LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/1 tsa. 6
  • Mulungu Angakulimbikitseni

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Angakulimbikitseni
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Mulungu Amatitonthozela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse N’cifukwa Ciani ni Yamtengo Wapatali?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi N’zoona Kuti Yesu Ananifela Ine?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Mphatso Yopambana Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/1 tsa. 6

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MULUNGU AMACITA NANU CIDWI?

Mulungu Angakulimbikitseni

“Mulungu, amene amalimbikitsa osautsika mtima, anatilimbikitsa.”—2 AKORINTO 7:6.

CIFUKWA CAKE ENA AMAKAIKILA: Ngakhale pamene afunikila kwambili cilimbikitso, anthu ena amaona kuti ndi kudzikonda kupempha Mulungu kuti awathandize kupilila mavuto ao. Mkazi wina dzina lake Raquel anati: “Ndikaona mavuto aakulu amene anthu padziko lonse amakumana nao, zimandicititsa kuona kuti mavuto anga ndi ocepa kwambili cakuti ndimazengeleza kupempha Mulungu kuti andithandize.”

ZIMENE MAU A MULUNGU AMAPHUNZITSA: Mulungu wapeleka kale njila yabwino koposa pofuna kuthandiza ndi kulimbikitsa anthu. Munthu aliyense padziko lapansi anatengela ucimo umene umatilepheletsa kucita zonse zimene Mulungu amafuna. Komabe, Mulungu “anatikonda ndi kutumiza Mwana wake [Yesu Kristu] monga nsembe yophimba macimo athu.” (1 Yohane 4:10) Kudzela m’nsembe ya dipo ya Yesu, Mulungu anakonza zakuti tizikululukidwa macimo, tikhale ndi cikumbumtima coyela komanso ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko latsopano lamtendele.a Koma kodi nsembe imeneyo anangopatsa mtundu wonse wa anthu kapena imaonetsanso kuti Mulungu amacita cidwi ndi inuyo panokha?

Taganizilani mtumwi Paulo, iye anakhudzidwa kwambili ndi nsembe ya Yesu moti analemba kuti: “Ndikukhala mokhulupilila Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” (Agalatiya 2:20) N’zoona kuti Yesu anafa Paulo asanakhale Mkristu. Komabe, Paulo anaona nsembeyo ngati mphatso yake yopatsidwa ndi Mulungu.

Conco nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu wapeleka kwa inunso. Mphatso imeneyo imaonetsa kuti ndinu amtengo wapatali kwa Mulungu. Mphatso imeneyi ‘ingakulimbikitseni m’njila yosalephela ndiponso ingakupatseni ciyembekezo cabwino . . . kukulimbikitsani muntchito yabwino iliyonse ndiponso m’mau.’—2 Atesalonika 2:16, 17.

Koma Yesu anapeleka moyo wake monga nsembe pafupifupi zaka 2,000 zapitazo. Kodi pali umboni woonetsa kuti Mulungu afuna kuti inuyo mukhale naye paubwenzi?

a Kuti mudziŵe zambili zokhudza nsembe ya Yesu, onani nkhani 5 mu buku lakuti, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani