LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 June masa. 2-7
  • “Samalani Kuti Wina Angakugwileni Ngati Nyama”!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Samalani Kuti Wina Angakugwileni Ngati Nyama”!
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • SATANA ANAKOPA AISIRAELI KUTI AYAMBE KULAMBILA MAFANO
  • NJILA ZITATU ZAMACENJELA ZIMENE SATANA ANASEŴENZETSA KUTI ASOCELETSE AISIRAELI
  • MACENJELA A SATANA MASIKU ANO
  • Khalani Maso! Satana Akufuna Kukumezani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • M’dziŵeni Mdani Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Ganizilani Za Mtundu Wa Munthu Amene Muyenela Kukhala
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Mungapambane Polimbana Ndi Satana
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 June masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 23

‘Samalani Kuti Wina Angakugwileni Ngati Nyama’

“Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”—AKOL. 2:8.

NYIMBO 96 Buku Lake la Mulungu ni Cuma

ZA M’NKHANI INOa

1. Malinga na Akolose 2:4, 8, kodi Satana amayesa bwanji kupotoza maganizo athu?

SATANA amafuna kuti tileke kumvela Yehova. Kuti akwanilitse colinga cake cimeneci, amayesa kupotoza kaganizidwe kathu. M’mawu ena, tingakambe kuti iye amayesa kusintha maganizo athu, n’colinga cakuti titengele kaganizidwe kake. Amacita izi mwa kuseŵenzetsa zinthu zokopa.—Ŵelengani Akolose 2:4, 8.

2-3. (a) N’cifukwa ciani tifunika kulabadila cenjezo la pa Akolose 2:8? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

2 Kodi zingatheke ife kusoceletsedwa na Satana? Inde. Kumbukilani kuti cenjezo limene Paulo analemba pa Akolose 2:8, linali lopita kwa Akhristu odzozedwa na mzimu woyela, osati anthu osakhulupilila. (Akol. 1:2, 5) Akhristu a m’nthawi imeneyo anafunika kukhala osamala kuti asasoceletsedwe. Koma masiku ano, m’pamene tifunika kukhala osamala kwambili. (1 Akor. 10:12) Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Satana anaponyedwa padziko lapansi, ndipo amafunitsitsa kusoceletsa atumiki a Mulungu okhulupilika. (Chiv. 12:9, 12, 17) Kuwonjezela apo, masiku ano anthu oipa komanso onyenga ‘akuipilaipilabe.’—2 Tim. 3:1, 13.

3 M’nkhani ino, tidzakambilana mmene Satana amaseŵenzetsela “cinyengo copanda pake,” pofuna kupotoza maganizo athu. Tidzaona njila zitatu za macenjela zimene iye amagwilitsila nchito kuti acite zimenezi. (Aef. 6:11) Ndipo m’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene tingacite ngati tayamba kukhala na maganizo olakwika cifukwa cosoceletsedwa na macenjela a Satana. Koma coyamba, tiyeni tikambilane mmene Satana anasoceletsela Aisiraeli pamene analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Ndipo tidzaona zimene tingaphunzilepo.

SATANA ANAKOPA AISIRAELI KUTI AYAMBE KULAMBILA MAFANO

4-6. Malinga na Deuteronomo 11:10-15, kodi n’kusintha kotani kumene Aisiraeli anafunika kupanga pa nkhani yaulimi ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa?

4 Kodi Satana anawakopa bwanji Aisiraeli kuti ayambe kulambila mafano? Iye anali kudziŵa kuti Aisiraeli afunika kulima kuti azipeza cakudya. Conco, anawakopa mwa kuwasonkhezela kucita miyambo yacikunja ya zaulimi. Pamene Aisiraeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, anafunika kusintha njila zawo zaulimi. Akali ku Iguputo, iwo anali kucita ulimi wothilila. Anali kuseŵenzetsa madzi a mu mtsinje wa Nile. Koma m’Dziko Lolonjezedwa munalibe mtsinje waukulu, ndipo ulimi unali kudalila mvula na mame. (Ŵelengani Deuteronomo 11:10-15; Yes. 18:4, 5) Conco, Aisiraeli anafunika kuphunzila njila zatsopano zaulimi. Kucita izi sikunali kopepuka, cifukwa Aisiraeli ambili odziŵa bwino nchito yaulimi anali atafela m’cipululu.

Aisiraeli akugwilizana na Akanani, ndipo akukopeka kuti ayambe kulambila Baala

Kodi Satana anakwanitsa bwanji kusoceletsa Aisiraeli, omwe anali alimi? (Onani ndime 4-6)b

5 Yehova atafotokozela anthu ake za kusintha kwa zinthu pa nkhani yaulimi, anawapatsa cenjezo limene linaoneka monga losagwilizana ndi nkhani yaulimi. Anati: “Samalani kuti mitima yanu isakopeke ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiwelamila.” (Deut. 11:16, 17) N’cifukwa ciani Yehova anacenjeza Aisiraeli kuti ayenela kupewa kulambila milungu yonama pamene anali kukamba nawo nkhani yaulimi?

6 Yehova anadziŵa kuti Aisiraeli akadzaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, adzafuna kuphunzila njila zina zaulimi zimene anthu a mitundu yowazungulila anali kuseŵenzetsa. N’zoona kuti anthuwo anali kuidziŵa bwino nchito yaulimi, ndipo Aisiraeli akanaphunzila maluso othandiza kwa iwo. Koma panali ngozi inayake. Alimi acikanani anali kulambila Baala, ndipo anali na maganizo olakwika. Anali kukhulupilila kuti Baala ndiye analenga kumwamba, komanso kuti ndiye anali kubweletsa mvula. Yehova sanafune kuti anthu ake asoceletsedwe na zikhulupililo zabodza zimenezo. Komabe, mobweleza-bweleza, Aisiraeli anali kuleka kulambila Yehova n’kuyamba kulambila Baala. (Num. 25:3, 5; Ower. 2:13; 1 Maf. 18:18) Ni macenjela otani amene Satana anagwilitsila nchito kuti agwile Aisiraeli monga akapolo? Tiyeni tione.

NJILA ZITATU ZAMACENJELA ZIMENE SATANA ANASEŴENZETSA KUTI ASOCELETSE AISIRAELI

7. Kodi cikhulupililo ca Aisiraeli cinayesedwa bwanji ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa?

7 Njila yoyamba yamacenjela imene Satana anaseŵenzetsa kuti asoceletse Aisiraeli ni kuwakopa na zinthu zabwino-bwino zimene iwo anali kulakalaka. Aisiraeli anali kulakalaka mvula. M’miyezi ya April mpaka September, m’Dziko Lolonjezedwa munali kugwa mvula yocepa kwambili. Kuti Aisiraeli akhale na cakudya komanso kuti akolole mbewu zoculuka, zinali kudalila mvula imene kaŵili-kaŵili inali kuyamba mu October. Satana anapangitsa Aisiraeli kukhulupilila kuti afunika kutengela miyambo ya Akanani kuti azikolola mbewu zambili. Akananiwo anali kukhulupilila kuti kucita miyambo inayake yacipembedzo kunali kofunika kuti milungu yawo ibweletse mvula. Aisiraeli ena amene analibe cikhulupililo mwa Yehova, anayamba kukhulupilila kuti kucita zimenezo kunalidi kofunika kuti asavutike na cilala. Conco, anayamba kucita miyambo yacikunja yacipembedzo polemekeza Baala, mulungu wonama.

8. Kodi njila yaciŵili imene Satana anaseŵenzetsa kuti asoceletse Aisiraeli ni iti? Fotokozani.

8 Njila yaciŵili imene Satana anaseŵenzetsa kuti asoceletse Aisiraeli ni kuwasonkhezela kucita ciwelewele. Polambila milungu yawo yonama, Akanani anali kucita miyambo yonyansa ya zaciwelewele. Anali na mahule aamuna ndi aakazi a pakacisi. Cinanso, anali kulekelela khalidwe la mathanyula (kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha), na makhalidwe ena a zaciwelewele, ndipo anali kuwaona monga abwino-bwino. (Deut. 23:17, 18; 1 Maf. 14:24) Akananiwo anali kukhulupilila kuti mwa kucita miyambo imeneyi, anali kusonkhezela milungu yawo kudalitsa nthaka. Aisiraeli ambili anakopeka na miyambo yaciwelewele imeneyi, moti anayamba kulambila milungu yonama. M’ceni-ceni, iwo anagwidwa ngati nyama na Satana.

9. Malinga ndi Hoseya 2:16, 17, kodi Satana anapangitsa bwanji Aisiraeli kuona kuti palibe kusiyana pakati pa Yehova na Baala?

9 Palinso njila yacitatu imene Satana anaseŵenzetsa kuti asoceletse Aisiraeli. Anawapangitsa kuona kuti palibe kusiyana pakati pa kulambila Yehova na kulambila Baala. M’masiku a mneneli Yeremiya, Yehova anakamba kuti aneneli onama anacititsa anthu ake kuiŵala dzina lake “cifukwa ca Baala.” (Yer. 23:27) Cioneka kuti pa nthawiyo Aisiraeli analeka kuseŵenzetsa dzina la Yehova, na kuyamba kuseŵenzetsa dzina lakuti Baala, limene litanthauza kuti “Mwiniwake” kapena kuti “Mbuye.” Kucita zimenezi, kunapangitsa kuti Aisiraeli aziona kuti palibe kusiyana pakati pa Yehova na Baala. Ndipo izi zinacititsa kuti iwo ayambe kusakaniza miyambo yolambila Baala na kulambila Yehova.—Ŵelengani Hoseya 2:16, 17, na mawu a munsi.

MACENJELA A SATANA MASIKU ANO

10. Ni macenjela otani amene Satana amaseŵenzetsa masiku ano?

10 Macenjela a Satana sanasinthe. Mofanana ndi nthawi ya Aisiraeli, iye amakola anthu mwa kuwakopa na zinthu zabwino-bwino zimene amalakalaka. Cina, amawasonkhezela kucita ciwelewele. Komanso, amawapangitsa kuona kuti palibe kusiyana pakati pa Yehova na milungu yonama. Tsopano tiyeni tikambilane macenjela atatu amenewa, kuyambila na mbali yotsilizila.

11. Kodi Satana wapangitsa bwanji kuti anthu asam’dziŵe bwino Yehova?

11 Satana amapangitsa anthu kuona kuti palibe kusiyana pakati pa Yehova na milungu yonama. Atumwi onse a Yesu atafa, Akhristu ampatuko anayamba kufalitsa ziphunzitso zabodza. (Mac. 20:29, 30; 2 Ates. 2:3) Zimene ampatuko amenewo anacita zinapangitsa kuti anthu asadziŵe Mulungu woona. Mwacitsanzo, anacotsa dzina la Mulungu m’Mabaibo awo, na kuikamo maina ena monga lakuti “Ambuye.” Kucotsa dzina la Mulungu m’Baibo na kuikamo dzina lakuti “Ambuye,” kunapangitsa kuti cikhale covuta kwa anthu oŵelenga Baibo kusiyanitsa pakati pa Yehova ndi “ambuye” ena ochulidwa m’Malemba. (1 Akor. 8:5) Cinanso, m’Mabaibo awo, anaseŵenzetsa dzina limodzi-modzi lakuti “Ambuye” pochula Yehova na Yesu. Izi zinapangitsa kuti cikhale covuta kwa anthu kudziŵa kuti Yehova na Mwana wake ni anthu aŵili osiyana, okhalanso na maudindo osiyana. (Yoh. 17:3) Msokonezo umenewu ni umene unapangitsa kuti payambike ciphunzitso ca Utatu. Ciphunzitso cimeneci si ca m’Malemba. Zotulukapo zake n’zakuti anthu ambili amaona kuti Mulungu ni wosamvetsetseka, ndipo sitingathe kumudziŵa bwino. Kodi si bodza lam’kunkhuniza limeneli?—Mac. 17:27.

Cikwangwani coitanila anthu ku chechi imene imalola khalidwe logonana amuna kapena akazi okha-okha

Kodi Satana waseŵenzetsa bwanji cipembedzo conama posonkhezela anthu kucita ciwelewele? (Onani ndime 12)c

12. Kodi cipembedzo conama cimalimbikitsa ciani? Malinga n’zimene Aroma 1:28-31 imakamba, kodi zotulukapo zake zakhala zotani?

12 Satana amasonkhezela anthu kucita ciwelewele. M’nthawi ya Aisiraeli, Satana anaseŵenzetsa cipembedzo conama posonkhezela Aisiraeli kucita ciwelewele. Masiku anonso, Satana amacita cimodzi-modzi. Cipembedzo conama cimalekelela khalidwe laciwelewele, ndiponso cimapangitsa anthu kuona khalidweli monga labwino-bwino. Pa cifukwa ici, anthu ambili amene amadzinenela kuti ni atumiki a Mulungu, satsatilanso mfundo zake zolungama za makhalidwe abwino. M’kalata yopita kwa Aroma, mtumwi Paulo anafotokoza zotulukapo zoipa zimene zakhalapo cifukwa cakuti cipembedzo conama cimalekelela khalidwe la ciwelewele. (Ŵelengani Aroma 1:28-31.) Zina mwa ‘zinthu zosayenela’ zochulidwa pa lembali ni ciwelewele camtundu uliwonse, kuphatikizapo mathanyula. (Aroma 1:24-27, 32; Chiv. 2:20) Conco, n’zoonekelatu kuti kutsatila mfundo za m’Baibo n’kofunika kwambili.

13. Ni njila ina iti ya macenjela imene Satana amaseŵenzetsa?

13 Satana amakopa anthu na zinthu zabwino-bwino zimene iwo amalakalaka. Aliyense wa ife amafuna kuphunzila maluso ena ake amene angamuthandize kupeza zofunikila mu umoyo wake ndi wa banja lake. (1 Tim. 5:8) Kuti tipeze maluso amenewa, kaŵili-kaŵili timafunika kupita ku sukulu komanso kuphunzila mwakhama. Koma tifunika kukhala osamala cifukwa cakuti, kuwonjezela pa maluso, m’maiko ambili anthu ku sukulu amaphunzitsidwanso nzelu za dziko. Mwacitsanzo, amaphunzitsidwa mfundo zimene zimawapangitsa kuti azikayikila zoti kuli Mulungu, komanso kuti asamalemekeze Baibo. Amauzidwa kuti ciphunzitso ca cisanduliko cokha n’cimene cimafotokoza zoona ponena za ciyambi ca moyo. (Aroma 1:21-23) Ziphunzitso zimenezi, n’zosagwilizana ndi nzelu za Mulungu.—1 Akor. 1:19-21; 3:18-20.

14. Kodi kuyendela nzelu za dziko kumasonkhezela anthu kucita ciani?

14 Anthu amene amayendela nzelu za dziko amanyalanyaza mfundo zolungama za Yehova, ngakhale kuzitsutsa kumene. Kuyendela nzelu za dziko, kumasonkhezela anthu kucita “nchito za thupi.” Sikuwalimbikitsa kukhala na makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala. (Agal. 5:19-23) Kumasonkhezela anthu kukhala onyada, odzikuza, ndi “odzikonda.” (2 Tim. 3:2-4) Koma Mulungu safuna kuti atumiki ake akhale na makhalidwe amenewa. M’malomwake, amafuna kuti akhale ofatsa ndi odzicepetsa. (2 Sam. 22:28) Akhristu ena amene anacita maphunzilo a ku yunivesite, anatengela nzelu za dziko m’malo motengela nzelu za Mulungu. Tiyeni tikambilaneko citsanzo cimodzi coonetsa zimene zingacitike ngati tinyalanyaza macenjezo amenewa okhudza kucita maphunzilo a ku yunivesite.

Mlongo wacitsikana amene aphunzila pa yunivesite, wayamba kukhulupilila maganizo a mphunzitsi wake. Ndiyeno, pamene ali ku misonkhano, mlongoyo wayamba kusuliza zimene akuphunzila.

Kodi nzelu za dziko zingapotoze bwanji maganizo athu? (Onani ndime 14-16)d

15-16. Kodi mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca mlongo wina amene anacita maphunzilo a ku yunivesite?

