Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda September-October
“Mukaona mavuto amene timakumana nao, kodi muganiza kuti mau a Yesu akuti musade nkhawa ndi othandiza? [Ŵelengani Mateyu 6:25, ndipo yembekezani yankho.] Magazini iyi, ifotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zingacepetsele nkhawa zokhudza ndalama, mavuto a m’banja, ndi mavuto aumwini.”
Galamukani! November
“Anthu mamiliyoni padziko lapansi asokonezedwa ndi cinyengo ndiponso ziphunzitso zonama za zipembedzo zosiyanasiyana. Kodi n’ciani cimene cidzacitikila zipembedzo zimenezi? [Yembekezani yankho.] Magazini ino ikufotokoza ulosi wosangalatsa wa m’buku la Chivumbulutso, umene unakambilatu za kucoka m’cipembedzo conyenga ndi mmene cidzaonongedwela.”