Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu Coyamba mu November
“Onani funso locititsa cidwi ili. [Ŵelengani funso loyamba limene lili kucikuto cothela ca Nsanja ya Mlonda ya November-December.] Kodi muganiza bwanji? [Ŵelengani ndime ziŵili zimene zili pansi pa funso limenelo ndi kuŵelengako lemba limodzi limene sitinaligwile mau.] Kodi ndingadzabwelenso liti kuti tidzakambilane cifukwa cake anthu adzapindula ndi Ufumu wa Mulungu?”
Nsanja ya Mlonda November–December
“Muona bwanji, kodi anthu adzaononga dziko lapansi kothelatu? [Yembekezani yankho] Baibulo limatitsimikizila kuti Mulungu, Mlengi wathu, sadzalola anthu kuononga cilengedwe kothelatu. Onani zimene Baibulo likufotokoza pa Salimo 115:16. [Ŵelengani.] Ndithudi, dziko lapansi ndi ‘mphatso yabwino’ imene atate wathu wakumwamba anatipatsa. [Ŵelengani Yakobo 1:17] Kodi Muganiza kuti Mulungu angatipatse mphatso yabwino koma yosakhalitsa? Kutalitali! Magazini iyi ya mutu wakuti, ‘Kodi Anthu Adzaononga Dziko Lapansi Kothelatu?’ ifotokoza mfundo zina zothandiza. Landilani magaziniyi.”
Galamukani! November
“Aliyense amafuna kukhala wokondwela, koma lelolino anthu ambili alibe cimwemwe. Kodi muganiza kuti ndi ciani cimene cimacititsa munthu kukhala ndi cimwemwe ceniceni? [Yembekezelani ayankhe.] Ine ndaona kuti Baibulo n’lothandiza kwambili kuti munthu akhale ndi cimwemwe. Mwacitsanzo onani mfundo iyi ya m’Baibulo. [Ŵelengani Aheberi 13:5.] Magazini imeneyi ifotokoza mfundo zinai zocokela m’Baibulo zimene zingatithandize kukhala ndi cimwemwe ceniceni.”