LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 4/1 masa. 22-26
  • Limbani Mtima—Yehova ndi Mthandizi Wanu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Limbani Mtima—Yehova ndi Mthandizi Wanu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KULIMBITSANSO BANJA NDI UMOYO WA KUUZIMU
  • SAMALILANI UDINDO WANU
  • MUZISAMALILA BANJA LANU
  • ZIMENE MUNGACITE NGATI ACIBALE AKUKAKAMIZANI
  • MUZIDALILA MULUNGU
  • MUZIKUMBUKILA KUTI YEHOVA NDI MTHANDIZI WANU
  • Yehova Amatitonthoza m’Masautso Athu Onse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Palibe Munthu Angatumikile Ambuye Aŵili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • “Mutu wa Mwamuna Aliyense Ndi Khristu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 4/1 masa. 22-26

Limbani Mtima Yehova ndi Mthandizi Wanu

“Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga.’”—AHEB. 13:6.

KODI MUGANIZA BWANJI?

  • Kodi makolo angathandize bwanji mabanja ao kukhalabe olimba kuuzimu?

  • Kodi mitu ya mabanja ingasamalile bwanji mabanja ao mwakuthupi popanda kupita ku dziko lina?

  • Kodi Akristu angagonjetse bwanji ciyeso cakuti apite ku dziko lina kukafunafuna ndalama zambili?

1, 2. Kodi anthu ambili opita kukagwila nchito ku maiko ena amakumana ndi mavuto ati akabwelako? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)

MWAMUNA wina wochedwa Eduardoa anati: “Nditapita kudziko lina ndinapeza nchito yabwino ndipo ndinali kulandila ndalama zambili. Koma pamene ndinayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinazindikila kuti ndili ndi udindo wofunika kwambili wosamalila banja langa mwakuthupi ndi kuuzimu. Conco, ndinabwelela kunyumba.”—Aef. 6:4.

2 Eduardo anadziŵa kuti ngati wapita kukakhalanso ndi banja lake adzasangalatsa Yehova. Koma kucita zimenezi kunali kovuta. Iye anafunika kulimbitsanso cikondi m’banja lake. Anafunikanso kupeza ndalama zokwanila kuti asamalile banja lake. Kodi akanapeza bwanji ndalama? Kodi mpingo ukanam’thandiza bwanji?

KULIMBITSANSO BANJA NDI UMOYO WA KUUZIMU

3. Kodi ana amakhudzidwa bwanji ngati kholo likhala kutali?

3 Eduardo anafotokoza kuti: “Ndinadziŵa kuti ndinanyalanyaza ana anga makamaka panthawi imene ndinafunikila kuwasonyeza cikondi ndi kuwalangiza. Sindikanatha kuwaŵelengela nkhani za m’Baibulo, kupemphela nao, kuwakumbatila ndi kuseŵela nao.” (Deut. 6:7) Anna, mwana wamkulu wa Eduardo anati: “Pamene atate anali kukhala kutali ndi ife ndinaona kuti sanali kundikonda. Ngakhale kuti ndinawazindikila atabwelako, sindinamasuke nao.”

4. N’cifukwa ciani zimakhala zovuta kuti tate asamalile banja lake ngati akhala kutali?

4 Ngati tate akhala kutali ndi banja lake, amalephela kusamalila udindo wake monga mutu wabanja. Ruby, mkazi wa Eduardo anati: “Ndinafunikila kusenza udindo wa mai ndi tate ndipo ndinazoloŵela kupanga zosankha m’banja. Mwamuna wanga atabwelako, ndinafunika kukhala wogonjela. Ngakhale kuti tsopano ndikhala ndi mwamuna wanga, nthawi zina ndimafunikila kudziletsa kuti ndisacite zinthu zina.” (Aef. 5:22, 23) Eduardo anati: “Ana athu anazoloŵela kupempha cilolezo kwa mkazi wanga akafuna kucita zinthu zina. Pokhala makolo, tinazindikila kuti tinafunika kucita zinthu m’njila yakuti ana athu aziona kuti ndife ogwilizana. Ndipo ndinafunika kutsogolela banja langa m’njila yacikristu.”

5. Kodi tate wina amene anali atapita kukagwila nchito kwina anacitanji kuti athetse vuto m’banja lake? Nanga panakhala zotsatilapo zotani?

5 Eduardo anayesetsa kucita zonse zimene akanatha kuti ayambenso kugwilizana ndi banja lake ndi kulithandiza kuuzimu. Iye anati: “Colinga canga cinali kufuna kukhomeleza coonadi m’mitima mwa ana anga mwa mau ndi zocita, osati cabe kunena kuti ndimakonda Yehova.” (1 Yoh. 3:18) Kodi Yehova anadalitsa khama la Eduardo? Anna anati: “Titaona khama la atate lofuna kukhala kholo labwino ndi kulimbitsa cikondi m’banja, tinayamba kuŵaona moyenela. Tinasangalala titaona kuti akukalamila maudindo mumpingo. Dziko linafuna kuticotsa kwa Yehova, koma titaona kuti makolo athu akuika patsogolo zinthu za kuuzimu, nafenso tinayesa kucita cimodzimodzi. Atate anatilonjeza kuti sadzatisiyanso, ndipo sanatisiyedi. Iwo akanatisiyanso, mwina sindikanakhalabe m’gulu la Yehova.”

SAMALILANI UDINDO WANU

6. Kodi makolo ena anaphunzila ciani panthawi ya nkhondo ku Balkans?

6 Ana amafuna kuti makolo ao azikhala nao. Mwacitsanzo, pamene kunali nkhondo ku Balkans, makolo ambili acikristu sanali kugwila nchito. Izi zinacititsa kuti makolo azikhala panyumba nthawi yaitali. Iwo anali kuseŵela, kulankhula ndi kuphunzila ndi ana ao. Ana anali osangalala kwambili kuposa mmene analili nkhondo isanayambe. Kodi tiphunzilapo ciani pa cocitikaci? Tiphunzilapo kuti ana amafuna kwambili kukhala ndi makolo ao kuposa kukhala ndi ndalama, mphatso kapena kukhala m’dela lotetezeka. Monga mmene Baibulo limanenela, ana amapindula ngati makolo amakhala nao ndi kuwaphunzitsa.—Miy. 22:6.

7, 8. (a) N’ciani cingakhumudwitse makolo pambuyo pobwelela kunyumba? (b) Kodi makolo angatani kuti ana ao ayambenso kuwakonda?

7 N’zacisoni kuti makolo ena pambuyo pobwelela kunyumba, amakhumudwa akaona kuti ana ao sawaonetsa cidwi. Iwo anganene kuti, “N’cifukwa ciani simuyamikila zonse zimene ndimakucitilani?” Koma kwenikweni ana samaonetsa cidwi kaamba kakuti kholo lao linali kwina nthawi yaitali. Kodi kholo lingathetse bwanji vutoli?

8 Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuzindikila mmene onse m’banja akumvelela. Ndipo onetsani kuti mumawakonda. Vomelezani kuti inunso munacititsa kuti pakhale vutolo, ndipo pepesani mocokela pansi pamtima. Ngati mkazi wanu ndi ana anu aona kuti mukuyesetsa kukonza zinthu, io adzazindikila kuti mumawakondadi. Ngati muleza mtima ndi kupitilizabe kukonza zinthu m’banja lanu, onse angayambenso kukukondani ndi kukulemekezani.

MUZISAMALILA BANJA LANU

9. N’cifukwa ciani tiyenela kukhutila ndi zimene tili nazo?

9 Mtumwi Paulo ananena kuti ngati Akristu acikulile sangathe kudzipezela zofunikila, ana ndi adzukulu ayenela ‘kubwezela makolo ndi agogo ao zowayenelela.’ Paulo ananenanso kuti Akristu ayenela kukhutila ndi zinthu zofunikila monga cakudya, zovala ndi pogona. Tisamagwile nchito mwakhama ndi colinga cakuti tikhale ndi umoyo wapamwamba kapena kuti tipeze ndalama zodzagwilitsila nchito mtsogolo. (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:4, 8; 6:6-10.) Mkristu sangafunikile kufunafuna cuma m’dzikoli limene lipita posacedwapa cabe kuti ‘asamalile banja lake.’ (1 Yoh. 2:15-17) Tisalole “cinyengo camphamvu ca cuma” ndi “nkhawa za m’nthawi ino” kulepheletsa banja lathu ‘kugwila mwamphamvu moyo weniweniwo’ m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.—Maliko 4:19; Luka 21:34-36; 1 Tim. 6:19.

10. N’cifukwa ciani n’kwanzelu kupewa nkhongole?

10 Yehova adziŵa kuti tifunikila ndalama. Koma mosiyana ndi nzelu yaumulungu, ndalama sizingacititse kuti tikhale otetezeka kapena okhutila. (Mlal. 7:12; Luka 12:15) Nthawi zambili, anthu amene amapita kukafunafuna ndalama ku maiko ena samazindikila kuti pali zambili zimene amafunikila kucita. Anthuwo akapita kukafunafuna ndalama sizimatanthauza kuti basi adzazipeza. Iwo amakumana ndi mavuto ambili ndipo ambili amabwelako ali ndi nkhongole zazikulu. M’malo mwakuti atumikile Mululungu mwaufulu, io amatumikila anthu amene ali nao ndi nkhongole. (Ŵelengani Miyambo 22:7.) Kupewa nkhongole nthawi zambili kumakhala kwanzelu.

11. Kodi kukonza bajeti kungathandize bwanji banja?

11 Eduardo anadziŵa kuti kuti akwanitse kusamalila banja lake pambuyo pobwelela kunyumba, anafunikila kuseŵenzetsa bwino ndalama. Iye ndi mkazi wake anali kupanga bajeti ya zinthu zofunikadi. Mosiyana ndi kale, io anali kucepetsa zinthu zogula. Onse anagwilizana ndipo sanali kuseŵenzetsa ndalama pa zinthu zosafunikila kwenikweni.b Eduardo anati: “Mwacitsanzo, ndinacotsa ana anga ku masukulu amene si a boma ndi kuwapeleka ku masukulu a boma.” Eduardo ndi banja lake anali kupemphela kuti iye apeze nchito imene siiombana ndi ndandanda yake yocita zinthu za kuuzimu. Kodi Yehova anayankha bwanji mapemphelo ao?

12, 13. Kodi tate wina anacita ciani kuti asamalile banja lake? Nanga Yehova anadalitsa bwanji cosankha cake cokhala ndi umoyo wosalila zambili?

12 Eduardo anati: “Kwa zaka ziŵili zoyamba tinalibe ndalama zokwanila. Nthawi zina ndalama zimene ndinali kupeza zinali zocepa kugulila zofunikila, ndipo ndinali kukhala wotopa. Koma ngakhale kuti zinthu zinali conco, tonse tinali kupezeka pa misonkano yonse ya mpingo ndi kupita mu utumiki mokhazikika.” Eduardo sanafune kuyamba nchito imene ikanam’cititsa kukhala kutali ndi banja lake kwa miyezi kapena zaka zambili. Iye anakamba kuti: “Ndinaphunzila nchito zosiyanasiyana kotelo kuti ngati nchito ina yasoŵa ndizitha kugwila ina.”

13 Eduardo anafunika kubweza nkhongole pang’onopang’ono, ndipo anafunikanso kupeleka ciongola dzanja pa ndalama zimene anakongola. Anaona kuti anafunikila kucita zimenezi kuti iye ndi banja lake apitilize kutumikila Yehova. Iye anati: “Tsopano ndimapeza ndalama zocepa kuyelekezela ndi zimene ndinali kupeza nditapita ku dziko lina. Ngakhale n’conco, sitisoŵa cakudya ndipo ‘dzanja la Yehova si lalifupi.’ Tinaganiza zoyamba upainiya. Titayamba upainiya, zinthu zinayamba kuyenda bwino ndipo sizinali zovuta kupeza zinthu zakuthupi.”—Yes. 59:1.

ZIMENE MUNGACITE NGATI ACIBALE AKUKAKAMIZANI

14, 15. Kodi banja lingatani ngati acibale akufuna kuti liziika patsogolo zinthu zakuthupi m’malo mwa zinthu za kuuzimu? Pangakhale zotsatilapo zotani ngati banja lionetsa citsanzo cabwino pankhaniyi?

14 M’madela ambili anthu amaona kuti ali ndi udindo wopatsa acibale ndi mabwenzi ao ndalama ndi mphatso. Eduardo anati: “Kucita zimenezi ndi mbali ya cikhalidwe cathu. Koma pali malile ocitila zimenezi. Mosamala ndimauza acibale anga kuti ndidzayesa kuwapatsa zimene afuna mmene ndingathele, malinga ngati kucita zimenezi sikungandilepheletse kusamalila banja langa mwa kuuzimu.”

15 Ena m’banja angakhumudwe ngati wacibale wasankha kusapita ndi kusiya banja lake kapena wasankha kubwelela kunyumba. Iwo angamuone kuti alibe cikondi ndi kuti ndi wodzikonda. N’cifukwa ciani angamuone conco? Cifukwa cakuti io afuna kuti wacibaleyo adziŵapatsa ndalama. (Miy. 19:6, 7) Anna anati: “Ngakhale n’conco, tikapewa kuika zinthu zakuthupi patsogolo acibale ena m’kupita kwa nthawi angazindikile mmene kuika zinthu za kuuzimu patsogolo kulili kofunika. Koma ngati tagonja ndi kucita zimene io afuna, kodi angazindikile bwanji kuti zinthu za kuuzimu ndizo zofunika kwambili?”—Yelekezelani ndi 1 Petulo 3:1, 2.

MUZIDALILA MULUNGU

16. (a) Kodi munthu ‘angazinyenge bwanji ndi maganizo onama’? (Yak. 1:22) (b) Ndi zosankha zotani zimene Yehova amadalitsa?

16 Mlongo wina atasiya banja lake ndi kupita kudziko lina, anauza akulu a kumeneko kuti: “Tinadzimana zinthu zambili kuti ndibwele kuno. Mwamuna wanga anasiya kutumikila monga mkulu. Conco, ndimapempha Yehova kuti andidalitse.” Nthawi zonse, Yehova amadalitsa zosankha zimene zimaonetsa kuti timam’dalila. Koma samadalitsa zosankha zimene sizigwilizana ndi cifunilo cake. Ndipo samakondwela ngati tasiya utumiki winawake popanda cifukwa comveka.—Ŵelengani Aheberi 11:6; 1 Yohane 5:13-15.

17. N’cifukwa ciani tiyenela kulola Yehova kuti atitsogolele tisanapange zosankha? Nanga tingacite bwanji zimenezo?

17 Muzilola Yehova kuti adzikutsogolelani musanapange zosankha, osati mutasankha kale. Muzipempha mzimu woyela, nzelu zake ndi citsogozo cake. (2 Tim. 1:7) Muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndiyenela kudzimana ciani kuti ndikwanitse kutumikila Yehova? Kodi ndidzatsatila mfundo zake pankhani yokhalabe ndi banja langa, ngakhale kuti zimenezo zidzacititsa kusakhala ndi zinthu zambili paumoyo?’ (Luka 14:33) Pemphani akulu kuti akuthandizeni, ndipo tsatilani malangizo a m’Baibulo amene io angakupatseni. Mukatelo, mudzaonetsa kuti mumakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzakuthandizani. Akulu sangakusankhileni zocita, koma angakuthandizeni kuti mupange zosankha zimene zidzakusangalatsani m’kupita kwa nthawi.—2 Akor. 1:24.

18. Ndani ali ndi udindo wosamalila banja? Nanga ndi zocitika ziti zimene zingatipatse mwai wakuti tiwathandize?

18 Yehova amafuna kuti mitu ya mabanja izisamalila mabanja ao nthawi zonse. Tiyenela kuyamikila ndi kupemphelela amene amakwanilitsa udindo wao wosamalila banja popanda kusiya mkazi ndi ana, ngakhale kuti ena angawakakamize kuti acite zimenezo. Zakugwa mwadzidzidzi monga ngozi kapena matenda, zimatipatsa mwai woonetsa cikondi ceniceni cacikristu. (Agal. 6:2, 5; 1 Pet. 3:8) Kodi tingawapatse ndalama zowathandiza pakagwa za mwadzidzidzi kapena kuwathandiza kuti apeze nchito? Tikatelo, io sangafunikile kusiya banja lao ndi kupita kukagwila nchito ku dela lina.—Miy. 3:27, 28; 1 Yoh. 3:17.

MUZIKUMBUKILA KUTI YEHOVA NDI MTHANDIZI WANU

19, 20. N’cifukwa ciani Akristu ayenela kukhala ndi cidalilo cakuti Yehova adzawathandiza?

19 Malemba amatiuza kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?’” (Aheb. 13:5, 6) Kodi tingatsatile bwanji malangizo amenewa?

20 Mkulu wina amene watumikila zaka zambili m’dziko lina losauka anati: “Nthawi zambili anthu amanena kuti Mboni za Yehova ndi anthu acimwemwe. Iwo amaonanso kuti ngakhale kuti Mboni zina ndi zosauka, nthawi zonse zimavala ndi kuoneka bwino kuposa anthu ena.” Zimenezi zimaonetsa kuti lonjezo limene Yesu ananena lokhudza kuika patsogolo Ufumu ndi loona. (Mat. 6:28-30, 33) Ndithudi, Atate wathu wakumwamba Yehova, amakukondani inu makolo ndi ana anu, ndipo amafuna kuti zinthu zizikuyendelani bwino. Baibulo limati: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mulungu watipatsa malamulo ake kuti tipindule. Ena mwa malamulo amenewa amakhudza umoyo wabanja ndi mmene tingapezele zosoŵa zathu zakuthupi. Ngati tiwatsatila, tidzaonetsa kuti timam’konda ndi kum’dalila. Baibulo limanena kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yoh. 5:3.

21, 22. N’cifukwa ciani muyenela kudalila Yehova kwambili?

21 Eduardo anati: “Ndidziŵa kuti nthawi imene ndinali kutali ndi banja langa sindingaibweze, koma sindimaganizila kwambili zinthu zakumbuyo. Anzanga ambili amene ndinali nao ndi olemela koma alibe cimwemwe. Mabanja ao ali ndi mavuto aakulu, koma banja lathu lili ndi cimwemwe cacikulu. Ndipo ndimasangalala ndikaona abale m’dziko lathu amene amaika patsogolo zinthu za kuuzimu ngakhale kuti ndi osauka. Tonse taona kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yesu.”—Ŵelengani Mateyu 6:33.

22 Tiyenela kulimba mtima, kumvela Yehova ndi kum’dalila. Kukonda Mulungu, mkazi wanu ndi ana anu kudzakuthandizani kusamalila bwino banja lanu. Mukatelo, mudzaona kuti ‘Yehova ndi mthandizi wanu.’

a Maina asinthidwa.

b Onani nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mungasamale Bwanji Ndalama”? mu Galamukani! ya September 2011

Kodi mungaphunzile nchito zosiyanasiyana kuti muzisamalila banja lanu? (Onani ndime 12)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani