Kodi Cidzacokapo N’ciani Ufumu wa Mulungu Ukadzabwela?
“Dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake, koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.”—1 YOH. 2:17.
1, 2. (a) N’cifukwa ciani dzikoli lili ngati cigaŵenga cimene cipita kukanyongedwa? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Kodi aliyense adzamvela bwanji dzikoli likadzawonongedwa?
“MTEMBO WOYENDA!” Umu ndi mmene asilikali ena olondela ndende anali kuitanila cigaŵenga coopsa pocitulutsa m’ndende kwinaku akutseka citseko ca ndendeyo. Alondawo anali kukamba zimenezo ngakhale kuti munthuyo anali kuoneka wathanzi ndithu, wosadwala. Nanga n’cifukwa ciani anali kukamba conco? Cifukwa cakuti anali kupita naye kumalo okamunyongela. Conco, ngakhale kuti munthuyo anali wamoyo, anali ngati mtembo cifukwa anaweluzidwa kuti anyongedwe.a
2 Tingakambe kuti dzikoli lili ngati munthu wopita kukanyongedwa ameneyu. Dziko loipali linaŵeluzidwa kale, ndipo ciwonongeko cake cayandikila kwambili. Baibo imati: “Dziko likupita.” (1 Yoh. 2:17) Ndithudi, dzikoli lidzawonongedwa. Koma pali kusiyana pakati pa ciwonongeko ca dzikoli ndi kunyongedwa kwa cigaŵenga. Pamene cigaŵenga catsala pang’ono kunyongedwa, anthu ena angacite zionetselo za kusakondwa ndi ciweluzoco. Angacite zimenezi cifukwa coganiza kuti sipanacitike cilungamo, kapena cifukwa congofuna kuti papiteko kanthawi munthuyo asananyongedwe. Koma ciŵeluzo ca dzikoli cinapelekedwa ndi Wolamulila wa cilengedwe conse, amene ndi wangwilo komanso wacilungamo. (Deut. 32:4) Mulungu sadzazengeleza powononga dzikoli, ndipo palibe amene adzakayikila kuti ciŵeluzo cimene capelekedwa n’colungama. Dzikoli likadzawonongedwa, aliyense kumwamba ndi padziko lapansi adzaona kuti Mulungu wacitadi cilungamo. Pambuyo pake, padziko lonse padzakhala mtendele woculuka.
3. Tidzakambilana zinthu ziti zimene zidzacotsedwa Ufumu wa Mulungu ukadzabwela?
3 Kodi “dziko” limene “likupita” liphatikizapo ciani? Liphatikizapo zinthu zambili zimene anthu amaona kuti n’zofunika ngako pa umoyo wawo. Zinthu zimenezo zidzawonongedwa. Kodi imeneyi ni nkhani yomvetsa cisoni? Kutalitali. Ni nkhani yokondweletsa, ndipo ni mbali yofunika kwambili ya ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mat. 24:14) Tsopano tiyeni tikambilane zinthu zimene zidzacotsedwa Ufumu wa Mulungu ukadzabwela. Tidzakambilana mbali zinayi zikulu-zikulu izi: anthu oipa, mabungwe acinyengo, makhalidwe oipa, ndi mavuto. Pa mbali iliyonse, tidzaona (1) mmene mbalizo zimatikhudzila masiku ano, (2) zimene Yehova adzacitapo, ndi (3) mmene Mulungu adzabweletselapo mbali zabwino.
ANTHU OIPA
4. Kodi zocita za anthu oipa zimatikhudza bwanji?
4 Kodi zocita za anthu oipa zimatikhudza bwanji masiku ano? Mtumwi Paulo atakamba kuti masiku otsiliza ano adzakhala “nthawi yapadela komanso yovuta,” anauzilidwanso kulemba kuti: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipilaipilabe.” (2 Tim. 3:1-5, 13) Kodi mwaona kukwanilitsidwa kwa mau amenewa? Ambili a ise tinacitilidwapo nkhanza ndi anthu oipa monga aciwawa, odana ndi anzawo, ndi zigaŵenga zoopsa. Ena mwa anthu amenewa amacita zoipa moonetsela. Koma ena ndi aciphamaso, amabisa zoipa zimene amacita n’kumadzionetsa monga anthu acilungamo. Ngakhale kuti mwina ise sitinacitilidwepo nkhanza zaconco, zocita za anthu oipa zimatikhudza ndithu. Cimatiŵaŵa kwambili tikamvela nkhanza zimene anthuwo amacitila ana, okalamba, ndi anthu ena ovutika. Masiku ano, anthu oipa amangocita zinthu monga vilombo kapena viŵanda. (Yak. 3:15) Koma cokondweletsa n’cakuti Mau a Yehova amatipatsa ciyembekezo cabwino.
5. (a) Kodi anthu oipa akali na mwayi wotani? (b) N’ciani cidzacitikila anthu oipa amene sadzasintha?
5 Kodi Yehova adzacita ciani? Palipano, iye wapeleka mwayi kwa anthu oipa kuti asinthe khalidwe lawo. (Yes. 55:7) Woipa aliyense payekha akalibe kulandila ciweluzo cake. Koma dziko loipali linaŵeluzidwa kale kuti lidzawonongedwa. Nanga bwanji za anthu oipa amene sadzasintha, amene adzapitiliza kucilikiza dongosolo loipali mpaka pamene cisautso cacikulu cidzayamba? Yehova anakamba kuti adzawawononga kothelatu. (Ŵelengani Salimo 37:10.) Anthu ena oipa angaganize kuti adzapulumuka ciwonongeko cimeneco. Ambili m’dzikoli amayesetsa kubisa zocita zawo zoipa, ndipo nthawi zambili salandila cilango pa zocita zawozo. (Yobu 21:7, 9) Koma, Baibo imati: “Maso [a Mulungu] amayang’anitsitsa njila za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse. Kulibe mdima wandiweyani woti amene akucita zopweteka ena abisaleko.” (Yobu 34:21, 22) Kukamba zoona, palibe amene angathawe ciŵeluzo ca Yehova Mulungu. Iye sanganamizidwe na munthu aliyense wacinyengo. Mulungu amaona ciliconse, ndipo palibe cimene cingamulepheletse kuona zoipa zimene munthu amacita ngakhale atabisa bwanji. Pambuyo pa Aramagedo, tidzaona pamene panali kukhala oipa, koma sadzapezekapo. Iwo sadzakhalakonso.—Sal. 37:12-15.
6. N’ndani adzakhala padziko oipa akadzacotsedwa? Nanga n’cifukwa ciani imeneyi ni nkhani yabwino?
6 Oipa akadzacotsedwa, n’ndani adzakhala padziko? Yehova anapeleka lonjezo lolimbikitsa lakuti: “Anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.” Vesi ina mu salimo imeneyi imati: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29) Kodi “ofatsa” ndi “olungama” amenewa n’ndani? Ofatsa ni anthu amene amamvela modzicepetsa malangizo a Yehova ndi ziphunzitso zake. Olungama ni anthu amene amakonda kucita zoyenela pamaso pa Yehova Mulungu. M’dzikoli, anthu olungama ni ocepa kwambili poyelekezela ndi anthu oipa. Koma m’dziko latsopano limene likubwela, mudzakhala anthu ofatsa ndi olungama okha-okha. Popeza kuti kudzakhala anthu abwino okha-okha, dziko lapansi lidzakhala paradaiso.
MABUNGWE ACINYENGO
7. Kodi zocita za mabungwe acinyengo zimatikhudza bwanji masiku ano?
7 Kodi zocita za mabungwe acinyengo zimatikhudza bwanji masiku ano? Zinthu zambili zoipa zimene zimacitika masiku ano zimacitidwa na mabungwe osati anthu paokha. Mwacitsanzo, ganizilani mmene zipembedzo zasoceletsela anthu mamiliyoni ambili kuti asadziŵe zoona ponena za Mulungu, Baibo, tsogolo la anthu, ndi zinthu zina zambili. Ganizilaninso maboma amene amalimbikitsa nkhondo ndi ciwawa pakati pa mitundu yosiyana-siyana ya anthu. Maboma ena amapondeleza anthu wamba osauka, ndiponso amakonda ziphuphu ndi tsankho. Nanga bwanji za makampani adyela amene amawononga cilengedwe ndi kudyela masuku pamutu makasitomala awo, pofuna kuunjikila cuma anthu oŵelengeka pamene anthu mamiliyoni ambili akuvutika ndi umphaŵi? Kunena zoona, mabungwe acinyengo amenewa ndiwo acititsa mavuto ambili amene asautsa anthu padzikoli.
8. Malinga n’zimene Baibo imakamba, n’ciani cidzacitikila mabungwe amene anthu ambili amaona kuti ni odalilika?
8 Kodi Yehova adzacita ciani? Cisautso cacikulu cidzayamba pamene magulu andale adzaukila zipembedzo zonama, zoimilidwa na hule lochedwa Babulo Wamkulu. (Chiv. 17:1, 2, 16; 18:1-4) Zipembedzo zimenezo zidzawonongedwa kothelatu. Nanga n’ciani cidzacitikila mabungwe ena onse oipa? Baibo imayelekezela mabungwe amenewo na mapili ndi zilumba cifukwa ambili mwa iwo amaoneka olimba ndi osasunthika kwa anthu a m’dzikoli. (Ŵelengani Chivumbulutso 6:14.) Koma Mau a Mulungu anakambilatu kuti maboma ndi mabungwe awo adzagwedezeka n’kucoka pa maziko awo. Cisautso cacikulu cidzafika pacimake pamene maboma onse a m’dzikoli adzawonongedwa, pamodzi ndi onse amene adzakhala kumbali yawo polimbana ndi Ufumu wa Mulungu. (Yer. 25:31-33) Pambuyo pake, sikudzakhalanso mabungwe acinyengo.
9. Tingatsimikize bwanji kuti anthu okhala m’dziko latsopano azidzacita zinthu mwadongosolo?
9 N’ciani cidzaloŵa m’malo mwa mabungwe acinyengo? Kodi padziko padzakhala dongosolo lililonse pambuyo pa Aramagedo? Baibo imatiuza kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela mogwilizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.” (2 Pet. 3:13) Kumwamba kwakale ndi dziko lakale zikutanthauza maboma oipa ndi anthu oipa amene amalamulidwa ndi mabomawo. Zonsezi sizidzakhalakonso. Nanga n’ciani cidzakhalapo pambuyo pakuti zimenezi zawonongedwa? Mau akuti “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” aonetsa kuti kudzakhala boma latsopano ndi anthu abwino amene adzalamulidwa na bomalo. Ufumu wa Mulungu, umene Mfumu yake ni Yesu Khristu, udzalamulila mogwilizana na cifunilo ca Yehova, amene ni Mulungu wadongosolo. (1 Akor. 14:33) Conco, “dziko lapansi latsopano” lidzakhala ladongosolo. Padzakhala anthu abwino otsogolela. (Sal. 45:16) Iwo azidzayang’anilidwa ndi Khristu ndi olamulila anzake okwana 144,000. Mabungwe onse oipa adzaloŵedwa m’malo na boma limodzi la Ufumu wa Mulungu, labwino ndi logwilizana. Nthawi imeneyo idzakhala yokondweletsa ngako.
MAKHALIDWE OIPA
10. Ni makhalidwe oipa ati amene ni ofala m’dela lanu? Nanga inu ndi a m’banja lanu amakukhudzani bwanji?
10 Kodi makhalidwe oipa amatikhudza bwanji masiku ano? M’dzikoli, makhalidwe oipa ali ponse-ponse. Anthu amakonda kucita zaciweleŵele, zacinyengo, ndi zankhanza. Ndipo nthawi zambili makolo amavutika kuteteza ana awo ku makhalidwe oipa amenewa. Zosangulutsa zambili zimacititsa anthu kuona zinthu zoipa zimenezi monga zabwino ndi kusukulutsa mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. (Yes. 5:20) Akhristu oona amayesetsa kupewa makhalidwe amenewa. Iwo amayesetsa kukhalabe okhulupilika m’dzikoli, limene limalimbikitsa anthu kusalemekeza mfundo za Yehova.
11. Tiphunzilapo ciani pa ciŵeluzo cimene Yehova anapeleka ku mizinda ya Sodomu ndi Gomora?
11 Kodi Yehova adzathetsa bwanji makhalidwe oipa? Kumbukilani mmene iye anathetsela makhalidwe oipa amene anali ofala mu Sodomu ndi Gomora. (Ŵelengani 2 Petulo 2:6-8.) Munthu wolungama Loti, anali kuzunzika ndi zoipa zimene zinali kucitika m’mizindayo. Koma Yehova anawononga mizindayo kuti athetse zoipazo. Zimene anacitazo ndi “citsanzo ca zinthu zimene zidzacitikile anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.” Mofanana ndi m’nthawi ya Loti, Yehova adzawononga dziko loipali kuti athetse zoipa zimene zicitika masiku ano.
12. Dziko loipali likadzawonongedwa, n’zinthu ziti zimene inuyo mufuna kudzacita?
12 N’ciani cidzayamba kucitika makhalidwe oipa akadzatha? Anthu okhala m’Paradaiso adzayamba kugwila nchito zokondweletsa zokha-zokha. Ganizilani nchito yokondweletsa imene tidzakhala nayo, yokonza dzikoli kukhala Paradaiso ndi kumanga nyumba zathu ndi za okondedwa athu. Ganizilaninso cisangalalo cimene tidzakhala naco polandila anthu mamiliyoni ambili amene adzaukitsidwa. Tidzasangalalanso kuwaphunzitsa njila za Yehova ndi zimene iye wakhala akucitila anthu. (Yes. 65:21, 22; Mac. 24:15) Tidzakhala na nchito zambili zokondweletsa, zimenenso zidzapangitsa kuti Yehova atamandike.
MAVUTO
13. Kodi kupanduka kwa Satana, Adamu, ndi Hava kunabweletsa mavuto otani padziko lapansi?
13 Kodi mavuto amatikhudza bwanji? Anthu oipa, mabungwe acinyengo, ndi makhalidwe oipa zabweletsa mavuto ambili padziko lapansi. N’ndani wa ise amene sanakhudzidwepo na nkhondo, umphawi, kapena kusankhana mitundu? Nanga n’ndani amene sanakhudzidwepo na matenda ndi imfa? Tonse timakhudzidwa ndi mavuto amenewa. Mavutowa anayamba cifukwa Satana, Adamu, ndi Hava anapandukila Yehova. Conco palipano, palibe munthu amene angapewe mavuto amenewa.
14. Kodi Yehova adzacitapo ciani pa mavuto amene tikumana nawo? Fotokozani zitsanzo.
14 Kodi Yehova adzacitapo ciani pa mavuto amenewa? Ganizilani za nkhondo. Yehova analonjeza kuti adzathetsa nkhondo, ndipo siidzakhalaponso. (Ŵelengani Salimo 46:8, 9.) Nanga bwanji za matenda? Adzawathetselatu. (Yes. 33:24) Imfa nayonso adzaimeza. (Yes. 25:8) Umphawi adzauthetsa. (Sal. 72:12-16) Mulungu adzathetsa mavuto ena onse amene anthu akumana nawo masiku ano. Adzacotsanso “mpweya” woipa wa m’dzikoli kapena kuti cisonkhezelo coipa ca Satana ndi ziwanda zake.—Aef. 2:2.
Yelekezani kuti muli m’dziko lopanda nkhondo, matenda, kapena imfa. (Onani palagilafu 15)
15. N’zinthu ziti zimene sizidzakhalakonso pambuyo pa Aramagedo?
15 Yelekezani kuti muli m’dziko lopanda nkhondo, matenda, kapena imfa. Dziko lopanda asilikali, zida za nkhondo, kapena zipilala zokumbukila zimene zinacitika pa nkhondo. Yelekezaninso kuti mukukhala m’dziko lopanda zipatala, madokota, manesi, makampani a inshuwalansi ya za umoyo, mamochale, nyumba za malilo, amalukula, kapena manda. Popeza upandu udzatha, sikudzakhalanso makampani a zacitetezo, ma alamu, apolisi, mwina ngakhale maloko ndi makiyi. Panthawiyo, sitidzakhalanso na nkhawa iliyonse.
16, 17. (a) Kodi anthu opulumuka Aramagedo adzakhala na umoyo wotani? Fotokozani citsanzo. (b) Tifunika kucita ciani kuti tidzapulumuke pamene dziko loipali liwonongedwa?
16 Kodi umoyo udzakhala bwanji mavuto akadzatha? Udzakhala wokondweletsa kwambili. Koma zingakhale zovuta kumvetsetsa palipano cifukwa takhala m’dziko loipali kwa nthawi yaitali, ndipo tazoloŵela mavuto amene timakumana nawo. Zili monga anthu amene akhala pafupi na msewu waukulu umene mumapita mamotoka ambili. Iwo amafika pojaila congo ca mamotokawo. Komanso amene amakhala kufupi na dzala, amajaila fungo loipa moti sadelanso nkhawa. Koma mavuto onse amene timakumana nawo akadzatha, tidzakondwela ngako.
17 Kodi tidzamvela bwanji mavuto akadzatha? Lemba la Salimo 37:11 limati, ‘Tidzasangalala ndi mtendele woculuka.’ Kodi mau amenewa si okhazika mtima pansi? Yehova afuna kuti inuyo mudzakhale na umoyo wotelo. Conco, citani zilizonse zimene mungathe kuti mupitilize kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova Mulungu ndi kugwilizana ndi gulu lake m’masiku otsiliza ovuta ano! Muziganizila za ciyembekezo cimeneci, muziciona kuti n’ceni-ceni, ndiponso muziuzako ena mwakhama za ciyembekezoci. (1 Tim. 4:15, 16; 1 Pet. 3:15) Mukatelo, mungakhale otsimikiza kuti mudzapulumuka pamene dziko loipali likuwonongedwa, ndipo mudzakhala ndi moyo wacimwemwe mpaka muyaya.
a Ndimeyi ifotokoza zimene zinali kucitika kale-kale m’ndende zina ku United States.