NKHANI YA PACIKUTO | KODI MULUNGU AMACITA NANU CIDWI?
Mulungu Amakudziŵani
“Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziŵa.”—SALIMO 139:1.
CIFUKWA CAKE ENA AMAKAIKILA: Anthu ambili amaganiza kuti Mulungu amangowaona monga anthu ocimwa, odetsedwa ndi osafunikila kuwaŵelengela. Kendra amene anadwalako matenda a maganizo anadziimba mlandu kwambili cifukwa anali kuona kuti sanali kucita zonse zimene Mulungu amafuna. Cifukwa ca zimenezi, iye anati, “Ndinaleka kupemphela.”
ZIMENE MAU A MULUNGU AMAPHUNZITSA: Yehova samangoona kupanda ungwilo kwanu, iye amadziŵa mmene inuyo mulili. Baibulo limati: “Iye akudziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndife fumbi.” Kuonjezela pamenepa, iye“ sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu,” koma mwacifundo amatikhululukila tikalapa.—Salimo 103:10, 14.
Ganizilani Davide, mfumu ya Isiraeli amene tam’chula m’nkhani yoyamba ya nkhani zino. Popemphela kwa Mulungu, Davide anati: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu . . . Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziŵa mtima wanga.” (Salimo 139:16, 23) Conco, Davide anali wotsimikiza kuti ngakhale kuti anacimwa, ndipo nthawi zina anacita macimo aakulu, Yehova anaona kuti anali ndi mtima wolapa.
Yehova amakudziŵani bwino kwambili kuposa munthu wina aliyense. Baibulo limati: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Mulungu amadziŵa cifukwa cake mumacita zinthu mwanjila imeneyo. Iye amadziŵa mmene cibadwa canu, kukula kwanu, malo amene mumakhala ndi cikhalidwe canu zimakhudzila umunthu wanu. Mukamayesetsa kukhala munthu wabwino, iye amaona ndipo amayamikila ngakhale kuti nthawi zina mungalakwitse.
Komabe, kodi Mulungu amagwilitsila nchito bwanji zimene amadziŵa zokhudza inu kuti akuthandizeni?