Ndandanda ya Mlungu wa January 7
MLUNGU WA JANUARY 7, 2013
Nyimbo 104 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 17 ndime 8-14, ndi bokosi patsamba 137 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Mateyu 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 5:21-32 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi N’ciani Cimene Cingapangitse Mapemphelo Kukhala Osavomelezeka Pamaso pa Mulungu?—rs tsamba 340, ndime 7 mpaka tsamba 341, ndime 7 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kupanga Yehova Kukhala “Colowa Canu” Kumatanthauzanji?—Num. 18:20 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 38
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu January. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pankhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lokopa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani!, komanso ngati nthawi ilola citaninso mofananamo ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Nyumba ya Ufumu Yaudongo Imalemekeza Yehova. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Yehova ndi Mulungu woyela, conco anthu ake afunika kukhala aukhondo. (Eks. 30:17-21; 40:30-32) Ngati malo athu olambilila akhala aukhondo ndi okonzedwa bwino, timalemekeza Yehova. (1 Pet. 2:12) Fotokozani cocitika ca kudelalo kapena colembedwa m’zofalitsa cosonyeza mmene Nyumba ya Ufumu yaukhondo inathandizila kucitila umboni m’delalo. Funsani m’bale amene amayang’anila nchito yoyeletsa ndi kusamalila Nyumba ya Ufumu kuti afotokoze makonzedwe amene alipo pa mpingo panu. Limbikitsani onse kuti azithandiza kusamalila Nyumba ya Ufumu.
Nyimbo 127 ndi Pemphelo