Phunzilo 6
Salimo 139:14
Yang’ana zala zako zakumanja, ndipo nyang’anyitsa zala zako zakumiyendo.
Loza makutu ako ndi mphuno yako.
Ona miyendo imene imacititsa kuti uzithamanga, uzilumpha ndi kuti uzizungulila. Komanso kuti uzicita zinthu zosangalatsa!
Yang’ana pa kalilole, uonapo ciani?
Yehova anapanga zinthu zonse zokongola!
ZOCITA
Muŵelengeleni mwana wanu:
Salimo 139:14
Uzani mwana wanu kuti aloze:
Zala zakumanja Zala zakumiyendo Mphuno yake
Makutu ake Pakamwa pake
Pezani zinthu zobisika.
Nkhanu Cona (Pusi)
M’funseni mwana wanu:
Ndani analenga iwe ndi ine?
[Cithunzi 14]
[Cithunzi 15]
[Cithunzi 15]
[Cithunzi 16]