LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 6/1 masa. 4-6
  • Kodi Mulungu Amakuona Bwanji Kukoka Fodya?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mulungu Amakuona Bwanji Kukoka Fodya?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KULEKA KUKOKA KUMAVUTA
  • KUKOKA FODYA KUMAONONGA THUPI
  • KUKOKA FODYA KUMAVULAZA ENA
  • ANTHU SADZAKOKANSO FODYA
  • Konzekelani Kukumana na Mavuto
    Galamuka!—2010
  • Vuto la Padziko Lonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Khalani Wotsimikiza
    Galamuka!—2010
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 6/1 masa. 4-6

NKHANI YA PACIKUTO | MMENE MULUNGU AMAONELA KUKOKA FODYA

Kodi Mulungu Amakuona Bwanji Kukoka Fodya?

Naoko, amene tam’chula m’nkhani yapita, anafotokoza cimene cinam’thandiza kuti aleke kukoka fodya. Iye anati: “Kuphunzila coonadi ponena za makhalidwe a Mulungu ndi colinga cake kunandithandiza kusintha umoyo wanga.” Coonadi cimeneci cipezeka m’Baibulo. Ngakhale kuti Baibulo silimachula za fodya, ilo limatithandiza kudziŵa mmene Mulungu amaonela kukoka fodya.a Cidziŵitso cimeneci cathandiza anthu ambili kuleka cizoloŵezi cokoka fodya. (2 Timoteyo 3:16, 17) Tiyeni tione mavuto atatu amene amabwela cifukwa cokoka fodya ndi zimene Baibulo limanena.

KULEKA KUKOKA KUMAVUTA

Fodya ali ndi mankhwala ochedwa nikotini amene amasokoneza ubongo kwambili. Nikotini amacititsa munthu kukhala wocangamuka ndi wosakondwa. Ngati munthu akoka fodya, nikotini amafika ku ubongo mofulumila ndi mobwelezabweleza. Nthawi iliyonse imene munthu wakoka, nikotini amaloŵa m’thupi mwake. Pa avaleji, munthu amene amakoka paketi imodzi ya fodya tsiku lililonse, amaloŵetsa nikotini woculuka kwambili m’thupi lake kuposa mankhwala ena onse osokoneza ubongo. Nikotini amacititsa kuti munthu avutike kwambili kuti aleke kukoka. Conco, munthu akazoloŵela kukoka amakhala ndi mavuto ena cifukwa coleka kukoka.

‘Mumakhala akapolo a munthu amene mumamumvela.’—Aroma 6:16

Ngati ndinu kapolo wa fodya kodi mungamveledi Mulungu??

Baibulo limatithandiza kukhala ndi maganizo oyenela pankhani yokoka fodya. Baibulo limati: “Kodi simukudziŵa kuti ngati mudzipelekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvela, mumakhala akapolo ake cifukwa cakuti mumamumvela?” (Aroma 6:16) Ngati cilakolako ca fodya cimalamulila maganizo ndi zocita za munthu, iye amakhala kapolo wa fodya. Komabe, Mulungu, amene dzina lake ndi Yehova, safuna cabe kuti timasuke ku zizoloŵezi zoipa zimene zimaononga thupi lathu. Koma afunanso kuti timasuke ku zizoloŵezi zimene zimaipitsa maganizo athu. (Salimo 83:18; 2 Akorinto 7:1) Conco, ngati munthu amayamikila ndi kulemekeza Yehova kwambili, amayesetsa kucita zimene angathe kuti am’kondweletse. Amazindikila kuti sangakondweletse Yehova ngati iye ndi kapolo wa zizoloŵezi zoipa. Kuzindikila zimenezi kumathandiza munthu kuti apewe zilakolako zoipa.

Olaf, wa ku Germany, anali kapolo wa fodya kwa zaka 16. Iye anayamba kukoka pamene anali ndi zaka 12. Olaf anati: “Nditakoka ndudu nthawi yoyamba, ndinaona ngati kuti panalibe vuto lililonse. Koma patapita zaka zambili ndinayamba kukoka ndudu zambili. Nthawi ina ndinalibe fodya ndipo ndinavutika kwambili. Ndinatenga fodya amene anatsalila pa kambale koikapo phulusa la ndudu, ndi kupanga ndudu ya fodya pa kapepala. Pambuyo pake ndinacita manyazi kwambili.” Kodi Olaf anathetsa bwanji cizoloŵezi cokoka fodya? Iye anati: “Cimene cinandithandiza kwambili ndi kufuna kukondweletsa Yehova. Cikondi ca Yehova pa anthu ndi ciyembekezo cimene wawapatsa zinandicititsa kuti ndilekeletu cizoloŵezi cimeneci.”

KUKOKA FODYA KUMAONONGA THUPI

Buku lina lochewa The Tobacco Atlas linati: “Asayansi anapeza kuti ngati munthu amakoka fodya, pafupifupi ziwalo zake zonse zimaonongeka ndipo nthawi iliyonse angadwale ndi kufa.” Anthu ambili adziŵa kuti kukoka fodya kumayambitsa matenda osapatsilana monga kansa, matenda a mtima, ndi kusagwila bwino nchito kwa mapapo. Koma malinga ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linakamba, anthu ambili amafa ndi matenda opatsilana monga TB cifukwa cokoka.

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—Mateyu 22:37

Ngati mumadetsa thupi limene Mulungu anakupatsani, kodi munganene kuti mumam’konda ndi kum’lemekeza?

Yehova Mulungu, kupyolela m’Mau ake Baibulo amatiphunzitsa kuona moyo ndi thupi moyenela. Amatiphunzitsanso kukhala ndi maganizo oyenela. Mwana wake Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Ndithudi, Mulungu afuna kuti tizigwilitsila nchito bwino moyo wathu ndi matupi athu ndi kuzisamalila. Tikamaphunzila za Yehova ndi malonjezo ake, timayamba kum’konda ndipo timayamikila zonse zimene waticitila. Kukonda Mulungu kumatithandiza kupewa kalikonse kamene kamadetsa thupi.

Dokotala wina wa ku India dzina lake Jayavanth anakoka fodya kwa zaka 38. Iye anati: “Pamene ndinaŵelenga magazini ndinadziŵa kuopsa kokoka fodya, ndipo ndinali kulimbikitsa anthu odwala kuti aleke kukoka. Komabe, ine ndinavutika kuleka ngakhale nditayesa kucita zimenezo pafupifupi maulendo 6.” Kodi n’ciani cinathandiza Dokotala ameneyo kuleka kukoka? Iye anati: “Ndinaleka kukoka cifukwa cophunzila Baibulo. Ndinaleka kukoka fodya kuti ndikondweletse Yehova.”

KUKOKA FODYA KUMAVULAZA ENA

Utsi umene munthu amatulutsa akamakoka, ndi umene umatuluka poumitsa fodya ndi wovulaza. Kupuma utsi umenewo kungabweletse matenda a kansa ndi ena. Caka ciliconse, anthu 600 sauzande amene sakoka amafa ndi utsi wa fodya. Ambili mwa io ndi akazi ndi ana. Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linacenjeza kuti: “Ngakhale anthu amene amapumako cabe utsi umene umatuluka wina akamakoka amakhala pangozi.”

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—Mateyu 22:39

Ngati muika pangozi umoyo wa acibale ndi anansi anu cifukwa cokoka fodya, kodi munganene kuti mumawakondadi?

Mogwilizana ndi zimene Yesu anakamba, tingakonde anansi athu, acibale, mabwenzi athu, ndi ena kokha ngati tikonda Mulungu coyamba. Iye anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mateyu 22:39) Ngati ticita zinthu zimene zingaike ena pangozi ndiye kuti sitikonda anansi athu. Cikondi ceniceni cimatisonkhezela kutsatila malangizo a m’Baibulo akuti: “Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 Akorinto 10:24.

Armen, wa ku Armenia, anati: “Banja langa linandipempha kuti ndileke kukoka cifukwa linali kuvutika ndi fodya. Koma, sindinakhulupilile zimene io anandiuza.” Iye anafotokoza cimene cinam’thandiza kusintha maganizo ake. Armen anati: “Zimene ndinali kuphunzila m’Baibulo ndi kukonda kwanga Yehova zinandithandiza kuti ndileke kukoka. Ndinavomeleza kuti fodya samangoononga cabe munthu wokoka koma amaononganso ena.”

ANTHU SADZAKOKANSO FODYA

Baibulo linathandiza Olaf, Jayavanth, ndi Armen kuleka cizoloŵezi coipa cimene cinali kuwaononga ndi kuononga anthu ena. Iwo analeke kukoka fodya osati cabe cifukwa codziŵa kuti fodya ndi wovulaza. Koma analeka cifukwa cakuti anayamba kukonda Yehova ndipo anafuna kum’kondweletsa. Lemba la 1 Yohane 5:3 limafotokoza cifukwa cake cikondi n’cofunika. Lembali limati: “Cifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” N’zoona kuti kusunga mfundo za m’Baibulo nthawi zina kungakhale kovuta, koma ngati munthu amakonda Mulungu kwambili sadzaona kuti kumvela Mulungu ndi mtolo.

Yehova Mulungu akuthandiza anthu ambili kumasuka ku ukapolo wokoka fodya kupyolela m’nchito yophunzitsa anthu ya padziko lonse. (1 Timoteyo 2:3, 4) Posacedwapa, Yehova adzagwilitsila nchito Ufumu wake, umene ndi boma la kumwamba lolamulilidwa ndi mwana wake Yesu Kristu, kuononga dongosolo la malonda la umbombo limene limacititsa anthu ambili kukhala akapolo a fodya. Mulungu adzathetselatu vuto lokoka fodya, ndipo adzacititsa anthu kukhala ndi matupi ndi maganizo angwilo.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 19:11, 15.

Ngati mumayesetsa kuti muleke kukoka fodya koma mumalephela, musataye mtima. Mwa kuphunzila kukonda Yehova ndi kudziŵa mmene iye amaonela fodya, inunso mungaleke kukoka. Mboni za Yehova zidzakondwa kukuthandizani kuphunzila ndi kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo. Khalani ndi cidalilo cakuti Yehova adzakupatsani mphamvu kuti mugonjetse cizoloŵezi cokoka fodya.—Afilipi 4:13

a M’nkhani ino, kukoka fodya kutanthauza kupuma mwacindunji utsi wa fodya pokoka ndudu. Komabe, mfundo zimene tafotokoza zikhudzanso aja amene amatafuna kapena kufwenkha fodya amene ali ndi nikotini.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani