Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu December
“Tikukambilana mwacidule ndi anthu za boma labwino. Kodi muganiza kuti pali boma limene lingathetse mavuto monga ciwawa ndi kupanda cilungamo?” Yembekezani ayankhe. Kumbutsani mwininyumba kuti m’Pemphelo la Ambuye, Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti boma labwino libwele. Boma limenelo ndi Ufumu wa Mulungu. Muonetseni kumbuyo kwa Nsanja ya Mlonda ya November-December ndi kukambilana nkhani imene ili pansi pa funso loyamba ndi kuŵelenga naye lemba limodzi losagwidwa mau. Kenako mugaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.
Nsanja ya Mlonda November–December
“Kodi muganiza kuti anthu adzaononga dziko lapansi kothelatu? [Yembekezani ayankhe.] Ngakhale kuti anthu sangakwanitse kukonza zimene io aononga padzikoli, Baibulo limanena kuti Mulungu adzakonza ndipo amafunitsitsa kucita zimenezo. Onani mau olimbikikitsa awa opezeka pa Salimo 65:9. [Ŵelengani.] Magazini iyi ya Nsanja ya Mlonda ikufotokoza mmene Mulungu adzakonzela zinthu padzikoli ndi zimene ifeyo tiyenela kucita kuti tidzalandile madalitso mtsogolo pano padziko lapansi. Kodi ndingakusiileni magaziniyi?”
Galamukani! December
“Tikuceza ndi anansi athu mwacidule cifukwa ca nkhawa imene anthu ali nayo pa matenda a maganizo amene afala. Malinga ndi kunena kwa bungwe lowona zaumoyo pa dziko lonse, munthu mmodzi pa anthu anai alionse amavutika ndi matenda amenewa. Kodi muganiza kuti matenda a maganizo akufala kwambili? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatipatsa ciyembekezo cakuti, moyo mtsogolo udzakhala wopanda matenda kapena zopweteka zilizonse. [Ŵelengani Civumbulutso 21:3, 4.] Magazini iyi ifotokoza zinthu zocepa zimene aliyense ayenela kudziŵa pa nkhani ya matenda a maganizo.”