LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 10/12 tsa. 8
  • Maulaliki Acitsanzo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maulaliki Acitsanzo
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Zofanana
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
km 10/12 tsa. 8

Maulaliki Acitsanzo

Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelo Coyamba mu November

“Ife tonse timafuna boma loyendetsa bwino zinthu. M’kuona kwanu, kodi ndi boma la mtundu wanji limene lingathetse mavuto onse a anthu? [Yembekezani yankho.] Onani zimene magazini iyi ikamba.” M’patseni Nsanja ya Olonda ya November 1, ndi kukambilana mfundo zimene zili pa kamutu koyamba patsamba 16, ndipo ŵelengani naye lemba ngakhale limodzi pa malembawo. M’gaŵileni magaziniyo, kenako panganani naye zokabwelanso kuti mudzakambilane funso lotsatila.

Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova November 1

“Tifuna kumvako maganizo anu. Ngati mungapatsidwe mwai wofunsa Mulungu funso limodzi, kodi mungam’funse ciani? [Yembekezani yankho.] Yesu anaonetsa kuti n’koyenela kufuna-funa mayankho pa mafunso athu ocokela pansi pa mtima. [Ŵelengani Mateyu 7:7.] Magazini iyi ili ndi mayankho ocokela m’Baibo pa mafunso atatu awa ofunika kwambili.” Muonetseni mafunso ali pansi pa tsamba 3.

Galamukani! November

“Lelo tikucezela mabanja. Masiku ano mabanja a kholo limodzi awanda kwambili. Kodi munganiza kuti mabanja a kholo limodzi ali ndi mavuto ambili kuposa amene ali ndi makolo aŵili? [Yembekezani yankho.] Makolo ambili apeza uphungu wothandiza m’Baibo. [Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16.] Magazini iyi ili ndi mfundo zimene zingathandize makolo amene ali okha kuti azisamalila bwino mabanja ao.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani