Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi
Kodi n’koyenela Mkhristu kukhala na mfuti yodzitetezela kwa anthu ena?
Akhristu amayesetsa kupeza njila zodzitetezela, koma pocita zimenezi, amatsatila mfundo za m’Baibo. Mfundo zimenezi sizilola Akhristu kukhala na mfuti ya mtundu uliwonse kuti adziteteze kwa anthu anzawo. Ganizilani mfundo zotsatilazi:
Yehova amaona moyo, maka-maka wa munthu, kukhala wopatulika. Wamasalimo Davide anadziŵa kuti Yehova ndiye “kasupe wa moyo.” (Sal. 36:9) Conco, ngati Mkhristu wasankha kucita zinazake kuti adziteteze iye mwini kapena kuteteza katundu wake, ayenela kuyesetsa kupewa kupha munthu kuopela kuti angakhale na mlandu wa magazi.—Deut. 22:8; Sal. 51:14.
N’zoona kuti kuseŵenzetsa cida ciliconse podziteteza kungapangitse munthu kukhala na mlandu wa magazi. Komabe, kukhala na mfuti kungapangitse munthu kupha wina mosavuta, kaya mwangozi kapena mwadala.a Kuwonjezala apo, wacifwamba amene ni waukali akaona kuti munthu ali na mfuti, zinthu zingafike poipa kwambili cakuti wina akhoza kuphedwa.
Pamene Yesu anauza otsatila ake kuti anyamule malupanga pa usiku wotsiliza wa moyo wake padziko, colinga cake sicinali cakuti awaseŵenzetse podziteteza. (Luka 22:36, 38) Koma anali kufuna kuseŵenzetsa malupangawo kuti awaphunzitse mfundo yakuti safunika kucita ciwawa, ngakhale pamene ayang’anizana ndi gulu la anthu onyamula zida. (Luka 22:52) Pamene Petulo anatenga lupanga n’kumenya nalo kapolo wa mkulu wa ansembe, Yesu anam’lamula kuti: “Bwezela lupanga lako m’cimake.” Ndiyeno, Yesu anachula mfundo ya coonadi yofunika kwambili imene ngakhale otsatila ake masiku ano amaitsatila. Iye anati: “Onse ogwila lupanga adzafa ndi lupanga.”—Mat. 26:51, 52.
Mogwilizana ndi Mika 4:3, anthu a Mulungu ‘asula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzila mitengo.’ Izi zimatidziŵikitsa kuti ndise Akhristu oona, ndipo n’zogwilizana ndi malangizo amene mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba akuti: “Musabwezele coipa pa coipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendele ndi anthu onse, monga mmene mungathele.” (Aroma 12:17, 18) Ngakhale kuti Paulo anakumana ndi mavuto ambili, monga “zoopsa za acifwamba,” iye anatsatila malangizo amene analemba. Sanaphwanye mfundo za m’Malemba pofuna kudziteteza. (2 Akor. 11:26) M’malomwake, anadalila Mulungu ndi nzelu zopezeka m’Mau ake, cifukwa zimaposa “kukhala ndi zida zomenyela nkhondo.”—Mlal. 9:18.
Akhristu amaona moyo kukhala wofunika kwambili kuposa zinthu zakuthupi. Baibo imati: “Moyo [wa munthu] sucokela m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Conco, ngati zigaŵenga zamfuti sizinasinthe maganizo awo, ngakhale pambuyo pokamba nazo mofatsa, Akhristu anzelu amatsatila mfundo imene Yesu anakamba, yakuti: “Usalimbane ndi munthu woipa.” Izi zingatanthuze kuzilola kutenga ciliconse cimene zifuna. (Mat. 5:39, 40; Luka 6:29)b Komabe, cinthu canzelu kwambili ni kupewa zinthu zimene zingakope acifwamba. Mwacitsanzo, ngati tipewa ‘kudzionetsela ndi zimene tili nazo pa moyo wathu,’ ndipo m’dela lathu timadziŵika monga Mboni ya Yehova yokonda mtendele, tingapewe kuvutitsidwa ndi anthu acifwamba.—1 Yoh. 2:16; Miy. 18:10.
Akhristu amalemekeza cikumbumtima ca ena. (Aroma 14:21) Akhristu ena angadabwe kapena kukhumudwa ngati adziŵa kuti wina mumpingo ali na mfuti yodzitetezela kwa anthu ena. Cikondi cidzatilimbikitsa kuika zofuna za ena patsogolo, ngakhale kuti kucita zimenezi kungafune kuti tidzimane zinthu zina zimene mwalamulo n’zololeka kwa ise.—1 Akor. 10:32, 33; 13:4, 5.
Akhristu amayesetsa kukhala zitsanzo zabwino. (2 Akor. 4:2; 1 Pet. 5:2, 3) Ngati Mkhristu apitiliza kusunga mfuti yodzitetezela kwa anthu, ngakhale pambuyo popatsidwa uphungu wa m’Malemba, ndiye kuti si wacitsanzo cabwino. Conco, sangayenelele kutumikila pa udindo uliwonse kapena kupatsidwa utumiki uliwonse wapadela mumpingo. Mfundo imeneyi imagwilanso nchito kwa Mkhristu amene apitiliza kugwila nchito imene imafuna kuti azinyamula mfuti. Mkhristu waconco afunika kupeza nchito ina.c
Mkhristu aliyense ali na ufulu wosankha mmene angadzitetezele, kapena mmene angatetezele banja lake ndi katundu wake. Alinso na ufulu wosankha nchito imene afuna. Komabe, mfundo za m’Baibo zimaonetsa nzelu za Mulungu ndi cikondi cake pa ise. Cifukwa cotsatila mfundo zimenezi, Akhristu ofikapo mwauzimu sakhala na mfuti yodzitetezela kwa anthu ena. Amadziŵa kuti anthu amene amadalila Mulungu mwa kutsatila mfundo za m’Baibo ndiwo amapeza citetezo ceni-ceni ndi cokhalitsa.—Sal. 97:10; Miy. 1:33; 2:6, 7.
Pa cisautso cacikulu, Akhristu adzadalila Yehova, osati kudziteteza okha
a Mkhristu angasankhe kukhala na mfuti n’colinga cakuti aziphela nyama kuti azidya kapena kuti adziteteze ku nyama zolusa. Koma panthawi imene sakuiseŵenzetsa, ayenela kucotsamo mpholopolo, kapenanso kuimasula, ndi kuisungila pa malo otetezeka. Kumene malamulo salola munthu kukhala na mfuti, kapena kumene kuli malamulo a kasewenzetsedwe ka mfuti, Akhristu ayenela kutsatila malamulowo.—Aroma 13:1.
b Kuti mudziŵe mmene munthu angadzitetezele ngati wina afuna kumugwilila, onani nkhani yakuti “Njira Zopeŵera Kugwiriridwa Chigololo,” mu Galamukani! ya March 8, 1993.
c Mfundo zina pankhani yoloŵa nchito imene imafuna kunyamula mfuti kapena zida zina, mungazipeze mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2005, peji 31, ndi Nsanja ya Cizungu ya July 15, 1983, mapeji 25-26..