Ndandanda ya Mlungu wa December 3
MLUNGU WA DECEMBER 3
Nyimbo 128 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 15, ndime 13-20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Nahumu1–Habakuku 3 (Mph. 10)
Na. 1: Habakuku 2:1-14 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulalikila za Coonadi Mopanda Mantha?—2 Tim. 1:7, 8 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingakhale Bwanji Odziŵa Zinthu Ndiponso Anzelu?—rs tsa. 136 ndime 1-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 106
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu December. Nkhani yokambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pankhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lokopa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani!, komanso ngati nthawi ilola citaninso mofananamo ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Zocitika Pogaŵila Tumapepala Tauthenga. Nkhani yokambidwa ndi Woyang’anila Nchito. Pemphani omvela kuti asimbe zocitika zimene anasangalala nazo pogaŵila tumapepala tauthenga mu November. Ofalitsa aŵili amene anasangalala kugaŵila tumapepalato aonetse mmene anacitila potugaŵila kunyumba ndi nyumba.
Nyimbo 96 ndi Pemphelo