Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu December
“Anthu ambili amayembekezela kubwelenso kwa Yesu. Tinene kuti Yesu wabwela, kodi n’ciani cimene mungafune kuti iye acite?” Yembekezelani ayankhe. Muonetseni tsamba lothela la Nsanja ya Mlonda ya December 1. Ndiyeno kambilanani naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndi kuŵelenga naye lemba limodzi kapena aŵili osagwidwa mau. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda December 1
“Umoyo wavuta masiku ano cakuti nthawi zina tingamuiŵale Mulungu. Kodi muganiza n’kofunika kuika Mulungu patsogolo mu umoyo wathu? [Yembekezani ayankhe.] Pa ulaliki wake wochuka wa paphili, Yesu anakamba kuti timafunikila zinthu za kuuzimu kuti tikhale odala. [Ŵelengani Mateyu 5:3.] Magazini iyi ifotokoza zifukwa zitatu zimene zionetsa cifukwa cake Mulungu ndi wofunika kwa ife.”
Galamukani! December
“Ambili a ife timakhulupilila zimene timaŵelenga kapena kumvetsela kwa ofalitsa nkhani. Kodi muganiza kuti nkhani zao zimakhala zolondola ndi zoona? [Yembekezani ayankhe.] Baibo imatiuza kuti tiyenela kusamala ndi nkhani zimene timamvela. [Ŵelengani Yobu 12:11.] Magazini iyi ifotokoza njila zina zimene zingatithandize kutsimikiza ngati zimene timvetsela ndi kuŵelenga n’zoona.”