LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 11/13 tsa. 3
  • Nkhani Zothandiza mu Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Nkhani Zothandiza mu Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Nkhani Yatsopano Imene Izipezeka mu Nsanja ya Olonda
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Mfundo Yothandiza Yokhudza Webusaiti Yathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Nkhani Zimene Si Zophunzila mu Nsanja ya Mlonda
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 11/13 tsa. 3

Nkhani Zothandiza mu Ulaliki

1. Kodi nkhani zakuti, “Kuceza ndi Mnzathu” zili ndi zolinga ziŵili ziti?

1 Nthawi ndi nthawi, Nsanja ya Mlonda yogaŵila imakhala ndi nkhani yakuti: “Kuceza ndi Mnzathu.” Nkhani zimenezi zili ndi zolinga ziŵili. Coyamba ndi kufotokoza ziphunzitso za m’Baibo m’njila yokopa, ndipo caciŵili ndi kutionetsa mmene tingafotokozele nkhani zina momveka. (1 Pet. 3:15) Kodi nkhani zimenezi tingazigwilitsile nchito bwino motani?

2. Kodi nkhani zimenezi tingaziseŵenzetse bwanji mu ulaliki?

2 Ziseŵenzetseni mu Ulaliki: Mungasunge Nsanja za Mlonda zina zimene zili ndi nkhani zimenezi. Mwininyumba, munthu wacidwi, kapena wophunzila Baibo akakufunsani funso logwilizana ndi nkhani zimenezi, mungam’patse Nsanja ya Mlonda imene ili ndi nkhani yogwilizana ndi zimene wafunsa ndi kukambilana naye. Ngati mulibe kope la Nsanja ya Mlonda imene ili ndi nkhani imene wafunsa, mungatenge nkhaniyo pa jw.org.

3. Kodi tingakambitsilane bwanji nkhani zimenezi ndi mwininyumba?

3 Kodi mungakambilane motani nkhani zimenezi ndi munthu wina? Ofalitsa ena amapempha munthu amene akambilana naye kuti aŵelenge mokweza mbali ya Mnzathu, pamene io aŵelenga mbali ya Mboni. Njila imeneyi imakhala yothandiza cifukwa imalola munthu kupenda zikhulupililo zathu popanda kutsutsa.—Deut. 32:2.

4. Kodi tingadziphunzitse motani ndi nkhani zimenezi?

4 Dziphunzitseni ndi Kuphunzitsa ena: Pamene muŵelenga nkhani zimenezi, onani mmene malemba, zitsanzo ndi mfundo zazikulu zikufotokozedwela. Onaninso mzimu wa nkhani zimenezi. Ndiyeno yesani kucita zimenezo pamene muli mu ulaliki. (Miy. 1:5; 9:9) Mlongo wina analemba kuti: “Kuŵelenga nkhani zimenezi kuli monga ukuphunzila kwa mpainiya waluso amene akufotokoza zinthu momveka.”

5. Kodi tingawathandizile bwanji ophunzila Baibo athu kukonzekela ulaliki?

5 Mungagwilitsilenso nchito zitsanzo zolembedwa zimenezi kuthandiza ophunzila Baibo anu kukonzekela ulaliki? Ŵelengeni nkhani zimenezi pamodzi, ndipo pemphani wophunzila wanu kuti acite mbali ya wofalitsa. Kucita zimenezi kudzathandiza wophunzila Baibo kufotokoza mwaluso zimene amakhulupilila. (Akol. 4:6) Nkhani zimenezi ndi imodzi mwa njila zambili mmene Yehova amatithandizila kuti ‘tikwanilitse mbali zonse’ za utumiki wathu.—2 Tim. 4:5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani