Palibe Munthu Angatumikile Ambuye Aŵili
“Kapolo sangatumikile ambuye aŵili. . . . Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.”—MAT. 6:24.
1-3. (a) Ndi mavuto ati a zacuma amene ena amakhala nao? Nanga amacita ciani pofuna kuwathetsa? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Kodi amakhala ndi nkhawa yotani pankhani yolela ana?
MLONGO wina wochedwa Marilyn anati: “Tsiku lililonse, mwamuna wanga James anali kukhala wotopa akaweluka kunchito. Koma ndalama zimene anali kulandila sizinali zokwanila kugulila zofunikila za tsiku ndi tsiku. Ndinali kufuna kupeputsila mwamuna wanga mtola ndi kugulila mwana wathu Jimmy zinthu zimene anzake ku sukulu anali nazo.”a Marilyn anali kufunanso kuthandiza acibale ake ndi kusunga ndalama zodzagwilitsila nchito mtsogolo. Anzake ambili anali atapita ku maiko ena kukafunafuna ndalama zambili. Koma ataganiza zakuti nayenso apite, anavutika kupanga cosankha cakuti apite kapena ai. N’cifukwa ciani?
2 Marilyn sanafune kusiya banja lake la mtengo wapatali ndi kusiya kucita zinthu za kuuzimu pamodzi ndi banja lake. Ngakhale n’conco, anaganizila anzake amene anapita ku maiko ena, koma mabanja ao anali kucitabe bwino kuuzimu. Panthawi imodzimodzi anaganizilanso za mmene akanalelela mwana wake Jimmy. Kodi akanalela mwana wake ‘m’malangizo a Yehova ndi kum’phunzitsa kaganizidwe kake’ pa Intaneti?—Aef. 6:4.
3 Marilyn anapempha ena kuti amuuzeko zocita pankhaniyi. Mwamuna wake sanafune kuti Marilyn apite. Koma anakamba kuti ngati Marilyn afuna kupita sadzamuletsa. Akulu ndi ofalitsa ena mumpingo anauza Marilyn kuti asapite, koma alongo ena anam’limbikitsa kuti apite. Iwo anamuuza kuti: “Ngati umakonda banja lako udzapita, ngakhale kumeneko ungatumikilebe Yehova.” Ngakhale kuti Marilyn anakaikila zakuti apite kapena ai, iye anatsanzika mwamuna wake James ndi mwana wake Jimmy ndi kupita kukagwila nchito ku dziko lina. Analonjeza banja lake kuti: “Sindidzakhalitsa kumene ndipita.”b
KUSAMALILA BANJA NDI KUTSATILA MFUNDO ZA M’BAIBULO
4. N’cifukwa ciani anthu ambili amapita ku maiko ena? Ndipo nthawi zambili amasiila ndani udindo wosamalila ana?
4 Yehova safuna kuti atumiki ake azisoŵa cakudya. (Sal. 37:25; Miy. 30:8) Kuyambila m’nthawi zakale, atumiki a Yehova anali kupita ku madela ena kukafunafuna cakudya. Yakobo anatuma ana ake kukagula cakudya ku Iguputo.c (Gen. 42:1, 2) Masiku ano, anthu ambili amapita ku maiko ena osati cifukwa cakuti mabanja ao akusoŵa cakudya, koma kukafunafuna ndalama kuti abwezele nkhongole zazikulu, ndipo ena amangofuna kulemela. Kuti acite zimenezi, ambili amasiya mabanja ao ndi kupita ku dela lina la m’dziko lao kapena kupita ku dziko lina. Nthawi zambili, io amasiya ana ao aang’ono kuti azileledwa ndi mnzao wa m’cikwati, mwana wao wamkulu, ambuye ao, acibale kapena anzao. Ngakhale kuti anthu opita ku maiko ena zimawapweteka mtima kusiya mnzao wa m’cikwati kapena ana, io amaona kuti amafunikabe kupita.
5, 6. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa kuti n’ciani cingatithandize kukhala acimwemwe ndi otetezeka? (b) Nanga Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupempha zinthu ziti? (c) Kodi Yehova amatidalitsa motani?
5 M’nthawi za Yesu, anthu ambili anali osauka. Mwina io anaganiza kuti kukhala ndi ndalama kukanacititsa kuti akhale ndi umoyo wabwino ndi wotetezeka. (Maliko 14:7) Koma Yesu sanafune kuti anthuwo aike ciyembekezo cao pa zinthu zosakhalitsa. Iye anafuna kuti io azidalila Yehova amene amapeleka madalitso osatha. Pa ulaliki wake wa paphili, Yesu anafotokoza kuti cimwemwe ceniceni ndi citetezo sizimabwela cifukwa ca zinthu zakuthupi kapena mphamvu zathu. Iye anafotokoza kuti kukhala paubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba ndi kumene kumabweletsa cimwemwe.
6 Yesu m’pemphelo lake lacitsanzo anatiphunzitsa kuti tizipempha zofunika za tsiku ndi tsiku, “cakudya cathu calelo” osati cuma. Mosapita m’mbali anauza omvetsela ake kuti: “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi. . . . Koma unjikani cuma canu kumwamba.” (Mat. 6:9, 11, 19, 20) Tili ndi cidalilo cakuti Yehova adzatidalitsa monga mmene akutilonjezela. Madalitso a Mulungu amaphatikizapo zambili osati cabe kukhala naye paubwenzi. Iye amatitsimikizila kuti adzatipatsa zonse zimene timafunikiladi. Kunena zoona, kudalila Atate wathu osati cuma ndiye njila yokha yopezela cimwemwe ceniceni ndi kukhala otetezeka.—Ŵelengani Mateyu 6:24, 25, 31-34.
7. (a) Ndani amene Yehova wapatsa udindo wolela ana? (b) N’cifukwa ciani makolo onse aŵili amafunika kulelela ana ao pamodzi?
7 ‘Kufunafuna coyamba cilungamo ca Mulungu’ kumaphatikizapo kuona udindo wosamalila banja mmene Yehova amauonela. Cilamulo ca Mose cinali ndi mfundo zimene zimakhudzanso Akristu masiku ano. (Ŵelengani Deuteronomo 6:6, 7.) Mulungu anapatsa makolo udindo wosamalila ana, osati ambuye ao kapena anthu ena. Mfumu Solomo anati: “Mwana wanga, tamvela malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako,” (Miy. 1:8) Yehova anatanthauza kuti makolo onse aŵili afunika kukhala pamodzi kuti azilangiza ndi kuphunzitsa ana ao. (Miy. 31:10, 27, 28) Ngati ana amamvela makolo ao akulankhula za Yehova ndi kuŵaona akum’tumikila tsiku lililonse, naonso angayambe kucita zimenezo.
ZOTSATILAPO ZOSAYEMBEKEZELEKA
8, 9. (a) Kodi pamakhala kusintha kotani ngati kholo likhala kutali ndi banja lake? (b) Kodi kusakhala pamodzi monga banja kungakhudze bwanji cikondi ndi khalidwe la banja?
8 Anthu ambili amene amaganiza zopita ku maiko ena amadziŵa kuti cosankha cao cingabweletse mavuto. Koma n’zosatheka kudziŵa mmene cosankha cimeneci cingakhudzile banja lanu. (Miy. 22:3)d Marilyn atangopita anayamba kusoŵa banja lake, ndipo nayenso mwamuna ndi mwana wake anayamba kumusoŵa. Jimmy anali kufunsa amai ake kuti, “Munandisiila ciani?” Colinga ca Marilyn cinali kukakhala miyezi yocepa cabe, koma atakhala zaka, iye anayamba kuona kuti zinthu zayamba kusintha m’banja lake. Jimmy analeka kuwasoŵa amai ake. Modandaula, amai ake anati, “Mwana wanga anasiya kundikonda.”
9 Ngati makolo ndi ana sakhala pamodzi monga banja, cikondi cao cingacepe ndipo khalidwe lao lingaonongeke.e Zimakhala zopweteka mtima kwambili kwa ana ang’onoang’ono akasiidwa kwa nthawi yaitali. Marilyn anauza Jimmy kuti anapita kukagwila nchito pofuna kupezela iye zinthu zofunika. Koma Jimmy anaona monga kuti amai ake analeka kum’konda. Poyamba iye sanakondwele kuti amai ake anapita, koma pamene amai ake anabwela kukaceza sanali wosangalala kuwaona. Mofanana ndi mmene ana ambili amamvelela akakhala kutali ndi makolo ao, Jimmy anaona kuti sanafunikilenso kukonda ndi kumvela amai ake.—Ŵelengani Miyambo 29:15.
10. (a) N’ciani cingacitike ngati makolo atumizila cabe ana mphatso m’malo mokhala nao? (b) Kodi kholo silingathe kucita ciani kwa ana ake ngati limakhala kutali?
10 Cifukwa cokhala kutali ndi Jimmy, Marilyn anayesa kulimbitsa cikondi cao mwa kum’tumizila ndalama ndi mphatso. Iye anazindikila kuti zimenezi sizinacititse mwana wake kuyamba kum’konda. Anazindikilanso kuti mwanayo anayamba kukonda kwambili zinthu zakuthupi osati za kuuzimu ndi banja lake. (Miy. 22:6) Jimmy anauza amai ake kuti: “Musakabwele, muzingonditumizila mphatso.” Marilyn anazindikila kuti sangalele mwana wake mwa kugwilitsila nchito foni, makalata, kapena mwa kukamba naye pa intaneti mwa kugwilitsila nchito kompyuta ya kamela. Marilyn anafotokoza kuti: “N’zosatheka kukumbatila mwana wako pa intaneti kapena kupita kukamugoneka.”
11. (a) Kodi cikwati cimakhudzidwa bwanji ngati okwatilana akhala motalikilana? (b) N’ciani cinathandiza mlongo wina kuzindikila kuti anafunika kukakhalanso ndi banja lake?
11 Ubwenzi wa Marilyn ndi Yehova ndiponso ndi mwamuna wake unasokonezeka. Iye analibe nthawi yokwanila yosonkhana ndi yolalikila. Ndipo anafunika kugonjetsa ciyeso cocokela kwa abwana ake cakuti agone naye. Popeza kuti Marilyn ndi James sanali kukambitsilana za mavuto ao, io anali kuuza anthu ena mmene anali kumvelela. Ndipo zimenezi zinacititsa kuti atsale pang’ono kucita cigololo. Marilyn anaona kuti ngakhale kuti iye ndi mwamuna wake sanacite cigololo, io analephela kutsatila malangizo a m’Baibulo okhudza cikondi ndi kupatsana mangawa a m’cikwati cifukwa cosakhala pamodzi. Iwo analibe nthawi yoceza ndi kusonyezana cikondi monga mwamuna ndi mkazi. (Nyimbo 1:2; 1 Akor. 7:3, 5) Iwo analibenso nthawi yolambila Yehova pamodzi ndi mwana wao. Marilyn anati: “Pamene ndinamva mfundo yakuti kulambila kwa pabanja kokhazikika n’kofunika kuti tikapulumuke tsiku lalikulu la Yehova, ndinaona kuti ndinafunikila kubwelela kunyumba. Ndinafunika kuyambanso kucita bwino kuuzimu ndi kukhalanso ndi banja langa.”
MALANGIZO ABWINO NDI MALANGIZO OIPA
12. Ndi malangizo ati a m’Baibulo amene angathandize Akristu amene akhala kutali ndi mabanja ao?
12 Pamene Marilyn anaganiza zobwelela kunyumba, anthu ena anam’limbikitsa kubwelela koma ena sanatelo. Akulu a mumpingo umene anali kugwilizana nao anamuyamikila kaamba ka cikhulupililo cake ndi kulimba mtima kwake. Komabe, ena amene anali kutali ndi mabanja ao sanafune kubwelela. M’malo motsanzila citsanzo cake cabwino io anamuuza mau ofooketsa kuti: “Udzabwelanso kuno posacedwa. Kodi udzakwanitsa bwanji kupeza zofunikila ukabwelela kunyumba?” M’malo molankhula mau ofooketsa ngati awa, Akristu ayenela ‘kukumbutsa akazi acitsikana kukonda amuna ao, kukonda ana ao . . . kugwila nchito pamakomo ao,’ “kuti mau a Mulungu asanyozedwe.”—Ŵelengani Tito 2:3-5.
13, 14. N’cifukwa ciani cikhulupililo colimba n’cofunika kuti Mkristu asacite zimene acibale akufuna? Pelekani citsanzo.
13 Anthu ambili amene amapita ku maiko ena anakulila m’mabanja mmene amalemekeza kwambili miyambo ndi makolo. Conco, Mkristu ayenela kukhala ndi cikhulupililo colimba kuti akane kucita zinthu zimene acibale ake afuna koma zimene sizisangalatsa Yehova.
14 Taganizilani citsanzo ca Carin. Iye anati: “Mwana wathu Don atabadwa, ine ndi mwamuna wanga tinali kuseŵenza kudziko lina, ndipo ndinali nditayamba kuphunzila Baibulo. Aliyense m’banja anayembekezela kuti ndidzatumiza mwana wanga kunyumba kuti makolo anga akamulele mpaka titapeza ndalama zambili.” Pamene Carin analimbikila kuti adzalela yekha mwana wake, acibale ndi mwamuna wake anamuseka ndi kumunena kuti wafuntha. Carin anakambanso kuti: “Kunena zoona, paciyambi ndinaona kuti panalibe vuto ndi kutumiza mwana wanga kwa makolo anga kuti akakhale naye zaka zocepa. Koma ndinadziŵa kuti Yehova anapatsa ine ndi mwamuna wanga udindo wolela mwana.” Carin atakhalanso ndi mimba, mwamuna wake wosakhulupilila anam’limbikitsa kuti aicotse. Cosankha cabwino cimene Carin anapanga poyamba cinam’thandiza kupanganso cosankha cimene cinasangalatsa Yehova. Carin, mwamuna wake ndi ana ao ndi osangalala kwambili kuti anasankha kuti azikhala pamodzi. Ngati Carin akanatumiza ana ake kwa makolo ake kuti aŵalele, pakanakhala zotsatilapo zoipa.
15, 16. (a) Fotokozani mmene mlongo wina analeledwela. (b) Nanga n’cifukwa ciani iye sanafune kupatsa amai ake udindo wolela mwana wake?
15 Mlongo wina wochedwa Vicky anati: “Kwa zaka zingapo ndinasungidwa ndi ambuye, koma mng’ono wanga anali kukhala ndi makolo anga. Nditabwelela kwa makolo anga ndinali kuwaona mosiyana ndi mmene ndinali kuwaonela kale. Mng’ono wanga anali ndi ufulu wolankhula nao, kuwakumbatila ndipo anali kuwakonda kwambili, koma ine ndinali wotalikilana nao. Ngakhale nditakula, zinali kundivuta kuwasonyeza mmene ndinali kumvelela. Ine ndi mng’ono wanga tinatsimikizila makolo athu kuti tidzaŵasamalila akadzakalamba. Komabe mosiyana ndi mng’ono wanga amene anali kudzawasamalila cifukwa cowakonda, ine ndinali kudzawasamalila cifukwa ca udindo.
16 “Tsopano amai anga afuna kuti ndiwatumizile mwana wanga kuti akamulele monga mmene io ananditumizila kwa ambuye, koma ndinakana m’njila yakuti asakhumudwe. Ine ndi mwamuna wanga tifuna kuti tilele mwana wathu m’malangizo a Yehova. Ndipo sindifuna kuti ndidzaononge ubwenzi wanga ndi mwana wanga.” Vicky anaona kuti cinthu cofunika kwambili ndi kuika Yehova ndi mfundo zake patsogolo osati zinthu zakuthupi. Yesu anati: “Kapolo sangatumikile ambuye aŵili,” Mulungu ndi Cuma.—Mat. 6:24; Eks. 23:2.
YEHOVA AMADALITSA KHAMA LATHU
17, 18. (a) N’ciani cimene Akristu amasankha kucita nthawi zonse? (b) Ndi mafunso ati amene tidzakambitsilana m’nkhani yotsatila?
17 Atate wathu, Yehova, watilonjeza kuti adzatipatsa zinthu zimene tifunikiladi ngati tiika Ufumu ndi cilungamo cake patsogolo. (Mat. 6:33) Conco, nthawi zonse Akristu oona amasankha kucita cifunilo cake. Yehova amatilonjeza kuti adzapeleka “njila yopulumukila” ngati sitinyalanyaza mfundo za m’Baibulo ngakhale pamene tili pa mavuto. (Ŵelengani 1 Akorinto 10:13.) Ngati ‘tiyembekezela’ Yehova ndi ‘kum’dalila’ mwa kum’pempha nzelu ndi citsogozo, ndiponso ngati titsatila malamulo ake ndi mfundo zake, “iye adzacitapo kanthu.” (Sal. 37:5, 7) Adzadalitsa khama lathu lofuna kulambila iye yekha monga Mbuye woona. Ngati tiika Mulungu patsogolo, iye ‘adzatidalitsa.’—Yelekezelani ndi Genesis 39:3.
18 Kodi tingacite ciani kuti tithetse mavuto obwela cifukwa cokhala kutali ndi banja lathu? Tingapezele bwanji banja lathu zinthu zofunika popanda kupita ku dela lina? Nanga mwacikondi tingalimbikitse bwanji ena kupanga zosankha zoyenela pankhaniyi? M’nkhani yotsatila tidzakambitsilana mafunso amenewa.
a Maina asinthidwa.
b Ngakhale kuti nkhaniyi ifotokoza za mkazi amene anasiya banja lake ndi kupita ku dziko lina kukagwila nchito, malangizo ake akhudzanso amuna.
c Nthawi zonse ana a Yakobo akasiya mabanja ao ndi kupita ku Iguputo ayenela kuti anali kukhala kumeneko milungu yosaposa itatu. Koma pamene Yakobo ndi ana ake aamuna anasamukila ku Iguputo, io anatenga akazi ndi ana ao.—Gen. 46:6, 7.
d Onani nkhani yakuti, “Kodi Osamukila kudziko lina Amakapezadi Zimene Akufuna?” mu Galamukani! ya February 2013.
e Malipoti a m’maiko ambili aonetsa kuti kusakhala pamodzi monga banja kwabweletsa mavuto aakulu. Ena mwa mavutowa ndi kucita cigololo, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, kapena kugonana ndi wacibale. Ndipo ana sangazicita bwino ku sukulu, angakhale aukali, ankhawa, ovutika maganizo kapena angakhale ndi maganizo ofuna kudzipha.