Kukhalabe Bwenzi Pakacitika Zinthu Zimene Zingasokoneze Ubwenzi
Gianni ndi Maurizio akhala mabwenzi kwa zaka pafupi-fupi 50. Komabe, panthawi ina ubwenzi wawo unatsala pang’ono kusokonezeka. Maurizio anafotokoza kuti: “Pa nthawi ina, n’nacita zolakwa zazikulu zimene zinacititsa kuti ine na mnzanga tisamagwilizanenso.” Nayenso Gianni anati: “Maurizio ndiye anali woyamba kuniphunzitsa Baibo. Kwa nthawi yaitali, iye anali kunithandiza ndi kunipatsa malangizo pa zinthu zauzimu. Conco, sin’nakhulupilile zimene anacita. N’nali na nkhawa cifukwa n’naona kuti ubwenzi wathu tsopano udzatha. Ndipo n’naona monga kuti natayika.”
MABWENZI abwino ni ofunika, ndipo pamafunika khama kuti ubwenzi ukhale wolimba. Ngati pacitika zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wanu, n’ciani cingakuthandizeni kuupulumutsa? Tingaphunzile zambili kwa anthu ochulidwa m’Baibo amene anali mabwenzi eni-eni, koma amene panthawi ina, ubwenzi wawo unali paciopsezo.
PAMENE MNZATHU WALAKWITSA CINACAKE
Davide, amene anali m’busa komanso mfumu, anali ndi mabwenzi abwino. Mwina tingakumbukile kuti mmodzi wa mabwenziwo anali Yonatani. (1 Sam. 18:1) Koma Davide analinso ndi anzake ena monga mneneli Natani. Baibo siikamba nthawi imene ubwenzi wawo unayamba. Komabe, panthawi ina, Davide anauza Natani za mumtima mwake monga mmene inu mungauzile mnzanu zakukhosi kwanu. Davide anali kulakalaka kumanga nyumba ya Yehova. Mfumuyo iyenela kuti inali yokonzeka kutsatila malangizo a Natani amene anali mnzake komanso munthu amene anali ndi mzimu wa Yehova.—2 Sam. 7:2, 3.
Komabe, panacitika zinazake zimene zikanasokoneza ubwenzi wawo. Mfumu Davide anacita cigololo ndi Batiseba. Pambuyo pake, anaphetsa Uriya, mwamuna wake. (2 Sam. 11:2-21) Kwa zaka zambili, Davide anali wokhulupilika kwa Yehova ndipo anali kucita zinthu mwacilungamo. Koma panthawiyi anacita chimo loopsa. N’ciani cinacititsa mfumu yabwino imeneyi kucita zimenezi? Kodi sanaone kuopsa kwa zimene anacita? Kodi anaganiza kuti Mulungu sadzaona zimene anacitazo?
Kodi Natani anacita ciani? Kodi anangokhala cete n’kuyembekezela kuti munthu wina adzapita kwa mfumu kukakamba nayo za colakwa cake? Anthu ena anali kudziŵa za ciŵembu cimene Davide anakonza kuti Uriya aphedwe. Ndiye kodi kuloŵelelapo pankhaniyi sikukanangopangitsa kuti Natani asokoneze ubwenzi wake ndi Davide, umene unakhalapo kwa nthawi yaitali? Komanso kucita zimenezo kukanaika moyo wa Natani paciopsezo. Kumbukilani kuti panthawiyi, Davide anali atapha kale Uriya, munthu wosalakwa.
Koma Natani pokhala mneneli wa Mulungu, anadziŵa kuti ngati sakamba kalikonse, cidzakhala comuvuta kupitiliza ubwenzi ndi Davide, ndipo cikumbumtima cake cidzamuvutitsa kwambili. Bwenzi lake Davide anacita zinthu zimene zinakhumudwitsa Yehova. Mfumuyo inafunikila kwambili thandizo la munthu wina kuti ibwelele pa njila yoyenela. Inde, Davide anafunikadi mnzake weni-weni. Ndipo Natani ndiye mnzake amene Davide anafunikila panthawiyi. Natani anayamba kukamba mwafanizo chimo limene Davide anacita. Fanizolo linamukhudza mtima Davide cifukwa iye anali m’busa panthawi ina. Natani anapeleka uthenga wa Mulungu kwa Davide. Koma anaufotokoza mwa njila imene inam’thandiza kuzindikila chimo lake ndi kucitapo kanthu.—2 Sam. 12:1-14.
Kodi inu mungacite ciani ngati mnzanu wacita colakwa cacikulu kapena chimo lalikulu? Mwina munganize kuti kukambapo pa colakwaco kudzawononga ubwenzi wanu. Mwinanso mungaganize kuti kuuza akulu za chimolo kuti am’thandize, kungaoneke ngati kusakhulupilika kwa mnzanuyo. Kodi mungacite ciani?
Gianni, amene tamuchula poyamba paja, anakamba kuti: “N’nazindikila kuti zina-zake zasintha. Maurizio sanali kunimasukila mmene anali kucitila poyamba. Conco, n’naganiza zopita kukakamba naye ngakhale kuti zinali zovuta. N’nadzifunsa kuti: ‘Nidzamuuza ciani pakuti zonse azidziŵa kale? Nanga bwanji ngati sakaniyankha bwino?’ Koma kukumbukila zimene tinaphunzila pamodzi kunanithandiza kuti nilimbe mtima n’kupita kukakamba naye. Maurizio nayenso ananithandiza pa nthawi imene ine n’nali kufunikila thandizo. Sin’nali kufuna kuti ubwenzi wathu uthe. Koma n’nali kufuna kumuthandiza cifukwa nimamukonda.”
Maurizio anati: “Gianni anali kukamba nane moona mtima ndipo anali kucita bwino. N’nadziŵa kuti mnzangayo kapena Yehova sindiwo anacititsa mavuto amene n’nali kukumana nawo. Koma anayamba cifukwa sin’nasankhe bwino zocita. Conco n’nalandila uphungu ndipo m’kupita kwa nthawi, n’nayambanso kucita bwino mwauzimu.”
PAMENE MNZATHU WAKUMANA NDI VUTO
Davide analinso ndi anzake ena okhulupilika amene anakhala kumbali yake panthawi yovuta. Mmodzi wa anzakewo anali Husai, amene Baibo limati anali “mnzake wa Davide.” (2 Sam. 16:16; 1 Mbiri 27:33) Iye ayenela kuti anali nduna ya panyumba ya mfumu komanso mnzake wa mfumuyo. Anali kum’tumanso pa nkhani zina zacinsinsi.
Pamene Abisalomu analanda ufumu Davide bambo ake, Aisiraeli ambili anakhala kumbali ya Abisalomu. Koma Husai sanatelo. Panthawi imene Davide anali kuthawa, Husai anapita kwa iye. Davide anakhumudwa kwambili cifukwa ca kusakhulupilika kwa mwana wake komanso anthu ena amene anali kuwadalila. Koma Husai anakhalabe wokhulupilika ndipo anali wokonzeka kuika moyo wake paciopsezo kuti alepheletse ciŵembu cimene Abisalomu anakonza. Husai sanangocita zimenezo n’colinga cakuti akwanilitse udindo wake monga nduna ya panyumba ya mfumu, koma cifukwa anali mnzake wokhulupilika wa Davide.—2 Sam. 15:13-17, 32-37; 16:15–17:16.
Masiku anonso, n’zolimbikitsa kuona kuti abale ndi alongo m’mipingo ndi ogwilizana mosasamala kanthu za kusiyana kwa mautumiki kapena udindo. Zocita zawo zimaonetsa kuti ubwenzi wawo ndi wozikidwa pa cikondi osati pa udindo kapena utumiki wawo.
Izi n’zimene zinacitikila m’bale wina dzina lake Federico. Iye anathandizidwa ndi mnzake Antonio, panthawi imene zinthu zinali zovuta pa umoyo wake. Federico anati: “Antonio atasamukila mumpingo wathu, tinayamba kugwilizana kwambili. Tonse tinali atumiki othandiza ndipo tinali kusangalala kutumikila pamodzi. Patangopita nthawi yocepa, Antonio anakhala mkulu. Kuwonjezela pa kukhala mnzanga, iye analinso citsanzo cabwino kwa ine pa zinthu zauzimu.” Kenako, Federico anacita chimo. Mwansanga iye anakapempha thandizo kwa akulu. Koma sanalinso woyenelela kukhala mpainiya kapena mtumiki wothandiza. Kodi Antonio anacita ciani?
Federico atakumana ndi vuto, mnzake Antonio anamumvetsela ndi kumulimbikitsa
Federico anati: “Antonio ananimvela cisoni. Anayesetsa kunilimbikitsa. Anali kufuna kunithandiza kuti nikonzenso ubwenzi wanga na Mulungu ndipo sananisiye. Ananithandiza kuti nipezenso mphamvu mwauzimu ndi kuti nisafooke.” Nayenso Antonio anati: “N’nali kuceza naye kaŵili-kaŵili Federico. N’nali kufuna kuti azikhala womasuka kukamba nane ciliconse, kuphatikizapo mmene anali kumvelela mu mtima.” Cokondweletsa n’cakuti m’kupita kwa nthawi, Federico anakhalanso wolimba kuuzimu, ndipo pambuyo pake anayambanso kutumikila monga mpainiya ndi mtumiki wothandiza. Pomaliza, Antonio anati: “Ngakhale kuti titumikila ku mipingo yosiyana, timakondana kwambili kuposa kale.”
KODI MUDZAKHUMUDWA?
Kodi mungamvele bwanji ngati mnzanu wapamtima wakulekelelani pamene mwakumana ndi vuto lalikulu? Mwacionekele zingakuŵaŵeni kwambili. Kodi mungathe kumukhululukila? Ngati mwamukhulukila, kodi ubwenzi wanu ungakhalebe wolimba monga mmene unalili poyamba?
Ganizilani zimene zinacitikila Yesu pa nthawi imene anatsala pang’ono kucoka padziko lapansi. Iye anali kuceza kwambili na atumwi ake okhulupilika, ndipo anali kugwilizana nawo mwapadela. N’cifukwa cake Yesu anawacha mabwenzi. (Yoh. 15:15) Komabe, kodi n’ciani cinacitika Yesu atamangidwa? Atumwiwo anamuthaŵa. Petulo anacita kulengeza poyela kuti sadzasiya Mbuye wake, koma tsiku limenelo usiku, anakana Yesu kuti samudziŵa.—Mat. 26:31-33, 56, 69-75.
Yesu anadziŵa kuti paciyeso comaliza, sadzafunika kudalila anthu ena. Ngakhale n’conco, iye akanakhumudwa poona anzake akum’thawa. Koma pokambilana ndi ophunzila ake, iye sanaonetsa kuti anali wokhumudwa kapena wowawidwa mtima ngakhale pang’ono. Yesu sanakumbutse ophunzila ake zolakwa zawo, ngakhale zimene iwo anacita pamene iye anamangidwa.
M’malomwake, Yesu anatsimikizila Petulo ndi atumwi ena kuti amawadalila. Anaonetsa kuti amawadalila mwa kuwapatsa malangizo okhudza nchito yofunika kwambili yophunzitsa anthu. Yesu anali kuonabe atumwiwo kukhala mabwenzi ake. Cikondi cimene iye anawaonetsa sanaciiŵale. Iwo anayesetsa kucita zimene akanatha kuti asakhumudwitse Mbuye wawo. Kunena zoona, iwo anacita zonse zimene Yesu anauza otsatila ake kucita.—Mac. 1:8; Akol. 1:23.
Mlongo wina dzina lake Elvira akumbukila bwino zimene zinacitika atasiyana maganizo na mnzake Giuliana. Elvira anati: “Pamene iye ananiuza kuti zimene nacita zamukhumudwitsa, n’nadziimba mlandu. Zinali zomveka iye kukhumudwa. Koma cimene cinanicititsa cidwi n’cakuti anali kunidela nkhawa kwambili. Ndipo anacita zimenezo cifukwa anaona kuti khalidwe langa lidzanibwetsela mavuto. Nthawi zonse nimayamikila kuti iye sanaike maganizo ake pa colakwa cimene ine n’namucitila, koma anali kufuna kunithandiza kuti nisakumane na mavuto. N’nayamikila Yehova cifukwa conipatsa mnzanga amene amanifunila zabwino.”
Malinga n’zimene taona, kodi bwenzi labwino limacita ciani ngati pacitika zinthu zina zimene zingawononge ubwenzi wawo? Bwenzi labwino limakambilana ndi mnzake mokoma mtima ndi momasuka. Bwenzi laconco lili ngati Natani ndi Husai, amene anakhalabe okhulupilika ngakhale pa nthawi yovuta. Ndiponso bwenzi lotelo lingafanane ndi Yesu, amene anali wofunitsitsa kukhululuka. Kodi inu ndinu bwenzi laconco?