CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 135-141
Tinapangidwa Modabwitsa
Davide anali kuganizila za umboni woonetsa makhalidwe abwino a Mulungu amene amaonekela m’zinthu zimene anapanga. Iye anaseŵenzetsa moyo wake kutumikila Yehova mokhulupilika.
Davide ataganizila kwambili za cilengedwe, anayamba kutamanda Yehova:
139:14
“Ndidzakutamandani cifukwa munandipanga modabwitsa”
139:15
“Mafupa anga sanali obisika kwa inu pamene munali kundipanga m’malo obisika, pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambili padziko lapansi”
139:16
“Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu”