Mungakwanitse—Ngakhale Muli ndi Zocita Zambili
1. Kodi ena amazengeleza kuyambitsa phunzilo la Baibo cifukwa ciani?
1 Ena amazengeleza kuyambitsa maphunzilo a Baibo cifukwa ndi otangwanika kwambili. Kusamalila wophunzila Baibo kumafuna nthawi; nthawi yokonzekela phunzilo, kulitsogoza, ndi kuthandizila wophunzilayo pa zothetsa nzelu za kuuzimu. Mtumwi Paulo anati anapeleka moyo wake kuthandiza anthu a ku Tesalonika kuti adziŵe Yehova. (1 Ates. 2:7, 8) Kodi tingacite ciani kuti tizitsogoza maphunzilo a Baibo ngakhale pamene tili otangwanika?
2. Ngati timam’kondadi Yehova, kodi nthawi yathu tidzaigwilitsila nchito motani?
2 Kulambila Kumalila Nthawi: Mfundo yosakanika ndi yakuti kulambila kumafuna nthawi. Mwacitsanzo, timapatula nthawi yokasonkhana, kulalikila, kuŵelenga Baibo, ndi kupemphela. Munthu wokonda mkazi wake kapena mwamuna wake salephela kupatula nthawi yoceza naye ngakhale kuti ndi wotangwanika. Kuli bwanji ndi kuombola nthawi kuti tilambile Yehova cifukwa timam’konda? (Aef. 5:15-17; 1 Yoh. 5:3) Malinga n’kunena kwa Yesu, nchito yopanga ophunzila ndi mbali yofunika kwambili pa kulambila kwathu. (Mat. 28:19, 20) Tikamakumbukila zimenezi, sitidzaopa udindo wathu wotsogoza maphunzilo a Baibo.
3. Kodi tingasamalile bwanji phunzilo la Baibo ngakhale ngati pali zododometsa utumiki wathu?
3 Nanga bwanji ngati nthawi imaticepela cifukwa ca nchito, kudwala-dwala, kapena nchito zina zaumulungu? Ofalitsa ena amene amayenda-yenda amatsogoza maphunzilo a Baibo pafoni, kapena mwa kukambilana pakompyuta. Amene ali ndi vuto la kudwala-dwala amakonza zakuti wophunzila wao azibwela kuti aziphunzilila kunyumba kwao. Enanso amalinganiza zakuti wofalitsa wina wodalilika aziwatsogozelako phunzilo pamene io sangathe.
4. Ndi madalitso ati amene timapeza tikamatsogoza maphunzilo a Baibo?
4 Paulo anasangalala kwambili kutaila nthawi yake ndi mphamvu zake kuthandiza ena kuphunzila coonadi. (Mac. 20:35) Iye pokumbukila anthu amene anawathandiza ku Tesalonika, anali kuyamikila Yehova. (1 Ates. 1:2) Tidzasangalala ndipo tidzakhutila kwambili ndi utumiki wathu tikapanda kulola zocita zina kutilepheletsa kutsogoza maphunzilo a Baibo.