukhala ogwilizana. Paulo anati cikondi “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” (Akol. 3:14) Mtumwi Yohane analembela okhulupilila anzake kuti: “Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.” (1 Yoh. 4:21) Tikamaonetsana cikondi pa wina na mnzake, timaonetsa kuti timakonda Mulungu. w23.11 8 ¶1, 3

Cinayi, November 13

Titaye colemela ciliconse.​—Aheb. 12:1.

Baibo imayelekezela umoyo wathu wacikhristu na mpikisano wothamanga. Othamanga amene adzafike pa mzele womaliza, adzawafupa na moyo wosatha. (2 Tim. 4:7, 8) Tiyenela kucita zonse zotheka kuti tisaleke kuthamanga, maka-maka pamene tatsala pang’ono kufika pa mzele womaliza. Mtumwi Paulo anachula cimene cingatithandize kupambana mpikisanowu. Iye anatilangiza kuti “titaye colemela ciliconse . . . Ndipo tithamange mopilila mpikisano umene talowawu.” Kodi Paulo anatanthauza kuti Mkhristu sayenela kunyamula kanthu? Ayi, mfundo yake si imeneyo. Iye anatanthauza kuti tiyenela kutaya colemela ciliconse cosafunikila. Zolemela zotelo zingatitopetse na kucepetsa liŵilo lathu. Kuti tipilile, tiyenela kuzindikila ciliconse cimene cingatilemetse, na kucitaya mwamsanga. Komabe, tiyenela kusamala kuti tisataye zinthu zofunikila kunyamula. Tikazitaya, sitingayenelele kuthamanga mpikisanowo.​—2 Tim. 2:5. w23.08 26 ¶1-2

Cisanu, November 14

Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa kunja kokha.​—1 Pet. 3:3.

Kukhala wololela kumatithandiza kulemekeza maganizo a anthu ena. Mwacitsanzo, alongo athu ena amakonda kuphauda pamene ena satelo. Akhristu ena amamwako moŵa mwacikatikati pamene ena amaupewelatu. Akhristu onse amafuna kukhala na thanzi labwino, koma amasankha njila zosiyana za cithandizo ca mankhwala. Ngati timaona kuti kapenyedwe kathu ndiye kabwino nthawi zonse, ndipo timalimbikitsa ena kutengela kapenyedwe kathuko, tingakhale copunthwitsa kwa ena, ndipo tingabweletse magaŵano mu mpingo. (1 Akor. 8:9; 10:23, 24) Mwacitsanzo, Yehova sanacite kutichulila kuti tizivala zakuti-zakuti. M’malo mwake, anangotipatsa mfundo zoyenela kutsatila. Tiyenela kuvala m’njila yoyenela atumiki a Mulungu, yoonetsa kuti ndife oganiza bwino, aulemu komanso ‘anzelu.’ (1 Tim. 2:9, 10) Cotelo, sitivala m’njila yoti anthu ena azingoti maso dwii pa ife. Mfundo za m’Baibo zingathandizenso akulu kupewa kuika malamulo awo-awo pa nkhani ya mavalidwe na kudzikongoletsa. w23.07 23-24 ¶13-14

Ciŵelu, November 15

Chelani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndipo mudzasangalala kwambili ndi zakudya zabwino.​—Yes. 55:2.

Yehova akutiphunzitsa mokhalila na tsogolo labwino. Aja amene amalabadila ciitano ca “mkazi wopusa,” amafuna kupeza cisangalalo m’zaciwelewele. Ndipo sadziŵa kuti zocita zawo mapeto ake ni “Manda.” (Miy. 9:13, 17, 18) Izi n’zosiyana na anthu amene amalabadila ciitano ca “nzelu yeniyeni.” (Miy. 9:1)Tikuphunzila kukonda zimene Yehova amakonda, komanso kudana na zimene amadana nazo. (Sal. 97:10) Ndipo timakhala acimwemwe tikamaitana ena kuti apindule na “nzelu yeniyeni.” Zili monga kuti ‘tapita pamwamba pa zitunda za m’mudzi na kuitanila anthu kuti: “Aliyense wosadziŵa zinthu apatukile kuno.”’ Mapindu amene ife komanso iwo amapeza si a palipano cabe. Koma ni amuyaya, ndipo tidzakhalabe na “moyo” kwamuyaya malinga ‘tiyenda mowongoka m’njila yomvetsa zinthu.’​—Miy. 9:3, 4, 6. w23.06 24 ¶17-18

Sondo, November 16

Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu, ndipo munthu amene amalamulila mtima wake amaposa munthu wogonjetsa mzinda.​—Miy. 16:32.

Mumamva bwanji ngati mnzanu wa kunchito kapena kusukulu wakufunsani pa zimene mumakhulupilila? Ambili a ife timacita mantha. Koma funso lake lingatithandize kudziŵa maganizo a munthuyo kapena zimene amakhulupilila. Zimenezi zingatipatse mpata wom’gaŵilako uthenga wabwino. Koma nthawi zina, ena angafunse funso pofuna kukangana nafe. Izi siziyenela kutidabwitsa cifukwa anthu ambili amauzidwa mabodza pa zimene timakhulupilila. (Mac. 28:22) Kuwonjezela apo, tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ nthawi imene ambili ni “osafuna kugwilizana ndi ena,” komanso “oopsa.” (2 Tim. 3:1, 3) Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’ciyani cinganithandize kukhala wodekha komanso wokoma mtima ngati wina ali na colinga coyambitsa mkangano pa zimene nimakhulupilila?’ Ni kukhala wofatsa. Munthu wofatsa sakwiya msanga akakumana na zokhumudwitsa kapena zodetsa nkhawa. w23.09 14 ¶1-2

Mande, November 17

Mudzaŵaika kuti akhale akalonga padziko lonse lapansi.​—Sal. 45:16.

Nthawi zina timalandila uphungu wotiteteza ku mavuto omwe angabwele cifukwa cokondetsetsa zinthu zakuthupi, komanso ku zinthu zomwe zingatiphwanyitse malamulo a Mulungu. Timapezanso madalitso tikatsatila citsogozo cimeneci. (Yes. 48:17, 18; 1 Tim 6:9, 10) Mosakayikila, Yehova adzapitilizabe kugwilitsa nchito anthu omuimilako popeleka citsogozo pa cisautso cacikulu, komanso mu ulamulilo wa zaka 1,000. Kodi tidzapitilizabe kutsatila citsogozo cimeneco? Zidzadalila kwambili pa mmene timacitila panopa tikalandila citsogozo ca Yehova. Conco, tiyeni nthawi zonse tipitilize kutsatila citsogozo ca Yehova kuphatikizapo copelekedwa na amuna amene anasankhidwa kuti azitiyang’anila. (Yes. 32:1, 2; Aheb. 13:17) Timatelo podziŵa kuti tili na zifukwa zomveka zodalila Wotilondolela Njila wathu, Yehova, amene amatipewetsa ngozi zauzimu na kutitsogolela kumene tikupita​—ku moyo wosatha m’dziko latsopano. w24.02 25 ¶17-18

Ciŵili, November 18

Mwapulumutsidwa cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu.​—Aef. 2:5.

Mtumwi Paulo anali kusangalala potumikila Yehova. Koma anakumana na zokhoma zambili. Kambili, anali kuyenda maulendo atali-atali, ndipo mayendedwe anali ovuta kwambili masiku amenewo. Pa maulendowo, nthawi zina anali kukumana na “zoopsa za m’mitsinje,” komanso “zoopsa za acifwamba.” Nthawi zinanso anali kumenyedwa na anthu otsutsa. (2 Akor. 11:23-27) Ndipo ngakhale Akhristu anzake si nthawi zonse pamene anayamikila pa zimene anali kucita kuti awathandize. (2 Akor. 10:10; Afil. 4:15) N’ciyani cinathandiza Paulo kuti asaleke kutumikila Yehova? Iye anaphunzila zambili zokhudza makhalidwe a Yehova m’Malemba, komanso pa zimene iye mwini anapitamo. Izi zinam’tsimikizila kuti Yehova anali kum’konda kwambili. (Aroma 8:38, 39; Aef. 2:4, 5) Ndipo nayenso anakulitsa cikondi cake pa Yehova. Anaonetsa cikondico ‘potumikila oyela na kupitiliza kuwatumikila.’​—Aheb. 6:10. w23.07 9 ¶5-6

Citatu, November 19

[Muzimvela] olamulila akulu-akulu.​—Aroma. 13:1.

Anthu ambili amavomeleza kut timafunikila otiyang’anila, ndiponso kuti tiyenela kumvela ku malamulo ena a “akulu-akulu” a boma. Koma anthu amodzi-modziwo amawayawaya kumvela malamulo amene amaoneka kuti ni opanda cilungamo komanso amene sanawakonde. Baibo imaonetsa kuti maulamulilo a anthu awonjezela mavuto, ali pansi pa ulamulilo wa Satana, komanso kuti adzawonongedwa posacedwa. (Sal. 110:5, 6; Mlal. 8:9; Luka 4:5, 6) Imatiuzanso kuti “amene akutsutsana ndi ulamulilo, akutsutsana ndi zimene Mulungu anakonza.” Pali pano Yehova walola olamulila akulu-akulu amenewa kuti akhalepo kwa kanthawi kuti asungitse dongosolo, ndipo amafuna kuti tiziwamvela. Conco, ‘tizipeleka kwa onse zimene amafuna,’ zomwe ziphatikizapo msonkho, ulemu, komanso kuwamvela. (Aroma 13:1-7) Tingaone lamulo lina kukhala losayenela, lopanda cilungamo, kapena lovuta kulitsatila. Koma timamvela Yehova, ndipo amatiuza kuti tiyenela kumvela olamulila malinga ngati satiuza kuphwanya malamulo ake.​—Mac. 5:29. w23.10 8 ¶9-10

Cinayi, November 20

Mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu.​—Ower. 15:14.

Pamene Samisoni anabadwa, Afilisiti ndiwo anali kulamulila Aisiraeli mowapondeleza. (Ower. 13:1) Ulamulilo wawo wankhanza unabweletsa mavuto ambili kwa Aisiraeli. Yehova anasankha Samisoni kuti “[adzatsogolele] populumutsa Isiraeli mʼmanja mwa Afilisiti.” (Ower. 13:5) Kuti akwanilitse utumiki wovuta umenewu, Samisoni anafunika kudalila Yehova. Panthawi ina, asilikali Acifilisiti anabwela kuti adzagwile Samisoni ku Lehi komwe mwina ni ku Yuda. Amuna a ku Yuda anacita mantha, conco anapeleka Samisoni m’manja mwa Afilisiti. Anthu a mtundu wake anam’manga na zingwe ziŵili zatsopano, ndipo anam’peleka m’manja mwa Afilisiti. (Ower. 15:9-13) Komabe, “mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu,” ndipo Samisoni anadula zingwezo. “Zitatelo, anapeza fupa laliŵisi la nsagwada za bulu wamphongo ndipo analitenga n’kupha nalo amuna 1,000” Acifilisiti!​—Ower. 15:14-16. w23.09 2 ¶3-4

Cisanu, November 21

Zimenezi nʼzogwilizana ndi colinga camuyaya cimene iye anakhala naco cokhudza Khristu, yemwe ndi Yesu Ambuye wathu.​—Aef. 3:11.

Yehova mwa pang’ono-pang’ono watiululila ‘colinga cake camuyaya’ m’Baibo. Yehova angaseŵenzetse njila iliyonse kuti akwanilitse colinga cake, cifukwa “amapangitsa kuti ciliconse cikwanilitse colinga cake.” (Miy. 16:4) Ndipo zotulukapo za nchito ya Yehova zimakhalapo kosatha. Kodi colinga ca Yehova n’ciyani? Nanga anapanga masinthidwe otani kuti acikwanilitse? Mulungu anafotokozela anthu oyambilila colinga cake kwa iwo. Iye anawauza kuti “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, muyang’anilenso . . . camoyo ciliconse coyenda padziko lapansi.” (Gen. 1:28) Kupanduka kwa Adamu na Hava, komanso kubweletsa ucimo padziko lapansi sikunalepheletse colinga ca Yehova. Nthawi yomweyo, iye anatsimikiza kuti adzakhazikitsa Ufumu kumwamba umene udzakwanilitsa colinga cake capoyamba cokudza mtundu wa ana a anthu komanso dziko lapansi.​—Mat. 25:34. w23.10 20 ¶6-7

Ciŵelu, November 22

Yehova akanapanda kundithandiza, bwenzi nditafa kalekale.​—Sal. 94:17.

Yehova angatithandize kuti tisafooke. Cingakhale covuta kupilila, maka-maka ngati takhala tikulimbana na zifooko zathu kwa nthawi yaitali. Nthawi zina, zofooka zathu zingakhale zazikulu kuposa zimene mtumwi Petulo anali nazo. Koma Yehova angatipatse mphamvu kuti tisafooke. (Sal. 94:18, 19) Mwacitsanzo, m’bale wina anali kucita mathanyula kwa zaka zambili asanaphunzile coonadi. Olo kuti analeka khalidweli, nthawi zina zilakolako zoipa zimabwelabe m’maganizo mwake. N’ciyani cimam’thandiza kusagonja? Mwiniwake anati: “Yehova amatilimbitsa.” Anatinso: “Mwa thandizo la mzimu woyela . . . , naona kuti n’zotheka kukhalabe na umoyo wokondweletsa Yehova . . . Iye wakhala akunigwilitsa nchito, ndipo amanilimbitsa mosasamala kanthu za zifooko zanga.” w23.09 23 ¶12

Sondo, November 23

Zotsatila za kudzicepetsa komanso kuopa Yehova ndi cuma, ulemelelo ndi moyo.​—Miy. 22:4.

Inu abale acinyamata, kukhala Mkhristu wokhwima sikumacitika pakokha. Muyenela kukhala na zitsanzo zabwino zimene mungatengele, kukhala oganiza bwino, komanso odalilika. Muyenelanso kuphunzila maluso othandiza pa umoyo, komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo. Nthawi zina mungade nkhawa mukamaganizila zinthu zimene muyenela kucita. Koma mungapambane. Kumbukilani kuti Yehova ni wofunitsitsa kukuthandizani. (Yes. 41:10, 13) Nawonso abale na alongo anu mu mpingo adzakuthandizani. Mukakwanitsa kukhala mwamuna wokhwima wacikhristu, mudzakhala na umoyo wabwino komanso wokhutilitsa. Timakunyadilani ngako inu abale acinyamata! Yehova akudalitseni pamene muyesetsa kukhala Mkhristu wokhwima. w23.12 29 ¶19-20

Mande, November 24

[Muzinyalanyaza] colakwa.​—Miy. 19:11.

Yelekezani kuti muli pa maceza na kagulu ka abale na alongo. Mukusangalala na maceza, ndiyeno mukujambula cithunzi ca gulu lonse. Mukujambulanso zithunzi zina ziŵili kucitila kuti mwina coyambaco sicinaoneke bwino. Tsopano muli na zithunzi zitatu. Koma mwazindikila kuti pa cimodzi mwa zithunzizo, m’bale wina sanamwetulile. Mungacifafanize cifukwa muli na zithunzi zina ziŵili pamene aliyense pa gulupo akumwetulila kuphatikizapo m’baleyo. Nthawi zambili timakumbukila zinthu zabwino zimene tinacita pamodzi na abale na alongo. Koma bwanji ngati pa cocitika cina m’bale kapena mlongo anakamba kapena kucita cinthu cimene cinakukhumudwitsani? Kodi mungatani na cocitika cimeneco? Kodi simungacifafanize m’maganizo mwanu monga mmene mungafafanizile cithunzi cija? (Aef. 4:32) Tingakwanitse cifukwa tili na zocitika zambili zabwino zokhudza m’baleyo. Izi ndiye zocitika zimene tiyenela kusunga m’maganizo mwathu na kuzinyadila. w23.11 12-13 ¶16-17

Ciŵili, November 25

Akazi ayenela kudzikongoletsa ndi zovala zoyenela, povala mwaulemu, . . . azidzikongoletsa mogwilizana ndi mmene akazi odzipeleka kwa Mulungu amayenela kudzikongoletsela.​—1 Tim. 2:9, 10.

