NKHANI YA PACIKUTO | KODI MULUNGU NDI WOFUNIKA KWA IFE?
Cifukwa Cake Mulungu Ndi Wofunika kwa Ife
Akatswili a za maganizo amakamba kuti anthu amafunikila zinthu zakuuzimu kuti akhaledi osangalala. Umboni wa zimenezi umaoneka pamene anthu amafuna kukwanilitsa colinga cina cake cacikulu paumoyo wao kapena kulambila wina wake wapamwamba. Kuti akhutilitse cikhumbo cimeneci, ena amataila nthawi yao kusangalala ndi cilengedwe, kucita zinthu zina za luso la zopanga-panga, kusangalala ndi nyimbo kapena kucita zinthu zina. Komabe, anthu ambili ngakhale atacita zimenezi samakhala ndi cisangalalo cokhalitsa.
Mfundo yakuti anthu mwacibadwa amafuna zinthu zakuuzimu ndi yosadabwitsa kwa anthu amene amaŵelenga Baibo. Macaputala oyambilila a buku la Genesis amaonetsa kuti pamene Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi woyamba, iye anali kulankhula nao nthawi zonse n’colinga cakuti anthuwo akhale naye paubwenzi. (Genesis 3:8-10) Mulungu sanalenge anthu kuti azidziimila paokha. Iwo amafunika kukhala paubwenzi wabwino ndi iye monga Mlengi wao. Ndipo Baibo kaŵili-kaŵili imakamba za kufunika kokhala paubwenzi ndi Mulungu.
Mwacitsanzo, Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu.” (Mateyu 5:3) Mau awa amaonetsa kuti munthu amakhala wosangalala akakhutilitsa cikhumbo cake cofuna kudziŵa Mulungu. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Yesu anapeleka yankho la funso limeneli pamene anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mau onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) Kodi mau a Mulungu, kapena kuti maganizo ake amene ali m’Baibo, angatithandize bwanji kukhala ndi moyo wosangalala ndi waphindu? Tiyeni tikambilane njila zitatu zofunika.
Tifunika Malangizo Abwino
Masiku ano pali akatswili ambili amene amapeleka malangizo pankhani za cikondi, kupeza mabwenzi abwino, umoyo wa banja, kuthetsa mikangano, cimwemwe, ndi mmene tingakhalile ndi umoyo waphindu. Palibe wina aliyense amene angapeleke malangizo abwino ndiponso othandiza pa nkhani zimenezi kuposa mlengi wathu, Yehova Mulungu.
Mwacitsanzo, mukagula ciwiya catsopano, monga kamela kapena kompyuta, nthawi zambili mumapatsidwa kabuku ka malangizo kocokela kwa amene anapanga ciwiyaco kuti mudziŵe mmene mungacigwilitsile nchito bwino. Baibo ili ngati kabuku ka malangizo kameneko. Iyo ndi buku la malangizo limene mlengi wathu, Mulungu, wapeleka kwa anthu. Buku limeneli limafotokoza colinga cimene Mulungu anatilengela ndi kupeleka malangizo amene tiyenela kutsatila kuti tikhale ndi moyo wabwino.
Mofanana ndi kabuku ka malangizo kolembedwa bwino, Baibo imacenjeza anthu za makhalidwe amene angaike moyo wao paciswe. Anthu ena angatipatse malangizo amene angaoneke kukhala osavuta kutsatila. Koma ndi nzelu kutsatila malangizo amene Mlengi wathu amatipatsa kuti tipewe mavuto ndi kukhala ndi umoyo waphindu.
Ngakhale kuti Yehova Mulungu amatipatsa malangizo, iye samatikakamiza kuwatsatila. Koma cifukwa cakuti amatikonda ndipo amafuna kutithandiza, amaticondelela kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Conco ngati timamvela malangizo a Yehova, tidzakhala ndi umoyo wabwino kwambili. M’mau ena tinganene kuti Mulungu ndi wofunika kwa ife kuti tikhale ndi moyo wabwino ndiponso kuti tikhale acimwemwe.
Tifunika Kudziŵa Cifukwa Cake Timavutika
Anthu ena amaona kuti Mulungu ndi wosafunika kwa io akaona mavuto ambili amene timakumana nao paumoyo, ndipo amati zimenezi sizigwilizana ndi ciphunzitso cakuti Mulungu ndi wacikondi. Mwacitsanzo, io angafunse kuti: ‘N’cifukwa ciani anthu abwino amavutika?’ ‘N’cifukwa ciani nthawi zina makanda osalakwa amabadwa olemala?’ ‘N’cifukwa ciani timakumana ndi zinthu zambili zopanda cilungamo?’ Amenewa ndi mafunso ofunika kwambili, ndipo kupeza mayankho okhutilitsa a mafunso amenewa kungatipindulitse kwambili. Koma m’malo mofulumila kuimba Mulungu mlandu cifukwa ca mavuto amenewo, tiyeni tione zimene Mau a Mulungu, Baibo, amanena pa nkhani imeneyi.
M’caputala cacitatu ca Genesis, muli nkhani yokhudza Satana amene kudzela mwa njoka anapangitsa anthu aŵili oyambilila kusamvela lamulo la Yehova Mulungu lakuti asadye cipatso ca mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Satana anauza Hava kuti: “Kufa simudzafai; cifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 2:16, 17; 3:4, 5.
Mwa kunena mau amenewa, Satana anasonyeza kuti Mulungu ndi wabodza ndiponso kuti Mulungu salamulila mwacilungamo. Mdyelekezi anaonetsa kuti ngati anthu amvela iye, zinthu zikhoza kuwayendela bwino. Kodi nkhanizo zikanathetsedwa motani? Yehova analola kuti papite nthawi yokwanila kuti onse aone ngati nkhani zimene Satana anam’neneza zinali zoona kapena ai. Mwa kutelo, Mulungu anapatsa mpata Satana ndi onse amene anakhala kumbali yake kuti aonetse ngati anthu angakhale ndi umoyo wabwino popanda Mulungu.
Kodi muganiza kuti zimene Satana ananeneza Mulungu zinali zoona? Kodi anthu angakhale ndi umoyo wabwino kapena kudzilamulila bwino-bwino popanda Mulungu? Kwa zaka zambili, mtundu wa anthu wakhala ukukumana ndi mavuto monga matenda, imfa, upandu, cisalungamo, kuloŵa pansi kwa makhalidwe, nkhondo, kupulula anthu ndiponso mavuto ena. Zimenezi ndi umboni wotsatsutsika wakuti anthu alephelelatu kudzilamulila okha. Baibo imaonetsa kuti Mulungu si ndiye amacititsa mavuto amene anthu amakumana nao. Koma imafotokoza cifukwa cacikulu cimene cimacititsa mavuto. Iyo imati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”—Mlaliki 8:9.
Mfundo imeneyi ikuonetsa kufunika kodalila Mulungu kuti atithandize kupeza mayankho a mafunso ovuta amene timakhala nao ndiponso kuti adzathetse mavuto amenewa. Kodi Mulungu adzacitapo ciani?
Tifunika Thandizo la Mulungu
Kwa nthawi yaitali, anthu akhala akulakalaka umoyo wopanda matenda, ukalamba, ndi imfa. Iwo ataya nthawi yaitali, mphamvu ndi cuma cambili kuti akhale ndi umoyo wathanzi, koma zimenezo sizinaphule kanthu kweni-kweni. Anthu ena ayesa kumwa mankhwala ena ake, kupita kwa okhulupilila mizimu kapena kucita maseŵela olimbitsa thupi ndi colinga cofuna umoyo wathanzi ndi wautali. Zoyesayesa zao zakhala zogwilitsa mwala.
Mulungu amafuna kuti anthu akhale ndi umoyo wathanzi ndi kuti akhale acimwemwe. Cimeneci ndi cimene cinali colinga cake pamene analenga anthu, ndipo colinga cimeneco sanaciiwale. (Genesis 1:27, 28; Yesaya 45:18) Yehova Mulungu amatitsimikizila kuti ciliconse cimene iye afuna kucita, cidzacitikadi. (Yesaya 55:10, 11) Baibo imakamba za lonjeza la Mulungu lokonzanso dziko kukhala Paladaiso imene anthu oyambilila anataya. M’buku lomalizila la m’Baibo, timapezamo mau akuti: “Iye [Yehova Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi Mulungu adzakwanilitsa bwanji zimenezi? Nanga n’ciani cimene tiyenela kucita kuti tidzapindule ndi malonjezo amenewa?
Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anaphunzitsa otsatila ake kuti azipemphela kuti cifunilo ca Mulungu cicitike. Anthu ambili amalidziŵa pemphelo limeneli kapena kulinena mobweleza-bweleza, ndipo ena amalicha Pemphelo la Ambuye. Pemphelo limeneli limati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ndithudi, Ufumu wa Mulungu ndiwo njila imene Yehova Mulungu adzagwilitsila nchito kuthetsa mavuto onse obwela cifukwa ca ulamulilo wa anthu. Ufumu umenewu udzabweletsa dziko lolungama limene Mulungu analonjeza.a (Danieli 2:44; 2 Petulo 3:13) Kodi tiyenela kucita ciani kuti tidzapindule ndi malonjezo a Mulungu?
Yesu Kristu anafotokoza cinthu cosavuta cimene tiyenela kucita. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Ndithudi, ndi thandizo la Mulungu, tikhoza kudzapeza moyo wosatha m’dziko latsopano lolonjezedwa. Kodi ciyembekezo cimeneci si cifukwa cina conenela kuti Mulungu ndi wofunikadi kwa ife?
Ino Ndi Nthawi Yoyenela Kuganizila za Mulungu
Zaka 2000 zapitazo pa Areopagi, kapena kuti pa Phiri la Mars, ku Atene, mtumwi Paulo analankhula ndi nzika za mu Atene ponena za Mulungu. Anthu amenewa anali ndi maganizo ao-ao pa zinthu, koma anali ofunitsitsa kuphunzila zina zatsopano. Paulo anawauza kuti: “Ndi iyeyo [Mulungu] amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. Pakuti cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo, monga mmene andakatulo ena pakati panu anenela kuti, ‘Pakuti ndife mbadwa zake.’”—Machitidwe 17:25, 28.
Mau amene Paulo anauza nzika za ku Atene ndi oona ngakhale masiku ano. Mlengi wathu amatipatsa mpweya, cakudya ndi madzi. N’zosatheka kukhala ndi moyo popanda zinthu zabwino zimene Yehova watipatsa zimene zimacilikiza moyo wathu. Koma kodi n’cifukwa ciani Mulungu amapeleka zinthu zimenezi kwa anthu onse amene amaganizila za iye ndi amene samam’ganizila? Paulo anakamba kuti: “Anacita zimenezi kuti anthuwo afune-fune Mulungu, amufufuze-fufuze ndi kumupezadi, ngakhale kuti kweni-kweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:27.
Kodi mungafune kumudziŵa bwino Mulungu, kutanthauza kudziŵa zolinga zake ndi mmene mungakhalile ndi moyo wabwino tsopano ndiponso kosatha? Ngati mufuna, tikukulimbikitsani kulankhula ndi munthu amene anakupatsani magazini ino kapena kulembela kalata amene amafalitsa magazini imeneyi. Iwo adzakhala okondwa kukuthandizani.
[Mau apansi]
a Kuti mudziŵe zambili za mmene Ufumu udzapangitsile cifunilo ca Mulungu kucitika padziko lapansi, onani nkhani 8 m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mukhoza kupeza buku limeneli kapena kulitenga pa webu saiti yathu ya www.jw.org.
[Cithunzi papeji 7]
Mulungu amafuna kuti tikhale acimwemwe masiku ano ndi kosatha
[Cithunzi papeji 4]
Mofanana ndi kabuku ka malangizo, Baibo imatitsogolela paumoyo
[Mau okopa papeji 5]
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”—Yesaya 48:17, 18
[Cithunzi papeji 6]
M’Baibo, timapezamo malangizo ndi thandizo limene timafunikila