Ndandanda ya Mlungu wa November 26
MLUNGU WA NOVEMBER 26
Nyimbo 62 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 15, bokosi patsamba 121 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Mika 1-7 (Mph. 10)
Na. 1: Mika 3:1-12 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi N’ciani Cikusonyeza Kuti Paladaiso Wochulidwa pa Luka 23:43 Adzakhala Padziko Lapansi Pompano?—rs tsa. 338 ndime 2-tsa. 339 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Timadziŵa Bwanji Kuti Yehova Ndi Wakumva Pemphelo?—1Yoh. 5:14 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 56
Mph. 5: Yambitsani Phunzilo la Baibo pa Ciŵelu Coyamba. Mwa kugwilitsila nchito ulaliki wacitsanzo uli patsamba 4, onetsani mmene tingayambitsile phunzilo pa Ciŵelu coyamba mu December. Limbikitsani onse kutengako mbali.
Mph. 10: Zoculuka Zao Zinathandizila Osowa. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya November 15, 2012 masamba 8-9.
Mph. 15: “Mungakwanitse—Ngakhale Muli ndi Zocita Zambili.” Mafunso ndi mayankho. Kambilananinso mwacidule ndi wofalitsa amene amatsogoza maphunzilo ngakhale kuti ali ndi zocita zambili.
Nyimbo 73 ndi Pemphelo