NKHANI YA PACIKUTO | N’CIFUKWA CIANI ZINTHU ZOIPA ZIMACITIKILA ANTHU ABWINO?
Zinthu Zoipa N’zoculuka
Smita,a mai wa zaka 35 ku Dhaka, Bangladesh, anali ndi khalidwe lokonda anthu ndi kuwasamalila. Anthu anali kumudziŵa kuti ndi munthu wolimbikila nchito, ndiponso mkazi wacimwemwe amene anali kufuna kuthandiza ena kudziŵa zimene anaphunzila ponena za Mulungu. Acibale ake ndi mabwenzi ake anadabwa kwambili, pamene mwadzidzidzi Smita anadwala ndipo anamwalila mlungu umodzi usanathe.
James ndi mkazi wake anali banja lacinyamata la zaka za m’ma 30. Iwo anali ndi khalidwe lofanana ndi la Smita. Nthawi ina capakati pa March ndi April anapita kukacezela anzao amene anali kukhala kudela la West Coast ku United States. Iwo sanabwelelenso kunyumba yao ku New York. Ali koceza, anacita ngozi yoopsa kwambili pagalimoto, ndipo zimenezi zinacititsa okondedwa ao ndi anzao akunchito kumva kuti cinacake cinali kusoŵeka pamoyo wao.
Simufunikila kucita kuyang’ana kutali kuti muone mavuto ndi zoipa zimene zaculuka masiku ano. Nkhondo zimapha anthu wamba ndi asilikali. Zaciwawa zimacitikila anthu osalakwa. Ngozi zoopsa kwambili ndi matenda aakulu amakhudza munthu wina aliyense mosasamala za msinkhu kapena umoyo wake. Ngozi zacilengedwe zimapha anthu ambilimbili kaya akhale olakwa kapena ai. Tsankhu ndi kupanda cilungamo n’zofala kwambili. Mwina munavutikapo cifukwa ca tsankhu ndi kupanda cilungamo.
N’zomveka kufunsa mafunso monga awa:
N’cifukwa ciani zinthu zoipa zimacitikila anthu abwino?
Kodi Mulungu ndi amene amacititsa zinthu zimenezi?
Kodi zoipa zimangocitika mwangozi, kapena munthu ndiye amazicititsa?
Kodi ena amavutika cifukwa ca zocita zao pamoyo wao wakale, kapena kuti Karma?
Ngati kuli Mulungu wamphamvuyonse, n’cifukwa ciani samateteza anthu abwino ku mavuto?
Moyo wopanda mavuto ndi zoipa udzakhalako?
Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tifunika kudziŵa mayankho a mafunso aŵili ofunika awa: N’cifukwa ciani zoipa zimacitika? Ndipo Mulungu adzacita ciani?
a Maina asinthidwa.