NKHANI YA PACIKUTO | KODI MULUNGU NDI WOFUNIKA KWA IFE?
N’kufunsilanji funso limeneli?
“Kodi mumaona kuti Mulungu ndi wosafunika kwa inu? Anthu ambili amaona conco.” Mau amenewa analembedwa pa cikwangwani cina caposacedwapa cimene anthu ena osakhulupilila Mulungu anapacika. Mwacionekele, io amaona kuti Mulungu ndi wosafunika kwa io.
Anthu ambili amanena kuti amakhulupilila Mulungu. Koma zosankha zao zimaonetsa kuti io amaona monga kulibe Mulungu. Ponena za mamembala a chalichi cao, Bishopu wamkulu wa Katolika, Salvatore Fisichella, anati: Masiku ano, n’zovuta kuti munthu adziŵe kuti ndife Akristu cifukwa cakuti makhalidwe athu amalingana ndi a anthu osapembeza.
Anthu ena alibiletu nthawi yoganizila za Mulungu. Iwo amaona kuti Mulungu amakhala kutali kwambili ndipo sangawathandize mwa njila iliyonse. Anthu a conco amaganizila za Mulungu pokhapo akakhala pa mavuto, kapena ngati afuna cina cake kwa iye. Iwo amamuona monga kapolo wao amene afunika kucita zimene io afuna.
Anthu ena samagwilitsila nchito zimene amaphunzila ku machalichi kwao, mwina cifukwa cakuti amaona monga zimene amaphunzila kumeneko n’zopanda phindu. Mwacitsanzo, Akatolika a ku Germany 76 pa 100 alionse, amakhulupilila kuti palibe vuto kuti mwamuna ndi mkazi azikhalila limodzi asanakwatilane. Ndipo maganizo amenewa ndi osiyana ndi zimene amaphunzila m’Baibo ndi kuchalichi kwao. (1 Akorinto 6:18; Aheberi 13:4) Anthu a zipembedzo zina amavomeleza mfundo yakuti anthu ambili amanena kuti ndi Akristu koma zocita zao zimakhala zosiyana ndi zimene amakhulupilila. Atsogoleli ambili a zipembedzo zosiyana-siyana, amadandaula kuti mamembala ao amacita zinthu monga anthu amene sakhulupilila Mulungu.
Zitsanzo zimenezi zimatipangitsa kufunsa kuti: Kodi Mulungu ndi wofunikadi kwa ife? Nkhani imeneyi si yacilendo. Imapezekanso m’macaputala oyambilila a m’Baibo. Koma coyamba, tiyeni tikambilane nkhani zingapo za m’buku la Genesis kuti tidziŵe ngati Mulungu ndi wofunika kwa ife kapena ai.