Mawu Acigiriki omasulidwa kuti mwaulemu komanso mwanzelu, aonetsa kuti nthawi zonse alongo afunika kuvala zoyenela na kuganizila mmene anthu ena angamvele. Timawayamikila ngako alongo athu okhwima mwauzimu povala mwaulemu! Kuzindikila ni khalidwe lina limene alongo okhwima mwauzimu amaonetsa. Kodi kuzindikila n’kutani? Ni luntha lokwanitsa kusiyanitsa cabwino na coipa kenako n’kusankha coyenela. Ganizilani citsanzo ca Abigayeli. Mwamuna wake anapanga cisankho colakwika cimene cikanabweletsa mavuto ku banja lake lonse. Abigayeli anacitapo kanthu mwamsanga. Ndipo kucita kwake zinthu mozindikila kunapulumutsa miyoyo. (1 Sam. 25:14-23, 32-35) Kuzindikila kumatithandizanso kudziŵa nthawi yolankhula komanso yokhala cete. Cina, kumatithandizanso kuonetsa cidwi kwa ena popanda kuwakhumudwitsa.​—1 Ates. 4:11. w23.12 20 ¶8-9

Citatu, November 26

Tingathe kusangalala cifukwa tili ndi ciyembekezo colandila ulemelelo wa Mulungu.​—Aroma 5:2.

Mtuwi Paulo analembela mawuwa mpingo wa ku Roma. Abale na alongo kumeneko anali ataphunzila za Yehova na Yesu, anaonetsa cikhulupililo cawo, ndipo anakhala Akhristu. Conco Mulungu anawayesa “olungama cifukwa cokhala ndi cikhulupililo,” ndipo anawadzoza na mzimu woyela. (Aroma 5:1) Inde, anakhala na ciyembekezo ceniceni komanso cokondweletsa. Pambuyo pake, Paulo analembela Akhristu odzozedwa a ku Efeso pa ciyembekezo cimene anapatsidwa. Ciyembekezoco cinaphatikizapo kulandila zinthu zimene anasungila “oyela monga colowa.” (Aef. 1:18) Cina, anauza Akolose kumene adzalandilila mphoto yawo. Iye anati “ciyembekezo codzalandila zimene akusungilani kumwamba.” (Akol. 1:4, 5) Ciyembekezo ca Akhristu odzozedwa n’cakuti adzaukitsidwa ku moyo wosatha kumwamba, kumene adzalamulila na Khristu.​—1 Ates. 4:13-17; Chiv. 20:6. w23.12 9 ¶4-5

Cinayi, November 27

Mtendele wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.​—Afil. 4:7.

Liwu limene linamasulidwa kuti “udzateteza” limapeleka lingalilo la asilikali amene anali kuteteza mzinda kuti usaukilidwe na adani. Anthu a mu mzindawo anali kugona mwamtendele podziŵa kuti asilikali akuuteteza mzindawo. Mofananamo, ngati mtendele wa Mulungu ukuteteza mitima na maganizo athu, timakhala odekha podziŵa kuti ndife otetezeka. (Sal. 4:8) Monga zinalili kwa Hana, ngakhale kuti zinthu sizingakhale bwino nthawi yomweyo, timapezabe mtendele. (1 Sam. 1:16-18) Ndipo tikakhala odekha, cimakhala copepuka kukhala woganiza bwino na kupanga zisankho zanzelu. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Tikavutika maganinzo, tizipempha Mulungu kuti atithandize, mwa kupemphela kwa iye mpaka titamva mtendele wake. (Luka 11:9; 1 Ates. 5:17) Ngati mukukumana na vuto lalikulu, limbikilani kupemphela, ndipo mudzaona mtendele wa Yehova ukuteteza mtima wanu na maganizo anu.​—Aroma 12:12. w24.01 21 ¶5-6

Cisanu, November 28

Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.​—Mat. 6:9.

Kuti ayeletse dzina la Atate wake, Yesu anapilila mazunzo, manyozo, komanso mabodza amene anamuneneza. Iye anadziŵa kuti anamvela Atate ake m’zinthu zonse; ndipo analibe cifukwa cocitila manyazi. (Aheb. 12:2) Anadziŵanso kuti Satana anali kum’tsutsa m’nthawi zovuta zimenezo. (Luka 22:2-4; 23:33, 34) Satana anali wofunitsitsa kucititsa Yesu kuti ataye cikhulupililo cake mwa Mulungu. Koma iye analemba m’madzi! Yesu anaonetsa poyela kuti Satana ni wabodza wankhalwe, ndiponso kuti Yehova ali na atumiki omwe amakhulupilikabe, ngakhale mayeso akhale ovuta bwanji! Kodi mukufuna kukondweletsa Mfumu yanu imene ikulamulila? Pitilizani kutamanda dzina la Yehova, pothandiza ena kudziŵa mmene Mulungu wathu alilidi. Mukatelo, mudzakhala mukutsatila mapazi a Yesu. (1 Pet. 2:21) Mofanana ni Yesu, mumakondweletsa mtima wa Yehova na kuonetsa poyela kuti mdani wake, Satana, ni wabodza lamkunkhuniza! w24.02 11-12 ¶11-13

Ciŵelu, November 29

Yehova ndidzamubwezela ciyani pa zabwino zonse zimene wandicitila?​—Sal. 116:12.

Pa zaka 5 zapitazo, anthu opitilila 1 miliyoni abatizika na kukhala Mboni za Yehova. Mukadzipatulila kwa Yehova, mumasankha kukhala wophunzila wa Yesu Khristu, ndipo kucita cifunilo ca Yehova kumakhala kofunika kwambili pa umoyo wanu. Kodi kudzipatulila kuti mukhale Mkhristu kumafuna kuti mucite ciyani? Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha.” (Mat. 16:24) Monga mtumiki wodzipatulila wa Yehova, kanani kucita ciliconse cosagwilizana na cifunilo ca Yehova. (2 Akor. 5:14, 15) Izi ziphatikizapo kukana “nchito za thupi,” monga ciwelewele. (Agal. 5:19-21; 1 Akor. 6:18) Kodi kutsatila malamulo ngati amenewa kungapangitse umoyo wanu kukhala wosasangalatsa? Sizingakhale telo ngati mumakonda Yehova, komanso ngati mumavomeleza kuti colinga ca malamulo akewo n’cakuti akupindulileni.​—Sal. 119:97; Yes. 48:17, 18. w24.03 2 ¶1; 3 ¶4

Sondo, November 30

Umandisangalatsa kwambili.​—Luka 3:22.

Yehova amapeleka mzimu wake woyela kwa amene amakondwela nawo. (Mat. 12:18) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi nimaonetsako zipatso za mzimu wa Mulungu mu umoyo wanga?’ Kodi mumaona kuti mwaphunzila kucita zinthu moleza mtima na ena kusiyana na mmene zinalili musanadziŵe Yehova? Pamene mukulitsa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala, mudzakhala otsimikiza kuti Yehova amakondwela nanu. Yehova amaseŵenzetsa mphamvu ya dipo kwa amene amakondwela nawo. (1 Tim. 2:5, 6) Koma bwanji ngati timaonabe kuti Yehova sakondwela nafe, ngakhale kuti timakhulupilila nsembe ya dipo, ndipo tinabatizika? Kumbukilani kuti mtima ni wonyenga. Koma tizim’khulupilila Yehova nthawi zonse. Amaona amene amakhulupilila nsembe ya dipo kukhala olungama, ndipo analonjeza kuti adzawadalitsa.​—Sal. 5:12; Aroma 3:26. w24.03 30 ¶15; 31 ¶17

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani