Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu January
“Tifuna kumvako maganizo anu. Kodi dzina la Mulungu ndani? [Yembekezani yankho.] Onani zimene magazini iyi ikamba.” M’patseni Nsanja ya Olonda ya January 1, ndi kumuonetsa nkhani ili patsamba lothela kucikuto. Ndiyeno kambilanani naye mfundo zili pakamutu koyamba ndipo ŵelengani naye lemba ngakhale limodzi pa malembawo. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye funso lotsatila.
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova January 1
“Anthu ambili amakamba za kutha kwa dziko. Kodi muganiza kuti tiyenela kuopa mapeto a dziko? [Yembekezani yankho.] Malinga ndi lemba ili, anthu ena adzapulumuka. [Ŵelengani 1 Yohane 2:17.] Magazini iyi ili ndi mayankho a m’Baibo a mafunso anai amene anthu ambili amafunsa ponena za mapeto a dziko.”
Awake! January
“Ticezela mabanja kuti tigaŵane nao mfundo zothandiza. Kodi muganiza n’kofunika kuti mabanja azitsatila mau a Yesu a pa lembali? [Ŵelengani Macitidwe 20:35b. Ndiyeno yembekezani yankho.] Kuphunzitsa ana kuti akhale osadzikonda n’kovuta kwambili cifukwa anthu ambili m’dziko ndi odzikonda. Magazini iyi ifotokoza njila zothandiza zimene makolo angagwilitsile nchito pophunzitsa ana ao kuti aziganizila anzao.”