Kodi Mumaona “Wosaonekayo”?
“Anapitiliza kupilila moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.”—AHEB. 11:27.
1, 2. (a) Fotokozani cifukwa cake zinaoneka kuti Mose anali pangozi. (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’cifukwa ciani Mose sanaope mfumu?
FARAO anali mfumu yamphamvu ndipo Aiguputo anali kumuona ngati mulungu wamoyo. Buku lina limati, Aiguputo anamuona kukhala “wanzelu ndi wamphamvu kuposa zamoyo zonse.” (When Egypt Ruled the East) Kuti Aiguputo azimuopa Farao, iye anali kuvala cisoti cacifumu cokhala ndi cifanizo ca njoka imene ifuna kuluma munthu. Cifanizo cimeneci cinali kuonetsa kuti mfumu inali yokonzeka kuononga adani ake nthawi iliyonse. Ganizilani cabe mmene Mose anamvelela pamene Yehova anamuuza kuti: “Ndikutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga ana a Isiraeli ku Iguputo.”—Eks. 3:10.
2 Mose anapita ku Iguputo kukapeleka uthenga wa Mulungu kwa Farao, ndipo zimenezo zinam’kwiitsa Farao. Pambuyo pakuti Aiguputo akanthidwa ndi milili 9, Farao mwaukali anauza Mose kuti: “Samala! Ndisadzakuonenso, cifukwa ndikadzangokuonanso udzafa.” (Eks. 10:28) Mose asanacoke pamaso pa Farao analosela kuti mwana wamwamuna woyamba wa mfumu adzafa. (Eks. 11:4-8) Ndiyeno, anauza mabanja aciisiraeli kupha mbuzi kapena nkhosa ndi kuwaza magazi pamakomo a nyumba zao. Nyama imeneyi inali yopatulika kwa mulungu wa Aiguputo wochedwa Ra. (Eks. 12:5-7) Kodi Farao akanacita ciani? Mose sanaope zimene Farao akanacita. N’cifukwa ciani sanaope? Cifukwa cakuti Mose anali kukhulupilila ndi kumvela Yehova. Iye ‘sanaope mfumu ayi, pakuti anapitiliza kupilila moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.’—Ŵelengani Aheberi 11:27,-28.
3. Kodi tikambilana mafunso ati okhudza cikhulupililo ca Mose coona “Wosaonekayo”?
3 Kodi cikhulupililo canu ndi colimba cakuti cimakucititsani ngati kuti ‘mukuona Mulungu’? (Mat. 5:8) Kuti tikhale ndi maso a kuuzimu amene angatithandize kuona “Wosaonekayo,” tiyeni tikambilane citsanzo ca Mose. Kodi kukhulupilila Yehova kunam’thandiza bwanji kuti asamaope anthu? Kodi Mose anaonetsa bwanji kuti anali kukhulupilila malonjezo a Mulungu? Nanga kuona “Wosaonekayo” kunam’thandiza bwanji pamene iye ndi anthu ake anali pa mavuto aakulu?
SANAOPE MFUMU
4. Malinga ndi kuona kwa munthu, kodi Mose anali munthu wotani pomuyelekezela ndi Farao?
4 Malinga ndi kuona kwa munthu, Mose sanali kanthu kwa Farao. Zinaoneka ngati kuti moyo ndi tsogolo la Mose zinali m’dzanja la Farao. Mose anafunsa Yehova kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?” (Eks. 3:11) Zaka 40 zimenezi zisanacitike, Mose anali atathaŵa kucoka ku Iguputo ndipo anakhala umoyo wothaŵathaŵa. Mwina anaganiza kuti, ‘Kodi ndi kwanzelu kuti ndipitenso ku Iguputo ndi kukakwiitsanso mfumu?’
5, 6. N’ciani cinathandiza Mose kuopa Yehova osati Farao?
5 Mose asanapite ku Iguputo, Mulungu anam’phunzitsa mfundo yofunika kwambili. Pambuyo pake, Mose analemba mfundoyi m’buku la Yobu kuti: “Kuopa Yehova ndiko nzelu.” (Yobu 28:28) Kuti Yehova athandize Mose kukhala ndi mantha ndi kucita zinthu mwanzelu, anamuonetsa kusiyana kumene kulipo pakati pa anthu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Mulungu anam’funsa kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?”—Eks. 4:11.
6 Kodi zimenezi zinam’phunzitsa ciani Mose? Mose sanafunikile kuopa cifukwa anatumidwa ndi Yehova. Ndipo Mulungu anali kudzam’thandiza kuti apeleke uthenga wake kwa Farao. Ndiponso, Farao sanali kanthu pomuyelekezela ndi Yehova. Ndipo iyi sinali nthawi yoyamba kuti moyo wa atumiki a Mulungu ukhale pa ngozi mu Iguputo. Mwina Mose anakumbukila mmene Yehova anatetezela Abulahamu, Yosefe ndi iye mwini pamene anali pansi pa ulamulilo wa mafumu ena aciiguputo. (Gen. 12:17-19; 41:14, 39-41; Eks. 1:22–2:10) Cifukwa cokhulupilila Yehova, “Wosaonekayo,” Mose molimba mtima anapita kwa Farao kukamuuza mau onse amene Yehova ananena.
7. Kukhulupilila Yehova kunathandiza bwanji mlongo wina?
7 Kukhulupilila Yehova kunathandizanso mlongo wochedwa Ella kupewa msampha woopa anthu. Mu 1949, Ella anamangidwa ndi apolisi a KGB ku Estonia. Anamuvula zovala pamaso pa apolisi acinyamata. Iye anati: “Ndinacita manyazi kwambili, koma nditapemphela kwa Yehova, ndinakhala ndi mtendele wa mumtima.” Ndiyeno, Ella anaikidwa m’ndende yokhalamo yekha kwa masiku atatu. Iye ananena kuti: “Apolisi mofuula anati: ‘Tidzatsimikiza kuti palibe adzakumbukanso dzina la Yehova mu Estonia! Upita ku ndende yozunzilako anthu, ndipo ena onse apita ku Siberia. Monyoza anati, ‘Yehova wako ali kuti?’” Kodi Ella anafunikila kuopa anthu kapena kukhulupilila Yehova? Atamufunsa ngati adzapitiliza kulalikila, iye molimba mtima anauza omunyozawo kuti: “Ndaiganizila kwambili nkhani imeneyi. Ndingakonde kukhala m’ndende ndi kukhalabe paubwenzi wolimba ndi Mulungu m’malo mwakuti ndimasulidwe ndi kukhala paudani ndi Mulungu.” Yehova anali munthu weniweni kwa Ella monga mmene apolisiwo analili. Iye anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu.
8, 9. (a) N’ciani cingatithandize kusaopa anthu? (b) Kodi tiyenela kukumbukila ndani ngati pali zinthu zimene zingaticititse kuopa anthu?
8 Kukhulupilila Yehova kudzakuthandizani kuthetsa mantha. Akuluakulu a boma akayesa kukuletsani kulambila Mulungu, zingaoneke ngati kuti moyo ndi tsogolo lanu zili m’dzanja mwao. Mwina mungaganize kuti ndi bwino kungosiya kutumikila Yehova kuti musakwiitse olamulila. Koma musaiŵale kuti: Kukhulupilila Mulungu ndiye kungakuthandizeni kusaopa anthu. (Ŵelengani Miyambo 29:25.) Yehova akutifunsa kuti: ‘Kodi n’cifukwa ciani iwe ukuopa munthu woti adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu wobiliŵila?’—Yes. 51:12, 13.
9 Muzikumbukila Atate wanu wamphamvuyonse. Iye amaona anthu amene amacitilidwa mopanda cilungamo. Ndipo amawacitila cifundo ndi kuwathandiza. (Eks. 3:7-10) Ngakhale pamene muyenela kuteteza cikhulupililo canu pamaso pa akuluakulu a boma, “musade nkhawa za mmene mukalankhulile kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule.” (Mat. 10:18-20) Olamulila aumunthu ndi akuluakulu a boma sali kanthu powayelekezela ndi Yehova. Tikalimbitsa cikhulupililo cathu tsopano, tidzaona Yehova kukhala Munthu weniweni amene ndi wofunitsitsa kutithandiza.
ANAKHULUPILILA MALONJEZO A MULUNGU
10. (a) Kodi Yehova anapeleka malangizo otani kwa Aisiraeli m’mwezi wa Nisani mu 1513 B.C.E.? (b) N’cifukwa ciani Mose anamvela malangizo a Mulungu?
10 M’mwezi wa Nisani m’caka ca 1513 B.C.E., Yehova anatuma Mose ndi Aroni kukapeleka malangizo awa kwa Aisiraeli: Sankhani nkhosa yaimuna kapena mbuzi yopanda cilema, muiphe ndi kuwaza magazi ake pamakomo a nyumba zanu. (Eks. 12:3-7) Kodi Mose anacita ciani? Patapita zaka zambili, mtumwi Paulo analemba izi ponena za iye: “Mwa cikhulupililo, iye anacita pasika ndiponso anawaza magazi pamafelemu a pakhomo, kuti woonongayo asakhudze ana ao oyamba kubadwa.” (Aheb. 11:28) Mose anadziŵa kuti Yehova ndi wokhulupilika, ndipo anakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzapha ana aamuna oyamba kubadwa aciiguputo.
