LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/1 tsa. 4
  • Mulungu Amakuyang’anilani

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Amakuyang’anilani
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Amvetseleni, Adziŵeni Bwino, Aonetseni Cifundo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Nkhani ‘Yophiphilitsila’ Yokhala na Tanthauzo kwa Ife
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Mpaka Anakhala na Mwana Wake!
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/1 tsa. 4

NKHANI YA PACIKUTO-KODI MULUNGU AMACITA NANU CIDWI?

Mulungu Amakuyang’anilani

“Maso ake [Mulungu] amayang’anitsitsa njila za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse.”—YOBU 34:21.

CIFUKWA CAKE ENA AMAKAIKILA: Malinga ndi kafukufuku waposacedwapa, mlalang’amba wathu ukhoza kukhala ndi mapulaneti pafupifupi 100 biliyoni. Anthu ambili akaganizila kukula kwa cilengedwe conse, amakhala ndi funso lakuti, ‘N’cifukwa n’ciani Mlengi wamphamvuyonse amayang’anila zocita za anthu otsika amene ali pa kapulaneti kakang’ono?’

ZIMENE MAU A MULUNGU AMAPHUNZITSA: Mulungu sanangotipatsa Baibulo kenako n’kungotiiŵala. Komabe, iye amatitsimikizila kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.”—Salimo 32:8.

Ganizilani za Hagara, mzimai waciiguputo wa m’zaka za m’ma 1900 B.C.E. Hagara anali wopanda ulemu kwa womulemba nchito wake, Sarai. Cifukwa ca zimenezi, Sarai anamuthamangitsa ndipo Hagara anathaŵila kucipululu. Popeza Hagara analakwitsa, kodi Mulungu anamuiwala? Baibulo limati: ‘Mngelo wa Yehova anamupeza.’ Mngeloyo anatsimikizila Hagara kuti: “Yehova wamva kulila kwako.” Ndiyeno Hagara anati kwa Yehova: “Inu ndinu Mulungu amene amaona ciliconse.”—Genesis 16:4-13.

“Mulungu amene amaona ciliconse” amakuonani inunso. Mwacitsanzo: Mai wacikondi amasamalila bwino ana ake aang’ono, cifukwa mwana akakhala wamng’ono amafunikila kwambili makolo ake kumusamalila. Mofananamo, Mulungu amatisamalila kwambili makamaka pamene tavutika maganizo ndipo tifunika cisamalilo. Yehova akuti: “Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyela. Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzicepetsa, kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.”—Yesaya 57:15.

Ngakhale zili conco, mungafunse kuti: ‘Kodi Mulungu amandiyang’anila bwanji? Kodi amandiweluza malinga ndi maonekedwe anga, kapena amaona zoposa pamenepa ndipo amandimvetsa bwino kwambili?’

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani