Zamkati
3 Mbili Yanga Kusiilana Citsanzo Cabwino
MLUNGU WA NOVEMBER 28, 2016–DECEMBER 4, 2016
MLUNGU WA DECEMBER 5-11, 2016
13 Khalanibe Auzimu Potumikila Mumpingo wa Cinenelo Cina
Masiku ano, m’mipingo yathu muli anthu a mitundu yosiyana-siyana ndiponso a kumaiko ena. Nkhani yoyamba idzatithandiza kudziŵa mmene tingaonetsele cikondi ceni-ceni kwa anthu a kumaiko ena amene amasonkhana nafe. Nkhani yaciŵili ifotokoza zimene anthu otumikila mumpingo wa cinenelo cina angacite kuti akhalebe auzimu.
18 Kodi ‘Mumasunga Nzelu Zopindulitsa’?
MLUNGU WA DECEMBER 12-18, 2016
21 Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene Muyembekezela
MLUNGU WA DECEMBER 19-25, 2016
26 Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova
Nkhani zimenezi zifotokoza bwino mbali ziŵili za cikhulupililo zofotokozedwa pa Aheberi 11:1. Nkhani yoyamba ionetsa mmene cikhulupililo cingakulile na kukhalabe colimba. Nkhani yaciŵili ifotokoza cifukwa cake cikhulupililo si kumvetsetsa cabe madalitso amene Yehova adzatipatsa.