Tsanzilani Cikhulupililo ca Mose
“Mwa cikhulupililo, Mose atakula anakana kuchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.”—AHEB. 11:24.
1, 2. (a) Kodi Mose anapanga cosankha cotani ali ndi zaka 40? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’cifukwa ciani Mose anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu?
MOSE anadziŵa kuti akanakhala ndi tsogolo labwino m’dziko la Iguputo. Dzikolo linali ndi nyumba zazikulu zokongola ndipo linali lotukuka. Iye anakulila m’banja lacifumu ndipo “anaphunzila nzelu zonse za Aiguputo.” Mwacionekele, iye anaphunzila luso losiyanasiyana, zinthu zakuthambo, masamu, ndi sayansi. (Mac. 7:22) Zikanakhala zosavuta kuti iye akhale ndi cuma, ulamulilo ndi udindo, zinthu zimene Aiguputo ena sakanakhala nazo.
2 Komabe, ali ndi zaka 40, Mose anapanga cosankha cimene cinadabwitsa banja lacifumu laciiguputo limene linali kum’sunga. Iye sanasankhe ngakhale umoyo wa Aiguputo wamba, koma anasankha kukhala pamodzi ndi akapolo. N’cifukwa ciani anasankha zimenezo? Cifukwa cakuti Mose anali ndi cikhulupililo. (Ŵelengani Aheberi 11:24-26.) Cifukwa ca cikhulupililo, Mose sanaike maganizo ake pa zinthu zooneka ndi maso. Iye anali kukhulupililabe “Wosaonekayo,” Yehova, ndi malonjezo ake.—Aheb. 11:27.
3. Kodi tikambilana mafunso atatu ati m’nkhani ino?
3 Mofanana ndi Mose, sitiyenela kuika maganizo athu pa zinthu zooneka ndi maso. M’malo mwake, tiyenela kukhala “mtundu wa anthu okhala ndi cikhulupililo.” (Aheb. 10:38, 39) Tiyeni tiphunzile mmene nkhani yokhudza Mose yopezeka pa Aheberi 11:24-26 ingatithandizile kulimbitsa cikhulupililo cathu. Pamene ticita zimenezi, tiyeni tipeze mayankho pa mafunso awa: Kodi cikhulupililo cinathandiza bwanji Mose kukaniza zilakolako zathupi? Pamene Mose anali kutonzedwa, kodi cikhulupililo cinam’thandiza bwanji kuona utumiki wake kukhala wofunika? Nanga n’cifukwa ciani Mose “anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandile”?
ANAKANIZA ZILAKOLAKO ZATHUPI
4. Kodi Mose anazindikila ciani pankhani ya ‘zosangalatsa zaucimo’?
4 Cifukwa ca cikhulupililo, Mose anazindikila kuti ‘zosangalatsa zaucimo’ zinali zosakhalitsa. Mwina anthu ena anadabwa kuona kuti dziko la Iguputo, mmene anthu anali kucita zamatsenga ndi kukhulupilila mizimu, linakhala ufumu wamphamvu padziko lonse koma anthu a Yehova anali akapolo m’dzikolo. Komabe, Mose anali ndi cidalilo cakuti Mulungu akanasintha zinthu. Ngakhale kuti anthu amene anali kufuna kukhutilitsa zilakolako zao zinthu zinali kuwayendela bwino, Mose anali kukhulupilila kuti oipa adzaonongedwa. Conco, iye sananyengedwe ndi ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo.’
5. N’ciani cingatithandize kukaniza ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo’?
5 Kodi tingakanize bwanji ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo’? Tiyenela kudziŵa kuti zosangalatsa zaucimo n’zosakhalitsa. Cikhulupililo cidzatithandiza kudziŵa kuti “dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake.” (1 Yoh. 2:15-17) Ndipo tiyenela kukumbukila zimene zidzacitikila anthu ocimwa osalapa. Iwo ali ‘pamalo otelela . . . mapeto ao ndi oopsa.’ (Sal. 73:18, 19) Mukayesedwa kuti mucite chimo, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimenezi zidzakhudza bwanji tsogolo langa?’
6. (a) N’cifukwa ciani Mose anakana “kuchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao”? (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti Mose anasankha zinthu mwanzelu?
6 Cikhulupililo cinathandizanso Mose kusankha zocita paumoyo. “Mwa cikhulupililo, Mose atakula anakana kuchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.” (Aheb. 11:24) Mose sanaganize kuti angatumikile Mulungu m’nyumba yacifumu ndi kugwilitsila nchito cuma cake kuthandiza abale ake Aisiraeli. M’malo mwake, anatsimikiza mtima kukonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse ndi mphamvu zake zonse. (Deut. 6:5) Zimene Mose anasankha zinam’thandiza kupewa mavuto aakulu. Cuma cambili ca Aiguputo cimene anakana cinafunkhidwa ndi Aisiraeli. (Eks. 12:35, 36) Farao anacititsidwa manyazi ndipo anaphedwa. (Sal. 136:15) Koma Mose anapulumutsidwa ndipo Mulungu anam’gwilitsila nchito kutsogolela Aisiraeli kuti apulumuke. Ndithudi, moyo wake unali waphindu.
7. (a) Malinga ndi Mateyu 6:19-21, n’cifukwa ciani tiyenela kudziunjikila cuma cosatha? (b) Pelekani citsanzo coonetsa mmene kuunjika cuma cakuthupi kumasiyanilana ndi kuunjika cuma ca kuuzimu.
7 Ngati ndinu mtumiki wacinyamata wa Yehova, kodi cikhulupililo cingakuthandizeni bwanji kusankha zimene mudzacita paumoyo wanu? Muyenela kukonzekela tsogolo lanu ndi kukhulupilila malonjezo a Mulungu. Ndipo muyenelanso ‘kudziunjikila’ cuma cosatha osati cakanthawi. (Ŵelengani Mateyu 6:19-21.) Izi n’zimene Sophie, amene anali ndi luso lovina anasankha. Iye anapatsidwa mwai womulipilila maphunzilo ndipo makampani ambili oyang’anila zovinavina m’dziko la United States anali kum’gwilitsila nchito. Iye anati: “Ndinasangalala kupatsidwa mwai umenewu. Ndipo ndinadziona kukhala wapamwamba kuposa anzanga, koma ngakhale zinali conco ndinalibe cimwemwe.” Pambuyo popenyelela vidiyo yakuti, Young People Ask—What Will I Do With My Life?, Sophie anati: “Ndinazindikila kuti dziko linandipatsa cipambano ndi ulemu mosinthanitsa ndi utumiki wanga kwa Yehova. Ndinapemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima, ndiyeno ndinaleka nchito yanga yovina.” Ponena za cosankha cake, iye anati: “Sindimalakalaka umoyo wanga wakale ndipo ndili ndi cimwemwe cacikulu kwambili masiku ano. Ineyo ndi mwamuna wanga tikucita upainiya. Sindife ochuka ndipo tilibe zinthu zambili zakuthupi, koma tili ndi Yehova, maphunzilo a Baibulo ndi zolinga za kuuzimu. Sindiona kuti ndinalakwitsa kupanga cosankha cimeneci.”
8. Ndi malangizo ati a m’Baibulo amene angathandize wacinyamata kusankha zocita?
8 Yehova amadziŵa zimene zingatipindulitse. Mose anati: “Kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzicita ciani, koposa kuopa Yehova Mulungu wanu kuti muziyenda m’njila zake zonse, kukonda ndi kutumikila Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lelo, kuti zinthu zikuyendeleni bwino?” (Deut. 10:12, 13) Pamene mukali acinyamata, pangani cosankha cimene cidzakuthandizani kukonda Yehova ndi kum’tumikila “ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.” Mukatelo mudzakhala otsimikiza kuti ‘zinthu zidzakuyendelani bwino.’
ANAONA UTUMIKI WAKE KUKHALA WOFUNIKA
9. Fotokozani cifukwa cake ziyenela kuti zinali zovuta kuti Mose akwanilitse utumiki wake.
9 Mose “anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa kukhala cuma coculuka kuposa cuma ca Iguputo.” (Aheb. 11:26) Pa lembali, Mose akunenedwa kuti “Wodzozedwa” cifukwa cakuti anasankhidwa ndi Yehova kuti atsogolele Aisiraeli kucoka mu Iguputo. Mose anadziŵa kuti kucita zimenezi kunali kovuta, ndi kuti ‘akanatonzedwa.’ Mwiisiraeli wina anali atanyozapo Mose kuti: “Anakuika iwe ndani kukhala kalonga ndi woweluza wathu?” (Eks. 2:13, 14) Panthawi ina Mose anafunsa Yehova kuti: “Nanga Farao akandimvela bwanji?” (Eks. 6:12) Mose anauza Yehova nkhawa zake kuti apilile citonzo. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Mose kuti akwanilitse nchito yovuta?
10. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Mose kuti akwanilitse utumiki wake?
10 Coyamba, Yehova anatsimikizila Mose kuti: “Ndidzakhala nawe.” (Eks. 3:12) Caciŵili, Yehova anam’patsa cidalilo mwa kumuuza tanthauzo la dzina lake kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.”a (Eks. 3:14) Cacitatu, anapatsa Mose mphamvu yocita zozizwitsa, imene inaonetsa kuti iye anatumidwa ndi Mulungu. (Eks. 4:2-5) Cacinai, Yehova anasankha Aroni kukhala wolankhulilako Mose ndi kum’thandiza kukwanilitsa utumiki wake. (Eks. 4:14-16) Ali pafupi kufa, Mose anali wotsimikiza kuti Mulungu amathandiza atumiki ake kukwanilitsa utumiki uliwonse. Iye anali kudalila Yehova kwambili cakuti anauuza Yoswa kuti: “Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye adzapitiliza kuyenda nanu. Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono. Conco musaope kapena kucita mantha.”—Deut. 31:8.
11. N’cifukwa ciani Mose anaona utumiki wake kukhala wofunika kwambili?
11 Cifukwa ca thandizo la Yehova, Mose anaona utumiki wake wovuta kukhala “cuma coculuka kuposa cuma ca Iguputo.” Palibe cinthu cofunika kwambili kuposa kutumikila Mulungu Wamphamvuyonse. Kukhala mtsogoleli wa Aisiraeli cinali cinthu cofunika kwambili kuposa kukhala kalonga mu Iguputo. Mose anadalitsidwa cifukwa ca maganizo ake oyenela. Iye anali paubwenzi wapadela ndi Yehova, amene anam’thandiza kucita “zinthu zazikulu” potsogolela Aisiraeli M’dziko Lolonjezedwa.—Deut. 34:10-12.
12. Kodi Yehova watipatsa mautumiki ati?
12 Nafenso tili ndi nchito. Kupyolela mwa Mwana wake, Yehova watipatsa nchito yolalikila, imenenso mtumwi Paulo ndi ena anali nayo. (Ŵelengani 1 Timoteyo 1:12-14.) Ife tonse tili ndi mwai wolengeza uthenga wabwino. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Ena ndi atumiki a nthawi zonse ndipo abale okhwima amatumikila ena mumpingo monga akulu ndi atumiki othandiza. Komabe, acibale anu osakhulupilila ndi ena sangaone ubwino wa utumiki umenewu. Ndipo io angayambe kukutonzani cifukwa ca kudzipeleka kwanu. (Mat. 10:34-37) Anthu amenewa akakufooketsani, mungayambe kuganiza kuti kudzipeleka kwanu ndi kopanda phindu ndi kuti simungakwanilitse utumiki wanu. Kodi cikhulupililo cingakuthandizeni bwanji kupilila ngati zimenezi zakucitikilani?
13. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tikwanilitse utumiki wathu?
13 Pemphani Yehova kuti akucilikizeni muli ndi cikhulupililo kuti adzakuthandizani, ndipo muuzeni nkhaŵa zanu. Popeza kuti ndiye anakupatsani nchitoyi, adzakuthandizani kuti muikwanilitse. Kodi adzakuthandizani bwanji? Adzakuthandizani monga mmene anathandizila Mose. Coyamba, Yehova amakutsimikizilani kuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.” (Yes. 41:10) Caciŵili, Mulungu amakukumbutsani kuti malonjezo ake ndi odalilika. Iye anati: “Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazicita. Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazicitadi.” (Yes. 46:11) Cacitatu, Yehova amakupatsani “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti mukwanilitse utumiki wanu. (2 Akor. 4:7) Ndipo cacinai, Atate wathu wacikondi wakupatsani ubale wapadziko lonse wa alambili oona amene ‘amapitilizabe kukutonthozani ndi kukulimbikitsani.’ (1 Ates. 5:11) Ngati Yehova wakuthandizani kuti mukwanilitse utumiki wanu, cikhulupililo canu cidzalimba. Zimenezi zidzakuthandizani kuona utumiki wanu kukhala wofunika kwambili kuposa ciliconse cimene dzikoli lingapeleke.
“ANAYANG’ANITSITSA PAMPHOTO IMENE ADZALANDILE”
14. N’cifukwa ciani Mose anali ndi cikhulupililo cakuti adzalandila mphoto?
14 Mose “anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandile.” (Aheb. 11:26) Ngakhale kuti Mose sanadziŵe zambili zokhudza zinthu zamtsogolo, iye anapanga zosankha mogwilizana ndi zocepa zimene anali kudziŵa. Mofanana ndi kholo lake Abulahamu, Mose anali ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzaukitsa akufa. (Luka 20:37, 38; Aheb. 11:17-19) Ciyembekezo ca madalitso amtsogolo cinathandiza Mose kusaona zaka 40 za umoyo wothaŵathaŵa ndi zaka 40 m’cipululu kuti kunali kutaya nthawi. Ngakhale kuti sanadziŵe zonse zokhudza kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Mulungu, cikhulupililo cinam’thandiza kuona mphoto yosaoneka.
15, 16. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuyang’anitsitsa pamphoto yathu? (b) Ndi madalitso ati amene mufunitsitsa kudzalandila mu Ufumu wa Mulungu?
15 Kodi inuyo ‘mumayang’anitsitsa pa pamphoto’ imene mudzalandila? Mofanana ndi Mose, sitimadziŵa zonse zokhudza malonjezo a Mulungu. Mwacitsanzo, sitidziŵa “nthawi yoikidwilatu” ya cisautso cacikulu. (Maliko 13:32, 33) Koma timadziŵa zambili zokhudza Paladaiso wamtsogolo kuposa zimene Mose anali kudziŵa. Ngakhale kuti sitidziŵa zonse, Mulungu watiuza zambili za mmene umoyo udzakhalila mu Ufumu wake umene ‘timayang’anitsitsa.’ Kukhala ndi cithunzi ca dziko latsopano m’maganizo mwathu kudzatithandiza kufuna Ufumuwo coyamba. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Mwacitsanzo, kodi mungapeleke ndalama kuti mugule nyumba imene simudziŵa bwino? Iyai simungatelo. Mofananamo, sitingaononge nthawi yathu kuganizila za ciyembezedzo cimene si ceniceni kwa ife. Cikhulupililo cidzatithandiza kuona cithunzi m’maganizo mwathu ca mmene umoyo udzakhalila mu Ufumu wa Mulungu.
16 Kuti mukhale ndi cithunzi ca Ufumu wa Mulungu m’maganizo mwanu, ‘yang’anitsitsani,’ kapena ganizilani mmene umoyo wanu udzakhalila m’Paladaiso. Mwacitsanzo, pophunzila za umoyo wa anthu a m’Baibulo, ganizilani zimene mungawafunse akadzaukitsidwa. Ganizilaninso zimene angadzakufunseni ponena za umoyo wanu m’masiku otsiliza. Onani cithunzi m’maganizo mwanu ca cimwemwe cimene mudzakhala naco podzawaonanso acibale anu amene anamwalila kalekale ndi podzawaphunzitsa zimene Mulungu adzakhala atawacitila. Onaninso cimwemwe cimene mudzakhala naco pophunzila zambili zokhudza nyama zakuthengo m’dziko lapansi lamtendele. Sinkhasinkhani mmene ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimbila mukadzayamba kukhala angwilo.
17. Kodi kukhala ndi cithunzi m’maganizo mwathu ca mphoto yosaoneka kungatithandize bwanji masiku ano?
17 Kukhala ndi cithunzi m’maganizo mwathu ca mphoto ya mtsogolo kudzatithandiza kupilila. Kudzatithandizanso kukhala ndi cimwemwe ndi kupanga zosankha zanzelu podziŵa kuti tidzakhala kwamuyaya. Paulo analembela Akristu odzozedwa kuti: “Ngati tikuyembekezela cimene sitikuciona, timacidikilabe mopilila.” (Aroma 8:25) Mfundoyi ikhudzanso Akristu onse amene ali ndi ciyembekedzo ca moyo wosatha. Ngakhale kuti tikalibe kulandila mphoto yathu, tili ndi cikhulupililo colimba cimene cimatithandiza kuyembekezela moleza mtima ‘mphoto imene tidzalandila.’ Mofanana ndi Mose, sitimaona kuti zaka zimene tatumikila Yehova ndi kutaya nthawi. M’malo mwake, ndife otsimikiza mtima kuti zinthu “zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.”—Ŵelengani 2 Akorinto 4:16-18.
18, 19. (a) N’cifukwa ciani tifunika kucita khama kuti tikhalebe ndi cikhulupililo? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
18 Cikhulupililo cimatithandiza kuona “umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheb. 11:1) Munthu wopanda cikhulupililo samaona kufunika kotumikila Yehova. Iye amaona zinthu za kuuzimu “ngati zopusa.” (1 Akor. 2:14) Mosiyana ndi anthu a m’dzikoli, ife tili ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha ndi kudzaona anthu akufa aukitsidwa. Anthu ena a m’nthawi ya Paulo anamunena kuti anali “wobwetuka” wosadziŵa zinthu. Cimodzimodzinso masiku ano, anthu ambili amaona kuti ciyembekezo cimene timalengeza n’copanda pake.—Mac. 17:18.
19 Popeza kuti tili m’dziko limene anthu alibe cikhulupililo, tifunika kucita khama kuti tikhalebe ndi cikhulupililo. Conco, pemphani Yehova ‘kuti cikhulupililo canu cisathe.’ (Luka 22:32) Mofanana ndi Mose, muziganizila zotsatilapo zaucimo, mwai wotumikila Yehova ndi ciyembekezo ca moyo wosatha. Kodi palinso zina zimene tingaphunzile kwa Mose? Inde. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene cikhulupililo cinathandizila Mose kuona “Wosaonekayo.”—Aheb. 11:27.
a Pofotokoza Mau a pa Ekisodo 3:14, katswili wina wolemba Baibulo anati: “Palibe cimene cingalepheletse Mulungu kukwanilitsa cifuno cake . . . Dzina limeneli [Yehova] linali citetezo kwa Aisiraeli, ndipo linali ciyembekezo ndi citonthozo cao.”