11. N’cifukwa ciani Mose anapeleka malangizo kwa Aisiraeli?
11 Mose anali kuwakonda Aisiraeli. Ngakhale kuti ana ake aamuna anali otetezeka ndipo anali kutali ku Midiyani, iye anapeleka malangizo ku mabanja aciisiraeli amene ana ao aamuna anali pa ngozi. (Eks. 18:1-6) Kuti awateteze kwa “woonongayo,” mwamsanga Mose “anaitana akulu onse a Isiraeli ndi kuwauza kuti: . . . ‘Muiphele nsembe ya pasika.’”—Eks. 12:21.a
12. Ndi uthenga wofunika uti umene Yehova watituma kukalengeza?
12 Anthu a Yehova akuthandizidwa ndi angelo kulengeza uthenga wofunika wakuti: “Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemelelo, cifukwa ola lakuti apeleke ciweluzo lafika. Cotelo lambilani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:7) Ino ndiyo nthawi yolengeza uthenga umenewo. Tifunika kucenjeza anansi athu kuti atuluke m’Babulo Wamkulu kotelo kuti ‘asalandileko ina ya milili yake.’ (Chiv. 18:4) A “nkhosa zina” akuthandiza Akristu odzozedwa kupempha anthu otalikilana ndi Mulungu kuti ‘agwilizanenso’ ndi iye.—Yoh. 10:16; 2 Akor. 5:20.
13. N’ciani cidzatithandiza kukhala wofunitsitsa kulalikila uthenga wabwino?
13 Ndife otsimikiza kuti “nthawi ya ciweluzo” yafika. Ndiponso, ndife otsimikiza mtima kugwila nchito yolalikila mwamsanga monga mmene Yehova akufunila. Mtumwi Yohane anaona masomphenya a “angelo anai ataimilila m’makona anai a dziko lapansi. Iwo anali atagwila mwamphamvu mphepo zinai za dziko lapansi.” (Chiv. 7:1) Ndi maso a cikhulupililo, kodi mumaona angelo amenewo kuti atsala pang’ono kusiya kugwila mphepo zoononga za cisautso cacikulu padziko lapansi? Pitilizani kukhulupilila malonjezo a Yehova. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kukhala wofunitsitsa kulalikila uthenga wabwino.
14. N’ciani cimatisonkhezela ‘kucenjeza anthu oipa kuti asiye njila zao zoipa’?
14 Akristu oona ali kale paubwenzi ndi Yehova ndipo ali ndi ciyembekezo ca moyo wosatha. Koma timadziŵa kuti ndi udindo wathu ‘kulankhula ndi anthu oipa ndi kuwacenjeza kuti asiye njila zao zoipa ndi colinga cakuti akhalebe ndi moyo.’ (Ŵelengani Ezekieli 3:17-19.) Koma sitimalalikila cabe kuti tipewe mlandu wa magazi. Timalalikila cifukwa cokonda Yehova ndi anansi athu. M’fanizo lake la Msamariya, Yesu anatithandiza kudziŵa tanthauzo la kuonetsa cikondi ndi cifundo. Mwina tingadzifunse kuti, “Kodi ndili ngati Msamariya kapena ndili ngati wansembe ndi Mlevi? Kodi ndimafunitsitsa kulalikila ena kapena sindimalalikila pa zifukwa zosamveka? (Luka 10:25-37) Kukhulupilila malonjezo a Mulungu ndi kukonda anansi athu, kudzatithandiza kutengamo mbali mokwanila m’nchito yolalikila madzi asanafike m’khosi.
“ANAOLOKA NYANJA YOFIILA”
15. N’cifukwa ciani Aisiraeli anaona kuti analibe kothaŵila?
15 Cikhulupililo ca Mose mwa “Wosaonekayo,” cinam’thandiza pamene Aisiraeli anali pa mavuto aakulu atacoka mu Iguputo. Baibulo limati: “Ana a Isiraeli anakweza maso ao ndipo anaona Aiguputo akuwathamangila. Pamenepo ana a Isiraeli anacita mantha kwambili ndipo anayamba kufuulila Yehova.” (Eks. 14:10-12) Kodi zimenezi zinayenela kukhala zodabwitsa kwa Aisiraeli? Iyai. Yehova anali atakambilatu kuti: “Ndidzalola Farao kuumitsa mtima wake, ndipo adzawathamangila. Ndidzapezelapo ulemelelo mwa kugonjetsa Farao ndi magulu ake onse ankhondo, ndipo Aiguputo adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.” (Eks. 14:4) Ngakhale ndi conco, Aisiraeli analibe cikhulupililo. Iwo anali kuona cabe Nyanja Yofiila kutsogolo kwao, magaleta ankhondo a Farao amene anali kuwalondola mofulumila m’mbuyo mwao ndi mtsogoleli wao wacikulile wa zaka 80. Iwo anaona kuti analibe kothaŵila.
16. Kodi cikhulupililo cinalimbikitsa bwanji Mose pa Nyanja Yofiila?
16 Komabe, Mose sanacite mantha. N’cifukwa ciani sanatelo? Cifukwa cakuti mwa cikhulupililo anaona cina cake ca mphamvu kwambili kuposa nyanja kapena gulu la asilikali. Iye ‘anaona cipulumutso ca Yehova,’ ndipo anadziŵa kuti Yehova adzamenyela nkhondo Aisiraeli. (Ŵelengani Ekisodo 14:13, 14.) Cikhulupililo ca Mose cinalimbikitsa anthu a Mulungu. Baibulo limati: “Mwa cikhulupililo, anthu a Mulunguwo anaoloka Nyanja Yofiila ngati kuti akudutsa pamtunda pouma, koma Aiguputo atalimba mtima ndi kulowa panyanjapo, nyanjayo inawamiza.” (Aheb. 11:29) Pambuyo pake, “Aisiraeli anayamba kuopa Yehova ndi kukhulupilila Yehova ndi mtumiki wake Mose.”—Eks. 14:31.
17. Ndi cocitika citi ca mtsogolo cimene cidzayesa cikhulupililo cathu?
17 Posacedwapa, tidzaoneka ngati kuti tilibe citetezo. Cisautso cacikulu cikadzafika pacimake, maulamulilo a dzikoli adzaonongelatu mabungwe acipembedzo amene ndi aakulu kwambili kuposa ifeyo. (Chiv. 17:16) Yehova analosela kuti tidzakhala ngati anthu opanda citetezo, monga ‘midzi yopanda mipanda . . . ilibe zotsekela ndiponso zitseko.’ (Ezek. 38:10-12, 14-16) Mwa kuona kwa munthu, tidzaoneka ngati anthu opanda citetezo. Kodi inuyo mudzacita ciani?
18. Fotokozani cifukwa cake sitidzafunikila kucita mantha pa cisautso cacikulu.
18 Sitidzafunikila kucita mantha. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Yehova analosela za kuukilidwa kwa anthu ake. Iye analoselanso zimene zidzatsatilapo pamene anati: “‘Pa tsiku limenelo, tsiku limene Gogi adzabwele m’dziko la Isiraeli, mkwiyo wanga udzatulukila m’mphuno mwanga,’ watelo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Ine ndidzalankhula mwaukali wanga woyaka moto komanso nditakwiya kwambili.’” (Ezek. 38:18-23) Ndiyeno Mulungu adzaononga anthu onse amene adzafuna kuononga anthu a Yehova. Ngati mumakhulupilila kuti Yehova adzakutetezani pa ‘tsiku lake lalikulu ndi locititsa mantha,’ mudzatha “kuona cipulumutso ca Yehova,” ndipo mudzakhala olimba.—Yow. 2:31, 32.
19. (a) Kodi ubwenzi wa Mose ndi Yehova unali wolimba motani? (b) Ndi madalitso ati amene tidzapeza ngati tikumbukila Yehova m’njila zathu zonse?
19 Muyenela kukonzekela tsopano zinthu zocititsa cidwi zimenezi mwa ‘kupitiliza kupilila moleza mtima ngati kuti mukuona Wosaonekayo.’ Limbitsani ubwenzi wanu ndi Yehova Mulungu mwa kuphunzila Baibulo ndi kupemphela nthawi zonse. Mose anali paubwenzi wathithithi ndi Yehova. Yehova anam’gwilitsila nchito cakuti Baibulo limanena kuti Mulungu anali kum’dziŵa “pamasom’pamaso.” (Deut. 34:10) Mose anali mneneli wapadela kwambili. Ngati muli ndi cikhulupililo, inunso mudzam’dziŵa bwino Yehova monga kuti mukumuona. Mau a Mulungu amatitsimikizila kuti ngati timam’kumbukila ‘m’njila zathu zonse, iye adzaongola njila zathu.’—Miy. 3:5-7.
a Yehova anatumiza angelo kukapha ana aamuna oyamba kubadwa aciiguputo.—Sal. 78:49-51.