NKHANI YA PACIKUTO | MMENE MULUNGU AMAONELA KUKOKA FODYA
Vuto la Padziko Lonse
Anthu amafa cifukwa cokoka fodya.
M’zaka za m’ma 1900, fodya unapha anthu 100 miliyoni.
Caka ciliconse, fodya umapha anthu pafupifupi 6 miliyoni.
Pa avaleji, munthu mmodzi amafa m’masekondi 6 alionse.
Palibe ciliconse cimene cionetsa kuti anthu angaleke kukoka fodya.
Akatswili amanena kuti ngati anthu apitilizabe kukoka fodya, podzafika mu 2030 ciŵelengelo ca anthu amene amafa caka ndi caka, cidzaonjezeka kuposa pa 8 miliyoni. Amanenanso kuti podzafika kumapeto kwa zaka za m’ma 2000, anthu 1 biliyoni adzafa cifukwa cokoka fodya.
Anthu amene amakoka fodya si okhawo amene amavutika. Acibale a munthu amene amakoka fodya amakhudzidwanso. Iwo amavutika maganizo ndipo amataya ndalama. Ndipo anthu 600 sauzande amene sakoka fodya amafa caka ciliconse cifukwa copuma utsi wake. Anthu okoka fodya komanso amene sakoka, amaononga ndalama zambili pofuna thandizo ku cipatala.
Matenda amene amabwela cifukwa cokoka fodya angacilitsidwe mosavuta, kusiyana ndi matenda obuka mwadzidzidzi amene amagometsa mitu madokotala kuti apeze mankhwala ake. Dokotala wina wochedwa Margaret Chan, mkulu wa Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, anati: “Popeza kuti anthu ndi amene acititsa matenda obwela cifukwa cokoka fodya, maboma ndi anthu ndi amenenso angathetse vutoli.”
Anthu padziko lonse lapansi ayesetsa kuti athetse vutoli koma alephela. Mwacitsanzo, pafupifupi maiko 175 anagwilizana zakuti aletse anthu kukoka fodya, ndipo izi zinayenela kucitika podzafika mu August 2012.a Koma amene acititsa kuti vutoli lipitilize ndi anthu. Caka ciliconse, makampani a fodya amaononga ndalama zambili potsatsa malonda ao kuti akope makasitomala atsopano. Ambili a makasitomala amenewa ndi akazi ndi acinyamata m’maiko osauka. Zioneka kuti pa anthu 1 biliyoni amene amakoka kwambili fodya, ambili adzapitilizabe kufa. Ndipo ngati anthu saleka kukoka tsopano, ciŵelengelo cidzaonjezeka kwambili m’zaka 40 mtsogolo.
Anthu apitilizabe kutsatsa malonda a fodya, ndipo ambili amene ali ndi cizoloŵezi cokoka zimawavuta kuleka. Izi n’zimene zinacitika kwa Naoko. Iye anayamba kukoka fodya ali wacinyamata. Potengela zimene anali kuona pa TV, m’magazini ndi m’manyuzipepala, iye anadziona monga ndi wotsogola. Ngakhale kuti makolo ake anafa ndi matenda a kansa ya m’mapapo, iye anapitilizabe kukoka fodya, uku akulela ana ake aŵili. Iye anati: “Ndinali kuopa kuti ndingadwale kansa ya m’mapapo. Ndinaopanso kuti ana anga angadwale. Koma sindinaleke kukoka, ndinaona monga n’zosatheka.”
Komabe, Naoko analeka kukoka. Cimene cinam’thandiza kuleka ndi cimene cathandiza anthu mamiliyoni kumasuka kucizoloŵezi cokoka. Kodi cinthu cimeneco n’ciani? Nanga cipezeka kuti? Ŵelengani nkhani yotsatila.
a Zimenezi zinaphatikizapo kuphunzitsa anthu kuopsa kokoka fodya, kuletsa makampani kupanga fodya wambili, kuonjezela msonkho wake, ndi kukhazikitsa mapulogalamu othandiza anthu kuti aleke kukoka.