LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/1 tsa. 7
  • Mulungu Ndi Amene Amakukokani

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Ndi Amene Amakukokani
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Ziphunzitso Zoona Ponena za Mulungu ndi Ziti?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Pemphani Thandizo Kuti Mumvetsetse Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Kodi Mulungu amamvela bwanji akaona kuti muvutika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • N’cifukwa ciani timalalikila?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/1 tsa. 7

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MULUNGU AMACITA NANU CIDWI?

Mulungu Ndi Amene Amakukokani

“Palibe munthu angabwele kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate.”—YOHANE 6:44.

CIFUKWA CAKE ENA AMAKAIKILA: Anthu ambili amene amakhulupilila Mulungu amaona kuti iye ali patali ndi io. Mai wina wa ku Ireland, dzina lake Christina, amene anali kupita ku chalichi mlungu uliwonse anati: “Ndinali kuona Mulungu ngati amene analenga zinthu zonse cabe. Koma sindinali kum’dziŵa. Ndipo sindinamvepo kuti ndili pafupi naye.”

ZIMENE MAU A MULUNGU AMAPHUNZITSA: Ngakhale pamene tiona kuti tilibe thandizo lililonse, Yehova saleka kutithandiza. Yesu anafotokoza mwafanizo mmene Mulungu amatisamalila. Iye anati: “Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusocela, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phili ndi kupita kukafunafuna yosocelayo?” Kodi pali phunzilo lanji? “Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mateyu 18:12-14.

Aliyense “wa tianati” ndi wofunika kwambili kwa Mulungu. Kodi Mulungu amafunafuna bwanji munthu wosocelayo? Malinga ndi mau a lemba limene tagwila mau kumayambililo a nkhani ino, Yehova amakokela anthu kwa iye.

Ganizilani mmene Mulungu anacitilapo kanthu pofuna kukoka anthu oyenelela. M’zaka za zana loyamba, Mulungu anatuma wophunzila Filipo kukakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya ndi kukambitsilana naye tanthauzo la maulosi a m’Baibulo amene ndunayo inali kuŵelenga. (Machitidwe 8:26-39) Pambuyo pake, Mulungu anatsogolela mtumwi Petulo kukacezela kapitawo waciroma dzina lake Koneliyo amene anali kupemphela kwa Mulungu ndi kuyesetsa kum’lambila. (Machitidwe 10:1-48) Mulungu anatsogolelanso mtumwi Paulo ndi anzake ku mtsinje wina kunja kwa mzinda wa Filipi. Kumeneko, anakumana ndi mai wina “wolambila Mulungu” dzina lake Lidiya, ndipo “Yehova anatsegula kwambili mtima wake kuti achele khutu” ku zimene zinali kulankhulidwa.—Machitidwe 16:9-15.

M’zocitika zonsezi, taona kuti Yehova anaonetsetsa kuti onse amene anali kum’funafuna anakhala ndi mwai wom’dziŵa. Kodi ndani masiku ano amene amapita ku makomo a anthu ndi kumalo ena kumene kumapezeka anthu kufalitsa uthenga wa m’Baibulo wonena za Mulungu? Anthu ambili angayankhe kuti, “ndi Mboni za Yehova.” Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi n’kutheka kuti Mulungu akugwilitsila nchito anthu amenewa kuti andithandize?’ Tikukulimbikitsani kupemphela kwa Mulungu kuti akuthandizeni kumvela pamene iye akukukokani.a

a Kuti mudziŵe zambili, onelelani vidiyo yakuti, N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? Pa www.jw.org/nya

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani