Zida zonse zankhondo zidzawonongewa
Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Kodi zidzatheka kuti padzikoli pakhale mtendele?
Kodi mungayankhe bwanji?
Inde
Iyai
Kapena
Zimene Baibo imakamba
Mu ulamulilo wa Yesu Khristu, “padzakhala mtendele woculuka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo,” kutanthauza kwamuyaya.—Salimo 72:7.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Anthu oipa adzacotsedwa padziko lapansi, koma anthu abwino “adzasangalala ndi mtendele woculuka.” —Salimo 37:10, 11.
Mulungu adzathetsa nkhondo zonse.—Salimo 46:8, 9.
Kodi n’zotheka kukhala na mtendele weni-weni wa m’maganizo lomba?
Anthu ena amakhulupilila kuti . . .
n’zosatheka kukhala na mtendele weni-weni wa m’maganizo m’dziko lino lodzala ndi mavuto na kupanda cilungamo. Nanga imwe muganiza bwanji?
Zimene Baibo imakamba
Ngakhale lomba, anthu amene ni mabwenzi a Mulungu angakhale na “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:6, 7.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Mulungu analonjeza kuti adzacotsapo mavuto na kupanda cilungamo. Adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.—Chivumbulutso 21:4, 5.
Tingakhale na mtendele wa m’maganizo ngati tisamalila ‘zosoŵa zathu zauzimu.’—Mateyu 5:3.