Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda January–February
“Zioneka kuti kuyambila kalekale, maboma akhala akucita ziphuphu. Kodi muganiza n’cifukwa ciani vuto limeneli silikutha? [Yembekezani ayankhe.] Onani mfundo yocititsa cidwi iyi ya m’Baibulo. [Ŵelengani Mlaliki 7:20.] Magazini iyi ikufotokoza cimene cingathetse ziphuphu malinga ndi zimene Baibulo limanena. Patulani nthawi yakuti muŵelenge magazini imeneyi. Tengani yanu iyi.”
Galamukani! January
“Anthu ambili amakhulupilila kuti moyo unasandulika kucoka ku zinthu zopanda moyo, koma ena amakaikila zimenezi. Kodi inuyo muganiza kuti moyo unayamba bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Pambuyo pofufuza kwa zaka zambili, anthu anapeza kuti n’zosatheka moyo kucokela ku zinthu zopanda moyo. Zimenezi zikugwilizana ndi mfundo yomveka bwino ya m’Baibulo iyi. [Ŵelengani Salimo 36:9.] Magazini iyi ikufotokoza cifukwa cake anthu ambili tsopano amakaikila zakuti moyo unakhalapo cifukwa ca cisanduliko.”