Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa December 31, 2012. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.
1. Kodi ulosi wa pa Yoweli 2:1-10, 28 wonena za tizilombo timene tinaloŵa m’dziko ukukwanilitsidwa bwanji? [Nov. 5, w07 10/1 tsa. 13 ndime 1]
2. Kodi tikuphunzila ciani pa uthenga wa Amosi wopita kwa Aisiraeli, Ayuda komanso anthu oyandikana nao, umene uli pa Amosi 5:4, 6 ndi 14? [Nov. 12, w07 10/1 tsa. 15 ndime 3]
3. Kodi zikuoneka kuti n’ciani cinacitsa Aedomu kuti akhale ndi mtima wonyada, ndipo ifeyo sitikuyenela kuiŵala mfundo iti? (Obadiya 3, 4) [Nov. 19, w07 11/1 p. 14 ndime 1]
4. Kodi Yehova anasintha bwanji maganizo ake pa nkhani ya tsoka limene ananena kuti ligwela anthu a ku Nineve? (Yona 3:8, 10) [Nov. 19, w07 11/1 tsa. 15 ndime 1]
5. Malinga ndi mau opezeka pa Yona 4:11, n’cifukwa ciani tiyenela kulalikila uthenga wabwino mwakhama komanso mwacifundo? [Nov. 26, w07 11/1 tsa. 15 ndime 2]
6. Kodi kukwanilitsidwa kwa ulosi umene uli pa Nahumu 2:6-10 kukutilimbikitsa bwanji? [Dec. 3, w07 11/15 tsa. 9 ndime 2; w88 2/15 tsa. 28 ndime 7]
7. Kodi lemba la Hagai 1:6 likutanthauza ciani, ndipo ifeyo tikuphunzilapo ciani? [Dec. 10, w06 4/15 tsa. 22 ndime 12-15]
8. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji malangizo othandiza amene ali pa Zekariya 7:10, akuti “musamakonzelane ciwembu mumtima mwanu”? [Dec. 17, jd-E tsa. 113 ndime 6; w07 12/1 tsa 11 ndime 3]
9. N’cifukwa ciani mau opezeka pa lemba la Zekariya 4:6, 7 ndi olimbikitsa kwa anthu amene akulambila Yehova masiku ano? [Dec. 17, w07 12/1 p. 11 tsa. 1]
10. Malinga ndi zimene zili pa lemba la Malaki 3:16, n’cifukwa ciani sitiyenela kufooka pamene tikuyesetsa kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu? [Dec. 31, w07 12/15 tsa. 29 ndime. 3]