LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 7/1 masa. 4-6
  • N’cifukwa Ciani Zinthu Zoipa Zimacitikila Anthu Abwino?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Zinthu Zoipa Zimacitikila Anthu Abwino?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUKHALA PAMALO OLAKWIKA PANTHAWI YOLAKWIKA
  • KODI ANTHU NDI AMENE AMACITITSA?
  • AMENE AKUCITITSA MAVUTO AMBILI
  • N’cifukwa Ciani Pa Dziko Pali Mavuto Ambili Conco?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Zimene Mulungu Adzacita Pothetsa Zinthu Zoipa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Zoipa Komanso Mavuto Zinakhalako Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 7/1 masa. 4-6

NKHANI YA PACIKUTO | N’CIFUKWA CIANI ZINTHU ZOIPA ZIMACITIKILA ANTHU ABWINO?

N’cifukwa Ciani Zinthu Zoipa Zimacitikila Anthu Abwino?

Yehova Mulungua ndiye Mlengi wa zinthu zonse ndipo ndi wamphamvuyonse. Cifukwa ca zimenezi, anthu ambili angaganize kuti iye ndiye amacititsa zinthu zonse zimene zicitika padziko kuphatikizapo zoipa. Komabe, onani zimene Baibulo limakamba ponena za Mulungu woona:

  • “Yehova ndi wolungama m’njila zake zonse.”—Salimo 145:17.

  • “Njila zake zonse[Mulungu] ndi zolungama. Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama. Iye ndi wolungama ndi woongoka.”—Deuteronomo 32:4.

  • “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.”—Yakobo 5:11.

Mulungu sindiye amacititsa zinthu zoipa. Koma kodi iye amalimbikitsa ena kucita zinthu zoipa? Iyai. Baibulo limati: “Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Mulungu sayesa munthu aliyense mwa kum’cititsa kukhala ndi khalidwe loipa. Iye sapangitsanso zinthu zoipa kucitika kapena kulimbikitsa ena kucita zinthu zoipa. Conco, zinthu zoipa zikacitika, ndani amene tiyenela kuimba mlandu?

KUKHALA PAMALO OLAKWIKA PANTHAWI YOLAKWIKA

Pofotokoza cifukwa cimodzi cimene anthu amavutikila, Baibulo limati: “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.” (Mlaliki 9:11) Pamene zinthu zosayembekezeleka kapena ngozi zacitika, kaya wina wakhudzidwa ndi zocitikazo kapena iyai, zimadalila kwambili malo amene munthuyo anali pamene ngoziyo inali kucitika. Pafupifupi zaka 2000 zapitazo, Yesu Kristu ananena za ngozi imene inapha anthu 18 pamene nsanja inawagwela. (Luka 13:1-5) Iwo anafa osati cifukwa ca khalidwe lao, koma cifukwa cakuti anali munsi mwa nsanja pamene inagwa. Posacedwapa, mu January 2010, civomezi coopsa kwambili cinacitika ku Haiti. Boma la dziko limeneli linati anthu oposa 300 sauzande anafa. Anthu onsewo anafa mosasamala kanthu zakuti anali anthu otani. N’cimodzimodzinso ndi matenda angafikile wina aliyense panthawi iliyonse.

N’cifukwa ciani Mulungu sateteza anthu abwino ku ngozi zimene zimacitika?

Ena angafunse kuti: ‘Kodi Mulungu sangaletse zinthu zoipa zimenezi kuti zisacitike? Kodi sangateteze anthu abwino ku mavuto amenewa?’ Mulungu akaloŵelelapo pa zocitika zimenezi, zingatanthauze kuti amadziŵilatu zinthu zoipa zisanacitike. N’zoona kuti Mulungu amatha kudziŵilatu zamtsogolo. Koma funso limene tifunika kuganizila ndi ili: Kodi Mulungu amaonetsa mphamvu zake zimenezi zodziŵilatu zinthu zamtsogolo popanda malile?—Yesaya 42:9.

Baibulo limati: ‘Mulungu ali kumwamba. Ciliconse cimene afuna kucita amacita.’ (Salimo 115:3) Yehova amacita zinthu zimene aona kuti n’zofunika kucita osati cim’citila. Mfundo imeneyi imagwilanso nchito pa zinthu zamtsogolo zimene afuna kudziŵa. Mwacitsanzo, pamene kuipa kunaculuka kwambili m’mizinda yakale ya Sodomu ndi Gomora, Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Ndiye nditsikilako kuti ndikaone ngati akucitadi monga mwa kudandaula kumene ndamva ndiponso ngati zocita zao zilidi zoipa conco. Ndikufuna ndidziŵe zimenezi.” (Genesis 18:20, 21) Panthawi imeneyo, Yehova anasankha kuti asadziŵe mmene kuipa kunaculukila m’mizinda imeneyo. Mofananamo, Yehova angasankhe kusadziŵilatu zinthu zonse. (Genesis 22:12) Zimenezi sizitanthauza kuti iye ndi wopanda ungwilo kapena ndi wofooka. Popeza kuti ‘nchito zake zonse ndi zangwilo,’ Mulungu amadziŵa bwino nthawi yoonetsa mphamvu zake zodziŵilatu zamtsogolo malinga ndi colinga cake. Iye sakakamiza anthu kutsatila njila ina yake.b (Deuteronomo 32:4) Conco tingakambe ciani pamenepa? Mwacidule tingakambe kuti: Mulungu amasankha nthaŵi imene angaonetse mphamvu yake yodziŵilatu zamtsogolo malinga ndi mmene afunila.

KODI ANTHU NDI AMENE AMACITITSA?

Tingakambe kuti zoipa zina ndi anthu amene amazicititsa. Onani mmene Baibulo limafotokozela cimene cingasonkhezele wina kucita zoipa, pamene limati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake. Ndiye cilakolako cikatenga pakati, cimabala chimo. Nalonso chimo likakwanilitsidwa, limabweletsa imfa.” (Yakobo 1:14, 15) Anthu akayamba kucita zinthu motsatila zilakolako zoipa kapena kugonja ku zilakolako zoipa, angakumane ndi mavuto. (Aroma 7:21-23) Malinga ndi mbili, anthu acita zinthu zoipa kwambili zimene zabweletsa mavuto aakulu kwambili. Komanso, anthu oipa angasonkhezele ena kucita zoipa, ndipo akatelo amaonjezela zinthu zoipa.—Miyambo 1:10-16.

Anthu acita zinthu zoipa kwambili zimene zacititsa mavuto aakulu kwambili

Kodi Mulungu ayenela kuloŵelelapo ndi kuletsa anthu kucita zinthu zoipa? Ganizilani mmene munthu anapangidwila. Baibulo limakamba kuti Mulungu analenga munthu m’cifanizilo cake, kutanthauza kuti ndi wofanana ndi Mulungu. Conco, anthu angaonetse makhalidwe a Mulungu. (Genesis 1:26) Iye anapatsa anthu ufulu wodzisankhila zocita, ndipo io angasankhe kum’konda ndi kukhala okhulupilika kwa iye mwa kucita zinthu zoyenela pamaso pake. (Deuteronomo 30:19, 20) Ngati Mulungu angakakamize anthu kutsatila njila ina yake, ndiye kuti akuwalanda ufulu wodzisankhila zocita. Anthu angakhale monga makina amene amangocita zimene anawakonzelatu kucita. Zimenezi zingaoneke monga kuti zocita zathu zonse, ndi zimene zimaticitikila zinaikidwilatu. Koma ndife okondwa kwambili cifukwa cakuti Mulungu anatilemekeza mwa kutilola kudzisankhila tokha zocita. Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti mavuto amene amabwela cifukwa colakwitsa zinthu ndi kusankha molakwika adzakhalapo kwamuyaya.

KODI MAVUTO AMACITIKA CIFUKWA CA KARMA?

Ngati mungafunse Mhindu kapena Mbuda funso limene lili pacikuto ca magazini ino, adzakuyankhani kuti: “Zinthu zoipa zimacitikila anthu abwino cifukwa ca lamulo la Karma. Iwo amati akututa zimene anacita m’miyoyo ina asanabadwenso.”c

Ponena za ciphunzitso ca Karma, ndi bwino kudziŵa zimene Baibulo limakamba zokhudza imfa. M’munda wa Edeni mmene anthu anayambila, Mlengi anauza munthu woyamba Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Ngati Adamu sanacimwe mwa kusamvela Mulungu, akanakhala ndi moyo kosatha. Imfa inakhalapo monga cilango cosamvela lamulo la Mulungu. Ndiyeno, pamene ana anali kubadwa, ‘imfa inafalikila kwa anthu onse.’ (Aroma 5:12) Conco tinganene kuti “malipilo a ucimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Baibulo limafotokozanso kuti: “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7) M’mau ena, anthu akamwalila, sapitiliza kulangidwa cifukwa ca macimo ao.

Masiku ano, anthu mamiliyoni amakamba kuti anthu amavutika cifukwa ca ciphunzitso ca Karma, kapena kuti zimene munthu anacita m’moyo wina asanabadwenso. Nthawi zambili munthu wokhulupilila ciphunzitso ca Karma amavomeleza mavuto ake ndi a anthu ena popanda kuthedwa nao nzelu. Koma mfundo ndi yakuti cikhulupililo cimeneci sicimapeleka ciyembekezo ciliconse cakuti mavuto adzatha. Anthu amakhulupilila kuti munthu amangomasuka ku moyo wobadwanso kukhala cinthu cina ngati akhala ndi moyo wabwino ndiponso cidziŵitso capadela. Koma zimenezi n’zosiyana kwambili ndi zimene Baibulo limanena.d

AMENE AKUCITITSA MAVUTO AMBILI

Munthu sindiye amacititsa mavuto ambili. Satana Mdyelekezi, amene poyamba anali mngelo wokhulupilika wa Mulungu, “sanakhazikike m’coonadi” ndipo anabweletsa ucimo m’dziko. (Yohane 8:44) Iye anayambitsa kupanduka m’munda wa Edeni. (Genesis 3:1-5) Yesu Kristu anamucha kuti “woipayo” ndi “wolamulila wa dziko.” (Mateyu 6:13; Yohane 14:30) Anthu ambili amatsatila Satana mwa kutengela maganizo ake onyalanyaza njila zabwino za Yehova. (1 Yohane 2:15, 16) Lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Palinso zolengedwa zina zauzimu zimene zinakhala zoipa ndipo zinagwilizana ndi Satana. Baibulo limanena kuti Satana ndi ziŵanda zake “akusoceletsa dziko lonse lapansi,” ndipo akucititsa ‘masoka padziko lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9, 12) Conco, Satana Mdyelekezi ndiye amacititsa mavuto ambili.

Mwacionekele, Mulungu sindiye amacititsa zinthu zoipa zimene zimacitikila anthu, ndipo sindiye amacititsa kuti anthu azivutika. Komabe, iye walonjeza kuti adzathetsa zoipa zonse, monga mmene nkhani yotsatila idzafotokozela.

a Yehova ndi dzina la Mulungu monga mmene Baibulo limanenela.

b Kuti mudziŵe cifukwa cimene Mulungu wololela zinthu zoipa kupitilizabe, onani nkhani 11, m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

c Kuti mudziŵe za ciyambi ca lamulo la Karma, onani masamba 8-12, m’kabuku kacingelezi kakuti What Happens to Us When We Die? kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

d Kuti mudziŵe zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za akufa ndi ciyembekezo cimene ali naco, onani nkhani 6 ndi 7 m’buku lakuti Zimene Baibulo Imaphunzitsa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani