Limbikitsani Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba
Kuyambila mwezi wa May m’caka ca 2011, ofalitsa analimbikitsidwa kuyambitsa maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu coyamba mwezi uliwonse. Kuti tikwanitse kucita zimenezi, pakonzedwa mbali ina mu Nsanja ya Mlonda yakuti “Kuyankha Mafunso a m’Baibo,” mbali imeneyi idzapitiliza kutuluka m’magazini. Conco, pa kukumana kokonzekela ulaliki kumene kumacitika pa Ciŵelu coyamba, muyenela kuonetsa mmene tingagwilitsile nchito mbali imeneyi poyambitsa maphunzilo a Baibo ndipo muyenela kucita citsanzo ca ulaliki.
Akulu angasankhe zakuti kagulu ka ulaliki kalikonse kazikumana pa kokha pa Ciŵelu coyamba, kapena angasankhe zakuti magulu onse aulaliki azikumana pa Nyumba ya Ufumu. Komabe, ngati Nyumba ya Ufumu imagwilitsidwa nchito ndi mipingo yambili, palibe mpingo umene uyenela kusinthila tsiku lapadela limeneli loyambitsa maphunzilo a Baibo pa tsiku lina n’colinga cakuti mukumane pamodzi monga gulu pokonzekela ulaliki.