LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 1/1 tsa. 32
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso a m’Baibo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Kulimbana ndi Zopanda Cilungamo m’Njira Yabwino Koposa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Zimene Zingatithandize Kupilila Zopanda Cilungamo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • “Woweluza wa Dziko Lonse” Amacita Cilungamo Nthawi Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 1/1 tsa. 32

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO

Kodi Mulungu ndi wotani?

Mulungu ali ndi thupi lauzimu ndipo sitingamuone. Iye analenga kumwamba, dziko lapansi ndi zamoyo zonse. Palibe amene analenga Mulungu ndipo iye alibe ciyambi. (Salimo 90:2) Mulungu amafuna kuti anthu azimufuna-funa ndi kudziŵa zeni-zeni ponena za iye.—Ŵelengani Machitidwe 17:24-27.

Mulungu ali ndi dzina limene amadziwika nalo. Tingadziŵe makhalidwe ake ena mwa kuganizila zinthu zimene anapanga. (Aroma 1:20) Koma kuti tim’dziŵe bwino Mulungu, tifunikila kuphunzila Mau ake, Baibo. Iyo imatithandiza kudziŵa kuti Mulungu ndi wacikondi.—Ŵelengani Salimo 103:7-10.

Kodi Mulungu amamva bwanji akaona kupanda cilungamo?

Mlengi wathu, Yehova, amadana ndi kupanda cilungamo. Ndipo analenga anthu m’cifanizilo cake. (Deuteronomo 25:16) N’cifukwa cake ambili a ife timadana ndi kupanda cilungamo. Si Mulungu amene amacititsa zinthu zopanda cilungamo zimene timaona. Mulungu analenga anthu ndi ufulu wosankha. Koma n’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili amagwilitsila nchito molakwa ufulu wao wosankha ndipo amacita zinthu zoipa. Zinthu zimenezi zimapweteka kwambili mtima wa Yehova.—Ŵelengani Genesis 6:5, 6; Deuteronomo 32:4, 5.

Yehova amakonda cilungamo, ndipo sadzalekelela zoipa mpaka kale-kale. (Salimo 37:28, 29) Baibo imalonjeza kuti posacedwapa Mulungu adzathetselatu zinthu zoipa.—Ŵelengani 2 Petulo 3:7-9, 13.

Baibo imalonjeza kuti Mulungu posacedwapa adzathetsa zinthu zonse zopanda cilungamo

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 1 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Buku limeneli likupezekanso pa www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani