LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 3 masa. 6-7
  • Tinalengedwa Kuti Tikhale na Moyo Kwamuyaya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tinalengedwa Kuti Tikhale na Moyo Kwamuyaya
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • UMBONI WOONETSA KUTI MULUNGU AMAFUNA TIKHALE NA MOYO KWAMUYAYA
  • ANAKHALA NA MOYO WAUTALI KWAMBILI
  • Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Yesu Kodi Zili ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • N’cifukwa Ciani Timakalamba Na Kufa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 3 masa. 6-7
Anthu akuyenda m’thengo ndipo akusangalala kuyang’ana cilengedwe

Tinalengedwa Kuti Tikhale Na Moyo Kwamuyaya

KODI NDANI wa ife amene safuna kukhala na moyo wautali komanso wacimwemwe? Ganizilani cabe mmene zikanakhalila zokondweletsa kukhala na moyo wamuyaya, tili na thanzi labwino, komanso acimwemwe! Sembe timakhala na nthawi yokwanila yoceza na anthu amene timakonda, kuyenda malo osiyana-siyana pa dziko lonse, kuphunzila maluso atsopano, kukulitsa luso lomvetsa zinthu, komanso kuphunzila na kuzimvetsa bwino zinthu zoticititsa cidwi.

Kodi n’cifukwa ciani anthu amafuna kukhala na moyo kwamuyaya? Malemba amatiuza kuti Mulungu anaika cifuno cimeneco mu mtima wathu. (Mlaliki 3:11) Amatiuzanso kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Ngati Mulungu wacikondi anatilenga na cifuno cokhala na moyo kwamuyaya, kodi angalepheletse cifuno cimeneco kukwanilitsika?

Mwacionekele, imfa si bwenzi lathu. Ndipo Baibo imafotokoza kuti imfa ni “mdani” wathu. (1 Akorinto 15:26) Ena amafa ali aang’ono, ena amafa atakula. Koma imfa siilephela, imabwela ndithu. Kwa ambili, kuganizila za imfa kumaŵasoŵetsa mtendele, ngakhalenso kuŵacititsa mantha. Kodi idzafika nthawi pamene mdani ameneyu adzagonjetsedwa? Kodi zingathekedi kum’gonjetsa mdaniyu?

UMBONI WOONETSA KUTI MULUNGU AMAFUNA TIKHALE NA MOYO KWAMUYAYA

Mwina mungadabwe kudziŵa kuti sicinali colinga ca Mulungu kuti anthufe tizifa. Buku la m’Baibo la Genesis, limapeleka umboni wakuti colinga ca Mulungu cinali cakuti anthu akhale na moyo pa dziko lapansi kwamuyaya. Yehova Mulungu analenga dziko na zonse zofunikila kuti anthu akhalepo. Kenako analenga munthu woyamba, Adamu, na kumuika m’paradaiso, inde m’munda wa Edeni. Pambuyo pake, “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambili.”—Genesis 1:26, 31.

Adamu analengedwa wangwilo, m’cifanizilo ca Mulungu. (Deuteronomo 32:4) Hava, mkazi wa Adamu, nayenso anali wangwilo. Anali na maganizo komanso thupi langwilo. Yehova anaŵauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile. Muyang’anilenso nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso colengedwa ciliconse cokwawa padziko lapansi.”—Genesis 1:28.

Kuti Adamu na Hava adzaze dziko lapansi, panafunika nthawi yaitali. Hava akanafunika kubala ana, ndipo anawo akanafunikanso kubala ana ena, mpaka dziko lonse kudzala na anthu monga mmene Mulungu anali kufunila. (Yesaya 45:18) Kodi Yehova akanauza Adamu na Hava kuti adzaze dziko lapansi, ngati anali kufuna kuti iwo azikhala na moyo wokwanitsa cabe kuona ana awo, kapena adzukulu awo kenako n’kumwalila, osaliona lonjezo la kudzadza dziko lapansi likukwanilitsidwa?

Ganizilaninso za nchito imene Adamu anapatsidwa yoyang’anila nyama. Iye anauzidwa kuti apatse nyama zonse maina, ndipo izi zikanatenga nthawi yaitali. (Genesis 2:19) Kuti aziyang’anile bwino nyamazo, anafunika kuzidziŵa bwino, komanso kudziŵa mmene angazisamalile. Izi zikanatenganso nthawi yaitali kwambili.

Conco, malangizo a Mulungu akuti adzaze dziko lapansi komanso kuyang’anila nyama, aonetsa kuti anthu oyambililawo, Adamu na Hava, analengedwa kuti akhale na moyo wautali. Ndipo Adamu anakhaladi moyo wautali kwambili.

COLINGA CA MULUNGU N’CAKUTI ANTHU AKHALE NA MOYO WOSATHA M’PARADAISO PA DZIKO LAPANSI

ANAKHALA NA MOYO WAUTALI KWAMBILI

Adamu

Adamu, zaka 930

Metusela

Metusela, zaka 969

Nowa

Nowa, zaka 950

Munthu wa masiku ano

Masiku ano, zaka 70 kufika 80

Baibo imaonetsa kuti kale-kale, anthu anali kukhala na moyo wautali kuposa masiku ano. Imakamba kuti: “Masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930.” Ndiyeno imapitiliza kuchula amuna ena 6 amene anakhala na moyo kupitilila zaka 900! Amuna amenewo anali Seti, Enosi, Kenani, Yaredi, Metusela, komanso Nowa. Onsewa anakhalako Cigumula ca Nowa cikalibe kucitika. Ndipo Nowa anakhala na moyo zaka 600 Cigumula cisanacitike. (Genesis 5:5-27; 7:6; 9:29) Kodi zinali kutheka bwanji anthu kukhala na moyo wautali conco?

Anthu onsewa anabadwa pasanapite nthawi yaitali kwambili, kucokela pamene Adamu na Hava, anthu angwilo anakhalako. Mwacionekele, ici ndiye cifukwa cake anthu anali kukhala na moyo wautali. Koma kodi pali mgwilizano wotani pakati pa kukhala moyo wautali na ungwilo? Nanga kodi imfa idzagonjetsedwa bwanji? Kuti tipeze mayankho pa mafunso aya, coyamba tifunika kudziŵa cifukwa cake timakalamba na kumwalila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani