Nkhani Yatsopano Imene Izipezeka mu Nsanja ya Olonda
Pa Ciŵelu coyamba ca mwezi uliwonse, takhala tikugwilitsila nchito nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yakuti “Phunzilani Zimene Mau a Mulungu Amanena,” poyambitsa maphunzilo a Baibo. Koma kuyambila mu January, nkhani imeneyi idzaloŵedwa m’malo ndi nkhani yakuti “Mafunso a m’Baibo Ayankhidwa,” imene idzayamba kupezeka patsamba lothela la Nsanja ya Olonda yogaŵila. Tingagwilitsile nchito nkhani yakuti “Mafunso a m’Baibo Ayankhidwa” mu ulaliki monga mmene tinali kugwilitsila nchito nkhani yakuti, “Phunzilani Zimene Mau a Mulungu Amanena.” (km 12/10 tsa. 2) Monga zinalili kale, Utumiki Wathu wa Ufumu uzikhala ndi ulaliki wacitsanzo umene tingagwilitsile nchito pa Ciŵelu coyamba ca mwezi.