Zamkati
January 1, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NKHANI ZOPHUNZILA
MARCH 3-9, 2014
Lambilani Yehova, Mfumu Yamuyaya
TSAMBA 7 • NYIMBO: 106, 46
MARCH 10-16, 2014
Kodi Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 100 Wakupindulitsani Bwanji?
TSAMBA 12 • NYIMBO: 97, 101
MARCH 17-23, 2014
Pangani Zosankha Mwanzelu Mukali Acinyamata
TSAMBA 17 • NYIMBO: 41, 89
MARCH 24-30, 2014
Tumikilani Yehova Asanafike Masiku Oipa
TSAMBA 22 • NYIMBO: 54, 17
MARCH 31, 2014–APRIL 6, 2014
“Ufumu Wanu Ubwele”—Kodi Udzabwela Liti?
TSAMBA 27 • NYIMBO: 108, 30
NKHANI ZOPHUNZILA
Lambilani Yehova, Mfumu Yamuyaya
Nkhani imeneyi idzatitsimikizila kuti Yehova nthawi zonse wakhala Mfumu ndipo idzaonetsa mmene wasonyezela ucifumu wake ku zolengedwa zake zakumwamba ndi za padziko lapansi. Nkhaniyi idzatilimbikitsanso kutsatila zitsanzo za anthu akale amene anasankha kulambila Yehova, Mfumu yamuyaya.
▪ Kodi Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 100 Wakupindulitsani Bwanji?
Nkhaniyi idzatilimbikitsa kuyamikila kwambili zimene Ufumu wa Mesiya wakwanilitsa pa zaka 100 zoyambilila. Idzalimbikitsanso aliyense wa ife kukhalabe nzika yokhulupilika ya Ufumu, ndiponso idzatilimbikitsa kusinkha-sinkha tanthauzo la lemba la caka ca 2014.
▪ Pangani Zosankha Mwanzelu Mukali Acinyamata
▪ Tumikilani Yehova Asanafike Masiku Oipa
Kodi moyo wanga ndidzaugwilitsila nchito motani? Ili ndi funso lofunika kwambili limene wina aliyense amene anadzipeleka kwa Yehova ayenela kudzifunsa. M’nkhanizi, tidzakambilana mfundo zimene zingathandize Akristu acinyamata kutumikila Mulungu mokwanila ndiponso mipata imene Akristu acikulile ali nayo yoonjezela utumiki wao.
▪ Ufumu Wanu Ubwele”—Kodi Udzabwela Liti?
Anthu ambili masiku ano asokonezedwa ndi zimene zikucitika m’dzikoli kapena cifukwa cofuna-funa zinthu zakuthupi. Nkhaniyi idzafotokoza maumboni atatu amene amathandiza Akristu kukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu udzaononga dongosolo loipali posacedwapa.