Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda November-December
“Kodi munadzifunsapo kuti n’cifukwa ciani timachedwa Mboni za Yehova? [Yembekezani yankho.] Yankho lake tingalipeze m’Baibulo mmene Mulungu amatiuza dzina lake. [Ŵelengani Salimo 83:18.] Monga Mboni za Yehova, timalengeza uthenga wabwino wokhudza Yehova ndi colinga cake kwa anthu. Magazini iyi iyankha mafunso amene anthu amakhala nao okhudza Mboni za Yehova.”
Galamukani! January
“Ndakubweletselani magazini iyi ya Galamukani! ya mwezi uno. [Patsani munthuyo magazini.] Onani funso limene lili pa tsamba 2 komanso mayankho amene alipo. Kodi inu muona bwanji? [Yembekezani yankho.] Magazini iyi itithandiza kuona mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuona zinthu moyenelela pamoyo wathu.”