LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp18 na. 2 masa. 6-7
  • Maulosi Amene Anakwanilitsidwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maulosi Amene Anakwanilitsidwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAULOSI AMENE AKUKWANILITSIDWA MASIKU ANO
  • Anthu A Mulungu Acoka Ku Babulo
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Kodi Tili mu “Masiku Otsiliza”?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
wp18 na. 2 masa. 6-7
Aphunzila maulosi a m’Baibo

Maulosi Amene Anakwanilitsidwa

M’nkhani yoyamba tafotokozamo cocitika cina cakale coonetsa kuti wolosela wina wa ku Delphi anasoceletsa mfumu Kolosase, zimene zinacititsa kuti agonjetsedwe na mfumu ya Peresiya. Koma m’Baibo muli ulosi wina wocititsa cidwi wokhudza mfumu ya ku Perisiya, umene unakwanilitsidwa ndendende monga mmene unakambila.

Kukali zaka pafupi-fupi 200 mfumuyo ikalibe kubadwa, mneneli waciheberi dzina lake Yesaya anatomolelatu dzina la mfumu imene idzagonjetsa mzinda wamphamvu wa Babulo, kuti idzakhala Koresi. Ndipo anafotokozanso mmene adzaugonjetsela.

Yesaya 44:24, 27, 28: “Yehova . . . wanena kuti, . . . ‘Ndine amene ndikuuza madzi akuya kuti, ‘‘Iphwa ndipo mitsinje yako yonse ndidzaiumitsa.’’ Ndine amene ndikunena za Koresi kuti, ‘‘Iye ndi m’busa wanga ndipo adzakwanilitsa bwinobwino zonse zimene ndikufuna,’’ ngakhale zimene ndanena zokhudza Yerusalemu zakuti, ‘‘Adzamangidwanso,’’ ndi zokhudza kacisi zakuti, ‘‘Maziko ako adzamangidwa.’””

Malinga n’zimene anakamba wolemba mbili yakale wa ku Greece, dzina lake Herodotus, asilikali a Koresi anapatutsa madzi a Mtsinje wa Firate, umene unali kuzungulila mzinda wa Babulo. Mapulani a Koresi anathandiza kuti asilikali ake aoloke mtsinje na kuloŵa mu mzinda pamene madzi anapunguka. Ataugonjetsa mzindawo, Koresi anamasula Ayuda amene anamangidwa ukapolo m’Babulo ndipo anawalola kubwelela kwawo kukamanganso Yerusalemu, amene anali ataonongedwa zaka 70 kumbuyoko

Yesaya 45:1: “Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga. Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwila dzanja lake lamanja kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, kuti ndimasule m’ciuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulile zitseko zokhala ziwiliziwili, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa.”

Aperisiya analoŵa mu mzindawo kupitila pa geti ya zitseko zolimba, zimene anazisiya zotseguka. Sembe Ababulo anadziŵa mapulani a Koresi, sembe anatseka mageti onse amene anali otseguka. Koma malinga na mmene zinakhalila, mzindawo unali wosatetezeka.

Ulosi wocititsa cidwi umenewu ni umodzi mwa maulosi ambili opezeka m’Baibo amene anakwanilitsidwa mosalephela olo pang’ono.a Mosiyana na zolosela za anthu zimene kaŵili-kaŵili zimacokela kwa milungu yawo yabodza, maulosi a m’Baibo amacokela kwa amene analengeza kuti: “Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi. Kuyambila kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinacitike”—Yesaya 46:10.

Mulungu woona yekha, amene dzina lake ni Yehova, ndiye angakambe zimenezi. Ndipo mwacionekele, dzina limeneli limatanthauza kuti, “Iye Amacititsa Kukhala,” kuonetsa kuti ali na mphamvu zokwanitsa kudziŵa na kuonelatu zocitika zam’tsogolo mogwilizana na cifunilo cake. Izi zimatitsimikizila kuti iye ni wofunitsitsa kukwanilitsa malonjezo ake onse.

MAULOSI AMENE AKUKWANILITSIDWA MASIKU ANO

Kodi mungakonde kudziŵa zimene maulosi a m’Baibo amakamba zokhudza masiku athu ano? Zaka 2,000 zapitazo, Baibo inakambilatu kuti, “nthawi yapadela komanso yovuta,” idzakhala ‘m’masiku otsiliza.’ Masiku otsiliza ciani? Osati otsiliza dziko kapena anthu, koma mavuto amene avutitsa anthu kwa zaka masauzande na kupondelezewa. Tiyeni tikambilane maulosi ocepa cabe amene ni zizindikilo za “masiku otsiliza.”

2 Timoteyo 3:1-5: “[M]’masiku otsiliza . . . , anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale awo, osafuna kugwilizana ndi anzawo, onenela anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipeleka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe.”

Kodi simuvomeleza kuti makhalidwe amenewa akuwonjezeleka masiku ano? Kodi simukuona kuti anthu kulikonse ni odzikonda, okonda ndalama, odzitukumula komanso onyada? Kodi simuona kuti anthu sayamikila ndipo sakumva za ena? Mosakaikila, mumaonanso kuti ambili samvela makolo, ndiponso anthu oculuka amakonda kwambili zosangalatsa kuposa Mulungu. Ndipo tsiku na tsiku zinthu zikuipila-ipila.

Mateyu 24:6, 7: “Mudzamva phokoso la nkhondo ndi mbili za nkhondo. . . . Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina.”

Ziŵelengelo zionetsa kuti, kuyambila mu 1914 anthu opitilila 100 miliyoni aphedwa pa nkhondo. Ciŵelengelo cimeneci cimaposa ziŵelengelo za anthu onse m’maiko ambili. Ganizilani cabe za cisoni, kulila, na kuvutika, kaamba ka anthu ambili-mbili amene anafa. Kodi maiko aphunzilapo kanthu pa zimenezi, na kuleka nkhondo?

Mateyu 24:7: “Kudzakhala njala.”

Bungwe la World Food Programme inati: “Dzikoli lili na cakudya cokwanila kudyetsa munthu aliyense, koma pa anthu 815 miliyoni, mmodzi pa anthu 9 alionse amagona na njala tsiku lililonse. Kuonjezela apo, mmodzi pa anthu atatu alionse amadwala matenda obwela cifukwa ca kupeleŵela kwa cakudya m’thupi.” Ndipo zioneka kuti caka na caka ana pafupi-fupi 3 miliyoni amafa cifukwa ca njala.

Luka 21:11: “Kudzakhala zivomezi zazikulu.”

Caka na caka, kumacitika zivomezi zazikulu pafupi-fupi 50,000 zimene zimakhudza anthu. Pafupi-fupi 100 zimaononga manyumba, ndipo civomezi cimodzi camphamvu kwambili cimacitika caka ciliconse. Malinga na ciŵelengelo cina, zioneka kuti pakati pa caka ca 1975 na 2000, zivomezi zinapha anthu 471,000.

Mateyu 24:14: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”

Mboni za Yehova zopitilila 8 miliyoni, zimalalikila na kucitila umboni uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi, m’maiko pafupi-fupi 240. Zimalalikila m’mizinda ikulu-ikulu, m’midzi ya kutali, ndi kwa anthu okhala m’nkhalango, na m’mapili. Nchito imeneyi ikadzacitika kufika pa mlingo umene Mulungu afuna, ulosi udzakwanilitsidwa wakuti: “Kenako mapeto adzafika.” Kodi cidzacitika n’ciani? Ulamulilo wa anthu udzatha ndipo ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu udzayamba. Kodi ni malonjezo ati amene adzakwanilitsidwa mu Ufumu wa Mulungu? Pitilizani kuŵelenga kuti mudziŵe.

a Onani nkhani yakuti, “Umboni Woonetsa Kuti Maulosi a M’Baibo Ni Azoona.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani