LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 4/1 masa. 27-31
  • Kodi Mumayamikila Cisamalilo Cacikondi ca Yehova?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumayamikila Cisamalilo Cacikondi ca Yehova?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YEHOVA AMATICENJEZA
  • ATATE WATHU WACIKONDI AMATIONGOLELA
  • KUTSATILA MFUNDO ZA M’BAIBULO KUMATIPINDULITSA
  • BWENZI LIMENE LIMATITHANDIZA KUPILILA MAYESELO
  • YEHOVA ADZAKUDALITSANI
  • ‘Mvela Mawu a Anthu Anzelu’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Atate Wathu Yehova, Amatikonda Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kodi Yehova Waonetsa Bwanji Kuti Amatikonda?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Maso a Yehova Ali pa Anthu Ake
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 4/1 masa. 27-31

Kodi Mumayamikila Cisamalilo Cacikondi ca Yehova?

“Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.”—MIY. 15:3.

MFUNDO ZIMENE TIYENELA KUKUMBUKILA

  • N’cifukwa ciani Yehova amatiyang’ana?

  • Kodi Yehova amaticenjeza, kutiongolela ndi kutitsogolela bwanji?

  • N’cifukwa ciani nthawi zina Yehova angalole kuti tiyesedwe?

1, 2. Kodi colinga ca Yehova potiyang’ana cimasiyana bwanji ndi colinga ca anthu pogwilitsila nchito makamela?

M’MAIKO ambili, anthu amaika makamela m’masitolo ao kuti aziona makasitomala ndi kugwila amene akuba zinthu m’sitolo. Cifukwa ca makamela amenewa, munthu akaba amagwidwa mosavuta.

2 Baibulo limati maso a Yehova “ali paliponse.” (Miy. 15:3) Kodi zimenezi zitanthauza kuti iye amatiyang’ana kuti aziona ngati tiphwanya malamulo ake? Kodi amafuna kutilanga tikangolakwitsa zinthu? Iyai. (Yer. 16:17; Aheb. 4:13) Yehova amatiyang’ana cifukwa amatikonda ndipo amafuna kuti tikhale otetezeka ndi acimwemwe.—1 Pet. 3:12.

3. Tidzakambitsilana njila zisanu ziti zoonetsa kuti Mulungu amatiyang’ana cifukwa cotikonda?

3 N’ciani cingatithandize kudziŵa kuti Mulungu amatiyang’ana cifukwa cotikonda? Tiyeni tikambitsilane mmene amacitila zimenezi. Amacita zimenezi mwa (1) kuticenjeza tikayamba kulakalaka zoipa, (2) kutiongolela tikalakwa, (3) kutitsogolela ndi mfundo za m’Baibulo, (4) kutithandiza tikakumana ndi mayeselo, ndi (5) kutidalitsa akaona zabwino mwa ife.

YEHOVA AMATICENJEZA

4. N’cifukwa ciani Yehova anacenjeza Kaini asanacimwe?

4 Coyamba, tiyeni tione mmene Mulungu amaticenjezela tikayamba kulakalaka zinthu zoipa. (1 Mbiri 28:9) Kuti timvetsetse cisamalilo cacikondi ca Mulungu, tiyeni tione mmene anacitila ndi Kaini. Pamene Kaini anaona kuti nsembe yake sinalandilidwe ndi Mulungu, “anapsa mtima kwambili.” (Ŵelengani Genesis 4:3-7.) Yehova anacenjeza Kaini kuti ngati ‘sasintha ndi kucita cabwino,’ adzacimwa. Zinali ngati kuti ucimo “wamyata pakhomo” kum’dikilila. Mulungu anafunsa Kaini kuti: “Kodi iweyo suugonjetsa?” Mulungu anafuna kuti Kaini amvele cenjezo ndi kuti ‘amuyanje.’ Kaini akanamvela cenjezo la Mulungu, akanapitiliza kukhala paubwenzi wabwino ndi iye.

5. Kodi Yehova amaticenjeza bwanji tikayamba kulakalaka zoipa?

5 Bwanji poneza za ife masiku ano? Yehova amaona mmene mtima wathu ulili. Amadziŵa zimene timaganiza ndi kulakalaka ndipo sitingamubise kalikonse. Atate wathu wacikondi amafuna kuti tizitsatila njila yacilungamo, koma samatikakamiza kucita zimenezi. Tikayamba kulakalaka zinthu zoipa, iye amaticenjeza kupyolela m’Mau ake, Baibulo. Kodi amaticenjeza bwanji? Tikamaŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku, timapeza nkhani zimene zingatithandize kugonjetsa zizoloŵezi ndi zilakolako zoipa. Zofalitsa zathu zingapeleke malangizo othandiza pa vuto limene tikulimbana nalo ndi mmene tingaligonjetsele. Ndiponso pamisonkhano yampingo, tonsefe timalandila malangizo a panthawi yake.

6, 7. (a) N’ciani cimaonetsa kuti Yehova amawasamalila atumiki ake onse? (b) Kodi aliyense wa ife angapindule bwanji ndi cisamalilo ca Yehova?

6 Macenjezo onsewa ndi umboni wakuti Yehova amasamalila mwacikondi aliyense wa ife. N’zoona kuti Baibulo, zofalitsa zathu ndi misonkhano yathu zimapindulitsa anthu ambili. Koma Yehova amafuna kuti tizimvela macenjezo ake opezeka m’Baibulo kuti tizicita zinthu zabwino. Zimenezi zionetsa kuti iye amasamalila aliyense wa ife.

7 Kuti tipindule ndi macenjezo a Mulungu, coyamba tiyenela kuzindikila kuti amasamala kwambili za ife. Caciŵili, tiyenela kutsatila Mau ake ndi kuyesetsa kuthetsa maganizo alionse amene sakondweletsa Mulungu. (Ŵelengani Yesaya 55:6, 7.) Ngati timvela macenjezo amene timapatsidwa, tidzapewa mavuto ambili. Koma bwanji ngati talakwa. Kodi Yehova adzapitilizabe kutisamalila?

ATATE WATHU WACIKONDI AMATIONGOLELA

8, 9. Kodi uphungu umene Yehova amapeleka kupyolela mwa atumiki ake, umaonetsa bwanji kuti amatisamalila kwambili? Pelekani citsanzo.

8 Timadziŵa kuti Yehova amatisamalila makamaka pamene atipatsa uphungu. (Ŵelengani Aheberi 12:5, 6.) N’zoona kuti kupatsidwa uphungu kapena cilango sikumasangalatsa. (Aheb. 12:11) Koma ngati wina wake watipatsa uphungu wocokela m’Baibulo, tiyenela kuzindikila cifukwa cake wacita zimenezo. Iye sanacite zimenezo kuti atikhumudwitse. M’malo mwake, wacita zimenezo cifukwa waona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova uli pangozi. Iye mofunitsitsa wapatula nthawi kuti atithandize kuona mmene tingagwilitsile nchito mfundo za m’Baibulo kuti tibwelele kwa Yehova. Timaona uphunguwo kukhala wamtengo wapatali cifukwa umacokela kwa Yehova.

9 Mwacitsanzo, m’bale wina asanakhale mboni anali ndi cizoloŵezi copenyelela zamalisece. Ataphunzila coonadi, analeka cizoloŵezi cimeneci. Patapita nthawi, iye anagula foni ina ndipo anayambanso kupenyelela zamalisece pa Intaneti. (Yak. 1:14, 15) N’zoonekelatu kuti iye anali kulakalakabe kupenyelela zamalisece. Tsiku lina m’baleyo anapatsa foni mkulu wina kuti aigwilitsile nchito, ndipo zithunzi zamalisece zinaonekela pafoniyo. Nthawi imeneyo, mkuluyo anapeleka uphungu kwa m’baleyo. M’baleyo anamvetsela uphungu ndipo m’kupita kwa nthawi anagonjetsa cizoloŵezi coipa cimeneco. Yehova amaona zimene timacita mseli ndipo amationgolela tisanaononge ubwenzi wathu ndi iye. Timayamikila kuti Yehova amatisamalila.

KUTSATILA MFUNDO ZA M’BAIBULO KUMATIPINDULITSA

10, 11. (a) Kodi tingatsatile bwanji citsogozo ca Mulungu? (b) Nanga zimene banja lina linacita zionetsa bwanji kuti kutsatila mfundo za m’Baibulo n’kwanzelu?

10 Wamasalimo anaimbila Yehova kuti: “Mudzanditsogolela ndi malangizo anu.” (Sal. 73:24) Ngati tifuna kuti Yehova atitsogolele, ‘tizim’kumbukila’ mwa kufufuza m’Baibulo kuti tidziŵe malingalilo ake. Kutsatila mfundo za m’Baibulo kumatipindulitsa mwa kuuzimu ndipo kumatithandiza kupeza zosoŵa zakuthupi.—Miy. 3:6.

11 Zimene zinacitikila mlimi wina amene anali kucita lendi malo olimapo m’dela la mapili ku Masbate m’dziko la Philippines, zionetsa kuti Yehova amatsogolela. Iye ndi mkazi wake ndi apainiya anthawi zonse ndipo amasamalila banja lalikulu. Tsiku lina, io anathedwa nzelu atalandila kalata yocokela kwa mwini malowo yoŵauza kuti acoke pamalowo. N’cifukwa ciani anawauza kuti acoke? Cifukwa cakuti munthu wina anawanamizila kuti anacita zinthu mwacinyengo. Ngakhale kuti m’baleyo anali ndi nkhawa ponena za kumene adzapeza malo okhala ndi banja lake, iye anati: “Yehova adzatithandiza kupeza malo ena. Iye amatipatsa zofunikila zivute zitani.” M’baleyo anadalila Yehova kwambili. Patapita masiku ocepa, mwini malowo anauza banjalo kuti lisacoke pamalopo. N’cifukwa ciani analiuza kuti lisacoke? Mwini malowo anaona kuti ngakhale kuti banjalo linanamizilidwa, ilo linali kutsatilabe mfundo za m’Baibulo, ndi kupitilizabe kusonyeza ulemu ndi kukhala mwamtendele. Zimenezi zinasangalatsa mwini malowo kwambili cakuti analola banjalo kukhalabe pamalopo ndipo analionjezela malo olimapo. (Ŵelengani 1 Petulo 2:12.) Ndithudi, Yehova amagwilitsila nchito Baibulo kuti atithandize kupilila mavuto paumoyo wathu.

BWENZI LIMENE LIMATITHANDIZA KUPILILA MAYESELO

12, 13. N’ciani cingacititse ena kukaikila ngati Mulungu amawasamaliladi?

12 Komabe, nthawi zina tingavutike kwa nthawi yaitali. Tingavutike ndi matenda osacilitsika, tingatsutsidwe ndi acibale kapena kuzunzidwa kwa nthawi yaitali. Ndiponso kusiyana maganizo ndi wina wake mumpingo ndi cinthu covuta kwambili kupilila.

13 Mwacitsanzo, zimene wina angakambe zingatikhumudwitse kwambili. Tinganene kuti: ‘Izi siziyenela kucitika m’gulu la Mulungu.’ Mwina Mkristu amene wakukhumudwitsani ali ndi maudindo ambili mumpingo ndipo ena amamuona kuti ndi Mkristu wabwino kwambili. Conco mungafunse kuti: ‘Kodi izi zingacitike bwanji? Kodi Yehova samaona zimene zicitika? Kodi sadzacitapo kanthu?’—Sal. 13:1, 2; Hab. 1:2, 3.

14. N’cifukwa ciani nthawi zina Mulungu sangacitepo kanthu ngati takhumudwitsidwa?

14 Yehova angakhale ndi zifukwa zomveka zimene sacitilapo kanthu. Mwacitsanzo, pamene inu muona kuti Mkristu wina ndi wolakwa kwambili, Mulungu angaone zinthu mosiyana. Mwina Iye angaone kuti ndinu amene muli ndi vuto. Ndipo mau amene mungakhumudwe nao angakhale uphungu umene muyenela kuganizilapo. M’nkhani yokhudza umoyo wake, M’bale Karl Klein, amene anali mu Bungwe Lolamulila anakamba kuti nthawi ina anapatsidwa uphungu ndi M’bale  J. F. Rutherford. Panthawi ina izi zitacitika kale, mwacimwemwe M’bale  Rutherford anapatsa moni M’bale Klein kuti, “Bwanji M’bale Karl!” Koma M’bale Klein anayankha mosakondwa cifukwa anali wokhumudwabe ndi uphungu umene anapatsidwa. M’bale Rutherford atazindikila kuti M’bale Klein anali kusunga cakukhosi, anamucenjeza kuti asamale cifukwa angagwidwe ndi Mdyelekezi. Patapita nthawi, M’bale Klein analemba kuti: “Ngati tisungila m’bale wathu cakukhosi, makamaka ngati m’baleyo ndi woyenelela kutipatsa uphungu, tingagwele mumsampha wa Mdyelekezi mosavuta.”a

15. Kodi muyenela kukumbukila ciani kuti musataye mtima poyembekezela Yehova kuti akuthandizeni kupilila mayeselo?

15 Koma ngati mayeselo apitilizabe mungataye mtima. Kodi n’ciani cingakuthandizeni kupilila? Mwacitsanzo, yelekezelani kuti muli pamzela wogaitsa cimanga kucigayo. Cifukwa ca kutalika kwa mzela simudziŵa nthawi imene mudzagaitsa cimanga. Kenako mwalephela kudikila ndipo mwacoka pamzele ndi kupita kucigayo cina. Koma kumene mwapita mwapeza mzela wautali kuposa umene mwasiya. Zimenezi zidzacititsa kuti mucedwe kugaitsa, koma mukanayembekezela pamzela kucigayo coyamba, mukanagaitsa mwamsanga. Mofananamo, ngati tifuna kuti Yehova atithandize kupilila, sitiyenela kutaya mtima koma tiyenela kutsatilabe mfundo zake za m’Baibulo.

16. N’cifukwa ciani nthawi zina Yehova angalole kuti tiyesedwe?

16 Nthawi zina tikamayesedwa, Yehova angalole mayeselowo kuti tiphunzilepo kanthu kena. (Ŵelengani 1 Petulo 5:6-10.) Tisamaganize kuti Mulungu ndi amene akutiyesa. (Yak. 1:13) “Mdani wanu Mdyelekezi,” ndi amene amacititsa mavuto ambili. Komabe, Mulungu angatithandize kukula kuuzimu mwa kulola kuti tiyesedwe ndi zinthu zovuta. Iye amaona mmene tivutikila ndipo ‘pakuti amatidela nkhawa,’ adzaonetsetsa kuti tiyesedwa “kwa kanthawi” cabe. Mukakumana ndi mayeselo, kodi mumayamikila cisamalilo cacikondi cimene Yehova amapeleka ndi kum’dalila kuti iye adzakuthandizani kupilila?—2 Akor. 4:7-9.

YEHOVA ADZAKUDALITSANI

17. Kodi Yehova amafufuza anthu otani? Nanga n’cifukwa ciani amacita zimenezi?

17 Yehova amafufuza mitima ya anthu kuti aone amene amam’konda. Kudzela mwa Haneni, Yehova anauza Mfumu Asa kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Ngakhale kuti Yehova anaona kuti Asa analibe mtima wathunthu, iye ‘adzaonetsa mphamvu zake’ kwa inu ngati mucitabe zinthu zabwino.

18. N’cifukwa ciani tingakhale ndi cidalilo cakuti Yehova adzatidalitsa ngati timacita zabwino? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)

18 Mulungu afuna kuti ‘tiziyesetsa kucita zabwino,’ ‘tizikonda cabwino,’ ndipo ‘tizicita zabwino,’ kuti ‘atikomele mtima.’ (Amosi 5:14, 15; 1 Pet. 3:11, 12) Yehova amakumbukila olungama ndipo amawadalitsa. (Sal. 34:15) Mwacitsanzo, ganizilani za Sifira ndi Puwa, anamwino aciisiraeli. Farao analamula akazi amenewa kuti azipha ana aamuna aciisiraeli akangobadwa. Akaziwa anamvela Mulungu m’malo momvela Farao ndipo anapulumutsa anawo. Yehova anaona nchito zabwino za Sifira ndi Puwa ndipo anawadalitsa mwa kuwapatsa ana aoao. (Eks. 1:15-17, 20, 21) Nthawi zina tingaganize kuti palibe amene amaona zabwino zimene timacita, koma Yehova amaona ndipo adzatidalitsa.—Mat. 6:4, 6; 1 Tim. 5:25; Aheb. 6:10.

19. Kodi mlongo wina anazindikila bwanji kuti Yehova amaona nchito zabwino zimene timacita?

19 Mlongo wina wa ku Austria anazindikila kuti Mulungu anaona nchito imene iye anagwila mwakhama. Mlongoyu anali wa ku Hungary ndipo analandila adilesi ya munthu amene amalankhula Cihangariya kuti aziphunzila naye. Posapita nthawi, mlongoyo anapita kunyumba ya munthuyo koma sanamupeze. Komabe, iye anali kupita kunyumbako mobwelezabweza. Nthawi zina, mlongoyo anali kumva kuti m’nyumbamo munali munthu koma sanali kuyankha. Mlongoyu anali kusiya zofalitsa, makalata, ndipo anasiyanso adilesi yake. Patapita caka cimodzi ndi hafu, mai wina anatsegula citseko. Maiyo anali waubwenzi ndipo anauza mlongoyo kuti: “Loŵani. Ndinaŵelenga zonse zimene munandisiila ndipo ndinali kukuyembekezelani.” Mwininyumbayo anali kulandila thandizo la mankhwala a kansa ndipo anali kukhala cabe m’nyumba. Maiyo anayamba kuphunzila Baibulo ndi mlongoyo. Ndithudi, Mulungu anadalitsa mlongoyo kaamba ka khama lake.

20. Kodi mumamva bwanji kudziŵa kuti Yehova amakusamalilani inu panokha?

20 Yehova amaona zonse zimene timacita ndipo adzatidalitsa. Kudziŵa kuti Mulungu amatiyang’ana, sikuyenela kuticititsa kuganiza kuti iye amafuna kuona zimene timalakwitsa monga mmene anthu ogwilitsila nchito makamela amacitila. M’malo mwake, kuyenela kuticititsa kukhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu amene amatisamalila kwambili.

a Nkhani yokhudza umoyo wa M’bale  Klein inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya Cilengezi ya October 1, 1984.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani