LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 7/1 tsa. 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amatilimbikitsa Kupemphela?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 7/1 tsa. 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela?

Yehova Mulungu nthawi zonse amafuna kuti tizimuuza zinthu zimene zikutivutitsa. (Luka 18:1-7) Amamvetsela mapemphelo athu cifukwa amatikonda. Monga Atate wathu wakumwamba, akutipempha mokoma mtima kuti tizipemphela kwa iye, kungakhale kupanda nzelu kulephela kucita zimenezi.—Ŵelengani Afilipi 4:6.

Pemphelo si njila yongofuna kupempha thandizo. Koma limatithandiza kuyandikila kwa Mulungu. (Salimo 8:3, 4) Ngati nthawi zonse timuuza Mulungu zakukhosi kwathu, timakhala naye paubwenzi wolimba kwambili.—Ŵelengani Yakobo 4:8.

Tizipemphela bwanji?

Tikamapemphela, Mulungu safuna kuti tizigwilitsila nchito mau odzionetsela kapena kumangobweleza mapemphelo oloweza. Safunanso kuti popemphela tizitsatila kakhalidwe ka thupi kapadela. Yehova amafuna kuti tizipemphela kucokela mumtima. (Mateyu 6:7) Mwacitsanzo, kale m’nthawi ya Isiraeli, Hana anapemphela kwa Mulungu za vuto linalake lokhudza banja lake. Patapita nthawi, mavuto ake anatha ndipo anakhala wokondwela. Hana anayamikila Mulungu mwa kupemphela mocokela pansi pamtima.—Ŵelengani 1 Samueli 1:10, 12, 13, 26, 27; 2:1.

Pemphelo ndi mwai wapadela kwambili! Tingamuuze Mlengi mavuto athu amene tili nao. Tingamutamande ndi kumuyamikilanso cifukwa ca zinthu zimene amaticitila. Ndithudi, sitiyenela kunyalanyaza mwai wapadela kwambili umenewu.—Ŵelengani Salimo 145:14-16.

Kuti mudziŵe zambili, onani Nkhani 17 ya buku limene taonetsa pano Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mungalipeze pa www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani