MBILI YANGA
Kusiilana Citsanzo Cabwino
“Mwati mudziŵa zaka zanga,”? n’nafunsa Izak Marais. Anayankha kuti: “Inde nidziŵa bwino-bwino,” pamene anali kutuma foni anali mu Colorado ku Patterson ku America. Lekani nifotokoze cimene cinayambitsa makambilano amenewa.
N’NABADWA pa 10 December mu 1936, ku Wichita ku Kansas mu America. Ndine woyamba pa ana 4. Makolo anga a William ndi a Jean anali kulambila Yehova modzipeleka. Atate anali mtumiki wa mpingo (dzina lakale la mgwilizanitsi). Amayi anaphunzila coonadi kwa amayi awo a Emma Wagner. Ambuya anga amenewa anaphunzitsa anthu ambili coonadi, kuphatikizapo Gertrude Steele, amene anatumikila monga mmishonale kwa zaka zambili ku Puerto Rico.a Conco, n’nali na zitsanzo zabwino zambili zimene ningatengele.
KUKUMBUKILA ZITSANZO ZABWINO
Atate ataimilila pa kona m’mbali mwa mumseu, akugaŵila magazini kwa anthu opita
Ciŵelu cina madzulo, apo nili na zaka 5, ine na atate tinali kugaŵila Nsanja ya Mlonda ndi Consolation (imene tsopano imachedwa Galamukani!) kwa anthu opita mu mseu. Panthawiyo m’dzikolo munali Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Panabwela dokota wina amene anali woledzela. Iye anayamba kunyoza atate cifukwa cosatengako mbali m’nkhondo. Anawanena kuti anali munthu wa mantha ndi wothaŵa usilikali. Iye anawayang’ana pamaso n’kukamba kuti, “Nimenye iwe cimunthu camantha!” N’nayopa kwambili koma n’nacita cidwi na zimene Atate anacita. Iwo anangopitiliza kugaŵila magazini anthu amene anali kutamba zimene zinali kucitika. Ndiyeno panafika msilikali, ndipo dokota ameneyo anakuwa kuuza msilikali kuti, “Cigwile ici cimunthu ca mantha!” Msilikaliyo anazindikila kuti dokotayo anali woledzela, conco anamuuza kuti “Yenda kunyumba ukhale bwino coyamba!” Onse anapita. Nikakumbukila izi, nimayamikila kuti Yehova anathandiza atate kulimba mtima. Iwo anali ndi ma babashopu aŵili m’tauni ya Wichita ndipo dokota ameneyo anali kasitoma wawo.
Pamene n’nali na zaka 8, makolo anga anagulitsa nyumba na mashopu awo, n’kupanga nyumba yamawilo (kalavani) imene tinali kuyenda nayo. Pambuyo pake, tinasamukila ku Colorado kukatumikila kosoŵa. Tinayamba kukhala pafupi na mzinda wa Grand Junction. Kumeneko makolo anga anali kucita upainiya komanso anali kuseŵenza kwa maola ocepa pa famu. Ndi dalitso la Yehova pamodzi na khama lawo panchito yolalikila, anakhazikitsa mpingo. Mu 1948 pa 20 June, Atate ananibatiza pamodzi ndi ena amene anaphunzila coonadi mu mtsinje wina kumbali kwa phili. Billie Nichols na mkazi wake anali ena mwa anthu amene n’nabatizika nawo. Patapita nthawi, Billie Nichols na mkazi wake anakhala wadela, ndipo mwana wawo ndi mkazi wake anadzakhalanso wadela.
Nili na makolo anga, tikuyenda ku msonkhano ku Wichita ca m’ma 1940
Tinali kugwilizana kwambili ndi atumiki a nthawi zonse, maka-maka a m’banja la Steele—Don ndi Earlene, Dave ndi Julia, komanso Si ndi Martha. Tinali kukambilana kwambili zinthu zauzimu ndipo ananilimbikitsa ngako. Ananionetsa mmene kuika zinthu za Ufumu patsogolo kumabweletsela madalitso na cimwemwe mu umoyo wa munthu.
KUSAMUKANSO
Pamene n’nali na zaka 19, Bud Hasty amene anali kugwilizana kwambili na banja lathu, ananipempha kuti niyambe kucita naye upainiya kum’mwela kwa America. Wadela anatipempha kuti tisamukile ku Ruston, mu mzinda wa Louisiana kumene Mboni zambili zinali zozilala. Anatiuza kuti tizicita misonkhano yonse mlungu uliwonse ngakhale kupezeke anthu ocepa. Tinapeza malo abwino osonkhanilapo na kuwakonza. Tinali kucita misonkhano yonse, koma kwa kanthawi tinali kupezekapo anthu aŵili cabe. Tinali kusinthana-sinthana pocita mbali za misonkhano, wina atsogoza wina ayankha mafunso. Ikakhala mbali ya citsanzo, tonse tinali kuyenda kupulatifomu popanda omvetsela. M’kupita kwa nthawi, mlongo wacikulile anayamba kupezekapo. Ndiyeno, ophunzila Baibo ndi ena ozilala nawonso anayamba kufika. M’nthawi yocepa kunakhadzikitsidwa mpingo wocita bwino.
Tsiku lina ine ndi Bud tinakumana na m’busa wa cipembedzo ca Church of Christ. Iye anakamba za malemba amene sin’nali kuwadziŵa bwino. N’nacita mantha pang’ono, ndiyeno n’naganizila mozama zinthu zimene nimakhulupilila. Kwa mlungu wonse n’nacezela kufufuza mayankho a mafunso amene ananifunsa. Zimenezi zinanithandiza kutenga coonadi kukhala canga, ndipo n’nali kulakalaka kukumana ndi m’busa wina.
Pambuyo pake, wadela ananipempha kusamukila ku Arkansas kukathandiza mpingo wa El Dorado. Nili kumeneko n’napita kaŵili-kaŵili ku Colorado kukaonekela kwa anthu amene amasankha anyamata oyenda ku nkhondo. Pa ulendo wina, apainiya anzanga ananipelekeza ndipo tinayendela m’motoka yanga. M’kati mwa ulendowo, tinacita ngozi mu Texas cakuti motoka yanga inawonongekelatu. Tinatumila foni m’bale wina amene anabwela ndi kutipeleka ku nyumba kwake na kumisonkhano ya mpingo. Kumeneko analengeza zakuti tinacita ngozi, ndipo abale mokoma mtima anatipatsa ndalama. M’baleyo ananigulitsilanso motoka ija pamtengo wa madola 25.
Tinakwanitsa kupeza thilansipoti yotipeleka ku Wichita, kumene m’bale E. F. “Doc” McCartney anali kucitila upainiya. Iwo anali kumvelana kwambili na banja lathu. Ana ake aŵili Frank ndi Francis ni amphundu ndipo ni anzanga apamtima. Anali ndi motoka yakale imene ananigulitsa madola 25, ndendende ndalama imene n’nagulitsa motoka ija yowonongeka. Iyi ndiyo inali nthawi yoyamba kuona dalitso la Yehova cifukwa coika zinthu za Ufumu patsogolo. Pa ulendo umenewu McCartney ananidziŵikitsa kwa mtsikana wina wauzimu, Bethel Crane. A Ruth amayi ake, anali Mboni yokangalika mu Wellington, ku Kansas. Iwo anapitiliza kucita upainiya ngakhale atafika zaka za m’ma 90. N’namanga banja ndi Bethel pasanapite caka cimodzi mu 1958, ndipo tinapitiliza kucita upainiya mu El Dorado.
ZIITANO ZOKONDWELETSA
Pambuyo polimbikitsidwa ndi anthu a zitsanzo zabwino amene tinali kudziŵa, tinadzipeleka kuti ticite ciliconse cimene gulu la Yehova lidzatipempha kucita. Tinatumidwa kukacita upainiya wapadela ku tauni ya Walnut Ridge ku Arkansas. Mu 1962, tinakondwela kwambili titaitanidwa ku sukulu ya Giliyadi ya namba 37. Tinakondwela kwambili kukhala mu kilasi imodzi na Don Steele. Titatsiliza maphunzilo ine na Bethel tinatumidwa ku Nairobi, ku dziko la Kenya. Tinali na nkhawa kwambili pamene tinali kucoka ku America, koma nkhawa yonse inasanduka cisangalalalo pamene abale a ku Nairobi anatilandila pa eyapoti.
Tili mu ulaliki na Mary ndi Chris Kanaiya
Posapita nthawi tinayamba kukonda dziko la Kenya ndi utumiki wathu. Phunzilo loyamba kupita patsogolo anali Chris na Mary Kanaiya. Iwo akali mu utumiki wa nthawi zonse ku Kenya. Caka cotsatila, tinauzidwa kukatumikila ku Kampala ku dziko la Uganda, ndipo tinali amishonale oyamba kumeneko. Nthawi imeneyi inali yosangalatsa cifukwa anthu ambili anali ofunitsitsa kuphunzila coonadi, ndipo anakhala Mboni. Komabe, titakhala zaka zitatu na hafu mu Africa, tinabwelela ku America kuti tikayambe udindo wolela ana athu. Pocoka ku Africa tinali ndi nkhawa kwambili kuposa pocoka ku America. Tinafika powakonda ngako anthu a mu Africa moti tinali ofunitsitsa kukabwelanso.
TINALANDILA UDINDO WATSOPANO
Titafika ku America, tinayamba kukhala kumadzulo kwa mzinda wa Colorado kumene makolo anga anali kukhala. Ndiyeno, mwana wathu woyamba wamkazi Kimberly anabadwa. Patapita miyezi 17, Stephany anabadwa. Udindo wathu waukholo tinaulandila ndi manja aŵili ndipo tinali okonzeka kukhomeleza coonadi mwa ana athu okondeka. Tinali kufuna kusiila ana athu zitsanzo zabwino zimene tinatengela kwa ena. Zinali zokhumudwitsa kuona kuti ana ena amaleka kutumikila Yehova ngakhale kuti pali zitsanzo zabwino kwambili zimene angatengele. Mwacitsanzo, ang’ono anga aŵili anasiya coonadi. Tingasangalale kuwaona atatengelanso zitsanzo zabwino.
Tinasangalala kwambili polela ana athu ndipo tinali kuyesetsa kucitila zinthu pamodzi nthawi zonse. Popeza tinali kukhala mu Colorado pafupi na malo ocitila maseŵela osheleleka pa aisi, tinaphunzila maseŵela amenewa kuti tiziseŵelela pamodzi monga banja. Pocita maseŵelawo, tinali kukambilana ndi ana athu. Tinalinso kuyenda nawo kumalo okaceza ndi kukagona m’matenti, tikumaceza pootha moto. Olo kuti anawo anali aang’ono, anali kufunsa mafunso monga akuti, “Nikacite ciani nikadzakula? Nanga ni mwamuna wabwanji amene afunika kunikwatila?” Tinayesetsa kukhomeleza mfundo za m’Baibo m’maganizo ndi m’mitima mwawo. Tinawathandiza kukhala na zolinga zoyamba utumiki wa nthawi zonse ndi ubwino womanga banja na munthu wofanana naye zolinga. Tinayetsesa kuwathandiza kudziŵa ubwino wopewa kukwatiwa akali aang’ono. Pali mau ena amene tinali kukonda kukamba akuti “Khala mbeta mpaka utakwanitsa zaka 23.”
Monga mmene makolo athu anacitila, tinacita zomwe tingathe kuti tizipezeka pamisonkhano ndi muulaliki nthawi zonse monga banja. Tinapanga makonzedwe akuti atumiki ena a nthawi zonse tiziwalandilako kunyumba kwathu. Komanso tinali kuwauza mmene tinali kukondela utumiki wa umishonale. Tinawauzanso kuti timalakalaka kuti tonse 4 tikapite kukayenda ku Africa. Ana athu anali ofunitsitsa kukaonako.
Nthawi zonse tinali kucita phunzilo la banja lotsatilika, ndipo tinali kuyelekezela zinthu zimene zingacitike kusukulu. Tinali kuuza atsikana athu kuyelekezela kuti ni Mboni imene ikuyankha mafunso. Anali kusangalala kuphunzila mwa njila imeneyi ndipo zinawathandiza kulimba mtima. Pamene anali kukula, nthawi zina anali kudandaula cifukwa cocita phunzilo la banja. Tsiku lina, mokhumudwa ninawauza kuti sitidzaphunzila apite kucipinda cawo akagone. Anawo anadabwa kwambili ndipo anayamba kulila na kukamba kuti afuna tiphunzile. Pamenepa tinazindikila kuti tinalidi kukhomeleza mfundo za coonadi m’mitima ya ana athu. Iwo anayamba kukonda kwambili phunzilo la banja, ndipo tinali kuwalola kufotokoza maganizo awo momasuka. Nthawi zina, sitinali kumvela bwino mumtima tikamvela ana athu akukamba kuti sakhulupilila mfundo zina za coonadi. Koma zinatithandiza kudziŵa zimene zinali m’mitima yawo. Pambuyo pokambilana nawo mfundo za m’malemba, anali kukhutila akadziŵa mmene Yehova amaonela zinthu.
MASINTHIDWE ENA
Nchito yathu yolela ana inaoneka kutha mwamsanga pamene iwo anakula na kucoka pakhomo. Potsatila malangizo a gulu la Mulungu tinakwanitsa kuthandiza ana athu kukonda Yehova. Kukamba zoona, tinakondwela maningi onse aŵili atayamba upainiya pambuyo potsiliza sukulu. Kuwonjezela apo anakhalanso na maluso ena owathandiza kuti azidzisamalila mwa kuthupi. Ndiyeno, anasamukila mu mzinda wa Cleveland, ku Tennessee pamodzi na alongo ena kukatumikila kosoŵa. Tinaŵayewa kwambili koma tinakondwela kuona kuti asankha kuseŵenzetsa umoyo wawo kucita utumiki wa nthawi zonse. Ndipo ine ndi Bethel tinayambanso upainiya ndipo unacititsa kuti tilandilenso mwayi wina wa utumiki. Tinali kutumikila monga woyang’anila dela wogwilizila ndi kucititsa misonkhano ikulu-ikulu.
Koma akalibe kuyenda ku Tennessee, atsikana athu anapanga ulendo wokaceza ku Beteli ya ku London m’dziko la England. Kumeneko, Stephany amene panthawiyo anali na zaka 19 anakumana ndi Paul Norton mtumiki wa pa Beteli wacicepele. Paulendo wina, Kimberly anakumana ndi mnzake wa Paul dzina lake Brian Llewellyn. M’kupita kwa nthawi Paul na Stephany anamanga banja pambuyo pokwanitsa zaka 23. Caka cotsatila, Brian na Kimberly anamanga banja, apo Kimberly anali na zaka 25. Conco, anakhaladi mbeta mpaka atakwanitsa zaka 23. Ndipo tinawakonda na mtima onse anyamata amene anasankha kuti amange nawo banja.
Tili na Paul, Stephany, Kimberly, na Brian pa ofesi ya nthambi ku Malawi mu 2002
Atsikana athu anatiuza kuti citsanzo cimene ise ndi ambuye awo tinawaonetsa cinawathandiza kumvela lamulo la Yesu lakuti, “pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba,” ngakhale pamene akumana na vuto la ndalama. (Mat. 6:33) Mu April 1998, Paul na Stephany anaitanidwa ku Sukulu ya Giliyadi ya namba 105. Atatsiliza maphunzilo amenewo anatumidwa kukatumikila ku Malawi mu Africa. Panthawi imodzi-modzi, Brian na Kimberly anaitanidwa kukatumikila pa Beteli ya ku London. Patapita nthawi, anatumidwa kukatumikila ku Beteli ya ku Malawi. Kukamba zoona, tinakondwela kwambili, cifukwa palibe njila ina yabwino imene acicepele angagwilitsile nchito umoyo wawo kuposa imeneyi.
CIITANO CINA COKONDWELETSA
Mu January 2001, ndiye pamene ananitumila foni imene nakamba kuciyambi kwa nkhani ino. M’bale Marais woyang’anila nchito yomasulila, anafotokoza kuti abale anali kukonza zoti pakhale kosi yophunzitsa Cizungu omasulila onse padziko lonse. N’nali na zaka 64, koma ananipempha kuti nikhale mmodzi wa aphunzitsi a kosi imeneyo. Tinaipemphelela nkhaniyi ndi mkazi wanga, ndipo tinakambilana ndi makolo athu okalamba kuti timvele maganizo awo. Onse anali kufuna kuti tipite ngakhale kuti zikanativuta kuwasamalila tili kutali. N’natumanso foni kwa m’bale Marais kumuuza kuti ndife okonzeka kucita utumiki wapadela umenewu.
Mwa tsoka lanji, amayi anapezeka na matenda a khansa. Ninawauza kuti sitidzapita kuti tizithandiza mlongosi wanga Linda kuwasamalila. “Usayese kucita zimenezo. Cidzaniŵaŵa maningi ngati sudzayenda,” anatelo Amayi. Linda nayenso anakamba cimodzi-modzi. Tinayamikila kwambili mzimu wawo wodzipeleka ndiponso thandizo la anzathu a kumalo kumeneko. Tsiku lotsatila, pambuyo popita ku Likulu la Maphunzilo la Watchtower ku Patterson, Linda anatuma foni kutiuza kuti Amayi amwalila. Koma tinasankha kuika maganizo athu pa nchito yatsopano monga mmene amayi akanafunila.
Utumiki woyamba, anatituma ku ofesi ya nthambi ya ku Malawi kumene ana athu ndi amuna awo anali kutumikila. Tinakondwela kwambili kuonananso monga banja. Ndiyeno, tinayenda kuphunzitsa ku Zimbabwe ndi ku Zambia. Pambuyo pophunzitsa kosi imeneyi kwa zaka zitatu na hafu, anatiuza kuti tibwelele ku Malawi kuti tikalembe zokumana nazo za Mboni zimene zinazunzidwa cifukwa cosatengako mbali m’nkhondo.b
Tili mu ulaliki na adzukulu athu
Mu 2005, tinabwelela kwathu ku Basalt, ku Colorado. Apanso tinali na nkhawa kwambili. Ine na Bethel tikupitiliza kucita upainiya kuno. Ndiyeno mu 2006, Brian na Kimberly anabwela kuno kudzalela ana awo akazi aŵili, Mackenzie na Elizabeth. Koma Paul na Stephany akali ku Malawi kumene Paul akutumikila mu Komiti ya Nthambi. Popeza posacedwa nidzakwanitsa zaka 80, nimakondwela kuona anyamata amene n’nathandizila zaka zakumbuyo akutumikila pa maudindo amene n’nali kutumikila. Tili na cimwemwe cifukwa ca zitsanzo zabwino zimene anatisiila, ndiponso cifukwa ca citsanzo cabwino cimene tayesetsa kusiila ana ndi adzukulu athu.
a Onani Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya May 1, 1956, masa. 269-272, na ya March 15, 1971, masa. 186-190, kuti mudziŵe za nchito ya umishonale ya banja la Steele.
b Mwacitsanzo, onani mbili ya moyo wa m’bale Trophim Nsomba mu Nsanja ya Mlonda ya April 15, 2015, masa. 14-18.