15 Mlongo wina amene watumikila mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 15, anati: “Monga Mboni yobatizika, n’nali n’taŵelenga na kumvetsela nkhani zofotokoza ngozi imene imakhalapo ngati Mkhristu acita maphunzilo a ku yunivesite. Koma n’nanyalanyaza uphungu umenewo. N’nali kuona kuti macenjezowo sanali kunikhudza.” Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Mlongoyo anati: “Kuŵelenga za ku sukulu kunali kuniwonongela nthawi na mphamvu zoculuka, cakuti sin’nali kupeza nthawi yopemphela kwa Yehova ngati mmene n’nali kucitila poyamba. N’nali kukhalanso wolema kwambili cakuti sin’nali kukwanitsa kulalikila na kukonzekela misonkhano. N’tazindikila kuti kucita maphunzilo apamwamba kukusokoneza ubale wanga na Yehova, n’naona kuti nifunika kuleka maphunzilowo, ndipo n’zimene n’nacita.”

16 Kodi maphunzilo a ku yunivesite anakhudza bwanji maganizo a mlongoyo? Iye anati: “Maphunzilo a ku yunivesite anapangitsa kuti nizikonda kupeza ena zifukwa, maka-maka abale na alongo. N’nayamba kuyembekezela zambili kwa iwo, ndiponso n’nali kudzipatula. Zinanitengela nthawi yaitali kuti nisinthe makhalidwe amenewa. Zimene zinacitikazo zinanithandiza kuona ngozi yaikulu imene imakhalapo, ngati tinyalanyaza macenjezo amene Atate wathu wakumwamba amatipatsa kupitila m’gulu lake. Yehova anali kunidziŵa bwino kuposa mmene n’nali kudzidziŵila ine mwini. Ndipo nikanacita bwino kumumvela.”

17. (a) Kodi sitiyenela kulola ciani? (b) Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

17 Conco, musalole kuti Satana akugwileni ngati nyama “mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake” ca dzikoli. Musalole kuti akusoceletseni. (1 Akor. 3:18; 2 Akor. 2:11) Cinanso, musalole kuti iye akucititseni kuiŵala Yehova komanso mmene tiyenela kumulambilila. Muzitsatila miyezo yapamwamba ya Yehova ya makhalidwe abwino. Kuwonjezela apo, musalole kuti Satana akucititseni kunyalanyaza malangizo a Yehova. Koma bwanji ngati mwaona kuti munayamba kale kutengela maganizo a dziko? Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene Mawu a Mulungu angatithandizile kuthetsa maganizo olakwika na zizoloŵezi zoipa zimene tingakhale nazo, ngakhale ‘zozikika molimba.’—2 Akor. 10:4, 5.

NI MACENJELA OTANI AMENE SATANA AMASEŴENZETSA . . .

  • pofuna kupangitsa kuti anthu asam’dziŵe bwino Yehova?

  • posonkhezela anthu kucita ciwelewele?

  • pokopa anthu na zinthu zabwino-bwino zimene amafuna?

NYIMBO 49 Tikondweletse Mtima wa Yehova

a Satana ni katswili posoceletsa anthu. Iye wasoceletsa anthu ambili mwa kuwapangitsa kuona kuti ali pa ufulu, pamene m’ceni-ceni wawagwila kukhala akapolo ake. M’nkhani ino, tidzakambilana macenjela angapo amene Satana amaseŵenzetsa posoceletsa anthu.

b MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Aisiraeli ayamba kugwilizana ndi Akanani, ndipo Akananiwo akuwanyengelela kuti azilambila Baala na kucita ciwelewele.

c MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Cikwangwani coitanila anthu ku chechi imene imalola khalidwe logonana amuna kapena akazi okha-okha.

d MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mlongo wacitsikana akuphunzila ku yunivesite. Iye na anzake a m’kilasi ayamba kukhulupilila zimene mphunzitsi wawo akukamba, zakuti sayansi ingathetse mavuto onse a anthu. Ndiyeno, pamene ali ku misonkhano, mlongoyo wayamba kusuliza zimene akuphunzila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani