Zamkati
3 Anadzipeleka na Mtima Wonse—ku Madagascar
WIKI YA FEBRUARY 26, 2018–MARCH 4, 2018
7 “Iye Amapeleka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”
Kodi tiyenela kucita ciani tikakumana na mavuto aakulu mu umoyo? Nkhani iyi idzafotokoza lemba lathu la caka ca 2018, ndipo ionetsa cifukwa cake timafunika kudalila Yehova kuti atipatse mphamvu. Ifotokozanso mmene iye amacitila zimenezi.
WIKI YA MARCH 5-11, 2018
12 Mgwilizano Wokondweletsa pa Cikumbutso
Cikumbutso ca Imfa ya Khristu cidzacitika pa Ciwelu, pa March 31, 2018. Kodi tingakonzekele bwanji cocitika cimeneci? Kodi tidzapindula bwanji tikadzapezekapo? Nanga Cikumbutso cimagwilizanitsa bwanji anthu a Mulungu pa dziko lonse? Nkhaniyi idzayankha mafunso amenewa.
WIKI YA MARCH 12-18, 2018
17 Kodi N’kumupatsilanji Amene Zonse N’zake?
Zonse zimene tili nazo n’zocokela kwa Yehova. Ngakhale zili conco, iye amafuna kuti tiziseŵenzetsa cuma cathu kucilikizila nchito ya gulu lake. Nkhani iyi idzafotokoza cifukwa cake timapindula ngati tilemekeza Yehova ndi zinthu zathu za mtengo wapatali. Idzafotokozanso mmene timapindulila.
WIKI YA MARCH 19-25, 2018
22 N’cikondi Cotani Cimene Cimabweletsa Cimwemwe Ceni-ceni?
WIKI YA MARCH 26, 2018–APRIL 1, 2018
27 Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
Nkhani yoyamba pa nkhani izi idzafotokoza mmene kukonda Mulungu kumatithandizila kukhala na cimwemwe ceni-ceni kusiyana na kukonda zinthu zina zimene anthu ambili amakonda ‘m’masiku otsiliza’ ano. (2 Tim. 3:1) Nkhani yaciŵili idzafotokoza mmene makhalidwe a anthu m’masiku otsiliza ano alili osiyana kwambili na makhalidwe a anthu a Mulungu.